LAMULUNGU LA 28 PA CHAKA – B.
“Tizifunafuna chuma chenicheni chokhutitsa mtima wa munthu.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA LUNTHA: LUNTHA 07: 07 – 11. (Chuma ndidachiyesa chachabe nditachilinganiza ndi luntha).
Tsono ine ndidapemphera, ndipo adandipatsa nzeru. Ndidapemphera kwa Mulungu, ndipo mzimu wa luntha udalowa mwa ine. Ndinkakonda luntha kupambana ndodo yaufumu ndi mipando yachifumu, chuma ndidachiyesa chachabe nditachilinganiza ndi luntha. Sindidalilinganize ndi miyala yamtengowapatali, chifukwa golide yense wa pansi pano ndi kamchenga chabe pafupi ndi luntha, ndipo siliva ali ngati fumbi poyerekeza ndi luntha. Ndinkakonda luntha kupambana moyo ndi kukongola. Ndinkakonda kukhala nalo kupambana kukhala ndi kuwala kwa dzuwa, chifukwa kuwala kwa lunthalo nkosalekeza. Zabwino zonse zidandidzera pamodzi ndi luntha.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 90: 12 – 17.
Tidzazeni ndi chikondi chanu kuti tisangalale.
Tsono tiphunzitseni kuwerenga masiku athu,
Kuti tikhale ndi mtima wanzeru,
Lezani mtima, Inu Chauta. Nanga mudzatikwiyira mpaka liti?
Achitireni chifundo atumiki anu.
Tidzazeni ndi chikondi chanu kuti tisangalale.
Tidzazeni m’mawa mulimonse ndi chikondi chanu chosasinthika,
Kuti tizikondwa ndi kusangalala masiku athu onse.
Tisangalatseni masiku amene mudatisautsira,
Zaka zambiri monga zaka zimene tidaona mavuto.
Tidzazeni ndi chikondi chanu kuti tisangalale.
Mulole kuti ntchito zanu ziwoneke kwa atumiki anu,
Mphamvu zanu zaulemerero ziwoneke kwa ana ao,
Inu Ambuye, Mulungu wathu, mutikomere mtima,
Ndithu mudalitse ntchito zonse za manja athu.
Tidzazeni ndi chikondi chanu kuti tisangalale.
-------------------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA AHEBRI: AHEBRI 04:12 – 13. (Mau a Mulungu amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m’mitima mwao).
Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lokuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m’mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m’mitima mwao. Pamaso pa Mulungu palibe kanthu kobisika, zonse zili poyera ndipo nzovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 05: 03.
Alleluia, Alleluia – Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 10: 17 – 30. (Kagulitse zonse zimene uli nazo. Kenaka ubwere, uzidzanditsata).
Pamene Yesu ankanyamuka kuti azipita, munthu wina adamuthamangira. Adadzamugwadira namafunsa kuti, “Aphunzitsi abwino, kodi ndizichita chiyani kuti ndikalandire moyo wosatha?” Yesu adamuyankha kuti, “unditchuliranji wabwino? Wabwinotu ndi mmodzi yekha, Mulungu basi. Malamulo ukuwadziwa: Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama, usadyerere mnzako, lemekeza atate ako ndi amai ako.” Munthu uja adati, “Aphunzitsi, zonsezi ndakhala ndikuzitsa kuyambira ndili mwana.” Yesu atamuyang’ana, adamkonda nkumuuza kuti, “ukusowabe chinthu chimodzi: pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.” Atamva zimenezo, munthu uja nkhope yake idagwa, adangochokapo ali wovutika mu mtima, chifukwa adaali munthu wa chuma chambiri. Yesu adayang’ana ophunzira ake amene adaamzungulira nawauza kuti, “nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akalowe mu Ufumu wa Mulungu.” Ophunzirawo adadabwa nawo kwambiri mau akewa. Koma Yesu adabwerezanso, adati, “ndithu, inu ana anga, nkwapatali kukalowa mu Ufumu wa Mulungu. Nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka Zingano, kupambana kuti munthu wachuma akalowe mu Ufumu wa Mulungu.” Pamenepo ophunzira aja adazizwa koposa, nayamba kufunsana kuti, “tsono nanga angathe kupulumuka ndani?” Yesu adawayang’ana nati, “kwa anthu nkosathekadi, koma ndi Mulungu ai, nkotheka. Paja ndi Mulungu zonse nzotheka.” Pamenepo Petro adayamba kulankhula naye, adati, “ifetu paja tidasiya zonse kuti tizikutsatani.” Yesu adati, “ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wosiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine, ndiponso chifukwa cha Uthenga Wabwino, ameneyo pansi pompano adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri kuposa kale: nyumba, abale, alongo, amai, ana, minda, komanso mazunzo. Ndipo kutsogoloko adzalandira moyo wosatha.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, wabwino ndi m’modzi yekha, ndiye Mulungu. Tiyeni tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti atsire madalitso ao pa anthu onse:
1. Atate, muthandize ansembe kupewa khumbo la chuma, aziwonetsa akhristu ao kuti chikondi chanu chikupambanadi zabwino zonse za m’dziko lapansi.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Atate, mufewetse mitima ya anthu opata kuti asanyadire chuma chawo, koma adziwe kuthandiza anzawo osauka.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Atate, mulimbitse mitima ya anthu ovutika, kuti azindikire kukoma mtima kwanu, polandira chithandizo kwa anzawo achifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Atate, mau anu asaleke kugwira ntchito m’mitima mwathu, kuti tithandize m’chikondi chanu ndi kumatumikira anzathu mosadziwerengera.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, popereka kwa Inu mapemphero athuwa tilikukuyamikani kukoma mtima kwanu, pakuti Inu nokha ndinu wabwino, ndipo chikondi chanu nchosasinthika. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment