LAMULUNGU LA 29 PA CHAKA – B.
“Mwana wa Munthu adabwera kuti adzatumikire anthu, ndipo kudzapereka moyo wake chifukwa cha onse.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 53: 10 – 11. (Iye adapereka moyo wake ukhale nsembe yokhululukira machimo.)
Komabe ndi Chauta yemwe amene adaafuna kuti amuzunze, ndipo adamsautsadi. Iye adapereka moyo wake kuti ukhale nsembe yokhululukira machimo. Choncho adzaona zidzukulu zake, adzakhala ndi moyo wautali, ndipo chifuniro cha Chauta chidzachitika mwa iye. Atatha mazunzo akewo, adzaona phindu lake, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzasenza machimo a anthu onse kuti iwo ambiri a iwo asadzapezekenso kuti ndiopalamula.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 33: 04 – 05, 18 – 20, 22.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Mau a Chauta ndi olungama,
Zochita zake zonse amazichita mokhulupirika,
Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera,
Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Chauta amayang’ana anthu omumvera,
Ndi odalira chikondi chake chosasinthika,
Iye amachita izi kuti awapulumutse ku imfa,
Ndi kuwasungira moyo anthuwo pa nthawi ya njala.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Mitima yathu ikuyembekeza Chauta,
Chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu,
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika,
Chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
-------------------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA AHEBRI: AHEBRI 04: 14 – 16. (Tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima.)
Tiyeni tsono, tigwiritse chikhulupiriro chimene timavomereza. Pakuti tili naye Mkulu wa ansembe wopambana, amene adapita mpaka kukafika kumwamba kwenikweni kwa Mulungu. Iyeyu ndi Yesu, Mwana wa Mulungu. Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse. Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthawi yake yeniyeni.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MARKO 10: 45.
Alleluia, Alleluia – Mwana wa Munthu adabwera kuti Iyeyo adzatumikire ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 10: 35 – 45. (Mwana wa Munthu adabwera kuti apereke moyo wake kuti aombole anthu ochuluka).
Yakobo ndi Yohane, ana aja a Zebedeo, adadzauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ife timati bwanji titakupemphani kanthu, mutichitire.” Yesu adaŵafunsa kuti, “Inuyo mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani?” Iwo adati, “Timafuna kuti pamene mudzakhale mu ulemerero wanu, mudzatiike wina ku dzanja lanu lamanja, wina ku dzanja lanu lamanzere.” Koma Yesu adati, “Simukudziŵa zimene mukupempha. Kodi inu mungathe kumwa nao chikho chamasautso chimene ndikudzamwera Ine? Kodi inu mungathe kulandira nao ubatizo wa mavuto umene ndikudzalandira Ine?” Iwo aja adayankha kuti, “Inde, tingathe.” Apo Yesu adati, “Chabwino, chikho chimene Ine ndikudzamwacho, inunso mudzamwa nao, ndipo ubatizo umene Ine ndikudzalandirawo, inunso mudzalandira nao. Koma Ineyo si udindo wanga kusankha munthu kuti akhale ku dzanja langa lamanja, kapena ku dzanja langa lamanzere. Mulungu ndiye adzapereke malo ameneŵa kwa omwe Iye mwini adaŵakonzera.” Pamene khumi ena aja adamva zimenezi, adapsera mtima Yakoboyo ndi Yohaneyo. Koma Yesu adaŵaitana ophunzira akewo, naŵauza kuti, “Mukudziŵa kuti pakati pa anthu akunja, anthu amene amati ngolamulira, amadyera anthu ao masuku pa mutu. Akuluakulu aonso amaonetsadi mphamvu zao pa anthu ao. Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, azikhala mtumiki wanu. Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, azikhala kapolo wa onse. Chitani monga m’mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, pamodzi ndi mapemphero athuwa tipereke kwa Mulungu zowawa ndi zovuta zamitundumitundu zimene anthu amapeza m’dziko lino lapansi:
1. Atsogoleri a Mpingo atumikire akhristu ao modzichepetsa ndi mosadziwerengera, ndipo asaope kumva zowawa ndi kutaya moyo wao womwe chifukwa cha iwo.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akhristu amene akuzunzidwa chifukwa chokhulupirira Mulungu, aonetse kulimba mtima, podziwa kuti mphotho yao idzakhala yaikulu Kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu odwala ndi ena onse amene akuvutika m'mitima mwao apeze mphamvu zopirira mavuto, polingalira za kuzunzidwa kwa Yesu Khristu Mpulumutsi.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tomwe tiyesetse kuiwala zowawa ndi zovuta zathu poganizira kusauka kwa anzathu, ndipo tiwathandize m’zowawa zao potsata chitsanzo chimene Ambuye adatisiyira.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, tikupereka kwa Inu mapemphero athu amenewa, podziwa kuti mudzatimvera chifundo ndi kutithandiza pa nthawi yake. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment