Thursday, April 17, 2025

LACHISANU LOYERA LA KUZUNZIKA NDI KUFA KWA AMBUYE—C

LACHISANU LOYERA LA KUZUNZIKA NDI KUFA KWA AMBUYE—C

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 52:13-53:12 (Adambaya chifukwa cha machimo athu).

 

Chauta akuti, “Mtumiki wanga adzapambana pa ntchito yake. Adzakwezedwa ndi kulemekezedwa, ndipo adzalandira ulemu waukulu kwambiri. Anthu ambiri atamuwona adadzidzimuka, chifukwa nkhope yake inali itasakazika, kotero kuti sinkachitanso ngati ya munthu. Maonekedwe ake sanalinso ngati a munthu. Chimodzimodzinso anthu a mitundu yonse adzadodoma naye, Mafumu omwe adzasowa naye chonena, popeza kuti zinthu zosawauzapo chiyambire adzaziona, ndipo zinthu zosamvapo nkale lonse, adzazimvetsa. Ndani wazikhulupirira zimene tamvazi? Ndani wazindikira mphamvu za Chauta pa zimenezi? Pajatu mtumiki wake uja adakula ngati chiphukira pamaso pa Mulungu, ndiponso ngati muzu m’nthaka youma. Iye analibe maonekedwe enieni kapena nkhope yabwino, kuti ife nkumamuyang’ana. Analibe kukongola koti ife nkukokeka naye. Iye uja anthu adamnyoza ndipo adamkana. Anali munthu wamasautso, wozolowera zowawa.

 

Anali ngati munthu amene anzake amaphimba kumaso akamuwona. Anthu adamnyoza, ndipo ife sitidamuyese kanthu. “Ndithudi, iye adapirira masautso amene tikadayenera kuwamva ifeyo, ndipo adalandira zowawa zimene tikadayenera kuzilandira ifeyo. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumlanga, ndi kumkantha ndi kumsautsa. Koma adam’baya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa. Tonse tidaasokera ngati nkhosa. Aliyense mwa ife ankangodziyendera. Ndipo Chauta adamsenzetsa iyeyo machimo athu. Anthu adamsautsa ndi kumzunza, koma iye sadalankhule kanthu. Monga momwe amachitira mwanawankhosa wopita naye kuti akamuphe, ndiponso monga momwe nkhosa imakhalira duu poimeta, nayenso adangokhala chete. Adamgwira mwankhanza namuzenga mlandu, ndipo adapita naye kukamupha. Mwa anthu anzake ndani adalabadako zoti iye adachotsedwa m’dziko la anthu amoyo? Ndani adalabadako kuti iye uja adalangidwa chifukwa cha machimo a anthu? Adamkonzera manda ake pakati pa manda a achifwamba. Adamuika m’manda pakati pa anthu olemera, ngakhale iye sadachitepo chosalungama chilichonse ndipo sadanene bodza lililonse. Komabe ndi Chauta yemwe amene adaafuna kuti amuzunze, ndipo adamsautsadi. Iye adapereka moyo wake kuti ukhale nsembe yokhululukira machimo.

 

Choncho adzaona zidzukulu zake, adzakhala ndi moyo wautali, ndipo chifuniro cha Chauta chidzachitika mwa iye. Atatha mazunzo akewo, adzaona phindu lake, ndipo adzakhutira. Mwanzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzasenza machimo a anthu onse kuti ambiri a iwo asadzapezekenso kuti ndiopalamula. Motero Ine ndidzampatsa ulemu woyenerera akuluakulu. Adzagawana zofunkha ndi ankhondo amphamvu, popeza kuti adapereka moyo wake mpaka kufa, ndipo adamuyesa mnzao wa anthu ophwanya malamulo. Adasenza machimo a anthu ambiri, ndipo adawapempherera ochimwawo kuti akhululukidwe.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 31:1. 5. 11-12. 14-16. 24.

 

Atate, ndikupereka Mzimu wanga m’manja mwanu.

 

Ndimathawira kwa Inu Chauta,

Musalole kuti ndichite manyazi,

Koma mundipulumutse chifukwa ndinu Mulungu wolungama,

Ndikupereka moyo wanga m’manja mwanu,

Inu Chauta wokhulupirika, mwandiwombola.

 

Atate, ndikupereka Mzimu wanga m’manja mwanu.

 

Adani anga onse amandinyodola,

Anzanga omwe amandiyesa chinthu chonyansa,

Anthu odziwana nawo amandiyesa chinthu choopsa.

 

Atate, ndikupereka Mzimu wanga m’manja mwanu.

 

Anthu ondiwona mu mseu amandithawa,

Andiwala kotheratu ngati munthu wakufa,

Ndasanduka ngati chiwiya chosweka.

 

Atate, ndikupereka Mzimu wanga m’manja mwanu.

 

Koma ndimadalira Inu Chauta,

Ndimati, “Inu ndinu Mulungu wanga,”

Masiku anga ali m’manja mwanu,

Pulumutseni kwa adani anga ndi kwa ondizunza.

 

Atate, ndikupereka Mzimu wanga m’manja mwanu.

 

Yang’aneni mtumiki wanune mwa kukoma mtima kwanu,

Pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika,

Khalani a mphamvu ndipo mulimbe mtima,

Inu nonse okhulupirira Chauta.

 

Atate, ndikupereka Mzimu wanga m’manja mwanu.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A MKALATA KWA AHEBRI: AHEBRI 4:14-16; 5:7-9. (Adaphunzira kumvera pakumva zowawa ndipo adakhala gwero la

chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye).

 

Abale, tiyeni tsono, tigwiritse chikhulupiriro chimene timavomereza. Pakuti tili naye Mkulu wa ansembe wopambana, amene adapita mpaka kukafika kumwamba kwenikweni kwa Mulungu. Iyeyu ndi Yesu, Mwana wa Mulungu. Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse. Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko

tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthawi yake yeniyeni. Yesu, pa nthawi imene anali munthu pansi pano, mofuula ndi molira misozi, adapereka mapemphero ndi madandaulo kwa Mulungu, amene anali nazo mphamvu zompulumutsa ku imfa. Ndiye popeza kuti Yesu adaadzipereka modzichepetsa, Mulungu adamvera mapemphero ake. Motero Yesu, ngakhale anali Mwana wa Mulungu, adaphunzira kumvera pakumva zowawa. Atasanduka wangwiro kotheratu, adakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye.

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AFILIPI 2:8-9.

 

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Ambuye, adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda. Chifukwa chake chimene Mulungu adamkweza kopambana, nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: KUSAUKA KWA YESU KHRISTU AMBUYE ATHU MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 18:1—19: 42.

 

W – Wowerenga; Y – Yesu; M – Munthu; A – Anthu ena.

 

Kusauka kwa Yesu Khristu Ambuye athu monga adalembera Yohane Woyera.

 

1. Ku Getsemani.

 

W. Yesu atanena zimenezi, adapita ndi ophunzira ake kutsidya kwa kamtsinje ka Kedroni. Kumeneko kunali munda, ndipo adalowa m’menemo. Yudasi yemwe, amene adapereka Yesu kwa adani ake, ankawadziwa malowo, pakuti Yesu ankapita kumeneko kawirikawiri ndi ophunzira ake. Yudasiyo adatenga gulu la asilikali achiroma pamodzi ndi asilikali a ku Nyumba ya Mulungu amene akulu a ansembe ndi Afarisi adaawatuma. Iwo adapita kumundako atatenga nyale ndi miyuni ndi zida zankhondo. Yesu adaadziwiratu zonse zimene zinalikudzamugwera. Nchifukwa chake Iye adaima poyera, nawafunsa kuti:

 

Y. Kodi mukufuna yani?

 

W. Adamuyankha kuti:

 

A. Tikufuna Yesu wa ku Nazarete.

 

W. Yesu adati:

 

Y. Ndine, ndilipo.

 

W. Yudasi, wompereka kwa adani ake uja, anali nao pomwepo. Pamene Yesu adawayankha kuti, “Ndine, ndilipo”, iwo adabwerera m’mbuyo nagwa pansi. Yesu adawafunsanso kuti:

 

Y. Mukufuna yani kodi?

 

W. Iwo aja adati:

 

A. Tikufuna Yesu wa ku Nazarete.

 

W. Yesu adati:

 

Y. Ndakuuzani kuti ndine, ndilipo. Tsono ngati mukufuna Ine, awa alekeni apite.

 

W. (Adaatero kuti zipherezere zimene lye adaanena kale kuti, “Sindidatayepo ndi m’modzi yemwe mwa amene mudandipatsa.”) Simoni Petro anali ndi lupanga. Adalisolola, natema kapolo wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu la ku dzanja lamanja. Kapoloyo dzina lake anali Malkusi. Apo Yesu adauza Petro kuti:

 

Y. Bwezera lupanga lako m’chimake. Kodi ukuti ndisamwe chikho cha masautso chimene Atate andipatsa?

 

W. Gulu la asilikali achiroma lija, pamodzi ndi mtsogoleri wao, ndiponso asilikali achiyuda, adagwira Yesu nam’manga. Poyamba adapita naye kwa Anasi, chifukwa anali mpongozi wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe onse chaka chimenecho. Kayafayo ndi yemwe uja amene adaalangiza anzake kuti nkwabwino koposa kuti munthu mmodzi afe m’malo mwa anthu onse.

 

Kanyimbo

 

2. Kwa mkulu wa ansembe

 

W. Simoni Petro ndi wophunzira wina adatsatira Yesu. Wophunzira winayo anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe onse. Tsono iye adalowa pamodzi ndi Yesu m'bwalo la nyumba ya

mkulu wa ansembeyo. Koma Petro adaima pa khomo kunja. Wophunzira wina uja, amene anali wodziwikayo, adatuluka nakalankhula ndi mtsikana wolonda pa khomo, nkumulowetsa Petroyo. Mtsikanayo adafunsa Petro kuti:

 

M. Kodi inu sindinunso mmodzi mwa ophunzira a munthuyu?

 

W. Iye adati:

 

M. Ineyo? Iyai.

 

W. Antchito pamodzi ndi asilikali achiyuda aja adaaimirira pamenepo atasonkha moto nkumaotha, chifukwa kunkazizira. Petro nayenso adaaimirira pomwepo kumaotha nao motowo. Tsono mkulu wa ansembe onse adafunsa Yesu za ophunzira ake, ndiponso za zimene Iye ankaphunzitsa. Yesu adati:

 

Y. Ine ndinkalankhula mosabisa pamaso pa anthu onse. Ndinkaphunzitsa m’nyumba zamapemphero ndiponso m’Nyumba ya Mulungu, m’mene anthu onse amasonkhana. Sindidalankhule kanthu mobisa ai. Nanga tsono mukundifunsiranji Ineyo? Funsani amene adamva zomwe ndinkawauza. Iwowo akudziwa zimene ndinkanena.

 

W. Atanena zimenezi, mmodzi mwa asilikali oimirira pomwepo adamenya Yesu kumaso, adati, Ungayankhe choncho kwa mkulu wa ansembe onse?

 

M. Yesu adamuyankha kuti:

 

Y. Ngati ndalankhula moipa, chitchule choipacho. Koma ngati ndalankhula moona, ukundimenyeranji?

 

W. Anasi adatumiza Yesu ali chimangire kwa Kayafa, mkulu wa ansembe onse. Simoni Petro anali chililibe akuwotha nao moto. Tsono ena adamufunsa kuti:

 

A. Kodi iwenso sindiwe mmodzi mwa ophunzira a munthu uja?

W. Petro adakana, adati:

 

M. Iyai.

 

W. Wantchito wina wa mkulu wa ansembe onse, mbale wa munthu uja amene Petro adaamusenga khutu, adamufunsa kuti:

 

M. Kodi sindidakuwone m’munda muja uli naye?

 

W. Petro adakananso, nthawi yomweyo tambala adalira.

 

Kanyimbo

 

3. Kwa Pilato

 

W. Adamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita naye ku bwalo la bwanamkubwa. Akuluakulu a Ayuda sadalowe nao m’bwalo la bwanamkubwalo, kuwopa kuti angaipitsidwe,

pakuti ankafuna kudya phwando la Pasaka. Motero Pilato adatulukira kwa iwo nawafunsa kuti:

 

M. Mwampeza cholakwa chanji munthuyu?

 

W. Iwo adati:

 

A. Akadapanda kuchita choipa ameneyu, sibwenzi titadzampereka kwa inu ai.

W. Choncho Pilato adawauza kuti:

 

M. Mtengenitu tsono inuyo, mukamuweruze potsata malamulo anu.

 

W. Koma Ayudawo adati:

 

Y. Ife sitiloledwa kupha munthu ai.

 

W. (Zidaatero kuti zipherezere zimene Yesu adaanena za imfa yake.) Pilato adalowanso m’nyumba yake ija, naitana Yesu. Adamufunsa kuti:

 

M. Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?

 

M. Yesu adati:

 

Y. Kodi mukunena zimenezi mwa inu nokha, kapena ena adakuuzani za Ine?

 

W. Pilato adati:

 

M. Ine ndine Myuda kodi? Anthu a mtundu wako womwe ndiponso akulu a ansembe ndiwo akupereka kwa ine. Udachita chiyani?

 

W. Yesu adayankha kuti:

 

Y. Ufumu wanga si wapansi pano ai. Ufumu wanga ukadakhala wapansi pano, bwenzi anyamata anga atamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa akulu a Ayuda. Komatu ai, ufumu wanga si wapansi pano.

 

W. Pilato adati:

 

M. Tsono ndiye kuti ndiwedi mfumu, ati?

 

W. Yesu adati:

 

Y. Mwanena nokha kuti ndine mfumu. Ine ndidabwera pansi pano ndipo ndidabadwa kuti ndidzachitire umboni choona. Aliyense wokonda choona amamva mau anga.

 

W. Pilato adamufunsa kuti:

 

M. Choona nchiyaninso?

 

W. Pilato atanena mau amenewa, adatulukiranso kwa Ayuda, nawauza kuti:

 

M. Ine munthuyu sindikumpeza chifukwa chilichonse. Koma potsata chizolowezi chanu, pa nthawi ya chikondwerero cha Pasaka ndimakumasulirani mkaidi mmodzi. Tsono kodi

mukufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayudayi?

W. Pamenepo iwo adafuulanso kuti:

 

A. Ameneyu ai, koma Barabasi.

W. (Barabasiyo anali chigawenga.)

 

Kanyimbo

 

4. Pilato alola kuti Yesu aphedwe.

 

W. Pamenepo Pilato adalamula kuti atenge Yesu ndi kumkwapula. Tsono asilikali adaluka nsangamutu yaminga naiika pamutu pake. Adamuveka chovala chofiirira, nadza kwa Iye

nkumanena kuti:

A. Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda!

W. Ndipo adayamba kumuwomba makofi. Pilato adatulukanso nauza Ayudawo kuti:

M. Onani, ndikumtulutsira kuli inu kuno kuti mudziwe kuti sindikumpeza chifukwa chilichonse.

W. Pamene Yesu adatuluka, atavala sangamutu ija ndi chovala chofiirira chija, Pilato adati:

M. Nayutu munthu uja.

W. Akulu a ansembe ndi asilikali a ku Nyumba ya Mulungu aja ataona Yesu, adafuula kuti:

 

A. Mpachikeni! Mpachikeni!

W. Pilato adawauza kuti:

M. Mtengeni inuyo mukampachike, ine ndiye sindikumpeza chifukwa.

W. Anthuwo adati:

A. Ife tili ndi lamulo, ndipo potsata lamulolo ayenera kufa, chifukwa ankati, ‘Ndine Mwana wa Mulungu.’

W. Pamene Pilato adamva mau amenewa, adachita mantha kwa basi. Tsono adalowanso m’nyumba ya bwanamkubwa ija nafunsa Yesu kuti:

M. Kodi iwe, kwanu nkuti?

W. Koma Yesu sadayankhe kanthu. Pamenepo Pilato adamufunsa kuti:

M. Sukundiyankha? Kodi sukudziwa kuti ine ndili ndi mphamvu zokumasula, ndiponso mphamvu zokupachika?

W. Yesu adati, “Akadapanda kukupatsani mphamvu zimenezo Mulungu, sibwenzi mutakhala nazo konse mphamvu pa Ine. Nchifukwa chake amene wandipereka kwa inu ali ndi tchimo

lalikulu koposa.”

 

W. Atamva mau amenewa, Pilato adafuna ndithu kummasula Yesu. Koma Ayuda adafuula kuti:

 

A. Mukammasula ameneyu, sindinu bwenzi la Mfumu ya ku Roma. Aliyense wodziyesa mfumu, ngwoukira Mfumu ya ku Romayo.

 

W. Pilato atamva zimenezo, adatulutsa Yesu, nakakhala pa mpando woweruzira milandu, pa malo otchedwa “Bwalo lamiyala” (pa Chiyuda amati “Gabata”). Linali tsiku lokonzekera chikondwerero cha Pasaka, ndipo nkuti nthawi ili ngati 12 koloko masana. Pilato adauza Ayuda kuti:

 

M. Nayitu Mfumu yanu.

 

W. Koma iwo adafuula kuti:

 

A. Mchotseni! Mchotseni! Kampachikeni pa mtanda!

 

W. Pilato adawafunsa kuti:

 

M. Ndipachike Mfumu yanu kodi?

 

W. Akulu a ansembe adati:

 

A. Tilibe mfumu ina ai, koma Mfumu ya ku Roma yokha.

W. Pamenepo Pilato adapereka Yesu kwa iwo kuti akampachike pa mtanda.

 

Kanyimbo

 

5. Ku Golgota.

 

W. Asilikali aja adamtenga Yesu. Iye atasenza mtanda wake, adatuluka naye mu mzinda kupita ku malo otchedwa “Malo a Chibade cha Mutu” (pa Chiyuda amati “Gologota”). Kumeneko adampachika pa mtanda. Adapachikanso anthu ena awiri, wina ku dzanja lake lamanja, wina ku dzanja lake lamanzere, Yesu pakati. Pilato adalemba chidziwitso nachiika pamtandapo. Adaalembapo kuti, “Yesu wa ku Nazarete, Mfumu ya Ayuda.” Ayuda ambiri adachiwerenga chidziwitsocho, chifukwa pamalo pamene Yesu adaapachikidwapo panali pafupi ndi minda wa Yerusalemu. Chidziwitsocho chidalembedwa m’chilankhulo cha Ayuda, cha Aroma, ndiponso cha Agriki. Akulu a ansembe a Ayuda adauza Pilato kuti, “Musalembe kuti, ‘Mfumu ya Ayuda ai, koma kuti, ‘Iyeyu ankati Ndine Mfumu ya Ayuda.’”

 

W. Koma Pilato adati:

M. Zimene ndalemba, ndalemba ndatha basi.

 

W. Asilikali aja atapachika Yesu, adatenga zovala zake, nazigawa panai, msilikali aliyense chigawo chake. Adatenganso mkanjo wake. Mkanjowo unali wolukidwa kuyambira pamwamba mpaka pansi, opanda msoko. Tsono asilikaliwo adauzana kuti:

 

A. Tisaung’ambe, koma tichite mayere kuti tiwone ukhala wa yani.

 

W. Zidaayenda choncho kuti zipherezere zimene Malembo adanena kuti, “Adagawana zovala zanga, ndipo mkanjo wanga adauchitira mayere.” Zimenezi adachitadi asilikali aja. Pafupi ndi mtanda wa Yesu padaaimirira amai ake, ndi m’bale wa amai akewo, Maria mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa ku Magadala. Pamene Yesu adaona amai ake ndi wophunzira uja amene Iye ankamukonda kwambiri, akuimirira pafupi, adauza amai ake kuti:

 

Y. Mai, nayu mwana wanu.

 

W. Adauzanso wophunzirayo kuti:

 

Y. Nawa amai ako.

 

W. Ndipo kuyambira pamenepo wophunzirayo adawatenga amaiwo kumakawasamala kwao. Yesu adaadziwa kuti tsopano zonse wakwaniritsa. Tsono kuti zipherezere zimene Malembo adaanena, Iye adati: Ndili ndi ludzu.

 

W. Pomwepo panali mbiya yodzaza ndi vinyo wosasa. Asilikali aja adaviika chinkhupule m’vinyo wosasayo, nkuchitsomeka ku kamtengo ka hisope, nachifikitsa pakamwa pake. Yesu atalandira vinyo wosasayo adati:

 

Y. Zonse ndakwaniritsa.

 

W. Kenaka adaweramitsa mutu, napereka mzimu.

 

Onse agwade ndi kukhala chete kwa kanthawi.

 

Kanyimbo

 

6. Aika maliro.

 

W. Linali tsiku lokonzekera chikondwerero cha Pasaka. Akulu a Ayuda sadafune kuti mitemboyo ikhalebe pa mtanda pa tsiku la Sabata, chifukwa Lasabata limenelo linali lalikulu. Nchifukwa chake adakapempha Pilato kuti alamule kuti akathyole miyendo ya anthu opachikidwa aja, nkuwachotsa. Tsono asilikali adabwera, nathyola miyendo ya mmodzi mwa awiri aja amene adaapachikidwa pamodzi ndi Yesu. Adateronso ndi mnzake uja. Koma pamene adafika pa Yesu, poona kuti wafa kale, sadathyole miyendo yake. Koma mmodzi mwa asilikali aja adamubaya m’nthiti mwake ndi mkondo, ndipo nthawi yomweyo mudatuluka magazi ndi madzi. Amene adaona zimenezi ndiye akuzichitira umboni, kuti inunso mukhulupirire. Umboni wakewo ngwoona, ndipo mwiniwakeyo akudziwa kuti zimene akunena zoona. Izi zidaatero kuti zipherezere zimene Malembo adanena kuti, “Sadzathyola fupa lake ndi limodzi lomwe.” Ndipo penanso Malembo akuti, “Anthu azidzamuyang’ana amene iwo adamubaya.”

 

Kanyimbo

 

W. Pambuyo pake Yosefe wa ku Arimatea adapempha Pilato kuti amlole kukachotsa mtembo wa Yesu. (Yosefeyo anali wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa choopa akulu a Ayuda.) Tsono Pilato atamlola, iye adakachotsa mtembowo. Kudabweranso Nikodemo, yemwe uja amene adaabwera kwa Yesu usiku poyamba paja. Iye adabwera ndi mafuta onunkhira a mure osanganiza ndi aloe, kulemera kwake ngati makilogaramu 32. Anthu awiriwo adatenga mtembo wa Yesu, naukulunga m’nsalu zoyera zabafuta pamodzi ndi zonunkhira zija, potsata mwambo wamaliro wachiyuda. Kumene Yesu adaapachikidwako kunali munda. Ndipo m’mundamo munali manda atsopano, amene anali asanaikemo munthu. Tsono popeza kuti linali tsiku la Ayuda lokonzekera chikondwerero cha Pasaka, ndipo mandawo anali pafupi, adaika Yesu m’menemo.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero aakulu a Akhristu.

 

1. Kupempherera Eklezia.

Abale okondeka, tipempherere Eklezia, Mpingo Woyera wa Mulungu, kuti Chauta Atate amphamvuzonse auwongolere ndi kuusonkhanitsa pamodzi, auteteze m’dziko lonse lapansi ndipo motero tizipembedza Mulungu wathu mwaufulu pokhala ndi moyo wabata ndi wamtendere.

 

Apemphera cha mumtima kwa kanthawi pang’ono.

 

Mulungu Wamphamvuzonse ndi wamuyaya, mwa Mwana wanu Yesu Khristu mudaonetsa anthu a mafuko onse ulemerero wanu. Mwa chifundo chanu chokonda Mpingo wanu, muusamale ndi kuuteteza kosalekeza, kuti ukhale ndi chikhulupiriro cholimba polalika dzina lanu ndi kubalalika ponse ponse m’dziko lino lapansi. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.

 

2. Kupempherera Papa.

Tipempherere Papa wathu Francisco amene Chauta Mulungu wathu adampatula kuti akhale mkulu woyang’anira Eklezia yense. Ambuye amteteze ndi kumlimbikitsa, kuti azitsogolera bwino mpingo Woyera wa Mulungu.

 

Mulungu wamphamvu zonse ndi wamuyaya, mumaongolera zinthu zonse monga momwe mudatsimikizira. Mwa chifundo chanu muteteze mkulu amene mudamsankha kuti akhale Papa wathu. Ndipo potitsogolera iyeyo mutithandize ife tonse a m’Mpingo mwanu kukhala ndi chikhulupiriro chozama. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.

 

3. Kupempherera Ansembe ndi Akhristu onse.

Tipempherere Episkopi wathu..., aepiskopi onse, ansembe, adikoni, ndi ena onse amene akutumikira Mpingo wanu, ndiponso akhristu eni ake onse.

 

Mulungu wamphamvuzonse ndi wamuyaya, Inu amene Mzimu wanu ukuyeretsa ndi kuwongolera Mpingo wanu wonse, mumvere mapemphero athu ndi kutithandiza kuti tizitumikira Mpingo wanu mokhulupirika, aliyense molingana ndi udindo wake. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.

 

4. Kupempherera Akatekumeni.

Tipempherere akatekumeni athu kuti Chauta Mulungu wathu aongolere nzeru zao ndi mitima yao, iwo azikhulupirira chikondi chake mpaka kuti adzakhululukidwe machimo ndi kusanduka anthu ake a Yesu Khristu pakubadwanso m’madzi a Ubatizo.

 

Mulungu wamphamvuzonse ndi wamuyaya, Inu amene mumadalitsa Mpingo wanu kosalekeza pakuupatsa ana atsopano, muwaonjezere nzeru ndi chikhulupiriro akatekumeni athu, kuti iwonso adzabadwe ndi moyo watsopano ndi kusanduka ana anu polandira Ubatizo. Mwa Yesu Khristu

Ambuye athu. Amen.

 

5. Kupempherera Umodzi wa Akhristu.

Tipempherere abale onse amene akhulupirira Yesu Khristu nayesetsa kutsata zoona, kuti Chauta Mulungu wathu awasonkhanitse pamodzi ndi kuwasunga onse mu Mpingo wake umodzi.

 

Mulungu wamphamvuzonse ndi wamuyaya, mumasonkhanitsa pamodzi anthu amene adamwazikana ndipo mumawakhazika pamodzi, muyang’ane ndi chifundo iwo onse amene atsata Mwana wanu Yesu Khristu. Pakuti onsewo adayeretsedwa ndi Ubatizo umodzi, muwalunzitse m’chikondi chanu kuti akhalenso ogwirizana m’chikhulupiriro chathunthu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.

 

6. Kupempherera Ayuda.

Tipempherere Ayuda, pakuti adayamba ndiwo kumva mau a Mulungu, kuti azinka nakonderakondera dzina la Chauta ndi kusunga chipangano chake mokhulupirika.

 

Mulungu wamphamvuzonse ndi wamuyaya, Inu amene mudapatula Abraham ndi zidzukulu zake kuti akhale fuko lanu loyenera kudzalandira madalitso omwe mudawalonjeza, mwa chifundo chanu mverani mapemphero a Mpingo wanu, muwafikitse anthu anuwo ku chipulumutso

chodzaza. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.

 

7. Kupempherera amene ali osakhulupirira Yesu Khristu.

Tipempherere anthu amene ali osakhulupirira Yesu Khristu, kuti Mzimu Woyera awaunikire ndi kuwandoloza m’njira ya chipulumutso.

Mulungu wamphamvuzonse ndi wamuyaya, muthandize iwo amene ali osakhulupirira Yesu Khristu, kuti aziyenda pamaso panu ndi mtima woona mpaka adzazindikire kuwala koona: ndipo mutithandize ife tonse kumvetsa mozama za moyo wanu wachikondi chanu chomwechi pamaso pa anthu onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.

 

8. Kupempherera amene ali osazindikira kuti Mulungu alipo.

Tipempherere iwo amene amakhulupirira kuti Mulungu palibe, kuti alimbikire kuchita zabwino pomvera umboni wamtima, mpaka adzazindikire kuti Mulungu alipo.

 

Mulungu wamphamvuzonse ndi wamuyaya, mudalenga anthu kuti iwo azikufunafunani ndi mtima wonse, ndipo atakupezani aone mtendere. Muwathandize onse kuti pakati pa zovuta za moyo uno athe kuzindikira chifundo chanu chowasamalira poona ntchito zabwino za akhristu anu: ndipo motero avomere mokondwera kuti inu nokha ndinu Mulungu woona ndi atate ao a anthu onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.

 

9. Kupempherera Akulu olamulira dziko.

Tipempherere atsogoleri olamulira dziko ndi akulu onse okhala ndi maudindo, kuti Chauta Mulungu wathu aongolere nzeru zao ndi mitima yao, iwo azisenza udindo wao monga momwe Mulungu afunira, ndipo motero anthu ao akhale ndi mtendere ndi ufulu.

 

Mulungu wamphamvuzonse ndi wamuyaya, mumafunira anthu onse moyo wabwino ndipo mumawateteza kuti aliyense akhale nazo zabwino zoyenerera. Muthandize akulu olamulira dziko ndi ena onse okhala ndi maudindo, kuti azisenza udindo wao mokhulupirika ndi motsata chilungamo, ndipo choncho pa dziko lonse lapansi pakhale bata ndi mtendere, pakhalenso chitukuko chenicheni ndi ufulu wokhudza chipembedzo. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.

 

10. Kupempherera onse amene ali m’mavuto.

Abale okondeka, tipemphe Chauta, Atate amphamvuzonse, kuti achitire chifundo anthu onse amene ali m’mavuto: odwala alandire mphamvu, amene ali kufa apulumuke, amene ali paulendo, ayende bwino, amene ali mu ndende amasulidwe, osautsidwa apezenso ufulu; maphunzitso onama, mliri, chilala ndi zina zotero zichokeretu m’dziko lino lapansi.

 

Mulungu wamphamvuzonse ndi wamuyaya, Inu mumathunzitsa mitima ya ovutika ndi kulimbitsa olemedwa, mverani mapemphero a anthu onse amene atembenukire kwa Inu m’mavuto ao. Onsewo akondwere pozindikira kukoma mtima kowasamalira m’zosowa zao. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...