Saturday, October 26, 2024

LAMULUNGU LA 30 PA CHAKA – B

LAMULUNGU LA 30 PA CHAKA – B.

“Inu Yesu, Mwana wa Davide, Mundichitire chifundo.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YEREMIYA: YEREMIYA 31: 07 – 09. (Ndidzasonkhanitsa akhungu ndi opunduka. Ine ndidzawaperekeza ndi mtima wachifundo).

 

Chauta akuti, “imbani mokweza ndi mosangalala chifukwa cha Yakobo. Fuulani chifukwa cha mtundu wopambana mitundu yonse. Lalikani, tamandani ndi kulengeza kuti, Chauta wapulumutsa anthu ake, wasunga otsala a Israele. Ndidzawatulutsa kuchokera ku dziko lakumpoto. Ndidzasonkhanitsa akhungu ndi opunduka, akazi amene ali ndi pakati ndi amene ali pa nthawi yao yochira. Chidzakhala chinamtindi cha anthu obwerera kuno. Adzabwerera kwao akulira, koma Ine ndidzawaperekeza ndi mtima wachifundo. Ndidzawatsogolera ku mitsinje yodzaza ndi madzi. Sadzaphunthwa, njira yao idzakhala yosalala kwambiri. Ine ndine bambo wake wa Israele, Efuremu ndi mwana wanga wachisamba.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 126: 01 – 02, 02 – 03, 04 – 05, 06.

 

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

 

Pamene Chauta adabwezera akapolo ku Ziyoni,

Tinali ngati anthu amene akulota,

Pamenepo tidasekera kwambiri,

Ndipo tidalulutira ndi chimwemwe.

 

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

 

Tsono mitundu ina ya anthu inkanena kuti,

“Chauta wawachitira zazikulu,”

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu,

Ndipo tasangalala.

 

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

 

Tibwezereni ufulu wathu, Inu Chauta,

Tikhale ngati mitsinje ya m’chipululu,

Anthu amene amafesa akulira,

Adzakolola akufuula ndi chimwemwe.

 

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

 

Munthu amene amapita akulira, atatenga mbeu zokafesa,

Adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe,

Atatenga mitolo yake yambiri.

 

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

-------------------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA AHEBRI: AHEBRI 05: 01 – 06. (Ndiwe Wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.)

 

Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa pakati pa anthu, namuika kuti aziwaimirira pamaso pa Mulungu. Ntchito yake nkupereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo. Popeza kuti iye yemweyo ali ndi zofooka zambiri, ndiye kuti angathe kuwalezera mtima amene ali opanda nzeru ndi osokera. Nchifukwa chake aumirizidwa kumapereka nsembe chifukwa cha machimo a iye yemwe, ndiponso machimo a anthu ena. Palibe munthu amadzitengera yekha ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma amachita kuitanidwa ndi Mulungu, monga momwe adaaitanidwira Aroni. Momwemonso Khristu sadadzikweze yekha ku ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma Mulungu ndiye adachita kumuuza kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga, Ine lero ndakubala. Penanso Mulungu adati, ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – 02 TIMOTEO 01: 10.

Alleluia, Alleluia – Mpulumutsi wathu Khristu Yesu adathetsa mphamvu za imfa, ndipo mwa Uthenga Wabwino adafalitsa moyo umene sungafe konse. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 10: 46 – 52. (Mbuyanga, ndikufuna kuti ndizipenyanso).

 

Yesu ndi ophunzira ake pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu adafika ku mzinda wa Yeriko. Tsono pamene ankatuluka mumzindamo, adapeza wakhungu wina wopemphapempha atakhala pansi pamphepete pa mseu. Munthuyo dzina lake anali Baratimeo, mwana wa Timeo. Tsono iyeyo atamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, adayamba kufuula kuti, “Inu Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.” Anthu ambiri adamzazira kuti akhale chete. Koma iye adafuulirafuulira kuti, “Inu Mwana wa Davide mundichitire chifundo.” Yesu adaima, nauza anthu kuti, “tamuitanani.” Anthu aja adamuitana wakhunguyo namuuza kuti, “limba mtima, nyamuka, akukuitana.” Pomwepo iye uja adadzambatuka, mwinjiro wake uko chi, kuthamangira kwa Yesu. Yesu adamufunsa kuti, “kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Wakhunguyo adayankha kuti, “Mbuyanga, ndikufuna kuti ndizipenyanso.” Yesu adamuuza kuti, “chabwino, ungathe kupita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Nthawi yomweyo adayambadi kupenya, nkumatsata Yesu paulendowo.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale mogwirizana ndi Yesu Khristu amene ali wansembe wathu wamkulu, tiyeni tipereke mapemphero athu kwa Atate athu a Kumwamba:

 

1.     Atate, muunikire Mpingo wanu kuti uunikire anthu a mafuko onse pakuwalalikira Mthenga Wabwino mosaopa ndi mosakaika.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate, mufewetse mitima ya onse amene sali mu Mpingo mwanu kuti azindikire kukoma mtima kwanu, polandira chithandizo kwa anthu anzao.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate, muthandize anthu akhungu ndi ena onse amene ali m'mavuto kuti azindikire kukoma mtima kwanu, polandira‚ chithandizo kwa anthu anzawo.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate, muwongolere nzeru zathu ndi mitima yathu, kuti ntchito zathu ziwonetse kuwala kwanu pamaso pa anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.

Mulungu Atate athu, tikukuthokozani chifukwa ndinu wa chifundo chopanda malire, ndipo simukhala kumvera mapemphero a anthu onse okhulupirira Inu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Sunday, October 20, 2024

CHIBALALITSO CHA MPINGO – B.

CHIBALALITSO CHA MPINGO – B.

“Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni anthu onse Mthenga Wabwino”.

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YONA: YONA 03: 10 – 04, 11.

 

Mulungu adawona zimene anthu a ku Ninive adachita, ndi m’mene adasiyira makhalidwe ao oipa. Choncho adakhululuka, osawapatsa chilango chimene adaati adzawapatsa. Chifukwa cha zimenezi Yona adakhumudwa kwambiri, nakwiya. Tsono adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, nzimenezitu zimene ndinkaopa ndili kwathu. Nchifukwa chake ndidaayetsetsa kuthawira ku Tarisisi. Ndidaadziwa kuti ndi Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, woleza mtima ndi wachikondi chosasinthika, ndiponso wokhululukira machimo nthawi zonse. Ndiye tsono Inu Chauta, ndapota nanu, ingondiphani basi. Nkwabwino kuti ndife, kupambana kukhala ndi moyo.” Chauta adamufunsa kuti, “kodi iwe wachita bwino pokwiya chotere?” Yona adatuluka mumzindamo nakakhala pansi chakuvuma kwake. Kumeneko adadzimangira chithando nakhala m’menemo mu mthunzi, kudikira kuti aone zimene zichitike mumzindamo. Tsono Chauta Mulungu adameretsa msatsi kuti umchitire Yona mthunzi ndi kumuchotsa mavuto ake. Yona adakondwa kwambiri chifukwa cha msatsiwo. Koma m’mawa mwake mbandakucha, Mulungu adatuma mphanzi kuti ukadye msatsiwo, ndipo udafota. Pamene dzuwa linkatuluka, Chauta adautsira Yona mphepo yotentha kuti iwombe kuchokera kuvuma. Dzuwa lidamtentha pa mutu Yoona, mpaka kulenguka nalo. Tsono adapempha kuti afe, adati, “nkwabwino kuti ndife, kupambana kukhala moyo.” Koma Mulungu adamufunsa kuti, “kodi wachita bwino pokwiya chifukwa cha msatsiwu?” Iye adati, “inde, ndachita bwino kukwiya. Kukwiya kwake nkofa nako.” Chauta adati, “iwe ukumvera chisoni msatsi umene sudaugwirire ntchito, sindiwe unaubzala ndi kukuuza. Udamera pa usiku umodzi, nafanso pa usiku umodzi. Nanga Ine, kodi sindiyenera kumvera chisoni mzinda waukulu wa Ninive? M’mene mujatu muli anthu opitirira zikwi 120, amene sadziwa kusiyanitsa kuti zabwino nziti, zoipa nziti, mulinso ziweto zochuluka.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 96: 01 – 03, 08, 10.

 

Simbani za ntchito zodabwitsa za Ambuye kwa anthu onse.

 

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano!

Imbirani Chauta, anthu a m’dziko lonse lapansi!

Imbirani Chauta, tamandani dzina lake!

 

Simbani za ntchito zodabwitsa za Ambuye kwa anthu onse.

 

Lengezani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse,

Simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m’maiko onse,

Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta,

Uzani mitundu ya anthu kuti, “Chauta ndiye Mfumu.”

 

Simbani za ntchito zodabwitsa za Ambuye kwa anthu onse.

-------------------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA 10: 09 – 18.

 

Mbale wanga, ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. Chifukwa munthu amati akakhulupirira ndi mtima wake, amapezeka wolungama pamaso pa Mulungu, ndipo amati akavomereza chikhulupiriro chakecho ndi pakamwa pake, amapulumuka. Paja malembo akuti, “munthu aliyense wokhulupirira Iye, sadzachita manyazi.” Choncho palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakuti Mulungu ndiye Ambuye a onse, ndipo amadalitsa moolowa manja onse otama dzina lake mopemba. Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.” Kodi anthu angatame Mulungu bwanji mopemba ngati sadamkhulupirire? Ndipo angamkhulupirire bwanji ngati sadamve za Iye? Ndipo angamve za Iye bwanji ngati palibe wina olalika? Ndipo anthu angalalike bwanji palibe owatuma? Paja mau a Mulungu akuti, “Nchokondweretsa zedi kuwona olalika Uthenga Wabwino akufika.” Koma si onse amene adalandira Uthenga Wabwinowo. Ndi monga mneneri Yesaya anenera kuti, “Ambuye, ndani adakhulupirira zimene tidalalika?” Motero munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva, ndipo zimene wamvanzo zimachokera ku zolalika za Khristu. Koma ntafunsa: kodi ndiye kuti Aisraele sadawamve mauwo? Iyai, kumva adamva ndithu. Ndi monga mau a Mulungu anenera kuti, “liwu lao lidamveka pa dziko lonse lapansi, mau ao adafika mpaka ku malekezero a dziko.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO –

Alleluia, Alleluia – Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni anthu onse Mthenga Wabwino.  – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 16: 15 – 20.

 

Panthawi imeneyo, Yesu adawauza kuti, “pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni anthu onse Uthenga Wabwino. Amene akakhulupirire ndi kubatizidwa, adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira, adzaweruzidwa kuti ngwolakwa. Okhulupirira azidzachita zozizwitsa izi: azidzatulutsa mizimu yoipa potchula dzina langa, azidzalankhula zilankhulo zachilendo, ndipo akagwira njoka kapena kumwa chakumwa chotha kuwapha, sadzapwetekedwa. Akasanjika manja pa anthu odwala, anthuwo azidzachira.” Ambuye Yesu atalankhula nawo, adatengedwa kupita Kumwamba, nakakhala pa dzanja lamanja la Mulungu. Tsono ophunzira aja adanka nalalika ponseponse. Ambuye ankagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo ankatsimikiza mau ao ndi zozizwitsa zimene ankachita.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------


Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pakuti Mulungu ndiye Ambuye a onse, ndipo amadalitsa moolowa manja onse amene apempha kuti awathandize, tiyeni, tipemphe Atate athu akumwamba kuti Ufumu wao udze ndi kukhazikika ku maiko onse:

 

1.     Tipempherere Eklezia, Mpingo woyera wa Mulungu, kuti aunikire anthu a mafuko onse ndi maphunzitso ake ndi ntchito zake zachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere akhristu amene akuzunzidwa chifukwa cha Mthenga Wabwino, kuti alimbike m’chikhulupiriro chao.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere anyamata ndi atsikana, kuti apezeke ambiri odzipereka ku ntchito yofalitsa Mthenga Wabwino, ku dziko la kwao ndiponso ku maiko akunja.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Tidzipempherere ife tomwe tili muno, kuti tikhale otekeseka ndi chipulumutso cha anthu onse, pakuwapempherera ndi pakuthandiza ntchito zamishoni ku maiko akunja.
Tikupemphani, mutivomereze.

Atate, Inu mufuna kuti anthu onse apulumuke ndipo adziwe zoona. Kuwala kwa Mthenga Wabwino kuwaunikire onse, kuti azindikire kukoma mtima kwanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, October 19, 2024

LAMULUNGU LA 29 PA CHAKA – B

LAMULUNGU LA 29 PA CHAKA – B.

“Mwana wa Munthu adabwera kuti adzatumikire anthu, ndipo kudzapereka moyo wake chifukwa cha onse.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 53: 10 – 11. (Iye adapereka moyo wake ukhale nsembe yokhululukira machimo.)

 

Komabe ndi Chauta yemwe amene adaafuna kuti amuzunze, ndipo adamsautsadi. Iye adapereka moyo wake kuti ukhale nsembe yokhululukira machimo. Choncho adzaona zidzukulu zake, adzakhala ndi moyo wautali, ndipo chifuniro cha Chauta chidzachitika mwa iye. Atatha mazunzo akewo, adzaona phindu lake, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzasenza machimo a anthu onse kuti iwo ambiri a iwo asadzapezekenso kuti ndiopalamula.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 33: 04 – 05, 18 – 20, 22.

 

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

 

Mau a Chauta ndi olungama,

Zochita zake zonse amazichita mokhulupirika,

Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera,

Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.

 

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

 

Chauta amayang’ana anthu omumvera,

Ndi odalira chikondi chake chosasinthika,

Iye amachita izi kuti awapulumutse ku imfa,

Ndi kuwasungira moyo anthuwo pa nthawi ya njala.

 

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

 

Mitima yathu ikuyembekeza Chauta,

Chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu,

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika,

Chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

 

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

-------------------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA AHEBRI: AHEBRI 04: 14 – 16. (Tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima.)

 

Tiyeni tsono, tigwiritse chikhulupiriro chimene timavomereza. Pakuti tili naye Mkulu wa ansembe wopambana, amene adapita mpaka kukafika kumwamba kwenikweni kwa Mulungu. Iyeyu ndi Yesu, Mwana wa Mulungu. Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse. Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthawi yake yeniyeni.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MARKO 10: 45.

Alleluia, Alleluia – Mwana wa Munthu adabwera kuti Iyeyo adzatumikire ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 10: 35 – 45. (Mwana wa Munthu adabwera kuti apereke moyo wake kuti aombole anthu ochuluka).

 

Yakobo ndi Yohane, ana aja a Zebedeo, adadzauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ife timati bwanji titakupemphani kanthu, mutichitire.” Yesu adaŵafunsa kuti, “Inuyo mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani?” Iwo adati, “Timafuna kuti pamene mudzakhale mu ulemerero wanu, mudzatiike wina ku dzanja lanu lamanja, wina ku dzanja lanu lamanzere.” Koma Yesu adati, “Simukudziŵa zimene mukupempha. Kodi inu mungathe kumwa nao chikho chamasautso chimene ndikudzamwera Ine? Kodi inu mungathe kulandira nao ubatizo wa mavuto umene ndikudzalandira Ine?” Iwo aja adayankha kuti, “Inde, tingathe.” Apo Yesu adati, “Chabwino, chikho chimene Ine ndikudzamwacho, inunso mudzamwa nao, ndipo ubatizo umene Ine ndikudzalandirawo, inunso mudzalandira nao. Koma Ineyo si udindo wanga kusankha munthu kuti akhale ku dzanja langa lamanja, kapena ku dzanja langa lamanzere. Mulungu ndiye adzapereke malo ameneŵa kwa omwe Iye mwini adaŵakonzera.” Pamene khumi ena aja adamva zimenezi, adapsera mtima Yakoboyo ndi Yohaneyo. Koma Yesu adaŵaitana ophunzira akewo, naŵauza kuti, “Mukudziŵa kuti pakati pa anthu akunja, anthu amene amati ngolamulira, amadyera anthu ao masuku pa mutu. Akuluakulu aonso amaonetsadi mphamvu zao pa anthu ao. Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, azikhala mtumiki wanu. Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, azikhala kapolo wa onse. Chitani monga m’mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pamodzi ndi mapemphero athuwa tipereke kwa Mulungu zowawa ndi zovuta zamitundumitundu zimene anthu amapeza m’dziko lino lapansi:

 

1.     Atsogoleri a Mpingo atumikire akhristu ao modzichepetsa ndi mosadziwerengera, ndipo asaope kumva zowawa ndi kutaya moyo wao womwe chifukwa cha iwo.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akhristu amene akuzunzidwa chifukwa chokhulupirira Mulungu, aonetse kulimba mtima, podziwa kuti mphotho yao idzakhala yaikulu Kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anthu odwala ndi ena onse amene akuvutika m'mitima mwao apeze mphamvu zopirira mavuto, polingalira za kuzunzidwa kwa Yesu Khristu Mpulumutsi.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe tiyesetse kuiwala zowawa ndi zovuta zathu poganizira kusauka kwa anzathu, ndipo tiwathandize m’zowawa zao potsata chitsanzo chimene Ambuye adatisiyira.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, tikupereka kwa Inu mapemphero athu amenewa, podziwa kuti mudzatimvera chifundo ndi kutithandiza pa nthawi yake. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, October 12, 2024

LAMULUNGU LA 28 PA CHAKA – B.

LAMULUNGU LA 28 PA CHAKA – B.

“Tizifunafuna chuma chenicheni chokhutitsa mtima wa munthu.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA LUNTHA: LUNTHA 07: 07 – 11. (Chuma ndidachiyesa chachabe nditachilinganiza ndi luntha).

 

Tsono ine ndidapemphera, ndipo adandipatsa nzeru. Ndidapemphera kwa Mulungu, ndipo mzimu wa luntha udalowa mwa ine. Ndinkakonda luntha kupambana ndodo yaufumu ndi mipando yachifumu, chuma ndidachiyesa chachabe nditachilinganiza ndi luntha. Sindidalilinganize ndi miyala yamtengowapatali, chifukwa golide yense wa pansi pano ndi kamchenga chabe pafupi ndi luntha, ndipo siliva ali ngati fumbi poyerekeza ndi luntha. Ndinkakonda luntha kupambana moyo ndi kukongola. Ndinkakonda kukhala nalo kupambana kukhala ndi kuwala kwa dzuwa, chifukwa kuwala kwa lunthalo nkosalekeza. Zabwino zonse zidandidzera pamodzi ndi luntha.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 90: 12 – 17.

 

Tidzazeni ndi chikondi chanu kuti tisangalale.

 

Tsono tiphunzitseni kuwerenga masiku athu,

Kuti tikhale ndi mtima wanzeru,

Lezani mtima, Inu Chauta. Nanga mudzatikwiyira mpaka liti?

Achitireni chifundo atumiki anu.

 

Tidzazeni ndi chikondi chanu kuti tisangalale.

 

Tidzazeni m’mawa mulimonse ndi chikondi chanu chosasinthika,

Kuti tizikondwa ndi kusangalala masiku athu onse.

Tisangalatseni masiku amene mudatisautsira,

Zaka zambiri monga zaka zimene tidaona mavuto.

 

Tidzazeni ndi chikondi chanu kuti tisangalale.

 

Mulole kuti ntchito zanu ziwoneke kwa atumiki anu,

Mphamvu zanu zaulemerero ziwoneke kwa ana ao,

Inu Ambuye, Mulungu wathu, mutikomere mtima,

Ndithu mudalitse ntchito zonse za manja athu.

 

Tidzazeni ndi chikondi chanu kuti tisangalale.

-------------------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA AHEBRI: AHEBRI 04:12 – 13. (Mau a Mulungu amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m’mitima mwao).

 

Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lokuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m’mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m’mitima mwao. Pamaso pa Mulungu palibe kanthu kobisika, zonse zili poyera ndipo nzovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 05: 03.

Alleluia, Alleluia – Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 10: 17 – 30. (Kagulitse zonse zimene uli nazo. Kenaka ubwere, uzidzanditsata).

 

Pamene Yesu ankanyamuka kuti azipita, munthu wina adamuthamangira. Adadzamugwadira namafunsa kuti, “Aphunzitsi abwino, kodi ndizichita chiyani kuti ndikalandire moyo wosatha?” Yesu adamuyankha kuti, “unditchuliranji wabwino? Wabwinotu ndi mmodzi yekha, Mulungu basi. Malamulo ukuwadziwa: Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama, usadyerere mnzako, lemekeza atate ako ndi amai ako.” Munthu uja adati, “Aphunzitsi, zonsezi ndakhala ndikuzitsa kuyambira ndili mwana.” Yesu atamuyang’ana, adamkonda nkumuuza kuti, “ukusowabe chinthu chimodzi: pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.” Atamva zimenezo, munthu uja nkhope yake idagwa, adangochokapo ali wovutika mu mtima, chifukwa adaali munthu wa chuma chambiri. Yesu adayang’ana ophunzira ake amene adaamzungulira nawauza kuti, “nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akalowe mu Ufumu wa Mulungu.” Ophunzirawo adadabwa nawo kwambiri mau akewa. Koma Yesu adabwerezanso, adati, “ndithu, inu ana anga, nkwapatali kukalowa mu Ufumu wa Mulungu. Nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka Zingano, kupambana kuti munthu wachuma akalowe mu Ufumu wa Mulungu.” Pamenepo ophunzira aja adazizwa koposa, nayamba kufunsana kuti, “tsono nanga angathe kupulumuka ndani?” Yesu adawayang’ana nati, “kwa anthu nkosathekadi, koma ndi Mulungu ai, nkotheka. Paja ndi Mulungu zonse nzotheka.” Pamenepo Petro adayamba kulankhula naye, adati, “ifetu paja tidasiya zonse kuti tizikutsatani.” Yesu adati, “ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wosiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine, ndiponso chifukwa cha Uthenga Wabwino, ameneyo pansi pompano adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri kuposa kale: nyumba, abale, alongo, amai, ana, minda, komanso mazunzo. Ndipo kutsogoloko adzalandira moyo wosatha.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, wabwino ndi m’modzi yekha, ndiye Mulungu. Tiyeni tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti atsire madalitso ao pa anthu onse:

 

1.     Atate, muthandize ansembe kupewa khumbo la chuma, aziwonetsa akhristu ao kuti chikondi chanu chikupambanadi zabwino zonse za m’dziko lapansi.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate, mufewetse mitima ya anthu opata kuti asanyadire chuma chawo, koma adziwe kuthandiza anzawo osauka.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate, mulimbitse mitima ya anthu ovutika, kuti azindikire kukoma mtima kwanu, polandira chithandizo kwa anzawo achifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate, mau anu asaleke kugwira ntchito m’mitima mwathu, kuti tithandize m’chikondi chanu ndi kumatumikira anzathu mosadziwerengera.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, popereka kwa Inu mapemphero athuwa tilikukuyamikani kukoma mtima kwanu, pakuti Inu nokha ndinu wabwino, ndipo chikondi chanu nchosasinthika. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, October 5, 2024

LAMULUNGU LA 27 PA CHAKA – B

LAMULUNGU LA 27 PA CHAKA – B.

“Za Ulemerero wa Moyo wa Banja.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS: GENESIS 02: 18 – 24.(Adzakhala thupi limodzi).

 

Chauta adati, “sibwino kuti munthuyo akhale yekha. Ndipanga mnzake woti azimthandiza.” Chauta adatenga dothi naumba nyama zonse ndi mbalame zonse, nabwera nazo kwa Adamu kuti azitche maina. Mwakuti maina amene Adamu adazitcha, maina ake ndi omwewo. Adamu adazitcha maina nyama zonse, mbalame ndi zamoyo zonse zakuthengo. Komabe panalibe mnzake woti azimthandiza. Tsono Chauta adagonetsa Adamu tulo tofanato, ndipo ali m’tulo choncho, Mulungu adamchotsako nthiti, natsekapo ndi mnofu pamalopo. Chauta Mulungu adapanga mkazi ndi nthiti imene adaichotsa kwa Adamu uja, ndipo mkaziyo Mulungu adabwera naye kwa iye. Adamu adati, “uyutu ndiye ndi fupa lochokera ku mafupa anga, mnofu wochokera ku mnofu wanga. Adzatchedwa Mkazi, chifukwa watengedwa kwa Mwamuna.” Nchifukwa chake mwamuna amasiya atate ndi amai, ndipo amaphatikana ndi mkazi wake, choncho

awiriwo amakhala thupi limodzi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 128.

 

Chauta atidalitse ife masiku onse a moyo wathu.

 

Ngwodala aliyense woopa Chauta,

Amene amayenda m’njira zake,

Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito,

Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.

 

Chauta atidalitse ife masiku onse a moyo wathu.

 

Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka,

M’kati mwa nyumba yako.

Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi,

Kuzungulira tebulo lako.

 

Chauta atidalitse ife masiku onse a moyo wathu.

 

Zoonadi, ndimo m’mene adzakhalire wodala munthu woopa Chauta,

Chauta amene amakhala ku Ziyoni akudalitse,

Uwone m’mene Yerusalemu zinthu zidzamuyendera bwino masiku onse a moyo wako,

Ukhale ndi moyo wautali kuti uwone zidzukulu zako,

Mtendere ukhale ndi Israele.

 

Chauta atidalitse ife masiku onse a moyo wathu.

-------------------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA AHEBRI: AHEBRI 02: 09 – 11. (Amene amayeretsa anthuyo, ndiponso anthu amene amayeretsedwawo, onse Tate wao ndi mmodzi).

 

Abale, tikuwona kuti Yesu, amene pa kanthawi pang’ono adaasanduka wochepera kwa angelo, adalandira mphotho ya ulemerero ndi ulemu chifukwa adamva zowawa za imfa. Zidatero chifukwa mwa kukoma mtima kwake Mulungu adaafuna kuti afere anthu onse. Paja Mulungu amene ndi mlengi wa zonse ndipo zonse zimalinga kwa Iye, adafuna kufikitsa ana ake ambiri ku ulemerero. Tsono kudaamuyenera kuti mwa njira ya zowawa, amsandutse Yesu mtsogoleri wangwiro wowatsogolera ku chipulumutso. Amene amayeretsa anthuyo, ndiponso anthu amene amayeretsedwawo, onse Tate wao ndi mmodzi. Nchifukwa chake Yesu sachita manyazi kuwatchula abale ake.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – 01 YOHANE 04: 12.

Alleluia, Alleluia – Tikamakondana, Mulungu amakhala mwa ife, ndipo chikondi chake chafika pake penipeni mwa ife. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 10: 02 – 16. (Chimene Mulungu wachimanga, munthu sangachisamale).

 

Pa kanthawi yomweyo, kudafika Afarisi ena, namafunsa Yesu kuti, “kodi nkololedwa kuti munthu asudzule mkazi wake?” Pomufunsa choncho ankangofuna pomupezera chifukwa. Koma Yesu poyankha adati, “kodi Mose adakulamulani zotani?” Iwo adati, “Mose Adalola kuti munthu azilembera mkazi wake kalata yachisudzulo kenaka nkumuchotsa.” Yesu adati, “Mose adaakulemberani lamulo limeneli chifukwa cha kukanika kwanuku. Komatu pachiyambi paja, pamene Mulungu adalenga zonse, adawalenga anthu, wina wamwamuna wina wamkazi. Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ndi amai, nakaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzasanduka thupi limodzi. Choncho tsopano salinso awiri, koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumikiza pamodzi, munthu asazilekanitse.” Pamene adalowanso m’nyumba, ophunzira adamufunsanso Yesu za nkhani yomweyi. Iye adawauza kuti, “aliyense amene asudzule mkazi wake nakwatira wina, akuchita chigololo, ndipo akumchimwira mkazi wakeyo. Chimodzimodzinso ngati mkazi asudzula mwamuna wake, kenaka nkukwatiwa ndi wina, nayenso akuchita chigololo.” Anthu ena ankabwera ndi ana kwa Yesu kuti awakhudze ndi kuwadalitsa, ophunzira ake nkumawazazira. Yesu ataona zimenezi, adakalipa nawauza kuti, “alekeni anawa azibwera kwa Ine, musawaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere. Ndithu ndikunenetsa kuti yemwe salandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, ameneyo sadzalowamo.” Atatero adayamba kuwafungata anawo, nawasanjika manja ndi kuwadalitsa.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Yesu sachita manyazi kutitcha abale ake. Tiyeni tsono, pamodzi naye, tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti atsire madalitso ao pa anthu onse:

 

1.     Tipempherere Eklezia, Mpingo wa Mulungu, kuti apitirize ntchito yake yochirikiza ndi yokometsa mabanja onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere akulu onse olamulira maiko, kuti ateteze ma-banja a anthu, ndipo awathandize kutukula miyoyo yao.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere mabanja onse, kuti eni ake adziwe kukhulupirirana ndi kupirirana pa moyo wao wonse, monga Mulungu afunira.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Tidzipempherere ife tomwe tili muno kuti tithandizane podzetsa mtendere ndi kuyanjana pakati pa anthu onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

Atate, tikukupemphani zonsezi ndi mtima wokhulupirira Inu, pakuti mudatipatsa Mwana wanu kuti atitsogolere ku ulemerero wosatha. Ma Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...