CHAKA CHA PENTEKOSTE – C(Adawauzira mpweya wopatsa moyo)
MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 02: 01 – 11. (Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula.)
Pamene tsiku la chikondwerero cha Pentekoste lidafika, iwo onse anali pamodzi m’nyumba imodzi. Mwadzidzidzi kudamveka kuchokera kumwamba mkokomo ngati wa mphepo yaukali, nudzaza nyumba yonse imene ankakhalamo. Ndipo adaona ngati timalawi ta moto tooneka ngati malilime tikugawikana nkukhala pa iwo, aliyense kakekake. Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankawalankhulitsira. Tsono, m’Yerusalemu muja munali Ayuda ena, anthu okonda Mulungu, ochokera ku maiko onse a pa dziko lapansi. Pamene mkokomo uja udamveka, anthu ambirimbiri adasonkhana. Onse adadodoma, chifukwa aliyense mwa iwo ankawamva akulankhula chilankhulo chake. Adadabwa, nathedwa nzeru ndipo adati, “kodi onse akulankhulawa, si Agalileya? Nanga bwanji aliyense mwa ife akuwamva akulankhula chilankhulo chakwawo? Ena mwa ife ndi Aparti ndi Amedi ndi Aelami, ena ndi okhala ku Mesapotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya, Ku Frijiya ndi ku Pamfiliya, ku Ejipito, ndi ku madera a Libiya kufupi ndi ku Kirene, ena ndi alendo ochokera ku Roma, ndiye kuti Ayuda ndi ena otsata za Chiyuda. Enanso ndi Akrete ndi Aarabu, komabe tonse tikuwamva anthuwa akulankhula m’zilankhulo zathu za ntchito zazikulu za Mulungu.”
Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.
-------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 104: 01, 24, 24, 29 – 31.
Tumizani
Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
Tamanda
Chauta, iwe mtima wanga,
Inu
Chauta, Mulungu wanga, ndinu aakulu kwambiri,
Inu
Chauta ntchito zanu zambiri,
Ndipo
dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu
Tumizani
Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
Mukazichotsera
mpweya, zimafa nkubwerera ku fumbi,
Mukatumiza
mpweya wanu zimalengedwa,
Ndipo
mumakonzanso maonekedwe a dziko lapansi.
Tumizani
Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
Ulemerero
wa Chauta ukhalebe mpaka muyaya,
Chauta
akondwe nazo ntchito zakezo,
Mapemphero
anga amkomere Chauta,
Popeza
kuti ndimakondwa mwa Iye.
Tumizani
Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
-------------------------
MAWU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA 08: 08 – 17. (Onse amene Mzimu wa Mulungu amawatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu.)
Abale, anthu oika mtima pa khalidwe limenelo, sangathe kukondweretsa Mulungu. Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lopendekera ku zoipa. Mumalamulidwa ndi Mzimu Woyera, ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu sali wake wa Khristu. Khristu akakhala mwa inu, ngakhale thupi lanu lidzafadi chifukwa cha uchimo, komabe mzimu wanu udzakhala ndi moyo, popeza kuti Mulungu wakuwonani kuti ndinu olungama pamaso pake. Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufawa. Motero abale, tili ndi ngongole, komatu ngongole yake si yakuti tizigonjera khalidwe lathu lokonda zoipa, ndi kumachita chifuniro chake. Pakuti ngati m’moyo mwanu mutsata khalidwelo, mudzafa. Koma ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo. Onse amene Mzimu wa Mulungu amawatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu. Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, ‘Abba! Atate!’ Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nso madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Mawu a Ambuye…Tithokoze Mulungu.
-------------------------
NYIMBO YA PENTEKOSTE (SEQUENCE) [Nyimboyi itha kunenedwa kapena kuyimbidwa]
1.
Bwerani
Mzimu Woyera,
Tumizani
kuwala kwanu,
Kufumira
kumwambako.
2.
Bwerani,
Tate wa amphawi,
Bwerani,
wopatsa mphatso,
Inu
muuni wa mitima.
3.
Ndinu
Msangalatsi ndithu,
Woyendera
mitima yathu,
Kuti
mudzaithuzitsa.
4.
Pa
ntchito ndinu Mpumulo,
Mumatichotsera
kutentha,
Ndi
kutsangula misozi yathu.
5.
Ndinu
kuwala kokoma,
Dzazani
mitima yathu,
Ya ife
anthu okumverani.
6.
Mutapanda
kudzamthandiza,
Munthu
sangapeze kanthu,
Zonse
zidzamuipira.
7.
Tsukani
zoipa zathu,
Dzatsirireni
zouma,
Chiritsani
mabala athu.
8.
Dzafewetseni
zolimba,
Funditsani
zozizira,
Lungamitsani
zokhota.
9.
Tipatseni
anthu anufe,
Okhulupirira
Inu,
Mphatso zisanu ndi
ziwiri.
10.
Kometsani
makhalidwe athu,
Katifikitseni
kumwamba,
Kukadala
nthawi zonse,
Amen.
Alleluia, Alleluia – Bwerani Mzimu Woyera, mudzaze m’mitima ya anthu okhulupirira ndipo chikondi chanu chikhazikike mwa iwo. – Alleluia, Alleluia.
-------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 14: 15 – 16, 23 – 26. (Mzimu Woyera ndiye adzakuphunzitseni zonse.)
Yesu adawauza ophunzira ake kuti: “Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga. Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse.” Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa ife. Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvawa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma. Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m’dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment