Nzeru ya Mulungu imafuula kuti: “Chauta adandilenga ine nzeru pa chiyambi cha ntchito zake. Mwa ntchito zake zakalekale woyambilira ndinali ine. Ndidapangidwa masiku akalekale, pachiyambiyambi, dziko lapansi lisanalengedwe. Nyanja zozama zisanalengedwe, padakalibe akasupe odzaza ndi madzi, nkuti ine nditabadwa kale. Mapiri asanaumbidwe, magomo asanakhalepo, Mulungu anali atandilenga ineyo; lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake, lisanakhaleponso dothi loyamba la dziko lapansi. Ine ndinalipo kale, pamene ankakhazikitsa zakumwamba, pamene ankalemba mzere wa malire anyanja yozama, pamene ankaika thambo m'malo mwake, pamene ankatsekula akasupe a m’nyanja yozama, pamene ankaika malire a nyanja kuti madzi ake asabzole malirewo, pamene ankaika maziko a dziko lapansi. Nthawiyo nkuti ndili pambalipa ngati mmisiri wake, ndikumkondweretsa tsiku ndi tsiku, ndikusangalala pamaso pake nthawi zonse. Ndinkasangalala m’dziko lake lokhalamo anthu, ndi kumakondwa nawo ana a anthu.”
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA
SALIMO: SALIMO 08: 04 – 05, 06 - 07, 08 – 09.
Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi.
Ndikamayang’ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu,
Ndikamaona mwezi ndi nyenyezi
zimene mudazikhazika kumeneko, ndimadzifunsa kuti,
“Kodi munthu nchiyani kuti
muzimkumbukira, mwana wa munthu nchiyani kuti muzimsamalira?”
Chauta, Ambuye athu, dzina lanu
ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi.
Ndiyetu mudamlenga mochepera pang’ono kwa Mulungu amene,
Mudampatsa ulemerero ndi ulemu
wachifumu,
Mudampatsa ulamuliro pa ntchito za
manja anu,
Mudamgonjetsera zolengedwa zonse.
Chauta, Ambuye athu, dzina lanu
ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi.
Nkhosa, ng’ombe ndi nyama zakuthengo,
Mbalame zamumlengalenga, nsomba za
m’nyanja,
Ndi zonse zoyenda pansi pa nyanja.
Chauta, Ambuye athu, dzina lanu
ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi.
MAWU ACHIWIRI A
M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 05: 01 –
05. (Tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.)
Abale, popeza kuti pakukhulupilira tapeza kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa Mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupilira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandilako ulemelero wa Mulungu. Koma sipokhapo ai, timakondweranso m’masautso athu. Pakuti tikudziwa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo. Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa la moto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA
MTHENGA WABWINO.
Alleluia,
Alleluia – Ulemu ukhale kwa Atate ndi Mwana ndi Mzimu Woyera, Mulungu amene
alipo, amene analipo, amene alikudza. Alleluia, Alleluia.
-------------------------
MTHENGA
WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE
16: 12 – 15. (Zonse za Atate nzanga. Nchifukwa chake ndanena kuti adzakutenga
zochokera kwa Ine, nadzakudziwitsani inu.)
Yesu adawauza ophunzira ake kuti: “ndili nawo mau ena ambiri oti ndikuuzeni, koma simungathe kuwamvetsa tsopano ayi. Koma akadzafika Mzimu wodziwitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ayi, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziwitsani zinthu zam’tsogolo. Adzandilemekeza, pakuti adzatenga zochokera kwa Ine nadzakudziwitsani. Zonse za Atate nzanga. Nchifukwa chake ndanena kuti adzatenga zochokera kwa ine, nadzakudziwitsani inu.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook:
https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment