LAMULUNGU LA 32 PA CHAKA – B.
“Ufulu Umaitana Ufulu Unzake.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LOYAMBA LA MAFUMU: 01 MAFUMU 17: 10 – 16. (“Pitani, mundiphikire kakeke.” Maiyo, nakachitadi monga momwe adaanenera Eliya).
Eliya adanyamuka napita ku Zarefati. Atafika pa chipata cha mzindawo, adangoona mai wamasiye akutola nkhuni. Tsono adaitana maiyo namuuza kuti, “patseniko madzi pang’ono, ndimwe.” Pamene mai uja ankapita kukatunga madziwo, Eliya adamuitananso namuuza kuti, “mundintengerekonso kabuledi.” Apo maiyo adati, “pali Chauta, Mulungu wanu, ine sindidaphike kanthu kalikonse, koma ndili ndi ufa pang’ono m’mbiya, ndi mafuta pang’ono m’nsupa. Tsono ndikutola nkhuni zoti ndikaphikire kaufako, kuti ndikadye ine ndi mwana wanga, kenaka kufa kukhala komweko.” Koma Eliya adauza maiyo kuti, “musade nkhawa. Pitani, mukachite monga mwaneneramo. Koma poyamba mutapeko kaufa pang’ono, mundiphikire kakeke, mubwere nako kuno. Pambuyo pake mukaphikenso kuti mudye inuyo ndi mwana wanu. Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘ufa umene uli m’mbiyawo sudzatha, mafutanso amene ali m’nsupawo sadzatha, mpaka tsiku limene Chauta adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’” Tsono maiyo adapita, nakachitadi monga momwe adaanenera Eliya. Maiyo ndi Eliya ndiponso onse a pa banja la maiyo adadya ufawo masiku ambiri. Ufa umene unali m’mbiyamo sudathe, mafuta amene anali m’nsupawo sadathenso, monga momwe Chauta adaalankhulira kudzera mwa Eliya.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 146: 07 – 10.
Mtima wanga, tamanda Chauta.
Amasunga malonjezo ake nthawi zonse,
Amachitira anthu opsinjidwa zolungama,
Amawapatsa chakudya anthu anjala,
Chauta amamasula am’ndende.
Mtima wanga, tamanda Chauta.
Chauta amatsekula maso a anthu osapenya,
Chauta amakweza anthu otsitsidwa,
Chauta amakonda anthu ochita chilungamo,
Chauta amateteza alendo.
Mtima wanga, tamanda Chauta.
Amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye,
Koma njira za anthu oipa amazipotoza,
Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya,
Mulungu wako, iwe Ziyoni,
Adzalamulira ku mibadwo yonse.
Mtima wanga, tamanda Chauta.
-------------------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA AHEBRI: AHEBRI 09: 24 – 38. (Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze machimo a anthu).
Abale, Khristu sadalowe m’malo opatulika omangidwa ndi anthu, malo ongofanizira malo enieni opatulika a Kumwamba. Iye adapita Kumwamba kwenikweniko, kuti tsopano aziwonekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife. Mkulu wa ansembe onse amalowa m’malo Opatulika Kopambana chaka ndi chaka atatenga magazi amene sali ake. Koma Khristu sadalowe Kumwamba kuti azidzipereka nsembe kawirikawiri. Zikadatero, akadayenera kumamva zowawa kawirikawiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma monga zilirimu, waoneka kamodzi kokha pakutha pake pa nthawi yotsiriza, kuti achotse uchimo pakudzipereka yekha nsembe. Munthu aliyense amafa kamodzi kokha, pambuyo pake nkumaweruzidwa. Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiwiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 05: 03.
Alleluia, Alleluia – Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO 12: 38 – 44. (Mai wamasiye wosaukayu waponyamo koposa anthu ena onsewa).
Pamenepo Yesu ankawaphunzitsa, adati, “chenjera nawoni aphunzitsi a Malamulo. Amakonda kuyenda atavala mikanjo yaitali, ndi kuti anthu aziwalonjera mwaulemu pa misika. Amakonda mipando ya ulemu kwambiri m’nyumba zamapemphero, ndiponso malo olemekezeka pa maphwando. Koma amawadyera chuma chao azimai amasiye, nkumapemphera mapemphero ataliatali monyengezera. Anthu amenewa adzalangidwa koposa.” Tsiku lina Yesu adaakhala pansi nkuyang’anana ndi bokosi loponyamo ndalama zopereka ku Nyumba ya Mulungu. Ankayang’anitsitsa m’mene anthu ankaponyera ndalama zao. Anthu ambiri achuma ankaponyamo ndalama zambiri. Koma padafika mai wina wamasiye, wosauka. Iyeyu adangoponyamo tindalama tiwiri. Tsono Yesu adaitana ophunzira ake nawauza kuti, “ndithu ndikunenetsa kuti mai wamasiye wosaukayu waponyamo koposa anthu ena onsewa, amene akuponya ndalama m’bokosimu. Chifukwa ena onsewa angoponyamo zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma maiyu, mwa umphawi wake, waponyamo zonse zimene anali nazo, ngakhale zimene akadagulira chakudya.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, pakuti Mulungu ngwachifundo, ifenso tiziwonetsa mtima womwewo pakupempherera anthu onse:
1. Tipempherere atsogoleri a Eklezia kuti asenze udindo wao molimbika, azitumikira akhristu anzawo modzichepetsa ndi mosaopa zowawa.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Tipempherere akhristu onse kuti aonetse mtima wachifundo posamala Mpingo wa Mulungu ndi pothandiza anzawo mzosowa zawo.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Tipempherere madotolo, anesi ndi anamwino, kuti onse agwire ntchito yao modzipereka ndi mwachikondi.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Tidzipereke ife tomwe tili muno, kuti tikhale achangu pa ntchito zothandiza Mpingo wa Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Mulungu Atate athu, mutikomere mtima pomvera mapemphero athuwa. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment