LAMULUNGU LA 1 MU NYENGO YA LENTI – C
“Yesu Khristu atipatsa mphamvu zogonjetsera zoipa.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA DEUTERONOMO: DEUTERONOMO 26:4-10. (Zikhulupiriro za anthu olonjezedwa).
Mose adauza anthu ake kuti, “Wansembeyo ndiye amene adzakulandireni dengulo ndi kuliika patsogolo pa guwa la Chauta, Mulungu wanu. Tsono pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, muzidzanena kuti, “Kholo langa linali Lachiaramu, munthu wongoyendayenda, amene adapita ku Ejipito ndi banja lake nakakhala kumeneko. Popita kumeneko, anthuwo adaali ochepa, koma pambuyo pake adachuluka nasanduka mtundu waukulu ndi wamphamvu. Aejipito adatichita zankhanza ndi kutizunza potigwiritsa ntchito mwaukapolo. Pamenepo ife tidalirira Chauta, Mulungu wa makolo athu, kuti atithandize. Iyeyo adatimva, ndipo adaona kusauka kwathu, ntchito yolemetsa imene iwo aja ankatigwiritsa, ndiponso moyo wathu wopsinjidwawo. Mwa mphamvu zake zazikulu ndiponso ndi dzanja lake lotambalitsa, Chauta adatitulutsa ku Ejipito. Padaoneka zozizwitsa ndi zizindikiro, ndipo padachitika zinthu zoopsa zambiri. Potsiriza adatifikitsa kuno, natipatsa dziko lino, dziko lamwanaalirenji. Motero tsopano, ndikubwera kwa Chauta ndi gawo la zokolola zoyamba za m’dziko limene wandipatsa."Apo mutatula pansi dengulo pamaso pa Mulungu, mumpembedze pomwepo.”
Mau a Ambuye...Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 91:1-2,10-15.
Mukhale nane, Ambuye, pa nthawi yamavuto.
Munthu amene amakhala m’linga la Wopambanazonse,
Iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
Adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothawira kwanga, ndi linga langa,
Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Mukhale nane, Ambuye, pa nthawi yamavuto.
Zoipa sizidzakugwera,
Zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako,
Chauta adzapatsa angelo ake,
Ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite.
Mukhale nane, Ambuye, pa nthawi yamavuto.
Adzakunyamula m’manja mwao,
kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala,
Udzatha kuponda mkango ndi njoka,
Zoonadi udzaponda ndi phazi lako,
Msona wa mkango ndiponso chinjoka.
Mukhale nane, Ambuye, pa nthawi yamavuto.
Pakuti amene amandikangamira, Ine Mulungu,
Mwachikondi, ndidzampulumutsa.
Ndidzamteteza popeza kuti amadziwa dzina langa.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha,
Ndidzakhala naye pa nthawi yamavuto,
Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Mukhale nane, Ambuye, pa nthawi yamavuto.
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA 10:8-13. (Zikhulupiriro za Akhristu).
Abale, Malembo akuti chiyani? Akuti, “Mau sali nawe kutali, ali pakamwa pako, ndiponso mumtima mwako.” Amenewa ndiwo mau a chikhulupiriro amene timawalalika. Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. Chifukwa munthu amati akakhulupirira ndi mtima wake, amapezeka wolungama pamaso pa Mulungu, ndipo amati akavomereza chikhulupiriro chakecho ndi pakamwa pake, amapulumuka. Paja Malembo akuti, “Munthu aliyense wokhulupirira lye, sadzachita manyazi.” Choncho palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakuti Mulungu ndiye Ambuye a onse, ndipo amadalitsa moolowa manja onse otama dzina lake mopemba. Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.”
Mau a Ambuye...Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 4:4b.
Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu – Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 4:1-13. (Mzimu Woyera yo ankamutsogolera m’chipululu masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana ankamuyesa).
Yesu, ali wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, adabwerako ku mtsinje wa Yordani kuja. Mzimu Woyerayo ankamutsogolera m’chipululu masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana ankamuyesa. Yesu sankadya kanthu masiku amenewo, ndipo pamene masikuwo adatha, adamva njala. Tsono Satana adamuuza kuti, “ngati ndinu Mwana wa Mulungu, lamulani mwala uli apawu kuti usanduke chakudya.” Koma Yesu adati. “Malembo akuti, ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha.’ Pambuyo pake Satana adatenga Yesu kupita naye pa malo okwera, ndipo pa kamphindi kakang’ono adamuwonetsa maiko a mafumu onse a pansi pano. Tsono adamuuza kuti, “Ndidzakupatsani ulamuliro ndi ulemerero wonsewu, chifukwa zidapatsidwa kwa ine, ndipo ndimazipatsa aliyense amene ndifuna. Choncho mukandipembedza, zonsezi zidzakhala zanu.” Apo Yesu adati, “Malembo akuti, Uzipembedza Ambuye Mulungu wako, ndipo uziwatumikira Iwo okha.” Potsiriza Satana adatenga Yesu kupita naye ku Yerusalemu, nakamuimika pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Adamuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, mudziponye pansi. Paja Malembo akuti, Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni ndiponso, Iwo adzakunyamulani m’manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.” Koma Yesu adati, “Malembo akuti, Usawayese Ambuye, Mulungu wako.” Tsono Satana atatha kumuyesa mwa zonsezi, adalekana naye, kudikira nthawi ina.
Mthenga wa Ambuye... Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, popeza kuti ndife anthu ochimwa, titembenukire kwa Atate athu ndi kuwadandaulira podziwa kuti aliyense amene awapempha kuti amthandize adzapulumuka:
1. Eklezia aunikire anthu onse ndi kuwatsogolera m’njira yakulapa pakuwalalikira Mthenga wa chipulumutso.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akhristu ofooka ndi olowelera adzidzimuke mu mtima mwao ndi kubwerera kwa Mulungu pokumbukira chifundo chozama cha Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Akatekumeni ndiponso anthu akunja avomere kuitana kwa Mulungu ndi kuyamba moyo watsopano, pokhulupirira Mthenga Wabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse tili muno tilimbikire kuchita zolungama ndi kuwonetsa anthu onse mtima wachifundo, podziwa kuti ino ndi nthawi ya chipulumutso.
Tikupemphani, mutivomereze.
Inu Atate, mukudziwa zosowa zathu ndi za anthu onse. Mverani mapemphero athu ndipo mutitsogolere ku chipulumutso chosatha. Mwa Yesu Khristu Ambuye.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB
No comments:
Post a Comment