Saturday, July 30, 2022

 


LAMULUNGU LA 18 PA CHAKA – C.

(Tipewe khumbo lofuna zinthu zambiri.)

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA; MLALIKI 01: 02; 02: 21 – 23 (Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhawa?)

Zonse nzopanda phindu, akutero Mlaliki. Zonse nzachabechabe! Ndithudi zonse nzopandapake. Paja nthawi zina munthu amene wagwira ntchito zolemetsa mwaluntha, mwanzeru ndi mwaluso, zonsezo ayenera kuzisiyira munthu amene sadakhetserepo konse thukuta, kuti akondwere nazo. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo nzoipa kwambiri. Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhawa zimene amazichita pansi pano? Masiku ake onse amakhala achisoni, ntchito yake imakhala yovuta. Ndi usiku womwe mtima wake supumula. Zimenezinso nzopanda phindu.

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 90: 03 – 06, 12 – 14.

 

Inu Ambuye, ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.

 

Inu mumabwezera anthu ku fumbi,

Ndipo mumati, “bwererani inu ana a anthu,”

Pakuti zaka chikwi chimodzi pamaso panu zili ngati dzulo chabe,

Kapena ngati kamphindi chabe kausiku.

 

Inu Ambuye, ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.

 

Inu mumachotsa moyo wa anthu mwadzidzidzi,

Ali ngati maloto, ali ngati udzu wongotsitsimuka m’mawa,

M’mamawamo umatsitsimuka ndipo umakondwa,

Madzulo umafota ndi kuuma.

 

Inu Ambuye, ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.

 

Tsono tiphunzitseni kuwerenga masiku athu,

Kuti tikhale ndi mtima wanzeru,

Lezani mtima, Inu Chauta,

Nanga mudzatikwiyira mpaka liti?

Achitireni chifundo atumiki anu.

 

Inu Ambuye, ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.

 

Tidzazeni m’mawa mulimonse ndi chikondi chanu chosasinthika,

kuti tizikondwa ndi kusangalala masiku athu onse,

Inu Ambuye, mutikomere mtima, ndipo mudalitse ntchito zonse za manja athu,

 

Inu Ambuye, ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.

--------------------------------------

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKOLOSE; AKOLOSE 03: 01 – 5, 09 – 11. (Ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala.)

Abale, ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano. Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. Khristu ndiye moyo wanu weniweni tsopano, choncho pamene Iye adzaonekerenso, inunso mudzaonekera mu ulemerero pamodzi naye. Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano: Musamauzana mabodza, pakuti mwachita ngati mwavula moyo wanu wakale, pamodzi ndi zochitachita zake zoipa, ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziwe kwenikweni ndi kufanafana naye. M’moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse.

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.

Alleluia, Alleluia – Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; 12: 13 – 21 (Nanga zonse zimene wadzisungirazi zidzakhala za yani?)

Munthu wina pakati pa anthu onse aja adapempha Yesu kuti, “Aphunzitsi, takandiwuzirani m’bale wanga kuti andigawireko chuma chamasiye.” Koma Yesu adati, “munthu iwe, ndani adandipatsa ntchito yokuweruzani kapena kumakugawirani chuma chanu chamasiye?” Atatero adauza anthu aja kuti, “chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.” Tsono Yesu adawaphera fanizo. Adati, “munthu wina wachuma m’munda mwake mudabereka dzinthu dzambiri. Ndiye iye uja adayamba kuganiza kuti, ‘nditani, poti ndilibe mosungira dzinthu dzanga?’ Tsono adati, ‘ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga nkumanga zina zazikulu, ndipo ndidzasungira dzinthu dzanga zonse ndi chuma changa m’menemo. Kenaka ndidzauza mtima wanga kuti, Iwe mtima wanga, uli ndi chuma chambiri chimene chidzakukwanira zaka zambiri. Upumule, uzidya, uzimwa ndi kusangalala!’ Koma Mulungu adamuuza kuti, ‘wopusawe! Usiku womwe uno akulanda moyo wako. Nanga zonse zimene wadzisungirazi zidzakhala za yani?”’ Potsiriza Yesu adati, “zimatero ndi munthu amene amadziwunjikira chuma, koma sali wachuma konse pamaso pa Mulungu.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Friday, July 22, 2022

 



LAMULUNGU LA 17 PA CHAKA – C.

(Ambuye mutiphunzitse kupemphera.) 

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS; GENESIS 18: 20 – 32. (Musapse mtima, Ambuye, tsopano ndifunsanso.)

Tsono Chauta adauza Abrahamu kuti, “pali zolakwa zoopsa zokhudza Sodomu ndi Gomora, ndipo tchimo lao ndi lalikulu kwambiri. Choncho ndikuti nditsikireko kuti ndikaone ngati zolakwa zimene ndamvazo ndi zoona. Ngati si choncho, ndidzadziwa.” Anthu aja adachoka, napita ku Sodomu, koma Abrahamu adatsalira ndi Chauta. Apo Abrahamu adayandikira kwa Chauta namufunsa kuti, “Kodi monga mudzaonongadi anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa? Nanga patakhala kuti pali anthu 50 osachimwa mumzindamo, kodi mudzaonongabe mzinda wonse? Kodi simudzauleka kuti musunge anthu 50 amenewo? Ndithu simudzaononga anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa. Chimenechi nchosatheka ndipo simungachite. Mukadatero bwenzi anthu osachimwa akulangidwira kumodzi ndi ochima. Kutalitali, Inu simungachite zotere! Kodi Muweruzi wa dziko lonse lapansi nkupanda chilungamo?” Chauta adayankha kuti, “ndikapeza anthu 50 osachimwa m’Sodomu, ndidzauleka mzinda wonsewo osauwononga, chifukwa cha anthu 50 amenewo.” Abrahamu adalankhulanso, adati, “chonde, ndalimba mtima pakulankhula nanu chotere, Ambuye. Inetu ndine munthu chabe pamaso panu. Nanga pa chiwerengero cha 50 pakangoperewera anthu asanu okha, bwanji? Kodi mudzaononga mzindawo popeza kuti asowa asanu okha?” Chauta adayankha kuti, “ndikapeza anthu 45 olungama, sindidzaononga mzindawo. Abrahamu adafunsanso kuti, “nanga pakapezeka anthu olungama 40 okha?” Chauta adayankha kuti, “ndikapeza anthu 40, sindidzauwononga.” Apo Abrahamu adati, “chonde ndapota nanu, musapse mtima, Ambuye, tsopano ndifunsanso. Nanga mutapezeka anthu olungama 30?” Chauta adati, “ndikapeza anthu 30, sindidzauwononga.” Tsono Abrahamu adati, “ndapota nanu, khululukireni kulimba mtima chotere polankhula ndi Inu Ambuye. Nanga mutapezeka olungama 20?” Chauta adati, “ndikapeza anthu olungama 20, sindidzauwononga mzindawo.” Abrahamu adati, “chonde, musandikwiyire Ambuye, koma ndilankhule kamodzi kokhaka. Nanga mutapezeka khumi okha?” Aponso Chauta adati, “ndikapeza olungama khumi, sindidzauwononga mzindawo.”

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 138: 01 – 03, 06 – 08.

Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, Ambuye.

 

Ndikukuthokozani Inu Chauta ndi mtima wanga wonse,

Ndikuimba nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu,

Ndikugwada mowerama, kumaso kwa Nyumba yanu yoyera.

 

Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, Ambuye.

 

Ndikutamanda dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika,

Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha,

Mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.

 

Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, Ambuye.

 

Ngakhale Chauta ndi wamphamvu, amasamalira anthu otsika,

Koma anthu odzikuza amawadziwira chapatali,

Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto,

Inu mumasunga moyo wanga.

 

Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, Ambuye.

 

Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya,

Dzanja lanu lamanja limandipulumutsa,

Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya,

Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.


Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, Ambuye.

--------------------------------------

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKOLOSE; AKOLOSE 02: 12 – 14. (Mulungu wakupatsani moyo pamodzi ndi Khristu. Adatikhululukira machimo athu onse.)

Abale, pamene mudabatizidwa, mudachita ngati kuikidwa m’manda pamodzi ndi Khristu. Ndipo ndi ubatizowo mudaukitsidwanso pamodzi naye, pakukhulupirira mphamvu za Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa. Inu kale munali akufa chifukwa cha machimo anu, ndiponso chifukwa munali osaumbalidwa mu mtima. Koma tsopano Mulungu wakupatsani moyo pamodzi ndi Khristu. Adatikhululukira machimo athu onse. Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.

Alleluia, Alleluia – Mzimu amene mudalandira amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, timati, “Abba! Atate!”. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAWU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 11: 01 – 13 (Funsani ndipo mudzapatsidwa.)

Nthawi ina Yesu ankapemphera pamalo pena. Pamene adatsiriza, wophunzira wake wina adampempha kuti, “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera, monga Yohane Mbatizi adaphunzitsira ophunzira ake.” Yesu adati, “pamene mukupemphera muziti, ‘Atate, dzina lanu lilemekezedwe. Ufumu wanu udze. Mutipatse ife tsiku lililonse chakudya chathu chamasiku wonse. Mutikhululukire ife machimo athu, pakuti ifenso timakhululukira aliyense wotilakwira. Ndipo musalole kuti tigwe m’zotiyesa.”’ Adawauzanso kuti, “tangoganizani: wina mwa inu ali ndi bwenzi lake, nkupita kunyumba kwake pakati pa usiku, nakamuuza kuti, iwe mnzanga, kodi ungakhale ndi buledi mtatu? Kwafika bwenzi langa, ali pa ulendo, ndipo ndilibe choti ndingampatse. Koma wam’nyumbayo nkuyankha kuti, ‘usandivute, ndatseka kale pa khomo, ndipo ine ndi ana anga tagona, sindingadzukenso kuti ndikupatse bulediyo.’ Ndithu ndikunenetsa kuti adzauka nkumupatsa, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha khama la wopempha uja. Ndipo adzampatsa zonse zimene akusowa. Motero ndikukuuzani kuti, pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani, ndipo adzakutsekulirani. Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira, amene amafunafuna, ndiye amapeza, ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira. Ndani mwa atatenu, mwana wake atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka? Kapena atampempha dzira, iye nkumupatsa chinkhanira? Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Friday, July 15, 2022

 

LAMULUNGU LA 16 PA CHAKA – C.

(Tizimva mau a Mulungu ndi mtima wotsekuka.)

 

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS; GENESIS 18: 01 – 10. (Mbuyanga, chonde musapitirire pakhomo pa mtumiki wanu.)

Chauta adaonekera Abrahamu ku mitengo ya thundu ya ku Mamure ija. Abrahamuyo atakhala pa khomo la hema lake nthawi yamasana kutatentha, mwadzidzidzi adangoona anthu atatu ataimirira potero. Atangowaona, adanyamuka mwamsanga kukawalonjera. Adaweramitsa mutu, nati, “Mbuyanga, ngati ndapeza kuyanja pamaso panu, chonde musapitirire pakhomo pa mtumiki wanu. Ndikupatseni madzi kuti mutsuke mapazi. Mungathe kubapuma patsinde pa mtengo pano. Ine tsopano ndikatenga chakudya, kuti mukadya mupeze mphamvu zopitirizira ulendo wanu. Mwabwera pakhomo panga pano, motero ndiyenera kukutumikirani.” Anthuwo adayankha kuti, “Chabwino, uchite monga waneneramo. Abrahamu adalowa msangamsanga m’hema, nauza Sara kuti, “utenge msanga nsengwa zitatu za ufa wosalala, uukande ndi kupanga buledi.” Pamenepo Abrahamu adathamanga nakatenga mwanawang’ombe wonenepa, nampereka kwa wantchito kuti akonze mwamsanga. Kenaka adatenga chambiko ndi mkaka wokama chatsopano, ndi nyama yokonzakonza ija nawapatsa zonsezo. Iye adakhala potero pamene anthuwo analikudya patsinde pa mtengo. Tsono anthuwo adafunsa Abrahamu kuti, “kodi mkazi wako Sara ali kuti?” Abrahamu adayankha kuti, “ali m’hemamu.” Chauta adati, “Ndikukulonjeza kuti pakapita miyezi isanu ndi inai ndidzabweranso, ndipo mkazi wako adzakhala ali ndi mwana wamwamuna.”

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 15: 02 – 05.

Anthu olungama adzayenda pamaso pa Mulungu.

Inu Chauta, kodi ndani angathe kukhala m'Nyumba mwanu?

Ndani angathe kukhala pa phiri lanu loyera?

Ndi munthu amene amayenda mosalakwa,

Amene amachita zolungama nthawi zonse,

Amene amalankhula zinthu ndi mtima woona.

Anthu olungama adzayenda pamaso pa Mulungu.

Ndi amene sasinjirira ndipo sachita anzake zoipa,

Kapena kumafalitsa mbiri yoipa ya anzake.

Ndi amene amanyoza munthu womkana Mulungu.

Koma amalemekeza anthu omvera Chauta.

Anthu olungama adzayenda pamaso pa Mulungu.

Ndi amene amachitadi zimene walonjeza,

Ngakhale zikhale zowawa chotani.

Ndi amene sakongoza ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja,

Amene salandira chiphuphu kuti azunze munthu wosalakwa.

Munthu wochita zimenezi, palibe chilichonse chimene chidzamgwedeze.

Anthu olungama adzayenda pamaso pa Mulungu.

--------------------------------------

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKOLOSE; AKOLOSE 01: 24 – 28. (Chinsinsi chobisika chikhalire, tsopano Mulungu wachiwululira anthu ake.)

Abale, tsopano ndakondwa kuti ndikukuvutikirani. Pakuti pakumva zowawazo, ndikutsiriza m’thupi mwanga zotsala za masautso a Khristu kuthandiza thupi lake, ndiye kuti Mpingo. Ndipo ine ndine mtumiki wa Mpingowu, pakuti Mulungu ndiye adandipatsa ntchitoyi yoti ndikulalikireni kwathunthu mau ake. Mauwo ndi chinsinsi chozama chimene chinali chobisika chikhalire kwa mibadwo yonse, koma tsopano Mulungu wachiwululira anthu ake. Cholinga cha Mulungu ndi cha kudziwitsa anthuwo kukoma kwake kwa chinsinsicho ndi ulemerero wake pakati pa anthu akunja. Chinsinsicho nchakuti Khristu ali mwa inu, ndipo Iye amakupatsani chiyembekezo cha kudzalandira ulemerero. Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu.

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.

Alleluia, Alleluia – Ngodala anthu amene amamva mau a Mulungu, nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, ndipo amalimbikira mpaka kubereka zipatso. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAWU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; 10: 38 – 42. (Marita adamlandira Yesu kunyumba kwake. Maria ndiye wasankhula chinthu chopambana.)

Pamene Yesu ndi ophunzira ake anali pa ulendo wao, Iye adalowa m’mudzi wina. Tsono mai wina, dzina lake Marita, adamlandira kunyumba kwake. Iyeyu anali ndi mng'ono wake, dzina lake Maria, amene adaadzakhala pansi ku mapazi a Ambuye, namamva mau ake. Koma Marita ankatanganidwa ndi ntchito zambiri. Choncho adapita kwa Yesu nati, “Ambuye, kodi simukusamalako kuti mng’ono wangayu akundilekera ndekha ntchito? Muuzeni adzandithandize.” Ambuye adati, “iwe Marita iwe, ukutekeseka nkuvutika ndi zinthu zambiri, koma chofunika nchimodzi chokha. Maria ndiye wasankhula chinthu chopambana, ndipo chimenechi palibe wina angamlande ai.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, July 9, 2022

 


LAMULUNGU LA 15 PA CHAKA – C.

(Tizionetsa chikondi choona pa zochita zathu.) 

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA DEUTERONOMO; DEUTERONOMO 30:10 – 14. (Lamulo muli nalo pompano, mungathe kulitsata.)

Mose anawauza anthu kuti, “komatu muzidzamvera Chauta, Mulungu wanu, ndikusunga malamulo ndi malangizo ake onse amene ali m’buku lino la malamulo ake. Mutembenukire kwa iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Lamulo ndikukupatsani leroli si lovuta kulimvetsa ndipo silapatali. Silili kumwamba, kuti muzichita kundifunsa kuti, “kodi amene akwere kumwamba kukatitsitsira lamulo kuti tilimve, ndani?” Komanso silili pa tsidya pa nyanja kuti muthe kundifunsa kuti, “kodi amene aoloke nyanja kukatitengera lamulo kuti tilimve, ndani?” Muli nalo pompano. Mukulidziwa, mumalitchula ndipo mungathe kulitsata.

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 69: 14, 30 – 34, 36 – 37.

Mufunefune Mulungu, inu ozunzika onse, ndipo mulimbenso mtima.

Koma ine ndimapemphera kwa Inu Chauta,

Mundiyankhe pa nthawi yabwino, Inu Mulungu,

Chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika,

Ndi chithandizo chanu chokhulupirika,

Mundiyankhe, Inu Chauta, pakuti chikondi chanu chosasinthika nchabwino.

Mufunefune Mulungu, inu ozunzika onse, ndipo mulimbenso mtima.

Koma ine ndazunzika ndipo ndikumva kuwawa,

Nyamuleni Inu Mulungu, kuti ndipulumuke,

Ndidzatamanda dzina la Mulungu pomuimbira nyimbo,

Ndidzalalika ukulu wake pomuthokoza.

Mufunefune Mulungu, inu ozunzika onse, ndipo mulimbenso mtima.

Ozunzika aone zimenezo ndipo asangalale,

Inu amene mumafunafuna Mulungu, mulimbenso mtima,

Paja Chauta amamvera anthu osowa,

Sanyoza anthu ake omangidwa ndi unyolo.

Mufunefune Mulungu, inu ozunzika onse, ndipo mulimbenso mtima.

Mulungu adzapulumutsa Ziyoni,

Ndipo adzamanganso mizinda ya Yuda,

Ana a atumiki ake nawonso adzalilandira kuti likhale lao,

Ndipo okonda Mulungu adzakhala m’menemo.

Mufunefune Mulungu, inu ozunzika onse, ndipo mulimbenso mtima.

--------------------------------------

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKOLOSE; AKOLOSE 01: 15 – 20. (Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalenga Iyeyo.)

Abale, Khristuyo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu wosaoneka. Iye ndiye mwana wake woyamba, wolamulira zolengedwa zonse. Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalenga ndi Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse padakalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi. Iye ndiyenso mutu wa mpingo thupi lake. Ndiye chiyambi chake, woyambirira mwa ouka kwa akufa, kuti pa zonse Iye akhale wopambana ndithu. Kudakomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristuyo. Mwa iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya mwana wake pamtanda.

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.

Alleluia, Alleluia – Mau anu, Ambuye, ndiwo amapatsa Mzimu wa Mulungu ndiponso moyo. Muli nawo ndinu mau opatsa moyo wosatha. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAWU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; 10: 25 – 37. (Nanga mnansi wanga ndani?)

Katswiri wina wa malumulo adaimirira kuti ayese Yesu. Adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?” Yesu adati, “kodi m’Malamulo mudalembedwa kuti chani? Mumawerengamo zotani?” Iye adayankha kuti, “uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe uzikondera iwe wemwe.” Yesu adati, “mwayankha bwino. Kachiteni zimenezi ndipo mudzakhala ndi moyo.” Koma munthuyo pofuna kudzionetsa ngati wolungama, adafunsa Yesu kuti, “nanga mnzangayo ndani?” Apo Yesu adati, “munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Panjira achifwamba adamgwira. Adamuvula zovala, nammenya, nkumusiya ali thasa, ali pafupi kufa. Ndiye zidangochitika kuti wansembe wina ankapita pa njira yomweyo. Pamene adaona munthu uja, adangolambalala. Chimodzimodzinso Mlevi wina adafika pamalopo, nayenso adangolambalala. Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, adafikanso pamalo pomwepo. Pamene adaona munthu uja, adamumvera chisoni. Adabwera kwa ovulalayo, namthira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuwamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino. M’mawa kutacha adatulutsa ndalama ziwiri zasiliva, nazipereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Adamuuza kuti, ‘msamalireni bwino, ndipo mukamwazanso ndalama zina, ndidzakubwezerani pobwera.”’ Tsono Yesu adafunsa katswiri wa Malamulo uja kuti, “inu pamenepa mukuganiza bwanji? Mwa anthu atatuwa, ndani adakhala ngati mzake wa munthu achifwamba adaamugwirayu?” Iye adati, “amene adamchitira chifundo uja.” Apo Yesu adamuuza kuti, “pitani tsono, nanunso muzikachita chimodzimodzi.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, July 2, 2022

LAMULUNGU LA 14 PA CHAKA – C.

(Mtendere wa Ambuye ukhale nanu.)

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA; YESAYA 66: 10 – 14c. (Ndidzakupatsa zabwino zochuluka ngati mtsinje wa madzi.)

Kondwera nayeni Yerusalemu musangalale chifukwa cha iye, inu nonse amene mumakonda mzinda umenewu. Kondwera nayeni mwachimwemwe, nonsenu amene mukumlira. Mudzalandira chitonthozo ndi kukondwera nacho kwambiri. Mudzagawana naye ulemerero wake ndi kusangalala nawo. Chauta akunena kuti, “ndidzakupatsa zabwino zochuluka ngati mtsinje wa madzi. Chuma cha mitundu ya anthu chidzafika kwa inu ngati mtsinje wotsefukira. Mudzakhala ngati mwana woyamwa amene mai wake wamnyamulira pambalipa, kapena akumluluza pa maondo. Ndidzakusangalatsani ku Yerusalemu monga momwe mai amasangalatsira mwana wake. Mudzasangalala poona zimenezi. Zidzakulimbitsani ndi kukupatsani moyo wamphamvu. Tsono mudzadziwa kuti ine Chauta ndimathandiza amene amandimvera, ndipo ndimakwiyira adani anga.’’

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 66: 01 – 07, 16, 20.

Tamandani Mulungu ndi Chimwemwe, inu anthu onse a pa dziko lapansi.

 Tamandani Mulungu ndi chimwemwe mokweza mau,

Inu anthu onse a pa dziko lapansi,

Imbani nyimbo zoyamika dzina lake laulemerero, mumtamande mwaulemu,

Muuzeni Mulungu kuti, “ntchito zanu nzodabwitsa kwambiri.

Tamandani Mulungu ndi Chimwemwe, inu anthu onse a pa dziko lapansi.

Anthu onse a pa dziko lapansi amakupembedzani,

Amaimba nyimbo zotamanda inu,

Amaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”

Bwerani mudzaona zimene Mulungu wachita,

Ntchito zake nzodabwitsa pakati pa anthu.

Tamandani Mulungu ndi Chimwemwe, inu anthu onse a pa dziko lapansi.

 Adasandutsa nyanja kuti ikhale nthaka youma,

Anthu adaoloka mtsinje uja poyenda pansi,

Nchifukwa chake timukondwerere Iye,

Iye amalamula ndi mphamvu zake mpaka muyaya.

Tamandani Mulungu ndi Chimwemwe, inu anthu onse a pa dziko lapansi.

Bwerani mudzamve, inu nonse opembedza Mulungu,

Ndidzakusimbireni zimene Iye wandichitira,

Chifukwa sadakane pemphero langa,

Sadachotse chikondi chake chosasinthika kwa Ine.

Tamandani Mulungu ndi Chimwemwe, inu anthu onse a pa dziko lapansi.

--------------------------------------

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA A GALATIYA; AGALATIYA 06: 14 - 18. (Zipsera zimene ine ndili nazo za thupi langa, zikutsimikiza kuti ndine wakewake wa Yesu.)

Abale, ine sindingadyadire kanthu kena kalikonse, koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu basi. Popeza kuti iye adafa pamtanda, tsopano zapansipano kwa ine zili ngati zakufa, ndipo inenso kwa zapansipano, ndili ngati wopachikidwa. Kuumbalidwa sikanthu, kusaumbalidwa sikanthunso, chachikulu nchakuti Mulungu apatse munthu moyo watsopano. Mulungu awapatse Mtendere, ndipo awachitire chifundo anthu a Mulungu onse amene amatsata njira imeneyi. Kuyambira tsopano asandivutenso munthu wina aliyense, pakuti zipsera zimene ine ndili nazo pa thupi langa, zikutsimikiza kuti ndine wakewake wa Yesu. Abale, Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni inu nonse. Amen.

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.

Alleluia, Alleluia – Ndikukutchulani abwenzi, atero Ambuye, chifukwa zonse zimene ndidamva kwa Atate anga, ndidakudziwitsani. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAWU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; 10: 01 – 12, 17 – 20. (Mtendere ukhale mwa munthu ameneyo.)

Pambuyo pake Ambuye adasankha anthu 72, nawatuma awiriawiri kuti atsogole kupita ku mudzi uliwonse ndi ku malo aliwonse kumene iye ankati apiteko. Adawauza kuti, “dzithu nzambiri, koma antchito ngochepa. Nchifukwa chake pemphani mwini zinthu kuti atume antchito kukatuta dzithudzo. Pitani tsono. Ndikukutumani ngati ana ankhosa pakati pa mimbulu. Musatenge chikwama cha ndalama, kapena thumba la paulendo, kapenanso nsapato zapadera ai. Musaimenso kuti mupereke moni panjira. Kunyumba kulikonse kumene mukalowe, muyambe mwanena kuti, ‘Mtendere ukhale m’nyumba muno.’ Ngati m’nyumbamo muli anthu amtendere, mtendere umene mwanenawo udzakhala pa iyeyo. Koma ngati mulibe munthu wofuna mtendere, mtendere umene mwanenawo udzabwerera kwa inu. Khalani m’nyumba yomweyo. Mudye ndi kumwa zimene akupatsani, pakuti wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake. Musamachoka kumene mwafikako nkulowa ku nyumba zina ai. Mukalowa m’mudzi, anthu nkukulandirani, mudye zimene akukonzerani. Muchiritse anthu odwala amene ali m’mudzimo, ndipo muwauze kuti, ‘tsopano ufumu wakumwamba wakufikirani’. Koma kumudzi kumene mukalowe, anthu nkupanda kukulandirani bwino, mukapite m’miseu yam’mudzimo, nkunena kuti, ‘tikukusansirani ngakhale fumbi la m’mudzi mwanu muno limene linamamatira ku mapazi athu. Komabe dziwani kuti ufumu wa Mulungu wafika.’ Kunena zoona, pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Sodomu koposa polanga mudzi umenewo.” Anthu 72 aja adabwerako ndi chimwemwe nati, “Ambuye, ngakhale mizimu yoipa yomwe imatigonjera tikamailamula m’dzina lanu.’’ Yesu adawauza kuti, “ndidaona satana ali kugwa ngati mphezi kuchokera kumwamba. Ndakupatsanitu mphamvu kuti muziponda njoka ndi zinkhanira, ndikumagonjetsa mphamvu zonse za mdani uja. Palibe kanthu kamene kangakupwetekeni. Komabe musakondwere chifukwa choti mizimu yoipa ikukugonjerani, koma muzikondwera kuti maina anu adalembedwa kumwamba.’’

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...