LAMULUNGU LA 13 PA CHAKA (CYCLE C)
(Wofuna kutsata Yesu asamayang’anenso zakumbuyo.)
MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LOYAMBA LA MAFUMU: 01 MAFUMU 19: 16b, 19 – 21. (Pambuyo pake adanyamuka namayenda ndi Eliya ndi kumamtumikira.)
Chauta adamuuza Eliya kuti, “Elisa, mwana wa Safati wa ku Abele-Mehola, ukamdzoze kuti akhale mneneri wolowa m’malo mwako.” Eliya atachoka kumeneko, adakapeza Elisa akulima ndi pulawo yokokedwa ndi ng’ombe. Panali magoli khumi ndi awiri, mwiniwakeyo nkumayenda ndi goli lotsiriza. Eliya adabwera kumene kunali iyeko, namuveka mwinjiro wake. Pomwepo Elisa adasiya ng’ombe zakezo, adathamangira Eliya uja nampempha kuti, “mundilore kuti ndikatsanzike bambo wanga ndi mayi wanga, ndipo pambuyo pake ndidzakutsatani.” Eliya adamuyankha kuti, “Chabwino, pita. Ndakuletsa ngati?” Apo Elisha adabwerera, ndipo adatenga ng’ombe zake ziwiri nazipha. Kenaka adatenga magoli a ng’ombezo nasonkhera moto nkuphikira nyamayo, ndipo adaipereka kwa anthu kuti adye. Pambuyo pake adanyamuka namayenda ndi Eliya ndi kumamtumikira.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 16: 01 – 02, 05, 07 – 11.
Chauta ndiye chuma changa ndi cholowa changa.
Mundisunge Inu
Mulungu, pakuti ndikuthawira kwa Inu.
Ndimamuuza
Chauta kuti, “Inu ndinu Ambuye anga.”
Chauta ndiye
chuma changa ndi cholowa changa.
Tsogolo langa lili m'manja mwanu.
Chauta ndiye chuma changa ndi cholowa changa.
Ndikutamanda
Chauta amene ali phungu wanga.
Mtima wanga
umandilangiza ndi usiku womwe.
Nthawi zina
ndimalingalira za Chauta.
Popeza kuti ali
ku dzanja langa lamanja,
palibe amene
angandiopse konse.
Chauta ndiye chuma changa ndi cholowa changa.
Nchifukwa chake mtima wanga ukukondwa,
Ndipo m’katikati
mwangamu ndikusangalala,
Thupi langanso
lidzakhala pabwino,
Chifukwa
simudzandisiya ku malo a anthu akufa,
Simudzalola
kuti wokondedwa wanune ndikaole kumeneko.
Chauta ndiye chuma changa ndi cholowa changa.
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo.
Ndimapeza
chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu,
Ndidzasangalala
mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Chauta ndiye chuma changa ndi cholowa changa.
--------------------------------------
MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA A GALATIYA; AGALATIYA 05: 01, 13 – 18. (Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu)
Abale, Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso m’goli la ukapolo. Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi. Paja malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “uzikonda mnzako monga momwe umazikondera iwe wemwe.” Koma ngati muyamba kulumana ndi kukadzulana, muchenjere kuti mungaonongane kotheratu. Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simuzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka. Pakuti khalidwelo limalakalaka zotsutsana ndi zimene Mzimu Woyera afuna, ndipo zimene Mzimu Woyera afuna zimatsutsana ndi zimene khalidwe lokonda zoipalo limafuna. Ziwirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mufuna kuchita. Koma ngati Mzimu Woyera akutsogolerani, ndiye kuti sindinunso akapolo a Malamulo a Mose.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.
Alleluia, Alleluia – Lankhulani, Inu Ambuye, poti mtumiki wanune ndilikumva. Muli nawo ndinu mau opatsa moyo wosatha. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA
WABWINO: MAWU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; 09: 51 – 62.
(Ndizikutsatani kulikonse kumene muzipita.)
Pamene masiku ankayandikira oti Yesu atengedwe kunka kumwamba, Iye adatsimikiza ndithu zopita ku Yerusalemu. Motero adatuma amithenga kuti atsogole, akalowe m’mudzi wina wa Asamariya kukamkonzera malo. Koma anthu a m’mudzimo sadafune kumulandira, chifukwa iye ankapita ku Yerusalemu. Ophunzira ake, Yakobe ndi Yohane ataona zimenezi adati, “Ambuye, bwanji tiitane moto kuchokera kumwamba kuti udzawapsereze anthu amenewa?” Koma Yesu adacheuka nadzudzula ophunzirawo. Pambuyo pake onse pamodzi adapita ku mudzi wina. Pamene iwo anali panjira, munthu wina adauza Yesu kuti, “ndidzikutsatani kulikonse kumene muzipita.” Yesu adamuyankha kuti, “nkhandwe zili ndi michembo yake, mbalame zili ndi zisa zake, koma mwana wa munthu alibe mpogoneka mutu womwe.” Pambuyo pake Yesu adauza munthu wina kuti, “Iwe, unditsate!” Iyeyo adati, “Ambuye mundilole ndiyambe ndakaika maliro a Atate anga.” Yesu adamuuza kuti, “aleke akufa aziika akufa anzao. Koma iwe, kalalike Ufumu wa Mulungu.” Munthu winanso adauza Yesu kuti, “ndidzakutsani, Ambuye, koma mundilole ndiyambe ndakatsanzikana ndi anthu kunyumba.” Yesu adati, “munthu amene wayambapo kulima, tsono nkumacheukiranso kumbuyo, Mulungu alibe naye ntchito mu ufumu wake.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment