LAMULUNGU LA 17 PA CHAKA – C.
(Ambuye mutiphunzitse kupemphera.)
MAWU
WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS; GENESIS 18: 20 – 32.
(Musapse mtima, Ambuye, tsopano ndifunsanso.)
Tsono Chauta adauza Abrahamu kuti, “pali zolakwa zoopsa zokhudza Sodomu ndi Gomora, ndipo tchimo lao ndi lalikulu kwambiri. Choncho ndikuti nditsikireko kuti ndikaone ngati zolakwa zimene ndamvazo ndi zoona. Ngati si choncho, ndidzadziwa.” Anthu aja adachoka, napita ku Sodomu, koma Abrahamu adatsalira ndi Chauta. Apo Abrahamu adayandikira kwa Chauta namufunsa kuti, “Kodi monga mudzaonongadi anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa? Nanga patakhala kuti pali anthu 50 osachimwa mumzindamo, kodi mudzaonongabe mzinda wonse? Kodi simudzauleka kuti musunge anthu 50 amenewo? Ndithu simudzaononga anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa. Chimenechi nchosatheka ndipo simungachite. Mukadatero bwenzi anthu osachimwa akulangidwira kumodzi ndi ochima. Kutalitali, Inu simungachite zotere! Kodi Muweruzi wa dziko lonse lapansi nkupanda chilungamo?” Chauta adayankha kuti, “ndikapeza anthu 50 osachimwa m’Sodomu, ndidzauleka mzinda wonsewo osauwononga, chifukwa cha anthu 50 amenewo.” Abrahamu adalankhulanso, adati, “chonde, ndalimba mtima pakulankhula nanu chotere, Ambuye. Inetu ndine munthu chabe pamaso panu. Nanga pa chiwerengero cha 50 pakangoperewera anthu asanu okha, bwanji? Kodi mudzaononga mzindawo popeza kuti asowa asanu okha?” Chauta adayankha kuti, “ndikapeza anthu 45 olungama, sindidzaononga mzindawo. Abrahamu adafunsanso kuti, “nanga pakapezeka anthu olungama 40 okha?” Chauta adayankha kuti, “ndikapeza anthu 40, sindidzauwononga.” Apo Abrahamu adati, “chonde ndapota nanu, musapse mtima, Ambuye, tsopano ndifunsanso. Nanga mutapezeka anthu olungama 30?” Chauta adati, “ndikapeza anthu 30, sindidzauwononga.” Tsono Abrahamu adati, “ndapota nanu, khululukireni kulimba mtima chotere polankhula ndi Inu Ambuye. Nanga mutapezeka olungama 20?” Chauta adati, “ndikapeza anthu olungama 20, sindidzauwononga mzindawo.” Abrahamu adati, “chonde, musandikwiyire Ambuye, koma ndilankhule kamodzi kokhaka. Nanga mutapezeka khumi okha?” Aponso Chauta adati, “ndikapeza olungama khumi, sindidzauwononga mzindawo.”
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 138: 01 – 03, 06 – 08.
Pa tsiku limene
ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, Ambuye.
Ndikukuthokozani
Inu Chauta ndi mtima wanga wonse,
Ndikuimba
nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu,
Ndikugwada
mowerama, kumaso kwa Nyumba yanu yoyera.
Pa tsiku limene
ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, Ambuye.
Ndikutamanda
dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika,
Pa tsiku limene
ndidakuitanani, Inu mudandiyankha,
Mumandilimbitsa
mtima ndi mphamvu zanu.
Pa tsiku limene
ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, Ambuye.
Ngakhale Chauta
ndi wamphamvu, amasamalira anthu otsika,
Koma anthu
odzikuza amawadziwira chapatali,
Ngakhale
ndiyende pakati pa mavuto,
Inu mumasunga
moyo wanga.
Pa tsiku limene
ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, Ambuye.
Mumatambasula
dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya,
Dzanja lanu
lamanja limandipulumutsa,
Chikondi chanu,
Inu Chauta, nchamuyaya,
Muipitirize
ntchito imene mwaiyambayo.
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, Ambuye.
--------------------------------------
MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKOLOSE; AKOLOSE 02: 12 – 14. (Mulungu wakupatsani moyo pamodzi ndi Khristu. Adatikhululukira machimo athu onse.)
Abale, pamene mudabatizidwa, mudachita ngati kuikidwa m’manda pamodzi ndi Khristu. Ndipo ndi ubatizowo mudaukitsidwanso pamodzi naye, pakukhulupirira mphamvu za Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa. Inu kale munali akufa chifukwa cha machimo anu, ndiponso chifukwa munali osaumbalidwa mu mtima. Koma tsopano Mulungu wakupatsani moyo pamodzi ndi Khristu. Adatikhululukira machimo athu onse. Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.
Alleluia, Alleluia – Mzimu amene mudalandira amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, timati, “Abba! Atate!”. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAWU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 11: 01 – 13 (Funsani ndipo mudzapatsidwa.)
Nthawi ina Yesu ankapemphera pamalo pena. Pamene adatsiriza, wophunzira wake wina adampempha kuti, “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera, monga Yohane Mbatizi adaphunzitsira ophunzira ake.” Yesu adati, “pamene mukupemphera muziti, ‘Atate, dzina lanu lilemekezedwe. Ufumu wanu udze. Mutipatse ife tsiku lililonse chakudya chathu chamasiku wonse. Mutikhululukire ife machimo athu, pakuti ifenso timakhululukira aliyense wotilakwira. Ndipo musalole kuti tigwe m’zotiyesa.”’ Adawauzanso kuti, “tangoganizani: wina mwa inu ali ndi bwenzi lake, nkupita kunyumba kwake pakati pa usiku, nakamuuza kuti, iwe mnzanga, kodi ungakhale ndi buledi mtatu? Kwafika bwenzi langa, ali pa ulendo, ndipo ndilibe choti ndingampatse. Koma wam’nyumbayo nkuyankha kuti, ‘usandivute, ndatseka kale pa khomo, ndipo ine ndi ana anga tagona, sindingadzukenso kuti ndikupatse bulediyo.’ Ndithu ndikunenetsa kuti adzauka nkumupatsa, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha khama la wopempha uja. Ndipo adzampatsa zonse zimene akusowa. Motero ndikukuuzani kuti, pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani, ndipo adzakutsekulirani. Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira, amene amafunafuna, ndiye amapeza, ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira. Ndani mwa atatenu, mwana wake atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka? Kapena atampempha dzira, iye nkumupatsa chinkhanira? Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment