LAMULUNGU LA 33 PA CHAKA – B.
“Potha Dziko Lino Kudzaoneka Zotani?”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI DANIELE: DANIELE 12: 01 – 03. (Pa nthawiyo anthu ako adzapulumuka).
Mulungu adalankhulitsa mneneri Daniele kuti, “pa nthawi imeneyo Mikaele, mngelo wamkulu amene amalonda anthu akwanu, adzafika. Nthawi imeneyo idzakhala ya mavuto oopsa amene sadaonekepo nkale lonse, chilengere cha mtundu woyamba wa anthu mpaka nthawi imeneyo. Pa nthawiyo anthu ako adzapulumuka, onse amene maina ao adalembedwa m’buku. Ambiri mwa amene agona m’nthaka yafumbi adzauka. Ena adzapita ku moyo wosatha ena ku manyazi ndi ku chilango chosatha. Ndipo amene adatsogolera anthu kuti ambiri m’njira ya chilungamo adzawala ngati Nyenyezi mpaka muyaya.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 16: 05, 08 – 11.
Mundisunge Inu Mulungu, pakuti ndikuthawira kwa inu.
Chauta ndiye chuma changa ndi cholowa changa,
Tsogolo langa lili m’manja mwanu,
Nthawi zonse ndimalingalira za Chauta,
Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja,
Palibe amene angandiopse konse.
Mundisunge Inu Mulungu, pakuti ndikuthawira kwa inu.
Nchifukwa chake mtima wanga ukukondwa,
Ndipo m’katikati mwangamu ndikusangalala,
Thupi langanso lidzakhala pabwino,
Chifukwa simudzandisiya ku malo a anthu akufa,
Simudzalola kuti wokondedwa wanune ndikaole kumeneko.
Mundisunge Inu Mulungu, pakuti ndikuthawira kwa inu.
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo,
Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu,
Ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Mundisunge Inu Mulungu, pakuti ndikuthawira kwa inu.
-------------------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA AHEBRI: AHEBRI 10: 11 – 14, 18. (Mwa nsembe imodzi yomweyo wasandutsa angwiro kwamuyaya onse amene Iye akuwayeretsa).
Abale, wansembe aliyense amaimirira tsiku ndi tsiku nkumatumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza. Komabe nsembe zimenezi sizingathe konse kuchotsa machimo. Koma Khristu adapereka nsembe imodzi yokha yochotsera machimo onse. Ndipo ataipereka, adakhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu amsandutse adani ake kukhala ngati chopondapo mapazi ake. Mwa nsembe imodzi yomweyo wasandutsa angwiro kwamuyaya onse amene Iye akuwayeretsa.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 21: 36.
Alleluia, Alleluia – Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthawi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 13: 24 – 32. (Iye adzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera ku mbali zonse).
Yesu adawauza ophunzira ake kuti, “masiku amenewo, mavutowo atatha, dzuwa lidzada, mwezi uzaleka kuwala. Nyenyezi zidzagwa kuchokera kuthambo, ndipo mphamvu zamumlengalenga zidzagwedezeka. Pamenepo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo, ali ndi mphamvu zazikulu ndi ulemerero. Tsono Iye adzatuma angelo ake kuti akasonkhanitse osankhidwa ake kuchokera ku mbali zonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso. Phunziraniko kwa mkuyu. Mukamaona kuti nthambi zake zayamba kukhala zanthete ndipo masamba akuphuka, mumadziwa kuti chilimwe chayandikira. Momwemonso mukadzaona zija ndanenazi zikuchitika, mudzadziwe kuti Mwana wa Munthu ali pafupi, ali pakhomo penipeni. Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unowo asanamwalire onse. Thambo ndi dziko lapansi zidzatha, koma mau anga sadzatha mphamvu konse. Koma za tsiku lake kapena nthawi yake, palibe amene amadziwa. Angelo omwe akumwamba sadziwa. Ngakhale Ineyo Mwanane sindidziwa, amadziwa ndi Atate okha basi.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, tamva lero kuti Yesu adzabweranso ndi ulemerero. Tiyeni tipemphe Mulungu Atate athu kuti alimbitse chikhulupiriro m’mitima ya anthu onse:
1. Tipempherere akhristu onse kuti aonetse anzao mtima wachifundo ndipo mayendedwe ao atsimikize kuti moyo wosatha ulipodi Kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Anthu amene maso ao anaima pa zinthu za pansi pano, maso ao atsekuke, azindikire kuti kwao kwenikweni ndi Kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu odwala ndi ena onse amene ali m’mavuto, akhale ndi chikhulupiriro cholimba, poyembekezera tsiku lodzabwera Ambuye.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tomwe, kuti tilimbikire kuchita ntchito zabwino, pozindikira kuti Ufumu wa Mulungu ulikukhazikikadi m’mitima ya athu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Mulungu Atate athu, mutiwunikire ndi kuwala kwa Mzimu wanu Woyera kuti tikukondweretseni pa zonse, polakalaka kudza kwa Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment