Saturday, July 9, 2022

 


LAMULUNGU LA 15 PA CHAKA – C.

(Tizionetsa chikondi choona pa zochita zathu.) 

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA DEUTERONOMO; DEUTERONOMO 30:10 – 14. (Lamulo muli nalo pompano, mungathe kulitsata.)

Mose anawauza anthu kuti, “komatu muzidzamvera Chauta, Mulungu wanu, ndikusunga malamulo ndi malangizo ake onse amene ali m’buku lino la malamulo ake. Mutembenukire kwa iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Lamulo ndikukupatsani leroli si lovuta kulimvetsa ndipo silapatali. Silili kumwamba, kuti muzichita kundifunsa kuti, “kodi amene akwere kumwamba kukatitsitsira lamulo kuti tilimve, ndani?” Komanso silili pa tsidya pa nyanja kuti muthe kundifunsa kuti, “kodi amene aoloke nyanja kukatitengera lamulo kuti tilimve, ndani?” Muli nalo pompano. Mukulidziwa, mumalitchula ndipo mungathe kulitsata.

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 69: 14, 30 – 34, 36 – 37.

Mufunefune Mulungu, inu ozunzika onse, ndipo mulimbenso mtima.

Koma ine ndimapemphera kwa Inu Chauta,

Mundiyankhe pa nthawi yabwino, Inu Mulungu,

Chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika,

Ndi chithandizo chanu chokhulupirika,

Mundiyankhe, Inu Chauta, pakuti chikondi chanu chosasinthika nchabwino.

Mufunefune Mulungu, inu ozunzika onse, ndipo mulimbenso mtima.

Koma ine ndazunzika ndipo ndikumva kuwawa,

Nyamuleni Inu Mulungu, kuti ndipulumuke,

Ndidzatamanda dzina la Mulungu pomuimbira nyimbo,

Ndidzalalika ukulu wake pomuthokoza.

Mufunefune Mulungu, inu ozunzika onse, ndipo mulimbenso mtima.

Ozunzika aone zimenezo ndipo asangalale,

Inu amene mumafunafuna Mulungu, mulimbenso mtima,

Paja Chauta amamvera anthu osowa,

Sanyoza anthu ake omangidwa ndi unyolo.

Mufunefune Mulungu, inu ozunzika onse, ndipo mulimbenso mtima.

Mulungu adzapulumutsa Ziyoni,

Ndipo adzamanganso mizinda ya Yuda,

Ana a atumiki ake nawonso adzalilandira kuti likhale lao,

Ndipo okonda Mulungu adzakhala m’menemo.

Mufunefune Mulungu, inu ozunzika onse, ndipo mulimbenso mtima.

--------------------------------------

MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKOLOSE; AKOLOSE 01: 15 – 20. (Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalenga Iyeyo.)

Abale, Khristuyo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu wosaoneka. Iye ndiye mwana wake woyamba, wolamulira zolengedwa zonse. Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalenga ndi Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse padakalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi. Iye ndiyenso mutu wa mpingo thupi lake. Ndiye chiyambi chake, woyambirira mwa ouka kwa akufa, kuti pa zonse Iye akhale wopambana ndithu. Kudakomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristuyo. Mwa iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya mwana wake pamtanda.

Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.

Alleluia, Alleluia – Mau anu, Ambuye, ndiwo amapatsa Mzimu wa Mulungu ndiponso moyo. Muli nawo ndinu mau opatsa moyo wosatha. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAWU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; 10: 25 – 37. (Nanga mnansi wanga ndani?)

Katswiri wina wa malumulo adaimirira kuti ayese Yesu. Adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?” Yesu adati, “kodi m’Malamulo mudalembedwa kuti chani? Mumawerengamo zotani?” Iye adayankha kuti, “uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe uzikondera iwe wemwe.” Yesu adati, “mwayankha bwino. Kachiteni zimenezi ndipo mudzakhala ndi moyo.” Koma munthuyo pofuna kudzionetsa ngati wolungama, adafunsa Yesu kuti, “nanga mnzangayo ndani?” Apo Yesu adati, “munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Panjira achifwamba adamgwira. Adamuvula zovala, nammenya, nkumusiya ali thasa, ali pafupi kufa. Ndiye zidangochitika kuti wansembe wina ankapita pa njira yomweyo. Pamene adaona munthu uja, adangolambalala. Chimodzimodzinso Mlevi wina adafika pamalopo, nayenso adangolambalala. Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, adafikanso pamalo pomwepo. Pamene adaona munthu uja, adamumvera chisoni. Adabwera kwa ovulalayo, namthira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuwamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino. M’mawa kutacha adatulutsa ndalama ziwiri zasiliva, nazipereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Adamuuza kuti, ‘msamalireni bwino, ndipo mukamwazanso ndalama zina, ndidzakubwezerani pobwera.”’ Tsono Yesu adafunsa katswiri wa Malamulo uja kuti, “inu pamenepa mukuganiza bwanji? Mwa anthu atatuwa, ndani adakhala ngati mzake wa munthu achifwamba adaamugwirayu?” Iye adati, “amene adamchitira chifundo uja.” Apo Yesu adamuuza kuti, “pitani tsono, nanunso muzikachita chimodzimodzi.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...