Saturday, April 19, 2025

LAMULUNGU LA PASAKA—C

LAMULUNGU LA PASAKA—C

“Yesu Khristu ndiye moyo wathu.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 10: 34, 37-43. (Adaonekera kwa ife, amene tinkadya ndi kumwa naye pamodzi atauka kwa akufa).

 

Petro adayamba kulankhula, adati, "Zoonadi ndazindikira tsopano kuti Mulungu alibe tsankho. Mukudziwa zimene zidachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa nthawi imene Yohane ankalalika za ubatizo wake. Mukudziwa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana. Ife ndife mboni za zonse zimene Iye adachita mu Yerusalemu ndi m'dziko lonse la Ayuda. Iwo adamupha pakumpachika pa mtanda. Komabe mkucha wake Mulungu adamuukitsa kwa akufa, nalola kuti aonekere poyera. Sadaonekere kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zimene Mulungu adazisankhiratu. Ndiye kuti adaonekera kwa ife, amene tinkadya ndi kumwa naye pamodzi atauka kwa akufa. Ndipo adatilamula kuti tikalalikire anthu onse, ndi kuchita umboni kuti Iyeyo ndiye amene Mulungu adamsankha kukhala Woweruza anthu amoyo ndi akufa omwe. Aneneri onse adamchitira umboni, ndi kunena kuti chifukwa cha dzina lake, Mulungu adzakhululukira machimo a munthu aliyense wokhulupirira Iyeyu.”

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 118:1-2, 16-17, 22-23.

 

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli. Kapena Alleluia, alleluia, alleluia!!

 

Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino,

ndipo chikondi chake nchamuyaya.

Aisraele anene kuti,

“Chikondi chake nchamuyaya.”

 

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli. Kapena Alleluia, alleluia, alleluia!!

 

Dzanja lamanja la Chauta lapambana,

dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu.”

Sindidzafa, ndidzakhala moyo,

ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta.

 

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli. Kapena Alleluia, alleluia, alleluia!!

 

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana,

womwewo wasanduka mwala wapangodya.

Chauta ndiye amene wachita zimenezi,

zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu.

 

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli. Kapena Alleluia, alleluia, alleluia!!

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKOLOSE: AKOLOSE 3:1-4 (Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano).

 

Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano. Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. Khristu ndiye moyo wanu weniweni tsopano, choncho pamene Iye adzaonekerenso, inunso mudzaonekera mu ulemerero pamodzi naye.

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – 1 Akorinto 5:7.

Alleluia, Alleluia!! – Kankhosa kathu ka Pasaka ndiye Yesu Khristu amene waphedwa ngati nsembe. Tiyeni tsopano, tichite chikondwerero choyamikira Ambuye. – Alleluia, Alleluia!!

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 20:1-9 (Yesu adzayenera kuuka kwa akufa).

 

Pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, m’mamaŵa ndithu kudakali kamdima, Maria wa ku Magadala adadza ku manda a Yesu. Adaona kuti chimwala chija chachotsedwa kale pa khomo la mandawo. Choncho adathamanga nakafika kwa Simoni Petro, ndi kwa wophunzira wina uja amene Yesu ankamukonda kwambiri. Adaŵauza kuti, “Aŵachotsa Ambuye m'manda muja, ndipo sitikudziŵa kumene akaŵaika.” Pamenepo Petro ndi wophunzira wina uja adatuluka napita ku manda. Onse aŵiri adathamanga pamodzi, koma wophunzira wina uja adathamanga kopambana Petro, nkuyambira ndiye kufika kumandako. Adaŵerama naona nsalu zija zili chikhalire, koma iye sadaloŵemo. Simoni Petro atafika akumutsatira, adaloŵa m'mandamo. Adaona nsalu zija zili chikhalire, ndiponso kansalu kamene kanali kumutu kwake. Kansaluko sikanali pamodzi ndi nsalu zina zija, koma padera pakokha, kali chipindire. Pamenepo wophunzira wina uja, amene adaayambira kufika ku manda, nayenso adaloŵa; ndipo ataona zimenezi, adakhulupirira. Mpaka nthaŵi imeneyo iwo aja anali asanamvetse Malembo akuti Yesu adzayenera kuuka kwa akufa.

 

Mthenga wa Ambuye… Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, kuuka kwa Yesu Khristu kwa akufa kwadzaza mitima yathu ndi chikhulupiriro ndi chimwemwe. Tiyeni, tiyamike Atate athu a Kumwamba, popempherera anthu onse a m’dziko lino lapansi:

 

1.     Apapa, Aepiskopi ansembe onse alimbitse chikhulupiriro cha akhristu ao, pakuwalalikira mosakayika za kuuka kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akhristu onse, kukondana kwawo kupite m’tsogolo, ndipo ntchito zao zisonyeze anthu onse kuwala kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Anthu odwala ndi onse amene ali m’mavuto, chikondwerero cha Pasaka chiwalimbitse mtima, podziwa kuti Yesu Khristu adagonjetsa imfa.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

4.     Ife tomwe tili muno, tikhaledi anthu atsopano ndi mboni zake za Yesu Khristu, poika mtima pa zinthu za kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, tikukuyamikani chifukwa mudatiwukitsa pamodzi ndi Yesu Khristu potininkha moyo wake. Mumvere mapemphero athuwa ndi kutisunga m’chikondi chanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...