CHAKA
CHA UKARISTIA [CORPUS CHRISTI] – CYCLE C
(Muzichita
zimenezi kuti mundikumbukire.)
MAWU WOYAMBA A
M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (CHIYAMBI); GENESIS 14: 18 – 20.
(Adatenga buledi ndi vinyo.)
Ndipo Melkizedeki, mfumu ya ku Salemu, wansembe wa Mulungu Wopambanazonse, adabwera kwa Abramu atatenga Buledi ndi Vinyo. Adadalitsa Abramuyo, adati, “Mulungu Wopambanazonse, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitse iwe Abramu. Atamandike Mulungu Wopambanazonse, amene adakupatsa mphamvu zogonjetsera adani ako onse.” Pamenepo Abramu adapereka kwa Melkizedeki chigawo chachikhumi cha zinthu zimene adaalandira.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO:
SALIMO 110: 01 – 04.
Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
Chauta adauza Mbuye wanga kuti,
“Khala ku dzanja langa lamanja,
mpaka nditasandutsa adani ako
kukhala ngati chopondapo mapazi ako.”
Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
Chauta adzakuza ufumu wako
wamphamvu
kuchokera ku Ziyoni.
Adzati, “Khala mfumu yolamulira adani ako.”
Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
Anthu ako adzadzipereka mwaufulu.
pa tsiku limene udzaonetse mphamvu
zako pa phiri loyera.
Anyamata ako adzabwera kwa iwe mu
unyinji wao,
monga m'mene mame amabwerera m'mamawa.
Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
Chauta walumbira
ndipo sadzasintha maganizo ake
akuti,
“Ndiwe wansembe mpaka muyaya,
unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.”
Ndiwe wansembe mpaka muyaya,
unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
--------------------------------------
MAWU ACHIWIRI A
M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO; 01
AKORINTO 11: 23 – 26. (Nthawi zonse mukamadya mkate umenewu, ndi kumwa chikho
chimenechi, mumalalika imfa ya Ambuye.)
Inetu zimene ndidalandira kwa Ambuye ndi zimene nanenso ndidazipereka kwa inu, zakuti usiku umene adaperekedwa uja, Ambuye Yesu adaatenga mkate. Ndipo atathokoza Mulungu, adaunyemanyema nati, “ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.’’ Momwenso atatha kudya, Ambuye Yesu adatenga chikho nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chotsimikizika ndi magazi anga. Nthawi zonse mukamamwa chikho chimenechi, muzindikumbukira.’’ Pakuti nthawi zonse mukamadya mkate umenewu, ndi kumwa chikho chimenechi, mumalalika imfa ya Ambuye, mpaka adzabwerenso.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.
Alleluia, Alleluia – Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. – Alleluia, Alleluia.
---------------------------------------
NYIMBO YA
UKARISTIA (SEQUENCE)
O SIYONI
UYAMIKE
Mbusa wabwino,
Buledi weniweni,
Mbuye Yesu,
mutichitire chisoni.
Muteteze,
nkulowetsa
Nkhosa zanufe
kumwamba.
1. O Siyoni,
uyamike
Mpulumutsi
wako, Mbuye,
Mfumu ndinso
Mbusa wako.
2. Sudzafika
kuimbira
Mlungu wako
mokwanira.
Ukwezetu mawu
ako.
3. Nkofunika
ndithu lero
Kutama Buledi
wamoyo,
Ngwopatsa moyo
womwewo.
4.Tidziwa
mosapeneka
Kuti Yesu
anapatsa
Bulediyu kwa
apositoli.
5. Tsono
tisankhule nyimbo
Zokoma kwambiri
lero
Ndi kuimba
mwachimwemwe.
6. Misa
itibweretsera
Tsiku lomwe la
kupanga
Phwando
loyerayerali.
7. Ndi Pasaka
yatsopano
Ya Mfumu
yatsopanonso
Miyambo yakale
yatha.
8. Zalero
zibadiritsa
Zakale, monga
kuyera
M'mawa
kuchotsatu mdima.
9. Yesu
anatilamula
Kubwereza zomwe
zija
Anazichita
tsikuli.
10. Pomvera
Yesu ifenso
Tisandutsa
buledi n'vinyo
Pa nsembe
yopulumutsa.
11. Buledi
asanduka Thupi
Ndiponso vinyo
Magazi
A Khristu,
Ambuye athu.
12. Sitimvetsa,
sitiona,
Koma ndithu
tizimvera
Zozizwitsa
zimenezi.
13. Buledi
ndinso vinyo ali
Chizindikiro
chophimba
Zazikulu
zobisika.
14. Tidya Thupi
la Ambuye
Ndi kumwa
Magazi ake:
Akhala
muziwirizi.
15. Aliyense
amlandira
Wathunthudi,
wosasweka,
Ndi wosagawika
konse.
16. Nayo Buledi
wa anjelo
Ngwa alendofe
tsopano
Manna wotipatsa
nyonga.
17. Mulungu
wamphamvuzonse
Ndiponso
wodziwa zonse,
Inu mutidyetsa
pano.
18.
Mutidyetsenso Kumwamba
M'phwando la
anthu oyera.
Amen. Amen.
Aleluya.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAWU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 09: 11b – 17. (Anthu onse aja adadya nakhuta.)
Anthu ambirimbiri ataona zimenezi, adamtsatira. Iye adawalandira bwino nayamba kulankhula nawo za ufumu wa Mulungu, nkumachiritsa odwala. Dzuwa lili pafupi kulowa, ophunzira khumi ndi awiri aja adadzauza Yesu kuti, “bwanji anthuwa azinyamuka tsopano, apite ku midzi ndi ku miraga ili pafupiyi, kuti akapeze malo ogona ndiponso chakudya, chifukwatu kuno nkuthengo.’’ Koma Yesu adawauza kuti, “inuyo apatseni chakudya.’’ Iwo adati, “tili ndi buledi msanu ndi nsomba ziwiri zokha. Kaya kapena tipite tikawagulire anthu onsewa chakudya?’’ Ndiye kuti amuna okha adaalipo ngati zikwi zisanu. Tsono Yesu adauza ophunzira ake kuti, “auzeni anthuwa akhale pansi m’magulumagulu, gulu lililonse anthu ngati makumi asanu.’’ Ophunzira aja adawakhalitsadi anthu onse aja pansi. Pambuyo pake Yesu adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziwiri zija, nayang’ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake kuti agawire anthuwo. Anthu onse aja adadya nakhuta. Ndipo ophunzira aja adatola zotsala, nkudzaza madengu khumi ndi awiri.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook:
https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment