Saturday, August 20, 2022

 

LAMULUNGU LA 21 PA CHAKA – C.

“Yesetsani kolowera pa khomo lophaphatiza.” 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA YESAYA; YESAYA 66: 18 – 21. (Adzabwera nawo abale anu onse kuchokera kwa anthu a mitundu yonse.)

Chauta akunena kuti, “ndikudziwa ntchito zawo ndi maganizo ao. Ndikubwera kudzasonkhanitsa anthu amitundu yonse ndi a zilankhulo zonse. Adzabweradi ndipo adzaona ulemelero wanga. Ndidzaika chizindikiro pakati pao. Mwa iwowo padzakhala ena opulumukako amene ndidzawatuma kwa anthu a mitundu ina, monga a ku Tarisisi, a ku Puti ndi aku Ludi, akatswiri a mauta, ndiponso Tubala, ku Yavani, ndi ku maiko akutali amene sadamvepo za mbiri yanga kapena kuona ulemelero wanga. Iwowo adzalalika za ulemelero wanga pakati pa anthu a mitundu ina. Ndipo adzabwera nawo abale anu onse kuchokera kwa anthu a mitundu yonse, kuti akhale mphatso kwa ine. Adzabwera nawo monga momwe Aisraele amabwerera ndi zopereka za chakudya ku Nyumba ya Mulungu, atazitenga m’ziwiya zotsukatsuka. Ndipo ena mwa iwo ndidzawasandutsa ansembe ndi Alevi.”

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO: 117: 01 – 02

Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni uthenga wabwino.

 

Tamandani Chauta, Inu mitundu yonse ya anthu,

Mlemekezeni kwambiri, inu anthu a m’maiko onse.

 

Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni uthenga wabwino.

 

Pakuti chikondi chake kwa ife nchachikulu,

Kukhulupirika kwa Chauta nkwamuyaya.

 

Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni uthenga wabwino.

--------------------------------------

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOLEMBERA AHEBERI; AHEBERI 12: 05 – 07, 11 – 13. (Ambuye amamlanga aliyense amene amamkonda.)

Mwaiwala kodi mau olimbitsa mtima aja, amene Mulungu amakulankhulani ngati ana ake? Mauwo ndi awa: “mwana wanga, usanyozere malangizo a Ambuye, kapena kutaya mtima pamene Iwo akudzudzula. Paja Ambuye amamlanga aliyense amene amamkonda, amakwapula mwana aliyense amene iwo amamlandira.” Muzipirira masautso kuti muphunzirepo makhalidwe oyenera. Mulungu amakutengani ngati ana ake m’zochita zake zonse. Kodi nkale lonse analipo mwana wake amene bambo wake sadamlange?  Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo olungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu ofooka. Muziyenda m’njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe.

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Yohane 14: 06.

Alleluia, Alleluia – Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 13: 22 – 30. (Adzachokera kuvuma ndi kuzambwe, nadzakhala podyera mu Ufumu wa Mulungu.)

Pa ulendo wake wopita ku Yerusalemu, Yesu ankayendera mizinda ndi midzi akuphunzitsa. Munthu wina adamufunsa kuti, “Ambuye, kodi adzapulumuka ndi anthu owerengeka okha?” Yesu adayankha kuti, “yesetsani kulowera pa khomo lophaphatiza, pakuti kunena zoona anthu ambiri adzafuna kulowa, koma adzalephera. Mwini nyumba adzanyamuka nkutseka pakhomo. Pamenepo okhala panjanu mudzayamba kugogoda nkumanena kuti, ‘Ambuye, titsekulireni.’  Koma iye adzakuyankhani kuti, ‘sindikudziwa kumene mukuchokera.’ Apo inuyo mudzayamba kunena kuti, ‘pajatu tinkadya ndi kumamwa nanu pamodzi, ndipo inuyo munkaphunzitsa m’misewu ya m’zinda mwathu.’ Koma iye adzakauuzani kuti, ‘pepani, sindikudziwa kumene mukuchokera. Chokani apa nonsenu, anthu ochita zoipa.’ Apo mudzayamba kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu ndi Isaki ndi Yakobe ndi aneneri onse mu Ufumu wa Mulungu, inuyo mukuponyedwa kunja. Anthu adzachokera kuvuma ndi kuzambwe, kumpoto ndi kumwera, nadzakhala podyera mu ufumu wa Mulungu. Pamenepo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira, ndipo amene anali oyambirira adzakhala otsirizira.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-10982647706729

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...