Saturday, August 13, 2022


                                                       LAMULUNGU LA 20 PA CHAKA – C.

“Ndinabwera kudzaponya moto pa dziko lapansi.”

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA YEREMIYA; YEREMIYA 38: 04 – 06, 08 – 10. (Munandilera kukhala munthu wosokoneza pa dziko)

Tsono akuluakulu adauza Mfumu kuti, “munthuyu ayenera kuphedwa. Akutayitsa mtima ankhondo ndi anthu onse otsatira mu mzinda, chifukwa cha zolankhula zakezi. Munthu ameneyu sakuwafunira zabwino anthu, angofuna kuti aonongedwe basi.’’ Mfumu Zedekiya adati, “suyu, ali m’manja mwanu. Ine sindingakuletseni ai.’’ Choncho iwo aja adatenga Yeremiya, nakamponya m’chitsime adaakumba Malakiya mwana wa Mfumu, m’bwalo la alonda a Mfumu. Adamtsitsira m’menemo ndi chingwe. M’chitsimemo munalibe madzi, munali maotope okhaokha. Ndipo Yeremiya adamira m’matopemo. Ebedemeleki adatuluka ku nyumba ya amfumu kukaiwuza kuti, “Mfumu mbuyanga, anthu awa amchita zoipa kwambiri mneneri Yeremiya. Amponya m’chitsime, ndipo poti buledi adatha mu mnzinda, adzafa ndi njala mmenemu.’’ Tsono mfumu idalamula Mkusi Ebedemeleki kuti, “tenga anthu atatu, mukamtulutse mneneri Yeremiya asanafe.’’

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 40: 02 – 04, 18.

Ambuye, bwerani kuti mudzandithandize.

 

Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize,

Adaweramira pansi kuyang’ana kwa ine, namva kulira kwanga.

 

Ambuye, bwerani kuti mudzandithandize.

 

Adanditulutsa m’dzenje la chiwonongeko, mchithaphwi chamatope,

Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyetsa bwino lomwe.

 

Ambuye, bwerani kuti mudzandithandize.

 

Mulungu waika nyimbo yatsopano m’kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye,

Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.

 

Ambuye, bwerani kuti mudzandithandize.

 

Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosowa, koma simunandiiwale,

Inu ndinu mthandizi wanga ndi mpulumutsi wanga.

Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza.

 

Ambuye, bwerani kuti mudzandithandize.

--------------------------------------

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOLEMBERA AHEBERI; AHEBERI 12: 01 – 04. (Tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.)

Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiliro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zowawa zapamtanda. Adawanyoza manyazi a imfa chotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja la lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu. Muziganiza za Iye amene adapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafookere ndi kutaya Mtima. Polimbana ndi uchimo, simudafike mpaka pokhetsa magazi. Mulungu amalanga ana ake.

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.

Alleluia, Alleluia – Nkhosa zanga zimamva mau anga, atero Ambuye. Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsatira. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 12: 49 – 53. (Sindidabwera kudzapereka mtendere ai, koma kugawanikana.)

Yesu adawauza ophunzira ake kuti, “ndidabwera kudzaponya moto pa dziko lapansi, ndipo ndikadakonda utayaka kale. Koma ndiyenera kuyamba ndalowa m’masautso akulu, ndipo mtima wanga sukhazikika mpaka zitachitika. Kodi mukuyetsa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Iyayi, kunena zoona, osati mtendere koma kugawikana. Kuyambira tsopano m’banja limodzi mudzakhala anthu asanu ogawikana, atatu adzakangana ndi awiri, ndipo awiri adzakangana ndi atatu. Bambo adzakangana ndi mwana wake wamwamuna, mwana wamwamuna adzakangana ndi bambo wake. Mai adzakangana ndi mwana wake wamkazi, mwana wamkazi adzakangana ndi mai wake. Apongozi adzakangana ndi mkazi wamwana wao, ndipo mkaziyo adzakangana ndi Apongozi akewo.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...