Friday, April 18, 2025

LOWERUKA LOYERA—C [MISA YA MADZULO/ USIKU YA KUUKA KWA AMBUYE]

LOWERUKA LOYERA—C

[MISA YA MADZULO/ USIKU YA KUUKA KWA AMBUYE]

 

1. MAU A M’BUKU LA GENESIS; GENESIS 1:1—2:2. (Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino kwambiri).

 

Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Dziko lapansilo linali lopanda maonekedwe enieni ndiponso losakonzeka. Mdima unali utaphimba nyanja yaikulu ponseponse, ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo. Tsono Mulungu adati, “kuyere,” ndipo kudayeradi. Mulungu adaona kuti kuyerako kunali kwabwino. Pomwepo adalekanitsa kuyerako ndi mdima. Kuyerako adakutcha Usana, mdima uja adautcha Usiku. Ndipo kudali madzulo ndiponso m’mawa, tsiku loyamba.

 

Kenaka Mulungu adati, “pakhale cholekanitsa madzi, kuti madziwo akhale pa malo awiri olekana,” ndipo zidachitikadi. Motero Mulungu adalenga cholekanitsa madzi chija, nawagawa madziwo, ena pansi pa cholekanitsacho ena pamwamba pake. Cholekanitsacho adachitcha dzina loti Thambo. Ndipo kudali madzulo ndiponso m’mawa, tsiku lachiwiri.

 

Mulungu adatinso, “Madzi apansiwa akhale pa malo amodzi, kuti paoneke mtunda,” ndipo zidachitikadi. Mulungu adautcha mtundawo Dziko, madzi adawasonkhanitsa aja adawatcha Nyanja. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. Tsono adati, “panthaka pamere zomera zobala njere, ndiponso mitengo yobala zipatso zanjere malinga ndi mtundu wake,” ndipo zidachitikadi. Motero panthaka padamera zomera za mitundu yonse, zipatso zokhala ndi njere ndi mitengo yobereka zipatso za njere, malingana ndi mitundu yao. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. Ndipo kudali madzulo ndiponso m’mawa, tsiku lachitatu.

 

Pambuyo pake Mulungu adati, “kuthambo kukhale miyuni kuti izilekanitsa usana ndi usiku, ndiponso kuti ikhale zizindikiro za nyengo, masiku ndi zaka. Miyuni imeneyi ikhale ku thambo ndi kumaunikira dziko lapansi,” ndipo zidachitikadi. Motero Mulungu adalenga miyuni iwiri yaikulu: dzuwa lowala masana, ndi mwezi wowala usiku. Adalenganso nyenyezi. Mulungu adaika miyuniyo ku thambo, kuti iziwunikira dziko lapansi, kuti iziwala usana ndi usiku, kulekanitsa kuyera ndi mdima. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. Ndipo kudali madzulo ndiponso m’mawa, tsiku lachinai.

 

Zitatero Mulungu adati, “m’nyanja mukhale zamoyo zambirimbiri, ndipo pakhale mbalame zouluka mu mlengalenga.” Motero Mulungu adalenga nsomba zazikulu zam’nyanja, pamodzi ndi zolengedwa zina zonse zokhala m’madzi, ndiponso mbalame ndi zouluka zina zamitundumitundu. Mulungu adaona kuti zonse Zimene adalengazo zinali zabwino. Adazidalitsa ponena kuti, “swanani ndipo mudzaze nyanja, mbalamenso ziswane pa dziko. Tsono kudali madzulo ndiponso m’mawa, tsiku lachisanu.

 

Ndipo Mulungu adati, “padziko pakhale mitundu yonse ya zamoyo potsata mitundu yake: zoweta, zokwawa, ndi nyama zakuthengo, potsata mitundu yake.” Ndipo zidachitikadi. Pomwepo Mulungu adalenga nyama zakuthengo potsata mitundu yake, ndi nyama zoweta potsata mitundu yake, ndiponso zokwawa zonse potsata mitundu yake. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino. Zitatha izo Mulungu adati, “tiyeni tipange munthu m'chifanizo chathu, adzakhale wonga Ifeyo. Adzalamulire nsomba zam’nyanja, mbalame zamumlengalenga, nyama zoweta, ndi zokwawa zonse za pa dziko lapansi.” Motero Mulungu adalenga munthu, m’chifanizo chake, adawalengadi m’chifanizo cha Mulungu. Adawalenga wina wamwamuna wina wamkazi. Adawadalitsa powauza kuti, “mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.” Ndipo Mulungu adati, “Ndikukupatsani zomera zonse za mtundu wokhala njere, ndi mitundu yonse ya zomera zobala zipatso zanjere, kuti muzidya. Koma nyama zonse zakuthengo, mbalame, ndi zokwawa zonse, ndazipatsa msipu kuti zizidya,” ndipo zidachitikadi momwemo. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino kwambiri. Tsono kudali madzulo ndiponso m’mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

 

Motero dziko lonse lapansi, thambo ndi zonse zokhala m’menemo, zidatha kulengedwa. Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi Mulungu adamaliza ntchito imene ankachitayo, ndipo adapumula pa tsiku lachisanu ndi chiwiri.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 3:4-7, 12-13, 20, 22.

 

Chauta amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.

 

Mau a Chauta ndi olungama,

Zochita zake zonse amazichita mokhulupirika,

Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera,

Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.

 

Chauta amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.

 

Chauta adalankhula ndipo zakumwamba zidalengedwa,

Zonse zakumeneko zidalengedwa pamene Iye adalankhula mau ake,

Adasonkhanitsa pamodzi madzi a m’nyanja zakuya,

Ndipo adaziikira malire kuti zisasefukire.

 

Chauta amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.

 

Ngwodala mtundu wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta,

Anthu amene Chauta wawasankha akeake,

Chauta ali kumwamba, amayang’ana pansi,

Ndi kuwona anthu onse.

 

Chauta amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.

 

Mitima yathu ikuyembekeza Chauta,

Chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu,

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika,

Chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

 

Chauta amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.

--------------------------------------


2. MAU A M’BUKU LA GENESIS; GENESIS 22:1-18. (Nsembe ya Abrahamu, bambo wathu wachikhulupiriro).

 

Pambuyo pake Mulungu adamuyesa Abrahamu. Adamuitana, adati, “Abrahamu!” Ndipo Abrahamu adayankha kuti, “Ee Ambuye.” Mulungu adati, “tenga Isaki, mwana wako mmodzi yekha uja amene umamkonda kwambiri, upite ku dziko la Moriya. Kumeneko ukampereke ngati nsembe yopsereza pa phiri limene ndidzakuuza. M’mawa mwake Abrahamu adakonza chishalo pa bulu wake nadulanso nkhuni zokaotchera nsembe, ndipo adatenga Isaki pamodzi ndi antchito ake awiri, nanyamuka ulendo wopita ku malo amene Mulungu adaamuuza. Pa tsiku lachitatu lake Abrahamu adaona malowo chapatali. Ndipo adauza antchito ake aja kuti, “inu bakhalani pano ndi buluyu. Ine ndi mnyamatayu tipita uko kukapemphera, pambuyo pake tidzakupezani.” Abrahamu adasenzetsa Isaki nkhuni zokaotchera nsembe yopsereza ija, iyeyo adaatenga moto m’manja mwake, pamodzi ndi mpeni, onse nkumayendera limodzi. Tsono Isaki adaitana bambo wake kuti, “Atate.” Abrahamu adavomera kuti, “Ee, mwana wanga.?” Isaki adafunsa kuti, “moto ndi nkhuni ndikuziwona, zilipo, koma nanga mwana wankhosa wokaotchera nsembe ali kuti?” Abrahamu adamuyankha kuti, “mwana wanga, Mulungu akatipatsa mwana wankhosa yo.” Choncho onse awiri adapitiriza ulendo wao limodzi. Atafika ku malo amene adaamuuza Mulungu aja, Abrahamu adamanga guwa, naika nkhuni pamwamba pa guwalo. Kenaka adamanga mwana wake uja, namgoneka pamwamba pa nkhunizo. Tsono adasolola mpeni kuti amuphe mwana wakeyo. Koma mngelo wa Chauta adamuitana kuchokera kumwamba, adati, “Abrahamu, Abrahamu!” Iye adayankha kuti, “Ee, Ambuye!” Mngeloyo adati, “usamuphe mnyamatayo, kapena kumchita kanthu kena kalikonse. Ndikudziwa kuti ndiwe womveradi Mulungu, chifukwa sudandimane mwana wako mmodzi yekhayo. Abrahamu atayang’ana, adaona kuti pali nkhosa yamphongo yogwidwa nyanga zake m'ziyangoyango. Adapita kukaigwira, naipha ngati nsembe yopsereza m’malo mwa mwana wake uja. Abrahamu adawatcha malowo kuti Chauta adapatsa. Ndipo mpaka lero lino anthu amati, “Paphiri la Chauta adzapatsa. Mngelo wa Chauta uja adamuitana Abrahamu kachiwiri kuchokera kumwamba, adati, “Chauta akunena kuti, ‘ndikulumbira kuti ndidzakudalitsa kwambiri iwe chifukwa wachita zimenezi, osandimana mwana wako mmodzi yekha uja. Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zakumwamba, kapenanso ngati mchenga wa m’mbali mwa nyanja. Zidzukulu zakozo zidzagonjetsa adani ao onse. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalandira madalitso kudzera mwa zidzukulu zako, chifukwa iwe wandimvera.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 6:5, 8-11.

                                                

Mundisunge Inu Mulungu, poti ndinu kothawira kwanga.

 

Chauta ndiye chuma changa ndi cholowa changa,

Tsogolo langa lili m’manja mwanu,

Nthawi zonse ndimalingalira za Chauta,

Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.

 

Mundisunge Inu Mulungu, poti ndinu kothawira kwanga.

 

Nchifukwa chake mtima wanga ukukondwa,

Ndipo m’katikati mwangamu ndikusangalala,

Thupi langanso lidzakhala pabwino,

Chifukwa simudzandisiya ku malo a anthu akufa,

Simudzalola kuti wokondedwa wanune ndikaole kumeneko.

 

Mundisunge Inu Mulungu, poti ndinu kothawira kwanga.

 

Mumandiwonetsa njira ya ku moyo.

Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu,

Ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja,

Mumagonjetsa adani anu ndi ulemerero wanu wopambana.

 

Mundisunge Inu Mulungu, poti ndinu kothawira kwanga.

--------------------------------------

 

3. MAU A M’BUKU LA EKSODO; EKSODO 14:15—15:1. (Aisraele onse aja adaoloka nyanjayo pansi pali pouma, madzi atangoima pa mbali zonse ziwiri).

 

Chauta adafunsa Mose kuti, “chifukwa chiyani ukulira kwa ine? Auze Aisraele kuti aziyenda. Tenga dodo yakoyo, ndipo utambalitse dzanja pa nyanja, kuigawa nyanjayo kuti Aisraele aoloke pouma. Ndidzawaumitsa mtima Aejipitowo, kotero kuti adzalondola Aisraele ndithu. Ndipo kugonjetsa kumene ndidzagonjetsa Farao pamodzi ndi ankhondo ake, magaleta ake ndi oyendetsa ake omwe, ndidzapeza nako ulemerero. Aejipitowo adzadziwa kuti Ine ndine Chauta, akadzaona m’mene ndipambanire Farao ndi magaleta ake ndi owayendetsa ake. Apo mngelo wa Mulungu, yemwe ankatsogolera Aisraele aja, adakakhala cha kumbuyo kwao. Mtambo womwe unkakhala patsogolo pao uja, udakakhalanso chakumbuyo kwao. Unali pakati pa gulu lankhondo la Aejipito ndi gulu lankhondo la Aisraele.

 

Choncho panali mtambo ndi mdima, kotero kuti magulu ankhondo awiriwo sadayandikane usiku wonse. Tsono Mose adatambalitsa dzanja lake pa nyanja, ndipo pompo Chauta adaumitsa nyanja ija, pogwiritsa ntchito mphepo yamkuntho yakuvuma, imene idaomba usiku wonse ndi kuumitsa nyanjayo. Madziwo adagawikana, ndipo adakhala ngati chipupa pa mbali zonse ziwiri, motero Aisraele adaoloka pouma. Aejipito aja adalondola Aisraelewo mpaka kukalowa nawo m’nyanja muja. Akavalo onse a Farao adalowa m’nyanja, pamodzi ndi magaleta ake ndi owayendetsa ake omwe. Tsono kusanache m’mawa ndithu, Chauta, ali m’chipilala chamtambo ndi chamoto, adayang’ana ankhondo a Aejipito ndipo adawachititsa mantha. Adapinda mikombero ya magaleta ao, kotero kuti magaletawo ankayenda movutika. Pamenepo Aejipito aja adati, “tiyeni tiwathawe Aisraelewa, chifukwa Chauta akuwamenyera nkhondo, kulimbana nafe.” Apo Chauta adauza Mose kuti, “tambalitsa dzanja lako kunyanjako kuti madziwo abwerere, ndi kumiza Aejipitowo pamodzi ndi magaleta ao ndi owayendetsa ake omwe.!”

 

Motero Mose adatambalitsa dzanja lake ku nyanja, ndipo m’mene kunkacha, nkuti madziwo akubwerera m’malo mwake. Aejipitowo adayesa kuthawa, koma Chauta adawabweza momwe m’nyanjamo. Ndipo madziwo adabwerera, namiza magaleta aja ndi owayendetsawo, pamodzi ndi gulu lonse lankhondo la Farao lija linkawatsatali. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adapulumuka. Koma Aisraele onse aja adaoloka nyanjayo pansi pali pouma, madzi atangoima pa mbali zonse ziwiri. Pa tsiku limenelo, Chauta adapulumutsa Aisraele kwa Aejipito. Aisraele adaona Aejipitowo ali ngundangunda m’mbali mwa nyanja. Choncho adaona mphamvu zazikulu zimene Chauta adaonetsa pogonjetsa Aejipito aja. Tsono adayamba kuwopa Chauta, ndipo ankakhulupirira Chautayo ndi Mose mtumiki wake. Tsono Mose pamodzi ndi Aisraele aja adaimba nyimbo iyi, kuimbira Chauta, adati,

 

A Choir ayimbe nyimbo ili pansipa.

 

Nyimbo ya Mose—Eksodo 15:1-6, 17-18.

 

Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana.

 

Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana,

Waponya m’nyanja akavalo pamodzi ndi okwerapo omwe,

Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira,

Ndiye chipulumutso changa.

Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda.

Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.

 

Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana.

 

Chauta ndi wankhondo, Chauta ndilo dzina lake,

Chauta adaponya m’nyanja magaleta a Farao,

Pamodzi ndi gulu lake lankhondo,

Adammizira Atsogoleri ake amphamvu m’Nyanja Yofiira,

Nyanja yozamayo idawaphimba onse,

Adamira mpaka pansi pa nyanja ngati miyala.

 

Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana.

 

Inu Chauta dzanja lanu lamanja ndi laulemerero,

Chifukwa cha nyonga zake, dzanja lanu lamanja limatswanya adani.

Mumagonjetsa adani anu ndi ulemerero wanu wopambana.

 

Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana.

 

Mudzawalowetsa ndi kuwakhazika pa phiri lanu,

Pa malo amene Inu Chauta mudawapanga kuti akhale anu,

M’nyumba yopembedzera imene Inu mudaimanga

Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya.

 

Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana.

--------------------------------------

 

4. MAU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA; YESAYA 54:5-14. (Ndidzakuwonetsa chikondi changa mpaka muyaya, akuterotu Chauta, Momboli wako).

 

Mlengi wako ali ngati mwamuna wako. Chauta Wamphamvuzonse ndiye dzina lake. Woyera Uja wa Israele ndiye Momboli wako, dzina lake ndi Mulungu wa dziko lonse lapansi. Iwe Israele, Chauta wakuitananso. Uli ngati msungwana wosiyidwa, amene ali wodzaza ndi chisoni mu mtima, ngati mkazi wapaunyamata amene wachotsedwa, akuterotu Mulungu wako. “Ndidaakusiya pa kamphindi kochepa, koma ndidzakutenganso ndi chikondi chachikulu. Ndidaakufulatira pa mphindi yaing’ono ndili wokwiya zedi, koma ndidzakuwonetsa chikondi changa mpaka muyaya,” akuterotu Chauta, Momboli wako. “Kwa ine zimenezi zili monga m’mene zinaliri nthawi ya Nowa: monga momwe ndidaalumbirira nthawi imeneyo kuti sindidzaononganso dziko lapansi ndi chigumula, chonchonso tsopano ndikulumbiranso kuti sindidzakupseranso mtima, ndipo sindidzakudzudzulanso. Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo. Chauta akunena kuti, “Iwe Yerusalemu ndiwe mzinda wozunzika, wosowa chithandizo, wopanda wokutonthoza. Ndidzakongoletsa miyala yako, ndidzamanganso maziko ako ndi miyala ya mtengo wapatali. Ndidzamanga nsanja zako ndi miyala yofira. Ndidzamanga zipata zako ndi miyala yochezimira ngati moto. Ndidzamanganso linga lokuzungulira ndi miyala ya mtengo wapatali. Anthu ako ndidzawaphunzitsa ndekha, Ine Chauta, ana ako ndidzawadalitsa ndi kuwapatsa mtendere waukulu. Udzakhazikika m’chilungamo chenicheni. Sudzakhalanso wopanikizika, chifukwa palibe choopa, sudzakhalanso ndi mantha, chifukwa manthawo sadzakufikira.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 30:1, 3-5, 10-12.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m’dzenje la imfa.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta,

Pakuti mwanditulutsa m’dzenje la imfa,

Simudalole kuti adani anga akondwere,

Inu Chauta, mwanditulutsa m’dziko la akufa,

Mwandibwezeranso moyo kuti ndingatsikire ku manda.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m’dzenje la imfa.

 

Imbani nyimbo zotamanda Chauta,

Inu anthu ake oyera mtima, mumthokoze chifukwa cha dzina lake loyera,

Mkwiyo wake ndi wa kanthawi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse,

Misozi kumabwera chimwemwe chokhachokha.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m’dzenje la imfa.

 

Imvani, Inu Chauta, ndipo mundikomere mtima,

Inu Chauta, mukhale mthandizi wanga,

Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina,

Chauta, Mulungu wanga ndidzakuthokozani mpaka muyaya.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m’dzenje la imfa.

--------------------------------------

 

5. MAU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA; YESAYA 55:1-11. (Mubwere kwa Ine, mumvere Ine, kuti mukhale ndi moyo. Ndidzachita nanu chipangano chosatha).

 

Chauta akunena kuti, “Inu nonse omva ludzu, bwerani, madzi ali pano. Ndipo inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule chakudya, kuti mudye. Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka, osalipira ndalama, osalipira chilichonse. Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene saadya? Chifukwa chiyani malipiro anu mukuwonongera zinthu zimene sizingakuchotseni njala? Mvetsetsani zimene ndikunena Ine, ndipo muzidya zimene zili zabwino, muzidzisangalatsa ndi zakudya zonona. Tcherani makutu, ndipo mubwere kwa Ine. Mumvere Ine, kuti mukhale ndi moyo. Ndidzachita nanu chipangano chosatha, ndipo ndidzakuwonetsani chikondi chosasinthika ndi chosapeneka, chimene ndidaalonjeza Davide. “Mudziwe kuti iye uja ndidamsankha kuti akhale mboni yanga kwa mitundu ya anthu, kuti akhale mtsogoleri ndi wolamulira anthu ambiri. Tsopano mudzaitana mitundu imene simuidziwa. Mitundu imene sikudziwani idzabwera ndi liwiro kuti ikhale nanu, chifukwa cha Ine Chauta, Mulungu wanu, Woyera uja wa Israele, amene ndidakupatsani ulemerero. Mufunefune Chauta pamene angathe kupezeka, mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi. Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo awachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye awakhululukire machimo ao mofewa mtima. Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu. Mvula ndi chisanu chambee zimatsika kuchokera kumwamba, ndipo sizibwerera komweko, koma zimathirira nthaka. Zimameretsa ndi kukulitsa zomera, kenaka nkupatsa alimi mbeu ndi chakudya. Ndimonso amachitira mau ochokera m’kamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine popanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo zimene ndidawatumira zidzayenda bwino.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 12:2-6.

 

Mudzakondwera pokatunga madzi m’zitsime za chipulumutso.

 

Zoonadi Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye,

Ndipo sindidzaopa pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa,

Ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga,

Mudzakondwera pokatunga madzi m’zitsime za chipulumutso.

 

Mudzakondwera pokatunga madzi m’zitsime za chipulumutso.

 

Thokozani Chauta, tamandani dzina lake,

Mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,

Mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.

 

Mudzakondwera pokatunga madzi m’zitsime za chipulumutso.

 

Imbirani Chauta nyimbo zotamanda, pakuti wachita zazikulu,

Zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi,

Fuulani ndi kuimba mokondwa, inu anthu a ku Ziyoni,

Pakuti Woyera Uja wa Israele ndi wamkulu pakati panu.

 

Mudzakondwera pokatunga madzi m’zitsime za chipulumutso.

--------------------------------------

 

6. MAU A M’BUKU LA MPROFETI BARUKI; BARUKI 3:9-15, 32—4:4. (Yenda molondola m’kuwala kwa kuyera kwa Ambuye).

 

Iwe Israele, imva malamulo opatsa moyo. Tchera khutu kuti udziwe nzeru. Zakhala bwanji, iwe Israele, zakhala bwanji kuti ukupezeka m’dziko la adani, ndipo kuti wayamba kukalamba m’dziko lachilendo? Zakhala bwanji kuti uli woipitsidwa pakati pa anthu akufa? Chifukwa chiyani wasanduka mnzao wa anthu akumanda? Iwetu udasiya kasupe wa nzeru. Ukadatsata njira ya Mulungu, bwenzi uli mu mtendere nthawi zonse. Phunzira kumene kuli luntha, kumene kuli mphamvu, kumene kuli nzeru zomvetsa zinthu. Pamenepo udzazindikira kumene kuli moyo weniweni wa zaka zambiri, kumene kuli kuyera kokuunikira, ndiponso kumene kuli mtendere. Ndani adapeza malo ake kumene kumakhala nzeru? Ndani adalowa m’nyumba yosungiramo chuma chake? Koma Iye amene amadziwa zonse, amadziwadi nzeru. Adazipeza chifukwa cha kumvetsa bwino zinthu. Ndiye amene adakonza dziko lapansi kuti likhalepo mpaka muyaya, nalidzaza ndi nyama zamitundumitundu. Amatuma kuwala, ndipo kumapitadi. Amakuitana kuwalako, ndipo kumamvera mau ake monjenjemera. Nyenyezi zimawala pamalo pamene adziikapo ndipo zimasangalala. Iye akaziitana, izo zimayankha kuti, “Tili pano” Ndipo zimawala mosangalala, kuwalira amene adazilenga. Ameneyu ndiye Mulungu wathu, palibe wina wofanafana naye. Iye adatulukira njira zonse zofikira ku nzeru, nzeruzo adazipatsa Yakobe mtumiki wake, adazipatsa Israele wokondedwa wake. Pambuyo pake nzeruzo zidadzaoneka pansi pano nkudzakhazikika pakati pa anthu. Nzeru ndiye Buku la Malamulo a Mulungu. Malamulo ake odzakhala mpaka muyaya. Onse ozigwiritsa nzeruzo, amakhala ndi moyo, koma olekana nazo amafa. Bwerera Yakobe, udzalandire nzeru, yenda molondola kuwala kwa kuyera kwake. Ulemerero wako usapatse munthu wina, madalitso ako usawapereke kwa anthu achilendo. Inu Aisraele, ifetu ndife odala, chifukwa timadziwa zokomera Mulungu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 19:8-11.

 

Muli ndi uthenga wopatsa moyo wosatha, Ambuye.

 

Malangizo a Chauta ndi olungama,

Amasangalatsa mtima,

Malamulo a Chauta ndi olungama,

Amapatsa mtima womvetsa.

 

Muli ndi uthenga wopatsa moyo wosatha, Ambuye.

 

Kuwopa Chauta ndiye chinthu changwiro,

Chimakhala mpaka muyaya.

Chiweruzo cha Chauta nchoona,

Ncholungama nthawi zonse.

 

Muli ndi uthenga wopatsa moyo wosatha, Ambuye.

 

Zonsezi nzoyenera kuzikhumbira kupambana golide,

Ngakhale golide wambiri wamtengowapatali,

Nzotsekemera kupambana uchi,

Ngakhale uchi wozuna kwambiri.

 

Muli ndi uthenga wopatsa moyo wosatha, Ambuye.

--------------------------------------

 

7. MAU A M’BUKU LA MPROFETI EZEKIELE; EZEKIELE 36:16-28. (Ndidzakuwazani madzi angwiro, ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano).

 

Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti: “Munthu iwe, pamene Aisraele ankakhala m’dziko lao, adaliipitsa ndi makhalidwe oipa ndiponso ndi zochita zao. Ndidaona kuti makhalidwe ao anali onyansa pa za chipembedzo, ngati mkazi amene ali kunthawi yake. Ndidawalanga mokalipa chifukwa cha magazi a anthu amene iwo adakhetsa m’dzikomo, ndiponso chifukwa cha mafano amene iwo adaipitsa nawo dzikolo. Ndidawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina, ndipo ndidawabalalitsira ku maiko osiyanasiyana. Ndidawalanga potsata makhalidwe ao ndi ntchito zao. Atafika pakati pa anthu a mitundu inayo, kulikonse kumene ankapita, adaipitsa dzina langa loyera. Zidatero chifukwa anthu ponena za iwowo ankati, ‘Awa ndi anthu a Chauta, koma onani adachotsedwa ku dziko lake.’ Komabe Ineyo ndinkadera nkhawa dzina langa loyera, limene Aisraele adaliipitsa pamene ankakhala pakati pa anthu a mitundu ina kumene adapita. Nchifukwa chake Aisraelewo uwauze kuti Ine Ambuye Chauta mau anga ndi awa: ‘Zimene nditi ndichite, sindichita chifukwa cha inuyo Aisraelenu ai, koma chifukwa cha dzina langa loyera limene mudalipiitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene mudapita. Dzina langa lotchuka limene lakhala lonyozeka pakati pa anthu a mitundu ina, ndidzaonetsa kuti nloyera. Tsono anthu a mitundu inayo atazindikira kuti ndaonetsa kuyera kwa dzina langa mwa inu, adzadziwa kuti Ine ndine Chauta. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Ndidzakutulutsani pakati pa mitundu inayo, ndidzakusonkhanitsani kuchokera ku dziko lililonse, ndipo ndidzakubwezani ku dziko lanu. Ndidzakuwazani madzi angwiro, ndipo mudzayera, zonse zokuipitsani zidzachoka. Ndiponso ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse. Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kulowetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzakuchotserani mtima wanu wouma ngati mwalawo ndi kukupatsani mtima wofewa ngati mnofu. Ndidzaika mzimu wanga mwa inu, ndipo ndidzakutsatitsani malangizo anga, ndi kukusungitsani malamulo anga mosamala kwambiri. Mudzakhala m’dziko limene ndidapatsa makolo anu. Inu mudzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wanu.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

A. Ngati palibe anthu oti abatizidwe

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 42: 02, 04; 43: 03, 04.

 

Monga momwe mbawala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m’mene mtima wanga

umakhumbira Inu Mulungu wanga.

 

Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Mulungu,

Mulungu wamoyo,

Kodi ndidzafika liti pamaso pa Mulungu?

 

Monga momwe mbawala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga

umakhumbira Inu Mulungu wanga.

 

Mtima wanga umawawa ndikamakumbukira m’mene ndinkayendera ndi chinamtindi cha anthu,

Powatsogolera ku Nyumba ya Mulungu.

Panali khwimbi la anthu ofuula mosangalala,

Akuimba nyimbo zothokoza ndipo akuchita chikondwerero.

 

Monga momwe mbawala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga

umakhumbira Inu Mulungu wanga.

 

Tumizani kuwala kwanu ndi choona chanu kuti zinditsogolere.

Zindifikitse ku phiri lanu loyera, kumalo kokhala Inu.

 

Monga momwe mbawala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga

umakhumbira Inu Mulungu wanga.

Tsono ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu,

Kwa Mulungu amene amandipatsa chimwemwe chopambana,

Ndipo ndidzakutamandani ndi pangwe, Inu Mulungu, Mulungu wanga.

 

Monga momwe mbawala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga

umakhumbira Inu Mulungu wanga.

--------------------------------------

 

B. Ngati pali anthu oti abatizidwe.

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 51:10-13,16,17.

 

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu.

 

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu,

Muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika,

Musandipirikitse pamaso panu,

Musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine.

 

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu.

 

Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu,

Mulimbitse mwa ine mtima womvera,

Pamenepo ochimwa ndidzawaphunzitsa njira zanu,

Ndipo iwo adzabwerera kwa Inu.

 

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu.

 

Si nsembe wamba imene Inu imakusangalatsani,

Ndikapereka nsembe yopsereza, sibwenzi Inu mutakondwera nayo.

Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika.

Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza.

 

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu.

--------------------------------------

 

8. MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 6:3-11. (Tikudziwa kuti Khristu adauka kwa akufa, ndipo sadzafanso).

 

Abale, kodi inu simukudziwa kuti tonse amene tidasanduka amodzi ndi Khristu Yesu pakubatizidwa, ndi ubatizo womwewo tidasandukanso amodzi ndi Iye mu imfa yake? Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m’manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano. Ngati takhala amodzi ndi Khristu mu imfa yake, momwemonso tidzakhala amodzi naye pa kuuka kwa akufa, monga momwe adaukira Iyeyo. Tidziwa kuti mkhalidwe wathu wakale udapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kuti khumbo lathu lokonda machimo liwonongeke, ndipo tisakhalenso akapolo a uchimo. Pakuti munthu akafa, ndiye kuti wamasuka ku mphamvu ya uchimo. Tsono ngati tidafa pamodzi ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo pamodzi ndi Iye. Tikudziwa kuti Khristu adauka kwa akufa, ndipo sadzafanso. Imfa ilibenso mphamvu pa Iye. Kufa kumene adafako kunali kufa kolekana ndi uchimo, ndipo adafa kamodzi kokhako. Tsono moyo umene ali nawo tsopano ndi moyo woperekedwa kwa Mulungu. Momwemonso inuyo mudziwone ochita ngati kufa nkulekana ndi uchimo, koma okhala ndi moyo wotumikira Mulungu, mogwirizana ndi Khristu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—SALIMO 118:1-2, 16-17, 22-23.

 

Alleluia – (Wansembe aimba katatu, ndipo anthu abwereza)

Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, ndipo chikondi chake nchamuyaya. Aisraele anene kuti, “Chikondi chake nchamuyaya.”

 

Alleluia – Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu, dzanja lamanja la Chauta lapambana, dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu. Sindidzafa, ndidzakhala moyo, ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta.

 

Alleluia – Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya. Chauta ndiye amene wachita zimenezi, zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu. – Alleluia, Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 24:1-12 (Mukudzafuniranji munthu wamoyo pakati pa anthu akufa?)

 

M’mamawa pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, azimai aja adapita ku manda, atatenga zonunkhira zimene adaakakonza. Adapeza chimwala chija chili chogubuduza kale kuchoka pakhomo pa manda aja. Adalowa m’mandamo koma sadaupeze mtembo wa Ambuye Yesu. Akadali othedwa nzeru choncho pa zimenezo, adangoona anthu awiri ovala zovala zonyezimira ataimirira pafupi ndi iwo. Akazi aja adachita mantha naweramitsa nkhope zao pansi. Anthuwo adawafunsa kuti, “Mukudzafuniranji munthu wamoyo pakati pa anthu akufa? Sali muno ai, wauka. Kumbukirani zimene adaakuuzani akadali ku Galileya. Paja adaakuuzani kuti, Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa m’manja mwa anthu ochimwa, kupachikidwa pa mtanda, ndi kuuka kwa akufa patapita masiku atatu.” Apo akazi aja adawakumbukiradi mauwo, ndipo atabwerako kumanda kuja, adasimbira zonsezo ophunzira khumi ndi mmodzi aja, ndi anthu ena onse. Azimaiwo anali Maria wa ku Magadala, Yohane, ndi Maria, amake a Yakobo. Iwo pamodzi ndi anzao ena adasimbira atumwi aja zonsezi. Koma zimenezo atumwiwo adangoziyesa zam’kutu, mwakuti sadawakhulupirire azimaiwo. Komabe Petro adanyamuka nathamangira ku manda. Adaweramiramo naona nsalu zamaliro zokha, kenaka nkubwerera kunyumba akudabwa ndi zimene zidaachitikazo.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, podziwa kuti Yesu Khristu wouka kwa akufa alikukhaladi pakati pathu, tiyeni, pamodzi naye, tiwapempherere anthu onse:

 

1.     Eklezia alimbitse chikhulupiriro m’mitima ya anthu a mafuko onse, pakuwalalikira za kuuka kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akhristu amene akuzunzika chifukwa cha Mthenga Wabwino alimbike m’chikhulupiriro pozindikira kuti Yesu Khristu ali nao pafupi.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akatekumeni amene alandira Ubatizo leroli nawonso amuchitire Yesu Khristu umboni pamaso pa anthu anzao pakuwaonetsa makhalidwe a chikondi.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe tili muno tizidzetsa chimwemwe cha Pasaka m’mitima ya anzathu pakuwatumikira mwachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, popereka kwa Inu mapemphero athu amenewa, tilikuyamika kukoma mtima kwanu, chifukwa simulephera kukwaniritsa malonjezo anu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...