Saturday, October 5, 2024

LAMULUNGU LA 27 PA CHAKA – B

LAMULUNGU LA 27 PA CHAKA – B.

“Za Ulemerero wa Moyo wa Banja.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS: GENESIS 02: 18 – 24.(Adzakhala thupi limodzi).

 

Chauta adati, “sibwino kuti munthuyo akhale yekha. Ndipanga mnzake woti azimthandiza.” Chauta adatenga dothi naumba nyama zonse ndi mbalame zonse, nabwera nazo kwa Adamu kuti azitche maina. Mwakuti maina amene Adamu adazitcha, maina ake ndi omwewo. Adamu adazitcha maina nyama zonse, mbalame ndi zamoyo zonse zakuthengo. Komabe panalibe mnzake woti azimthandiza. Tsono Chauta adagonetsa Adamu tulo tofanato, ndipo ali m’tulo choncho, Mulungu adamchotsako nthiti, natsekapo ndi mnofu pamalopo. Chauta Mulungu adapanga mkazi ndi nthiti imene adaichotsa kwa Adamu uja, ndipo mkaziyo Mulungu adabwera naye kwa iye. Adamu adati, “uyutu ndiye ndi fupa lochokera ku mafupa anga, mnofu wochokera ku mnofu wanga. Adzatchedwa Mkazi, chifukwa watengedwa kwa Mwamuna.” Nchifukwa chake mwamuna amasiya atate ndi amai, ndipo amaphatikana ndi mkazi wake, choncho

awiriwo amakhala thupi limodzi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 128.

 

Chauta atidalitse ife masiku onse a moyo wathu.

 

Ngwodala aliyense woopa Chauta,

Amene amayenda m’njira zake,

Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito,

Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.

 

Chauta atidalitse ife masiku onse a moyo wathu.

 

Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka,

M’kati mwa nyumba yako.

Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi,

Kuzungulira tebulo lako.

 

Chauta atidalitse ife masiku onse a moyo wathu.

 

Zoonadi, ndimo m’mene adzakhalire wodala munthu woopa Chauta,

Chauta amene amakhala ku Ziyoni akudalitse,

Uwone m’mene Yerusalemu zinthu zidzamuyendera bwino masiku onse a moyo wako,

Ukhale ndi moyo wautali kuti uwone zidzukulu zako,

Mtendere ukhale ndi Israele.

 

Chauta atidalitse ife masiku onse a moyo wathu.

-------------------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA AHEBRI: AHEBRI 02: 09 – 11. (Amene amayeretsa anthuyo, ndiponso anthu amene amayeretsedwawo, onse Tate wao ndi mmodzi).

 

Abale, tikuwona kuti Yesu, amene pa kanthawi pang’ono adaasanduka wochepera kwa angelo, adalandira mphotho ya ulemerero ndi ulemu chifukwa adamva zowawa za imfa. Zidatero chifukwa mwa kukoma mtima kwake Mulungu adaafuna kuti afere anthu onse. Paja Mulungu amene ndi mlengi wa zonse ndipo zonse zimalinga kwa Iye, adafuna kufikitsa ana ake ambiri ku ulemerero. Tsono kudaamuyenera kuti mwa njira ya zowawa, amsandutse Yesu mtsogoleri wangwiro wowatsogolera ku chipulumutso. Amene amayeretsa anthuyo, ndiponso anthu amene amayeretsedwawo, onse Tate wao ndi mmodzi. Nchifukwa chake Yesu sachita manyazi kuwatchula abale ake.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – 01 YOHANE 04: 12.

Alleluia, Alleluia – Tikamakondana, Mulungu amakhala mwa ife, ndipo chikondi chake chafika pake penipeni mwa ife. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 10: 02 – 16. (Chimene Mulungu wachimanga, munthu sangachisamale).

 

Pa kanthawi yomweyo, kudafika Afarisi ena, namafunsa Yesu kuti, “kodi nkololedwa kuti munthu asudzule mkazi wake?” Pomufunsa choncho ankangofuna pomupezera chifukwa. Koma Yesu poyankha adati, “kodi Mose adakulamulani zotani?” Iwo adati, “Mose Adalola kuti munthu azilembera mkazi wake kalata yachisudzulo kenaka nkumuchotsa.” Yesu adati, “Mose adaakulemberani lamulo limeneli chifukwa cha kukanika kwanuku. Komatu pachiyambi paja, pamene Mulungu adalenga zonse, adawalenga anthu, wina wamwamuna wina wamkazi. Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ndi amai, nakaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzasanduka thupi limodzi. Choncho tsopano salinso awiri, koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumikiza pamodzi, munthu asazilekanitse.” Pamene adalowanso m’nyumba, ophunzira adamufunsanso Yesu za nkhani yomweyi. Iye adawauza kuti, “aliyense amene asudzule mkazi wake nakwatira wina, akuchita chigololo, ndipo akumchimwira mkazi wakeyo. Chimodzimodzinso ngati mkazi asudzula mwamuna wake, kenaka nkukwatiwa ndi wina, nayenso akuchita chigololo.” Anthu ena ankabwera ndi ana kwa Yesu kuti awakhudze ndi kuwadalitsa, ophunzira ake nkumawazazira. Yesu ataona zimenezi, adakalipa nawauza kuti, “alekeni anawa azibwera kwa Ine, musawaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere. Ndithu ndikunenetsa kuti yemwe salandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, ameneyo sadzalowamo.” Atatero adayamba kuwafungata anawo, nawasanjika manja ndi kuwadalitsa.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Yesu sachita manyazi kutitcha abale ake. Tiyeni tsono, pamodzi naye, tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti atsire madalitso ao pa anthu onse:

 

1.     Tipempherere Eklezia, Mpingo wa Mulungu, kuti apitirize ntchito yake yochirikiza ndi yokometsa mabanja onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere akulu onse olamulira maiko, kuti ateteze ma-banja a anthu, ndipo awathandize kutukula miyoyo yao.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere mabanja onse, kuti eni ake adziwe kukhulupirirana ndi kupirirana pa moyo wao wonse, monga Mulungu afunira.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Tidzipempherere ife tomwe tili muno kuti tithandizane podzetsa mtendere ndi kuyanjana pakati pa anthu onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

Atate, tikukupemphani zonsezi ndi mtima wokhulupirira Inu, pakuti mudatipatsa Mwana wanu kuti atitsogolere ku ulemerero wosatha. Ma Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...