LAMULUNGU LA 19 PA CHAKA – C.
(Tilimbike m’chikhulupiriro poyembekeza kudza kwa Ambuye.)
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA LUNTHA; LUNTHA 18: 06 – 09. (Njira yomwe mudalangira adani athu, idakhala njira yoti mutichitire ife zaulemu potiitana kwa Inu.)
Usiku umenewo makolo athu anali ataudziwiratu kuti azilimba mtima ndi kukondwa podziwa kuti apherezera malumbiro aja ankawakhulupirirawa. Choncho anthu anu ankayembekeza chipulumutso cha olungama ndiponso chiwonongeko cha adani ao. Njira yomwe mudalangira adani athu, idakhala njira yoti mutichitire ife zaulemu potiitana kwa Inu. Adzukulu oyera mtima a ulungama aja ankapereka nsembe mobisala. Ankavomerezana kuti adzasunga ndi kugawana molingana zinthu zimodzimodzi, kaya zikhale madalitso, kaya zoopsa. Motero adaayambiziratu kuimba nyimbo zotamanda za makolo ao.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 33: 01, 12, 18 – 22.
Ngwodala mtundu
wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta.
Kondwerani mwa
Chauta, inu anthu ake,
Zoonadi ochita
zolungama azitamanda,
Ngwodala mtundu
wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta,
Anthu amene
Chauta wawasankha akeake.
Ngwodala mtundu
wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta.
Chauta amayang’ana
anthu omumvera,
Ndi odalira
chikondi chake chosasinthika,
Iye amachita
izi kuti awapulumutse ku imfa,
Ndi kuwasungira
moyo anthuwo pa nthawi ya njala.
Ngwodala mtundu
wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta.
Mitima yathu
ikuyembekeza Chauta,
Chifukwa Iye
ndiye chithandizo ndi chishango chathu,
Mitima yathu
imasangalala mwa Chauta,
Popeza kuti
timadalira dzina lake loyera.
Ngwodala mtundu
wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA KWA AHEBRI; AHEBRI 11: 01 – 02, 08 – 12. (Abrahamu adayang’ana maso kutsogolo ku mzinda umene Mulungu adaumanga mwakaso.)
Tikati kukhulupirira, ndiye kuti kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndiponso kutsimikiza kuti zinthu zimene sitikuziwona zilipo ndithu. Pokhala ndi chikhulupiriro, makolo athu akale aja Mulungu adaonetsa kuti ankakondwera nawo. Pokhala ndi chikhulupiriro, Abrahamu adamvera pamene Mulungu adamuitana kuti apite ku dziko lina limene adaamlonjeza kuti lidzakhala lake. Ngakhale sankadziwa kumene ankapita, adapitabe. Pokhala ndi chikhulupiriro chomwecho, ankakhala ngati mlendo m’dzikolo limene Mulungu adaamlonjeza. Ankakhala m’mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, amene nawonso anali atalandira lonjezo lomwelo la Mulungu. Monsemo Abrahamu ankadikira mzinda wa maziko okhazikika. Mzindawo, Mmisiri woganiziratu mamangidwe ake ndiponso woumanga, ndi Mulungu. Pokhala ndi chikhulupiriro, Sara yemwe adalandira mphamvu zakutenga pathupi, ngakhale zaka zake zakubala mwana zinali zitapita kale. Zimenezi zidatheka chifukwa adaavomera kuti amene adazilonjezayo ngwokhulupirika. Nchifukwa chake mwa munthu mmodzi, wotinso anali ngati wakufa, mudatuluka mibadwo yochuluka ngati nyenyezi, ndi yosawerengeka ngati mchenga wa pa gombe la nyanja.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.
Alleluia, Alleluia – Khalani maso, chifukwa simudziwa tsiku limene Mwana wa Munthu adzabwera. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 12: 32 – 48 (Khalani okonzeka kutumikira.)
Yesu anawauza ophunzira ake kuti. “Inu nkhosa zanga, ngakhale muli owerengeka, musaope, pakuti kudakomera Atate anu kuti akupatseni Ufumu wake. Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupatse amphawi. Mudzipezere matumba a ndalama amene safwifwa, ndi kudziwunjikira chuma chokhalitsa Kumwamba; kumeneko mbala sizingafikeko, ndipo njenjete sizingachiwononge. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko. Khalani okonzeka kutumikira, ndipo nyale zanu zikhale zoyaka. Khalani ngati antchito amene akudikira mbuye wao wochokera ku phwando la ukwati, kuti pamene afike ndi kugogoda, iwo amtsekulire msanga. Ngodala antchito amene mbuye wao pofika, awapeza ali maso. Ndithu ndikunenetsa kuti adzadzikonzekera, nadzawakhazika podyera, ndipo adzabwera nkumawatumikira. Ngodala antchitowo mbuye waoyo akadzawapeza ali choncho pamene iye adzafike, ngakhale pakati pa usiku kapena kuli pafupi kucha. Koma kumbukirani kuti, mwini nyumba akadadziwiratu nthawi yoti mbala ifika, sibwenzi atalola kuti ithyole nyumba yake. Choncho inunso khalani okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthawi imene simukuyembekeza.” Pamenepo Petro adati, “Ambuye, kodi fanizoli mukuphera ife tokha, kapena mukuuza onse?” Yesu adati, “tsono kapitao wokhulupirika ndi wanzeru ndani, amene mbuye wake adzamuike kuti aziyang’anira onse a m’nyumba mwake, nkumawagawira chakudya chao pa nthawi yake? Ngwodala wantchito ameneyo, ngati mbuye wake pofika adzampeza akuchitadi zimenezi. Ndithu ndikunenetsa kuti adzamuika woyang’anira chuma chake chonse. Koma ngati ndi wantchito woipa, mumtima mwake azidzati, ‘mbuye wanga akuchedwa kubwera.’ Ndiye adzayamba kumenya antchito anzake, amuna ndi akazi, ndiponso kumadya, kumamwa ndi kuledzera. Tsono mbuye wake adzangoti mbwe mwadzidzidzi, pa tsiku limene iye sakumuyembekeza. Choncho adzamlanga koopsa, ndipo adzamtaya ku malo a anthu osakhulupirika. Wantchito amene akudziwa zimene mbuye wake amafuna, koma osakonzekera kuzichita, adzamkwapula kwambiri. Koma wantchito amene sadziwa zimene mbuye wake amafuna, tsono nkumachita zoyenera kumlanga nazo, adzamkwapula pang’ono. Aliyense amene adalandira zambiri, adzayenera kubweza zambiri. Ndipo amene adamsungiza zambiri, adzamlamula kuti abweze zochuluka koposa.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment