LAMULUNGU LA 2 LA PASAKA—C
[LAMULUNGU LA CHIFUNDO CHA AMBUYE]
“Iwo adakondwera kwambiri poona Ambuye.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 5:12-16 (Anthu okhulupirira Ambuye, amuna ndi akazi, ankachulukirachulukira).
Atumwi ankachita zizindikiro ndi zozizwitsa zambiri pakati pa anthu. Onse okhulupirira Khristu ankasonkhana ndi mtima umodzi m’Khonde la Solomoni. Mwa anthu enawo panalibe ndi m’modzi yemwe amene adaalimba mtima kuti azisonkhana nawo, komabe anthu onse ankawatama. Ndipo anthu okhulupirira Ambuye ankachulukirachulukira, mwakuti linali ndithu gulu lalikulu la amuna ndi akazi omwe. Tsono anthu ankatulutsira odwala ao m’miseu ya mumzinda, nkumawagoneka pa mabedi ndi pa mphasa, kuti Petro podutsapo, chithunzithunzi chake chokha ena mwa iwo chiwafike. Kunkasonkhananso anthu ochuluka ochokera ku midzi yozungulira Yerusalemu. Anali atanyamula anthu odwala, ndiponso ena osautsidwa ndi mizimu yowaipitsa. Onsewo ankachiritsidwa.
Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 118:2-04. 22-27.
Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.
Aisraele anene kuti, Chikondi chake nchamuyaya.
Banja la Aroni linene kuti, Chikondi chake nchamuyaya.
Anthu oopa Chauta anene kuti, Chikondi chake nchamuyaya.
Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.
Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya.
Chauta ndiye amene wachita zimenezi, zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga.
Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.
Tipulumutseni, tikukupemphani Inu Chauta,
Chauta, tikukupemphani kuti zinthu zitiyendere bwino.
Ngwodala amene alikudza m’dzina la Chauta.
Tikufunirani madalitso ochokera m’Nyumba ya Chauta.
Chauta ndi Mulungu, ndipo watipatsa kuwala.
Tamandani Chauta pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA CHIVUMBULUTSO: CHIVUMBULUTSO 1:9-13. 17-19 (Ndidaafa, koma tsopano ndili moyo mpaka muyaya).
Ndine, Yohane, mbale wanu, ndipo ngati mnzanu wokhulupirira Yesu, ndili nanu limodzi mu ufumu wa Mulungu, komanso m’masautso ndi m’kupirira kosatepatepa. Ndidaponyedwa pa chilumba cha Patimosi, chifukwa cha kulalika mau a Mulungu ndi kuchitira Yesu umboni. Pa tsiku la Ambuye ndidaagwidwa ndi Mzimu Woyera, nkumva kumbuyo kwanga liwu la mphamvu ngati kulira kwa lipenga. Liwulo lidati, “zimene ukuwonazi, uzilembe m’buku ndipo ulitumize kwa mipingo isanu ndi iwiri iyi: wa ku Efeso, wa ku Smirina, wa ku Pergamo, wa ku Tiatira, wa ku Sardi, wa ku Filadelfiya ndi wa ku Laodikea.” Nditacheuka kuti ndiwone akundilankhula ndani, ndidaona ndodo zoikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide. Pakati pake pa ndodo za nyalezo ndidaona wina wooneka ngati mwana wa munthu. Anali atavala mkanjo wautali, atamangira lamba wagolide pa chifuwa. Nditamuwona, ndidagwa kumapazi kwake ngati munthu wakufa. Koma Iye adandisanjika dzanja lake lamanja nati: “Usaope. Woyamba ndiponso wotsiriza ndine. Wamoyo uja ndine. Ndidaafa, koma tsopano ndili moyo mpaka muyaya. Imfa ndi malo a anthu akufa makiyi ake ali ndi Ine. Lemba tsono zimene waziona, ndiye kuti zimene zikuchitika tsopano ndi zimene zidzachitike bwino lino.”
Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Yohane 20:29.
Alleluia, Alleluia!! – Yesu adati, wakhulupirira chifukwa wandiona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone. – Alleluia, Alleluia!!
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 20:19-31 (Patapita masiku asanu ndi atatu, Yesu adabwera).
Madzulo kutada pa tsiku Lamulungu lomwelo, ophunzira aja anali pamodzi. Zitseko zinali zokhoma, chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Tsono Yesu adadza naimirira pakati pao nkunena kuti, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adawaonetsa manja ake ndi m’nthiti mwake, ndipo ophunzira aja adakondwa kwambiri powaona Ambuyewo. Yesu adatinso, “Mtendere ukhale nanu. Monga Atate adandituma, Inenso ndikukutumani.” Pambuyo pake adawauzira mpweya nati, “Landirani Mzimu Woyera. Anthu amene mudzawakhululukira machimo ao, adzakhululukidwadi, koma amene simudzawakhululukira, sadzakhululukidwa ai.” Mmodzi mwa ophunzira aja khumi ndi awiri, Tomasi (wotchedwa Didimo), sanali pamodzi ndi anzake pamene Yesu adaabwera. Tsono ophunzira anzake aja adamuuza kuti, “Ife tawaonatu Ambuye.” Koma Tomasi adati, “ndikapanda kuwona mabala a misomali m’manja mwao, ndi kupisa chala changa m'mabala a misomaliwo, ndipo ndikapanda kupisa dzanja langa m’nthiti mwao, sindingakhulupilire konse.” Patapita masiku asanu ndi atatu, ophunzira aja analinso m’nyumbamo, ndipo Tomasi anali nawo. Zitseko zinali chikhomere koma Yesu adadza, naimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adauza Tomasi kuti, “Ika chala chako apa, ona manja anga. Tambalitsa dzanja lako, ulipise m'nthiti mwangamu. Leka kukayika, uyambepo kukhulupirira.” Tomasi adati, “Ambuye anga! Mulungu wanga!” Yesu adati, “kodi wakhulupirira chifukwa wandiwona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone.” Yesu adachitanso zizindikiro zina zambiri zozizwitsa pamaso pa ophunzira ake, zimene sizidalembedwe m’buku muno. Koma izi zalembwedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, ndipo kuti pakukhulupirira mukhale ndi moyo m’dzina lake.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, popeza kuti Yesu Khristu wouka kwa akufa akutitsogolera, tiyeni, mokondwera ndi mosakayika, tikweze mapemphero athu kwa Atate athu a Kumwamba:
1. Tipempherere aepiskopi ndi ansembe onse, kuti alimbitse chikhulupiriro cha akhristu ao powalalikira za kuuka kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Tipempherere akhristu amene alikuzunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chao, kuti akondwerere lero potamanda Yesu Khristu wouka kwa akufa.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Tipempherere anthu amene akadali mu mdima namakayikakayika, kuti maso ao atsekuke pakumva Mthenga Wabwino wa Pasaka.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Tidzipempherere ife tomwe kuti tilimbikire kuchitira anzathu zabwino, kusonyeza kuti Khristu alikukhazikitsadi ufumu wake m’mitima mwathu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Mulungu Atate athu, mudakwaniritsa malonjezo anu pakuukitsa Mwana wanu kwa akufa. Mverani mapemphero athu ndi kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB
No comments:
Post a Comment