Saturday, October 26, 2024

LAMULUNGU LA 30 PA CHAKA – B

LAMULUNGU LA 30 PA CHAKA – B.

“Inu Yesu, Mwana wa Davide, Mundichitire chifundo.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YEREMIYA: YEREMIYA 31: 07 – 09. (Ndidzasonkhanitsa akhungu ndi opunduka. Ine ndidzawaperekeza ndi mtima wachifundo).

 

Chauta akuti, “imbani mokweza ndi mosangalala chifukwa cha Yakobo. Fuulani chifukwa cha mtundu wopambana mitundu yonse. Lalikani, tamandani ndi kulengeza kuti, Chauta wapulumutsa anthu ake, wasunga otsala a Israele. Ndidzawatulutsa kuchokera ku dziko lakumpoto. Ndidzasonkhanitsa akhungu ndi opunduka, akazi amene ali ndi pakati ndi amene ali pa nthawi yao yochira. Chidzakhala chinamtindi cha anthu obwerera kuno. Adzabwerera kwao akulira, koma Ine ndidzawaperekeza ndi mtima wachifundo. Ndidzawatsogolera ku mitsinje yodzaza ndi madzi. Sadzaphunthwa, njira yao idzakhala yosalala kwambiri. Ine ndine bambo wake wa Israele, Efuremu ndi mwana wanga wachisamba.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 126: 01 – 02, 02 – 03, 04 – 05, 06.

 

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

 

Pamene Chauta adabwezera akapolo ku Ziyoni,

Tinali ngati anthu amene akulota,

Pamenepo tidasekera kwambiri,

Ndipo tidalulutira ndi chimwemwe.

 

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

 

Tsono mitundu ina ya anthu inkanena kuti,

“Chauta wawachitira zazikulu,”

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu,

Ndipo tasangalala.

 

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

 

Tibwezereni ufulu wathu, Inu Chauta,

Tikhale ngati mitsinje ya m’chipululu,

Anthu amene amafesa akulira,

Adzakolola akufuula ndi chimwemwe.

 

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

 

Munthu amene amapita akulira, atatenga mbeu zokafesa,

Adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe,

Atatenga mitolo yake yambiri.

 

Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.

-------------------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA AHEBRI: AHEBRI 05: 01 – 06. (Ndiwe Wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.)

 

Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa pakati pa anthu, namuika kuti aziwaimirira pamaso pa Mulungu. Ntchito yake nkupereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo. Popeza kuti iye yemweyo ali ndi zofooka zambiri, ndiye kuti angathe kuwalezera mtima amene ali opanda nzeru ndi osokera. Nchifukwa chake aumirizidwa kumapereka nsembe chifukwa cha machimo a iye yemwe, ndiponso machimo a anthu ena. Palibe munthu amadzitengera yekha ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma amachita kuitanidwa ndi Mulungu, monga momwe adaaitanidwira Aroni. Momwemonso Khristu sadadzikweze yekha ku ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma Mulungu ndiye adachita kumuuza kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga, Ine lero ndakubala. Penanso Mulungu adati, ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – 02 TIMOTEO 01: 10.

Alleluia, Alleluia – Mpulumutsi wathu Khristu Yesu adathetsa mphamvu za imfa, ndipo mwa Uthenga Wabwino adafalitsa moyo umene sungafe konse. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 10: 46 – 52. (Mbuyanga, ndikufuna kuti ndizipenyanso).

 

Yesu ndi ophunzira ake pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu adafika ku mzinda wa Yeriko. Tsono pamene ankatuluka mumzindamo, adapeza wakhungu wina wopemphapempha atakhala pansi pamphepete pa mseu. Munthuyo dzina lake anali Baratimeo, mwana wa Timeo. Tsono iyeyo atamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, adayamba kufuula kuti, “Inu Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.” Anthu ambiri adamzazira kuti akhale chete. Koma iye adafuulirafuulira kuti, “Inu Mwana wa Davide mundichitire chifundo.” Yesu adaima, nauza anthu kuti, “tamuitanani.” Anthu aja adamuitana wakhunguyo namuuza kuti, “limba mtima, nyamuka, akukuitana.” Pomwepo iye uja adadzambatuka, mwinjiro wake uko chi, kuthamangira kwa Yesu. Yesu adamufunsa kuti, “kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Wakhunguyo adayankha kuti, “Mbuyanga, ndikufuna kuti ndizipenyanso.” Yesu adamuuza kuti, “chabwino, ungathe kupita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Nthawi yomweyo adayambadi kupenya, nkumatsata Yesu paulendowo.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale mogwirizana ndi Yesu Khristu amene ali wansembe wathu wamkulu, tiyeni tipereke mapemphero athu kwa Atate athu a Kumwamba:

 

1.     Atate, muunikire Mpingo wanu kuti uunikire anthu a mafuko onse pakuwalalikira Mthenga Wabwino mosaopa ndi mosakaika.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate, mufewetse mitima ya onse amene sali mu Mpingo mwanu kuti azindikire kukoma mtima kwanu, polandira chithandizo kwa anthu anzao.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate, muthandize anthu akhungu ndi ena onse amene ali m'mavuto kuti azindikire kukoma mtima kwanu, polandira‚ chithandizo kwa anthu anzawo.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate, muwongolere nzeru zathu ndi mitima yathu, kuti ntchito zathu ziwonetse kuwala kwanu pamaso pa anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.

Mulungu Atate athu, tikukuthokozani chifukwa ndinu wa chifundo chopanda malire, ndipo simukhala kumvera mapemphero a anthu onse okhulupirira Inu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...