Saturday, March 15, 2025

LAMULUNGU LA 2 MU NYENGO YA LENTI – C

LAMULUNGU LA 2 MU NYENGO YA LENTI – C

“Opanda mtanda, palibe moyo wosatha.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU GENESIS: GENESIS 15:5-12.17-18. (Mulungu adachita pangano ndi Abrahamu, Tate wa chikhulupiriro).

 

Chauta adatulutsira Abramu panja, namuuza kuti, “tayang’ana kuthamboku, ndipo uwerenge nyenyezizo ngati ungathe. Iwe udzakhala ndi zidzukulu zochuluka ngati nyenyezizo.” Apo Abramu adakhulupirira Chauta, ndipo chifukwa cha chimenecho, Chauta adamuwona kuti ndi wolungama. Tsono Chauta adamuuza kuti, “Ine ndine Chauta amene ndidakutulutsa ku Uri wa ku Kaldeya, kuti ndikupatse dziko lino kuti likhale lakolako.” Koma Abramu adati, “Ambuye Chauta, kodi ndingadziwe bwanji kuti dziko limeneli lidzakhaladi langa?” Chauta adamuyankha kuti, “tandipatsa ng’ombe ya zaka zitatu, mbuzi ya zaka zitatu, nkhosa ya zaka zitatu, ndiponso njiwa ndi nkhunda.” Abramu adabwera nazo nyama zonsezo kwa Mulungu, naziduladula pakati. Adaika mabanduwo awiriawiri mopenyanapenyana, m’mizere iwiri. Koma mbalame zija sadazidule. Miphamba idadzatera kuti idye nyama zimene adaaphazo, koma Abramu adaipirikitsa. Pamene dzuwa linkalowa, Abramu adagwidwa ndi tulo tofanato, ndiponso adachita mantha kwambiri. Dzuwa litangolowa, kachisisira katagwa, mwadzidzidzi padaoneka mphika wogaduka ndi moto, pamodzi ndi nsakali yoyaka, ndipo ziwirizi zidadutsa pakati pa nyama zodulidwa zija. Pa tsiku limeneli mpamene Chauta adachita chipangano ndi Abramu nati, “ndikulonjeza kuti ndidzapatsa zidzukulu zako dziko lonseli kuyambira ku mtsinje wa ku Ejipito mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 27: 1.7-9.13-14.

 

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.

 

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa,

Ndidzaopa yani?

Chauta ndiye linga la moyo wanga,

Nanga ndichitirenji mantha?

 

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.

 

Imvani, Inu Chauta, pamene ndikulira mofuula,

Mundikomere mtima ndi kundiyankha,

Pajatu Inu mudati, “muzifunafuna nkhope yanga.”

 

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.

 

Inu Chauta, ndidzafunafuna nkhope yanu,

Musandibisire nkhope yanu,

Musandipirikitse ine mtumiki wanu mokwiya,

Inu amene mwakhala mukundithandiza.

 

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.

 

Ndikhulupirira kuti ndidzaona ubwino wake wa Chauta,

m'dziko la amoyo. Tsono khulupirira Chauta,

Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima,

Ndithu, khulupirira Chauta.

 

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AFILIPI: AFILIPI 3:17–4:1 (Iyeyo adzasandutsa matupi athu achabewa kuti akhale ofanafana ndi thupi lake laulemerero).

 

Abale anga, nonse pamodzi muzinditsanzira ine, ndipo muziwapenyetsetsa amene amayenda motsata chitsanzo chimene ife timakupatsani. Ndakhala ndikukuuzani kawirikawiri, ndipo tsopano ndikubwerezanso molira misozi, kuti pali ambiri amene mayendedwe ao akutsimikiza kuti amadana ndi mtanda wa Khristu. Mathero ao nkuwonongeka. Zosangalatsa thupi chabe ndizo zili ngati mulungu wao. Amanyadira zimene akadayenera kuchita nazo manyazi, ndipo amangoika mtima pa zapansipano zokha. Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu. Iyeyo adzasandutsa matupi athu achabewa kuti akhale ofanafana ndi thupi lake laulemerero. Adzachita zimenezi ndi mphamvu zake zomwe zija zimene angathenso kugonjetsa nazo zinthu zonse. Tsono abale anga, ndimakukondani ndipo ndikukulakalakani. Mumandisangalatsa ndipo ndinu mphotho yanga imene ndimainyadira. Okondedwa anga, limbikani choncho mogwirizana ndi Ambuye.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—MATEYO
17:5.

 

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu – Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.”Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

 

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 9:28-36 (Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake adasandulika).

 

Patapita ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau amenewa, Yesu adatenga Petro, Yohane ndi Yakobo, nakwera nawo ku phiri kukapemphera. Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake adasandulika, ndipo zovala zake zidachita kuti mbee kuyera. Nthawi yomweyo anthu awiri adayamba kucheza naye; anali Mose ndi Eliya. Maonekedwe ao anali aulemerero, ndipo ankakambirana za imfa ya Yesu imene ankayenera kukafera ku Yerusalemu. Nthawi imeneyo nkuti Petro ndi anzake ali m’tulo tofa nato. Koma pamene adadzuka, adaona ulemerero wa Yesu, ndiponso anthu awiri aja ali naye. Pamene iwo aja ankalekana naye, Petro adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Tiloleni timange misasa itatu, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.” (Sankadziwa zimene ankanena.) Akulankhula choncho, padafika mtambo nuwaphimba, ndipo ophunzirawo adagwidwa ndi mantha. Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndidamsankha, muzimumvera.” Mauwo atamveka choncho, ophunzira aja adaona kuti Yesu ali yekha. Iwo adangokhala chete masiku amenewo, osauza wina aliyense zimene adaaziwonazo.

 

Mthenga wa Ambuye… Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, potiwonetsa lero ulemerero wake, Yesu walimbitsa chikhupiriro chathu. Pokhala limodzi ndi Iyeyo, tiyeni tidziwitse Mulungu Atate athu zovuta ndi zosowa za anthu onse:

 

1.     Tipempherere akhristu onse kuti atsanzire Yesu Khristu pa zonse makamaka posenza mtanda wao.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere akatekumeni onse kuti aike mtima pa kalasi, adzakhale akhristu okhulupirika.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere odwala onse kuti apirire mavuto ao mosataya mtima pokhulupirira Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Tidzipempherere ife tomwe kuti tiziwonetsa ulemerero wachikhristu potumikira anzathu.

Tikupemphani, mutivomereze.

Inu Mulungu Atate athu, mutithandize kutsanzira Mwana wanu molimbika kuti tidzalandireko ulemu wake kutsogoloko. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...