Saturday, November 2, 2024

LAMULUNGU LA 31 PA CHAKA – B.

 

LAMULUNGU LA 31 PA CHAKA – B.

“Kodi Mwa Malamulo onse, Lamulo Loposa Nliti”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA DEUTORONOMO: DEUTORONOMO 06: 02 – 06. (“Mverani, Inu Aisraele, muzikonda Chauta, ndi mtima wanu wonse”).

 

Mose analankhula ndi anthu ake nawauza kuti, “muzikaopa Chauta, Mulungu wanu, ndipo muzikamvera malamulo ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsaniwa, kuti pakutero mukhale moyo nthawi yaitali. Inu Aisraele, mutchere khutu, ndipo muchenjere, mumveredi malamulowa. Tsono zinthu zidzakuyenderani bwino, ndipo mudzakhala mtundu wochuluka zedi ndi kumakhala m’dziko lamwanaalirenji, monga momwe Chauta, Mulungu wa makolo anu, adakulonjezerani. Mverani, Inu Aisraele, Chauta Mulungu wanu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse. Muziwasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani lerowa.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 18: 02 – 04, 47, 51.

 

Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga.

 

Ndimakukondani Chauta, inu mphamvu zanga,

Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi Mpulumutsi wanga,

Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathawirako,

Ndiye chishango changa, ndiye Mtetezi wanga, ndiye linga langa,

Ndimaitana Chauta, amene ayenera kumtamanda,

Ndipo amandipulumutsa kwa adani anga.

 

Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga.

 

Chauta ndi wamoyo. Litamandike thanthwe langa,

Alemekezeke Mulungu wondipulumutsa,

Amathandiza mfumu yake, kuti izipambana,

Amaonetsa chikondi chake chosasinthika kwa wodzozedwa wake.

 

Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga.

-------------------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA AHEBRI: AHEBRI 07: 23 – 28. (Yesu ngwamuyaya, motero unsembe wake ngwosasinthika).

 

Abale, ansembe akale aja anali ambiri, chifukwa ankafa, sankatha kupitirira ndi udindo waowo. Koma Yesu ngwamuyaya, motero unsembe wake ngwosasinthika. Nchifukwa chake angathe kuwapulumutsa kwathunthu anthu amene akuyandikira kwa Mulungu kudzera mwa Iye, pakuti Iyeyo ali ndi moyo nthawi zonse kuti aziwapempherera. Tsono padaafunika kuti tikhale naye wotere mkulu wa ansembe: woyera mtima, wopanda choipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kubzola zonse zakumwambaku. Yesu ameneyu sali ngati akulu a ansembe ena aja. Palibe chifukwa chakuti tsiku ndi tsiku azipereka nsembe poyamba chifukwa cha machimo ake, kenaka chifukwa cha machimo anthu. Zimenezi adachitiratu kamodzi kokha, pakudzipereka yekha ngati nsembe. Malamulo a Mose amaika anthu amene ali ndi zofooka, kuti akhale akulu a ansembe onse. Koma mau a lumbiro la Mulungu lija limene lidabwera pambuyo pa Malamulowo, adaika Mwana wake, amene wakhala wangwiro kwamuyaya kuti akhale mkulu wa ansembe onse.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 14: 23.

Alleluia, Alleluia – Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO 12: 28 – 34. (Uzikonda Chauta, Mulungu wako. Uzikonda mnzako).

 

Mphunzitsi wina wa Malamulo adawamva akutsutsana. Ataona kuti Yesu wawayankha bwino Asaduki aja, adadza pafupi, namufunsa kuti, “kodi mwa malamulo onse, lalikulu ndi liti?” Yesu adamuyankha kuti, “lamulo lalikulu ndi ili, tamverani, inu Aisraele, Chauta, Mulungu wathu, Iye yekha ndiye Mulungu. Motero, uzikonda Chauta, Mulungu wakoyo, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse. Lamulo lachiwiri lake ndi ili, uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe. Palibe lamulo lina loposa malamulo amenewa.” Mphunzitsi wa Malamulo uja adati, “ai, mwayankha bwino, Aphunzitsi. Monga mwaneneramo, nzoonadi kuti Mulungu ndi mmodzi yekhayo, ndipo palibe winanso koma Iye yekha. Mwalondolanso ponena chinthu chopambana ndicho kumkonda Mulungu ndi mtima wonse, ndi nzeru zonse, ndi mphamvu zonse, ndiponso kukonda mnzako monga umadzikondera iwe wemwe. Kuteroko nkoposa kupereka nsembe zopsereza ndiponso nsembe zina zonse.” Yesu adaona kuti munthuyo wayankha mwanzeru. Tsono adamuuza kuti, “iwe suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu.” Ndipo kuyambira apo panalibenso wina woti ayesere kumufunsa kanthu.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pakuti Mulungu amatikonda modabwitsa, timupemphe kuti adzaze mitima yathu ndi ya anthu onse ndi mzimu wake wachikondi:

 

1.     Tipempherere akhristu onse kuti aonetse mtima wachikondi pa moyo wao wonse, makamaka pomathandiza anzao osauka.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere atsogoleri a Mpingo kuti aongolere anthu ao m’njira ya chikondi ndi kudzetsa ubale weniweni pakati pa anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere anthu odwala, ovulala ndi onse amene akuvutika kuti apeze anzao achifundo odzawasamala ndi kuwalimbitsa mtima.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe a m'Parishi ino, kukondana kwathu kupite m’tsogolo, kusonyeza kuti Mbuye akukhaladi pakati pathu.
Tikupemphani, mutivomereze.

Mulungu wathu, popereka kwa Inu mapemphero athuwa, tikukutchulani kuti, “Atate” pokhulupirira chikondi chanu chosasinthika. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...