LAMULUNGU LA 16 PA CHAKA – C.
(Tizimva mau a Mulungu ndi mtima wotsekuka.)
MAWU
WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS; GENESIS 18: 01 – 10.
(Mbuyanga, chonde musapitirire pakhomo pa mtumiki wanu.)
Chauta adaonekera Abrahamu ku mitengo ya thundu ya ku Mamure ija. Abrahamuyo atakhala pa khomo la hema lake nthawi yamasana kutatentha, mwadzidzidzi adangoona anthu atatu ataimirira potero. Atangowaona, adanyamuka mwamsanga kukawalonjera. Adaweramitsa mutu, nati, “Mbuyanga, ngati ndapeza kuyanja pamaso panu, chonde musapitirire pakhomo pa mtumiki wanu. Ndikupatseni madzi kuti mutsuke mapazi. Mungathe kubapuma patsinde pa mtengo pano. Ine tsopano ndikatenga chakudya, kuti mukadya mupeze mphamvu zopitirizira ulendo wanu. Mwabwera pakhomo panga pano, motero ndiyenera kukutumikirani.” Anthuwo adayankha kuti, “Chabwino, uchite monga waneneramo. Abrahamu adalowa msangamsanga m’hema, nauza Sara kuti, “utenge msanga nsengwa zitatu za ufa wosalala, uukande ndi kupanga buledi.” Pamenepo Abrahamu adathamanga nakatenga mwanawang’ombe wonenepa, nampereka kwa wantchito kuti akonze mwamsanga. Kenaka adatenga chambiko ndi mkaka wokama chatsopano, ndi nyama yokonzakonza ija nawapatsa zonsezo. Iye adakhala potero pamene anthuwo analikudya patsinde pa mtengo. Tsono anthuwo adafunsa Abrahamu kuti, “kodi mkazi wako Sara ali kuti?” Abrahamu adayankha kuti, “ali m’hemamu.” Chauta adati, “Ndikukulonjeza kuti pakapita miyezi isanu ndi inai ndidzabweranso, ndipo mkazi wako adzakhala ali ndi mwana wamwamuna.”
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 15: 02 – 05.
Anthu olungama adzayenda pamaso pa Mulungu.
Inu Chauta, kodi ndani angathe kukhala m'Nyumba mwanu?
Ndani angathe
kukhala pa phiri lanu loyera?
Ndi munthu
amene amayenda mosalakwa,
Amene amachita
zolungama nthawi zonse,
Amene
amalankhula zinthu ndi mtima woona.
Anthu olungama adzayenda pamaso pa Mulungu.
Ndi amene sasinjirira ndipo sachita anzake zoipa,
Kapena
kumafalitsa mbiri yoipa ya anzake.
Ndi amene
amanyoza munthu womkana Mulungu.
Koma
amalemekeza anthu omvera Chauta.
Anthu olungama adzayenda pamaso pa Mulungu.
Ndi amene amachitadi zimene walonjeza,
Ngakhale
zikhale zowawa chotani.
Ndi amene
sakongoza ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja,
Amene salandira
chiphuphu kuti azunze munthu wosalakwa.
Munthu wochita
zimenezi, palibe chilichonse chimene chidzamgwedeze.
Anthu olungama adzayenda pamaso pa Mulungu.
--------------------------------------
MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKOLOSE; AKOLOSE 01: 24 – 28. (Chinsinsi chobisika chikhalire, tsopano Mulungu wachiwululira anthu ake.)
Abale, tsopano ndakondwa kuti ndikukuvutikirani. Pakuti pakumva zowawazo, ndikutsiriza m’thupi mwanga zotsala za masautso a Khristu kuthandiza thupi lake, ndiye kuti Mpingo. Ndipo ine ndine mtumiki wa Mpingowu, pakuti Mulungu ndiye adandipatsa ntchitoyi yoti ndikulalikireni kwathunthu mau ake. Mauwo ndi chinsinsi chozama chimene chinali chobisika chikhalire kwa mibadwo yonse, koma tsopano Mulungu wachiwululira anthu ake. Cholinga cha Mulungu ndi cha kudziwitsa anthuwo kukoma kwake kwa chinsinsicho ndi ulemerero wake pakati pa anthu akunja. Chinsinsicho nchakuti Khristu ali mwa inu, ndipo Iye amakupatsani chiyembekezo cha kudzalandira ulemerero. Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu.
Mawu a
Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.
Alleluia, Alleluia – Ngodala anthu amene amamva mau a Mulungu, nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, ndipo amalimbikira mpaka kubereka zipatso. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAWU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; 10: 38 – 42. (Marita adamlandira Yesu kunyumba kwake. Maria ndiye wasankhula chinthu chopambana.)
Pamene Yesu ndi ophunzira ake anali pa ulendo wao, Iye adalowa m’mudzi wina. Tsono mai wina, dzina lake Marita, adamlandira kunyumba kwake. Iyeyu anali ndi mng'ono wake, dzina lake Maria, amene adaadzakhala pansi ku mapazi a Ambuye, namamva mau ake. Koma Marita ankatanganidwa ndi ntchito zambiri. Choncho adapita kwa Yesu nati, “Ambuye, kodi simukusamalako kuti mng’ono wangayu akundilekera ndekha ntchito? Muuzeni adzandithandize.” Ambuye adati, “iwe Marita iwe, ukutekeseka nkuvutika ndi zinthu zambiri, koma chofunika nchimodzi chokha. Maria ndiye wasankhula chinthu chopambana, ndipo chimenechi palibe wina angamlande ai.”
Mthenga
wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment