LAMULUNGU LA 18 PA CHAKA – C.
(Tipewe khumbo lofuna zinthu zambiri.)
MAU
WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA; MLALIKI 01: 02; 02: 21 – 23
(Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhawa?)
Zonse nzopanda phindu, akutero Mlaliki. Zonse nzachabechabe! Ndithudi zonse nzopandapake. Paja nthawi zina munthu amene wagwira ntchito zolemetsa mwaluntha, mwanzeru ndi mwaluso, zonsezo ayenera kuzisiyira munthu amene sadakhetserepo konse thukuta, kuti akondwere nazo. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo nzoipa kwambiri. Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhawa zimene amazichita pansi pano? Masiku ake onse amakhala achisoni, ntchito yake imakhala yovuta. Ndi usiku womwe mtima wake supumula. Zimenezinso nzopanda phindu.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 90: 03 – 06, 12 – 14.
Inu Ambuye,
ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.
Inu mumabwezera
anthu ku fumbi,
Ndipo mumati,
“bwererani inu ana a anthu,”
Pakuti zaka
chikwi chimodzi pamaso panu zili ngati dzulo chabe,
Kapena ngati
kamphindi chabe kausiku.
Inu Ambuye,
ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.
Inu mumachotsa
moyo wa anthu mwadzidzidzi,
Ali ngati
maloto, ali ngati udzu wongotsitsimuka m’mawa,
M’mamawamo
umatsitsimuka ndipo umakondwa,
Madzulo umafota
ndi kuuma.
Inu Ambuye,
ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.
Tsono
tiphunzitseni kuwerenga masiku athu,
Kuti tikhale
ndi mtima wanzeru,
Lezani mtima,
Inu Chauta,
Nanga mudzatikwiyira
mpaka liti?
Achitireni
chifundo atumiki anu.
Inu Ambuye,
ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.
Tidzazeni
m’mawa mulimonse ndi chikondi chanu chosasinthika,
kuti tizikondwa
ndi kusangalala masiku athu onse,
Inu Ambuye,
mutikomere mtima, ndipo mudalitse ntchito zonse za manja athu,
Inu Ambuye,
ndinu kothawira kwathu pa mibadwo yonse.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKOLOSE; AKOLOSE 03: 01 – 5, 09 – 11. (Ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala.)
Abale, ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano. Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. Khristu ndiye moyo wanu weniweni tsopano, choncho pamene Iye adzaonekerenso, inunso mudzaonekera mu ulemerero pamodzi naye. Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano: Musamauzana mabodza, pakuti mwachita ngati mwavula moyo wanu wakale, pamodzi ndi zochitachita zake zoipa, ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziwe kwenikweni ndi kufanafana naye. M’moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.
Alleluia, Alleluia – Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; 12: 13 – 21 (Nanga zonse zimene wadzisungirazi zidzakhala za yani?)
Munthu wina pakati pa anthu onse aja adapempha Yesu kuti, “Aphunzitsi, takandiwuzirani m’bale wanga kuti andigawireko chuma chamasiye.” Koma Yesu adati, “munthu iwe, ndani adandipatsa ntchito yokuweruzani kapena kumakugawirani chuma chanu chamasiye?” Atatero adauza anthu aja kuti, “chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.” Tsono Yesu adawaphera fanizo. Adati, “munthu wina wachuma m’munda mwake mudabereka dzinthu dzambiri. Ndiye iye uja adayamba kuganiza kuti, ‘nditani, poti ndilibe mosungira dzinthu dzanga?’ Tsono adati, ‘ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga nkumanga zina zazikulu, ndipo ndidzasungira dzinthu dzanga zonse ndi chuma changa m’menemo. Kenaka ndidzauza mtima wanga kuti, Iwe mtima wanga, uli ndi chuma chambiri chimene chidzakukwanira zaka zambiri. Upumule, uzidya, uzimwa ndi kusangalala!’ Koma Mulungu adamuuza kuti, ‘wopusawe! Usiku womwe uno akulanda moyo wako. Nanga zonse zimene wadzisungirazi zidzakhala za yani?”’ Potsiriza Yesu adati, “zimatero ndi munthu amene amadziwunjikira chuma, koma sali wachuma konse pamaso pa Mulungu.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment