LAMULUNGU LA 14 PA CHAKA – C.
(Mtendere wa Ambuye ukhale nanu.)
MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA; YESAYA 66: 10 – 14c. (Ndidzakupatsa zabwino zochuluka ngati mtsinje wa madzi.)
Kondwera nayeni
Yerusalemu musangalale chifukwa cha iye, inu nonse amene mumakonda mzinda
umenewu. Kondwera nayeni mwachimwemwe, nonsenu amene mukumlira. Mudzalandira
chitonthozo ndi kukondwera nacho kwambiri. Mudzagawana naye ulemerero wake ndi
kusangalala nawo. Chauta akunena kuti, “ndidzakupatsa zabwino zochuluka ngati
mtsinje wa madzi. Chuma cha mitundu ya anthu chidzafika kwa inu ngati mtsinje
wotsefukira. Mudzakhala ngati mwana woyamwa amene mai wake wamnyamulira
pambalipa, kapena akumluluza pa maondo. Ndidzakusangalatsani ku Yerusalemu
monga momwe mai amasangalatsira mwana wake. Mudzasangalala poona zimenezi.
Zidzakulimbitsani ndi kukupatsani moyo wamphamvu. Tsono mudzadziwa kuti ine
Chauta ndimathandiza amene amandimvera, ndipo ndimakwiyira adani anga.’’
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 66: 01 – 07, 16, 20.
Tamandani Mulungu ndi Chimwemwe, inu anthu onse a pa dziko lapansi.
Inu anthu onse
a pa dziko lapansi,
Imbani nyimbo
zoyamika dzina lake laulemerero, mumtamande mwaulemu,
Muuzeni Mulungu
kuti, “ntchito zanu nzodabwitsa kwambiri.
Tamandani Mulungu ndi Chimwemwe, inu anthu onse a pa dziko lapansi.
Anthu onse a pa dziko lapansi amakupembedzani,
Amaimba nyimbo
zotamanda inu,
Amaimba nyimbo
zotamanda dzina lanu.”
Bwerani
mudzaona zimene Mulungu wachita,
Ntchito zake nzodabwitsa pakati pa anthu.
Tamandani Mulungu ndi Chimwemwe, inu anthu onse a pa dziko lapansi.
Anthu adaoloka
mtsinje uja poyenda pansi,
Nchifukwa chake
timukondwerere Iye,
Iye amalamula
ndi mphamvu zake mpaka muyaya.
Tamandani Mulungu ndi Chimwemwe, inu anthu onse a pa dziko lapansi.
Bwerani mudzamve,
inu nonse opembedza Mulungu,
Ndidzakusimbireni
zimene Iye wandichitira,
Chifukwa
sadakane pemphero langa,
Sadachotse
chikondi chake chosasinthika kwa Ine.
Tamandani Mulungu ndi Chimwemwe, inu anthu onse a pa dziko lapansi.
--------------------------------------
MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA A GALATIYA; AGALATIYA 06: 14 - 18. (Zipsera zimene ine ndili nazo za thupi langa, zikutsimikiza kuti ndine wakewake wa Yesu.)
Abale, ine sindingadyadire kanthu kena kalikonse, koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu basi. Popeza kuti iye adafa pamtanda, tsopano zapansipano kwa ine zili ngati zakufa, ndipo inenso kwa zapansipano, ndili ngati wopachikidwa. Kuumbalidwa sikanthu, kusaumbalidwa sikanthunso, chachikulu nchakuti Mulungu apatse munthu moyo watsopano. Mulungu awapatse Mtendere, ndipo awachitire chifundo anthu a Mulungu onse amene amatsata njira imeneyi. Kuyambira tsopano asandivutenso munthu wina aliyense, pakuti zipsera zimene ine ndili nazo pa thupi langa, zikutsimikiza kuti ndine wakewake wa Yesu. Abale, Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni inu nonse. Amen.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.
Alleluia, Alleluia – Ndikukutchulani abwenzi, atero Ambuye, chifukwa zonse zimene ndidamva kwa Atate anga, ndidakudziwitsani. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA
WABWINO: MAWU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; 10: 01 – 12,
17 – 20. (Mtendere ukhale mwa munthu ameneyo.)
Pambuyo pake Ambuye adasankha anthu 72, nawatuma awiriawiri kuti atsogole kupita ku mudzi uliwonse ndi ku malo aliwonse kumene iye ankati apiteko. Adawauza kuti, “dzithu nzambiri, koma antchito ngochepa. Nchifukwa chake pemphani mwini zinthu kuti atume antchito kukatuta dzithudzo. Pitani tsono. Ndikukutumani ngati ana ankhosa pakati pa mimbulu. Musatenge chikwama cha ndalama, kapena thumba la paulendo, kapenanso nsapato zapadera ai. Musaimenso kuti mupereke moni panjira. Kunyumba kulikonse kumene mukalowe, muyambe mwanena kuti, ‘Mtendere ukhale m’nyumba muno.’ Ngati m’nyumbamo muli anthu amtendere, mtendere umene mwanenawo udzakhala pa iyeyo. Koma ngati mulibe munthu wofuna mtendere, mtendere umene mwanenawo udzabwerera kwa inu. Khalani m’nyumba yomweyo. Mudye ndi kumwa zimene akupatsani, pakuti wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake. Musamachoka kumene mwafikako nkulowa ku nyumba zina ai. Mukalowa m’mudzi, anthu nkukulandirani, mudye zimene akukonzerani. Muchiritse anthu odwala amene ali m’mudzimo, ndipo muwauze kuti, ‘tsopano ufumu wakumwamba wakufikirani’. Koma kumudzi kumene mukalowe, anthu nkupanda kukulandirani bwino, mukapite m’miseu yam’mudzimo, nkunena kuti, ‘tikukusansirani ngakhale fumbi la m’mudzi mwanu muno limene linamamatira ku mapazi athu. Komabe dziwani kuti ufumu wa Mulungu wafika.’ Kunena zoona, pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Sodomu koposa polanga mudzi umenewo.” Anthu 72 aja adabwerako ndi chimwemwe nati, “Ambuye, ngakhale mizimu yoipa yomwe imatigonjera tikamailamula m’dzina lanu.’’ Yesu adawauza kuti, “ndidaona satana ali kugwa ngati mphezi kuchokera kumwamba. Ndakupatsanitu mphamvu kuti muziponda njoka ndi zinkhanira, ndikumagonjetsa mphamvu zonse za mdani uja. Palibe kanthu kamene kangakupwetekeni. Komabe musakondwere chifukwa choti mizimu yoipa ikukugonjerani, koma muzikondwera kuti maina anu adalembedwa kumwamba.’’
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment