Saturday, July 27, 2024

LAMULUNGU LA 17 PA CHAKA – B.

LAMULUNGU LA 17 PA CHAKA – B.

“Mulungu ndiye amene amachotsa Njala imene ili mu Mtima Mwathu.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LACHIWIRI LA MAFUMU: 02 MAFUMU 04: 42 – 44. (Anthuwo adzadya ndipo chakudyachi chidzatsalako).

 

Tsiku lina munthu wina wochokera ku Baala-Salira adabwera kwa Elisa atamtengerako buledi wopangidwa ndi zokolola zatsopano, mitanda makumi awiri ya buledi wa barele ndiponso ngala zitirigu zatsopano. Zonsezi adazitengera m’thumba mwake. Tsono Elisa adati, “Agawire anthu chakudyachi kuti adye.” Koma wantchito wake adamufunsa kuti, “kodi chakudya chimenechi ndingachigawe motani kwa anthu 100 onsewa?” Elisayo adanenanso kuti, ‘apatseni anthuwo, pakuti Chauta akunena kuti, ‘Anthuwo adzadya ndipo chakudyacho chidzatsalako.”’ Motero wantchitoyo adagawira anthuwo chakudyacho, naadya, ndipo adasiyako, monga momwe Chauta adaanenera.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 145: 10 – 11, 15 – 18.

 

Mumafumbatula dzanja lanu, Inu Ambuye, ndipo mumatipatsa zofuna zathu.

 

Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta,

Anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani,

Adzalankhula za ulemerero wa ufumu wanu,

Adzasimba za mphamvu zanu.

 

Mumafumbatula dzanja lanu, Inu Ambuye, ndipo mumatipatsa zofuna zathu.

 

Maso onse amayang’anira kwa Inu,

Ndipo mumawapatsa chakudya pa nthawi yake,

Mumafumbatula dzanja lanu,

Ndipo mumapatsa chamoyo chilichonse zofuna zake.

 

Mumafumbatula dzanja lanu, Inu Ambuye, ndipo mumatipatsa zofuna zathu.

 

Chauta ndi wolungama m’zochita zake zonse,

Ndi wachifundo pa zonse zimene achita,

Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba,

Ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba,

 

Mumafumbatula dzanja lanu, Inu Ambuye, ndipo mumatipatsa zofuna zathu.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO: AEFESO 04: 01 – 06. (Pali thupi limodzi, Mbuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi).

 

Abale, ine, womangidwa m’ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako. Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthawi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi, ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu woyera pa kulunzana mu mtendere. Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu woyera m’modzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene Mulungu adakuitanirani. Pali Mbuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi. Pali mulungu mmodzi amene ali Atate a anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse, amagwira ntchito kudzera mwa onse, amagwira ntchito kudzera mwa onse, ndipo ali mwa onse.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Luka 07: 16.

Alleluia, Alleluia – Mneneri wamkulu waoneka pakati pathu, Mulungu wadzathandiza anthu ake. – – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 06: 01 – 15. (Yesu adatenga buledi uja, adawagawira monga momwe anthuwo ankafunira).

 

Pa nthawi yomweyo, Yesu adaoloka nyanja ya Galileya – dzina lake lina ndi nyanja ya Tiberiasi. Khamu lalikulu la anthu lidamtsatira, chifukwa lidaaona zizindikiro zozizwitsa zimene adaachita pakuchiritsa anthu odwala. Yesu adakwera m’phiri nakhala pansi ndi ophunzira ake. Chikondwerero chija chachipembedzo chotchedwa Pasaka chidaayandikira. Pamene Yesu adayang’ana, adafunsa Filipo kuti, “Kodi tingakagule kuti chakudya chodyetsa anthu onsewa?’ (Adafunsa zimenezo dala kuti amuyese Filipoyo, koma mwiniwakeyo adaadziwiratu choti achite.) Filipo adayankha kuti, “ngakhale ndalama mazana awiri sizingakwanire konse kugula chakudya choti aliyense mwa anthuwa adyeko ngakhale pang’ono.” Wophunzira wake wina, dzina lake Andrea, mbale wake wa Simoni Petro, adauza Yesu kuti, “Pali mnyamata pano, ali ndi buledi msanu wabarele, ndi tinsomba tiwiri. Koma zimene zingachitenji kwa anthu onsewa?”  Yesu adati, “auzeni anthu akhale pansi.” (Pamenepo panali msipu wambiri.) Anthuwo adakhaladi pansi. Amuna okha analipo ngati zikwi zisanu. Tsono Yesu adatenga buledi uja, ndipo atayamika Mulungu, adagawira anthu amene adaakhala pansiwo. Adateronso ndi tinsomba tija, nawagawira monga momwe anthuwo ankafunira, anthu onsewo atakhuta, Yesu adauza ophunzira ake kuti, “tolani zotsala kuti pasatayikepo kanthu.” Adatoladi zotsala zonse za buledi msanu uja, nadzaza madengu khumi ndi awiri. Pamene anthu aja adaona chizindikiro chozizwitsa chimene Yesu adachitacho, adati, “Zoonadi ameneyu ndi Mneneri uja amene ankanena kuti adzabwera pansi panoyu.” Yesu adaadziwa kuti anthuwo ankati adzamgwire ndi kumlonga ufumu. Motero adawachokera nakakweranso m’phiri payekha.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, tiyeni tipereke mapemphero athu kwa Chauta Atate athu, chifukwa Iye ngwachifundo, amafuna kuti anthu onse akhale ndi moyo:

 

1.     Atate, muthandize akhristu onse kuti aonetse anzao kukoma mtima kwanu, pakuwatumikira ndi kuwachitira zabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate, anthu ambiri sadziwa kuti ndinu kasupe wa moyo weniweni; muwaunikire kuti akutsekuleni mitima yao.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate, anthu ena amasunga chidani m’mitima mwao, posaona mtendere. Muwaongolere ndi Mzimu wanu Woyera, kuti ayanjane ndi kulandira moyo wanu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate, muitane anyamata ndi atsikana ambiri ku ntchito zotumikira Mpingo wanu: aphunzire kuphathana ndi Yesu Khristu, mpaka alowe unsembe, kapena ubrazala, kapena usisiteri.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Chauta Atate athu, mutithandize kugwirizana ndi Mwana wanu pa ntchito zotumikira anzathu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, July 20, 2024

LAMULUNGU LA 16 PA CHAKA – B.

LAMULUNGU LA 16 PA CHAKA – B.

“Yesu Yekha Ndi Mtsogoleri Woona Wokhulupirika.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YEREMIYA: YEREMIYA 23: 01 – 06. (Ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, ndidzazipatsa abusa oziweta bwino).

 

“Tsoka kwa abusa amene amaononga ndi kumwaza nkhosa za pabusa panga,” akutero Chauta. Nchifukwa chake Chauta, Mulungu wa Israele, ponena za abusa oyang’anira anthu ake, akuti, “mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga, simudazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu. Pambuyo pake Mwiniwakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kudzichotsa ku malo onse amene ndidazimwazira. Ndidzazibwezera ku ubusa lakwao, ndipo zidzaswana ndi kuchuluka. Ndidzazipatsa abusa oziweta bwino. Sizidzaopanso kapena kuchita mantha, kapena kusokera,” akutero Chauta. Chauta akunena kuti, “akubwera masiku pamene ndidzaphukitsira Davide nthambi yoongoka imene idzakhala mfumu yanzeru ndi yoweruza m’dzikomo mwachilungamo ndi mosakondera. Pa masiku akewo Yuda adzapulumuka, ndipo Israele adzakhala pabwino. Adzamutcha dzina lake lakuti, ‘Chauta ndiye chilungamo chathu.”’

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 23.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu,

Amandigoneka pa busa lamsipu,

Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako,

Amatsitsimutsa moyo wanga.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

 

Amanditsogolera m’njira za chilungamo,

Malinga ndi ulemerero wa dzina lake,

Ngakhale ndiyende m’chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse,

Pakuti Inu Ambuye mumakhala nane, chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

 

Inu mumandikonzera chakudya, adani anga akuwona,

Mumandilandira bwino podzoza mutu wanga,

Mumadzaza chikho changa mpaka kusefukira.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

 

Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu,

Zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga,

Ndidzakhala m’Nyumba mwanu moyo wanga onse.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO: AEFESO 02: 13 – 18. (Khristu mwini wake ndiye Mtendere wathu. Iye adasasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi).

 

Abale, tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu. Khristu ndiye mwini wake wa mtendere wathu. Iye adasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi. Pakupereka thupi lake, adagamula khoma la chidani limene linkatilekanitsa. Iye adathetsa Malamulo a Mose pamodzi ndi malangizo ake ndi miyambo yake. Adachita zimenezi kuti kuchokera ku mitundu iwiri ija, alenge mtundu umodzi watsopano, wokhala mwa Iye, kuti choncho adzetse mtendere. Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m’thupi limodzi mitundu iwiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu. Khristu adadzalalika Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu a mitundu inanu, amene munali kutali ndi Mulungu, ndiponso kwa Ayuda, amene anali pafupi naye. Tsopano kudzera mwa Khristu ife tonse, Ayuda ndi a mitundu ina, tingathe kufika kwa Atate mwa Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 10: 27.

Alleluia, Alleluia – Nkhosa zanga zimamva mau anga, atero Ambuye. Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsatira. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 06: 30 – 34. (Anali ngati nkhosa zopanda mbusa woziyang’anira).

 

Atumwi aja adabwerera kwa Yesu namufotokozera zonse zimene adaachita ndi kuphunzitsa. Yesu adawauza kuti, “tiyeni tipite kwatokha kumalo kosapitapita anthu, kuti mukapumule pang’ono.” Adaatero chifukwa anthu anali piringupiringu, Mwakuti iwo sankatha kupeza ndi mpata wodyera womwe. Tsono adalowa m’chombo napita kwaokha kumalo kosapita anthu. Komabe anthu ambiri adawaona akupita, nawazindikira. Motero adathamanga pa mtunda kuchokera ku mizinda yonse, nakafika kumaloko, Yesu ndi ophunzira ake aja asanafike. Pamene Yesu adatuluka m’chombomo, adaona chikhamu chachikulu cha anthu. Adawamvera chifundo anthuwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa, choncho adayamba kuwaphunzitsa zambiri.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, tiyeni tipereke mapemphero athu kwa Mulungu, Mbusa wathu wamkulu; tiyamike chifundo chake chotisamalira:

 

1.     Atate, muthandize akulu a Mpingo kuti atsate chitsanzo cha Ambuye Yesu, Mbusa wabwino, posamala akhristu ao.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate, thandizani atsogoleri athu kuti ayendetse bwino dziko lathu, potsata chitsanzo cha Yesu Khristu, Mbusa wawo.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate, muthandize akatekumeni ndi akunja onse, kuti avomere kutsata Yesu Khristu, Mbusa wolondola nkhosa zotayika.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate, muthandize akhristu onse akugwa, kuti abwerere kwa Mbusa wao, Yesu Khristu, amene akufuna kuti pakhale khola limodzi lokha.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, tikukupemphani modzichepetsa, mumvere mapemphero athuwa kuti nkhosa zanu zonse zikhale pamodzi. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, July 13, 2024

LAMULUNGU LA 15 PA CHAKA – B.

LAMULUNGU LA 15 PA CHAKA – B.

“Yesu Khristu Akutituma Kukalalika Mthenga Wabwino.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI AMOSI: AMOSI 07: 12 – 15. (Pita, ukalalikire anthu anga, Aisraele).

 

Amaziya adauza Amosi kuti, “Mlosi iwe, choka kuno! Thawira ku dziko la Yuda! Uzikalosa kumeneko, ndipo anthu akumeneko azikakudyetsa. Koma usakalosenso ku Betele poti kumeneko ndi malo opatulika a mfumu, ndiponso ndi Nyumba ya Mulungu ya dziko lino.” Amosi adayankha Amaziya kuti, “Ine sindine mneneri konse, kapenanso wa m’gulu la aneneri. Inetu ndine woweta nkhosa, ndiponso wolima nkhuyu. Chauta adachita kukanditenga, kundileketsa ntchito yoweta nkhosa, nandiwuza kuti, pita, ukalalikire anthu anga, Aisraele.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 85: 09 – 14.

 

Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse.

 

Ndimve zimene Chauta adzalankhula,

Chifukwa adzalankhula za Mtendere kwa anthu ake,

Zoonadi, Mulungu ali wokonzeka kuti apulumutse amene amamuwopa,

Kuti ulemerero wake ukhale m’dziko lathu.

 

Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse.

 

Chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika zidzakumana,

Chilungamo ndi Mtendere zidzagwirizana,

Anthu ake adzakhala okhulupirika pansi pano,

Ndipo Mulungu wakumwamba adzawalungamitsa.

 

Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse.

 

Inde, Chauta adzapereka zabwino,

Ndipo dziko lathu lidzabereka zokolola zambiri,

Mulungu ndi wolungama chikhalire,

Chilungamo chake chimaongolera zochita zake zonse.

 

Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO: AEFESO 01: 03 – 14. (Mulungu asanalenge dziko lapansi, adatisankhiratu mwa Khristu).

 

Abale, tiyamike Mulungu, Atate Ambuye athu Yesu Khristu. Mwa Khristu Iye adatipatsa madalitso onse auzimu Kumwamba. Mulungu asanalenge dziko lapansi, adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi opanda cholakwa pamaso pake. Chifukwa chotikonda, adakonzeratu kuti mwa Yesu Khristu atilandire ngati ana ake. Adachita zimenezi chifukwa adaafuna kutero mwa kukoma mtima kwake. Adaafuna kuti tizitamanda ulemu wake chifukwa adatikomera mtima kopambana, pakutipatsa Mwana wake wokondedwa ngati mphatso yaulere. Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere zimene Mulungu adatipatsa mochuluka. Mwa luntha ndi nzeru adatiwululira chifuniro chake chimene kale chinali chobisika. Zimene adaati achite mwa kukoma mtima kwake ndi zomwe Iye mwini adaakonzeratu kale. Chimene Mulungu adalongosola kuti achite itakwana nthawi, nchakuti asonkhanitse pamodzi mwa Khristu zinthu zonse za Kumwamba ndi zapansipano. Paja Mulungu amaongolera zinthu zonse monga momwe Iye wafunira ndi m’mene watsimikizira. Iye adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale akeake. Adazikonzeratu kuti ziyenera kukhala choncho. Adafuna kuti ife, amene tinali oyamba kuyembekeza Khristu, tilemekeze ulemerero wake. Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza. Mzimu Woyerayo ndiye chikole chotsimikizira kuti tidzalandiradi madalitso onse amene Mulungu adalonjeza kupatsa anthu ake, ndipo kuti Mulungu adzapulumutsa kwathunthu anthu amene adawaombola kuti akhale ake enieni. Cholinga cha zonsezi ndi chakuti tilemekeze ulemerero wake.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AEFESO 01: 17 – 18.

Alleluia, Alleluia – Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu akuunikireni m’mitima mwanu, kuti mudziwe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 06: 07 – 13. (Yesu adaitana ophunzira ake khumi ndi awiri aja, nawatuma awiriawiri).

 

Pa nthawi yomweyo, Yesu adaitana ophunzira ake khumi ndi awiri aja, nawatuma awiriawiri. Adawapatsa mphamvu zotulutsira mizimu yoipitsa anthu. Adawalamula kuti, “musatenge kanthu kena kalikonse pa ulendo, koma ndodo yokha. Musatenge kamba, kapena thumba lapaulendo, kapena ndalama m’chikwama. Nsapato muvale inde, koma musakhale ndi mikanjo iwiri.” Adawauzanso kuti, “mukafika pa mudzi, mudzikhala nao kunyumba kumene mudafikirako, mpaka itakwana nthawi yoti muchoke kumudziko. Ngati kumudzi kwina anthu sakulandirani, nakana kumva mau anu, pochoka musanse fumbi la kumapazi kwanu. Chimenechi chidzakhala chizindikiro choti apalamula.” Ophunzira aja adapitadi, namakalalikira anthu kuti atembenuke mtima. Ankatulutsa mizimu yoipa yochuluka, ndiponso ankadzoza mafuta anthu odwala ambiri nkumawachiritsa.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Mulungu adatipatsa Mzimu Woyera, natitsimikizira kuti tidzalandira madalitso onse amene Ambuye adalonjeza. Tiyeni, tikweze mapemphero athu kwa Atate athu a Kumwamba kuti atsire madalitsowo pa anthu onse:

 

1.     Atate, mulimbitse Apapa ndi Aepiskopi onse kuti akhazikitse akhristu ao m’chikhulupiriro choona, pakuwalalikira Mthenga Wabwino mwachangu.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate, muunikire atsogoleri a maiko onse kuti atumikire anthu ao ndi kuwasamala mwachilungamo ndi mwachikondi.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate, musankhule ena mwa ana athu kuti alowe unsembe kapena m’zipani za mu Mpingo kuti azidzakutumikirani pa moyo wao wonse.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate, mutiwongolere ife tomwe tili muno, kuti mau athu ndinso ntchito zathu zotumikira anzathu, zisonyeze kukoma mtima kwanu kofuna kuwapulumutsa.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, pakuti zinthu zonse zimachitika monga momwe Inu mufunira, tikulemekeza ulememero wanu ndi kudala kokoma mtima kwanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, July 6, 2024

LAMULUNGU LA 14 PA CHAKA – B

LAMULUNGU LA 14 PA CHAKA – B.

“Anthu a Kumudzi kwao Sadamkhulupirire.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI EZEKIELE: EZEKIELE 02: 02 – 05. (Anthu ake ndi okanika; koma adzadziwa ndithu kuti mneneri wafikadi pakati pao).

 

Pamene ankalankhula, Mzimu wa Mulungu udalowa mwa ine nundiimiritsa, ndipo ndidamva Mulungu akulankhula. Adandiwuza kuti, “iwe mwana wa munthu, ndikukutuma kwa Israele, mtundu wa anthu aupandu amene andipandukira. Iwowo ndi makolo ao akhala akundichimwira mpaka lero lino. Anthu ake ndi okanika ndiponso achipongwe. Ndikukutuma kuti ukanene zimene Ine Ambuye Chauta ndikuwauza. Ndiye popeza kuti iwowo ngaupandu, kaya akamvera kaya akakana, (pakuti ndi anthu opanduka) koma adzadziwa ndithu kuti mneneri wafikadi pakati pao.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 123.

 

Timayang’anira ife kwa Chauta, mpaka atatichitira chifundo.

 

Ndikukweza maso anga kwa Inu,

Inu amene mumakhala pa mpando wachifumu kumwamba,

Monga momwe anyamata amayang’anira,

Ku dzanja la bwana wao.

 

Timayang’anira ife kwa Chauta, mpaka atatichitira chifundo.

 

Monga momwe adzakazi amayang’anira ku dzanja la dona wao,

Ndi momwemonso timayang’anira ife,

Kwa Chauta Mulungu wathu,

Mpaka atatichitira chifundo.

 

Timayang’anira ife kwa Chauta, mpaka atatichitira chifundo.

 

Mutichitire chifundo, Inu Chauta, mutichitire chifundo,

Pakuti adani athu atinyoza kopitirira malire,

Pa nthawi yaitali, anthu olemera akhala akutinyodola,

Anthu onyada akhala akutinyoza.

 

Timayang’anira ife kwa Chauta, mpaka atatichitira chifundo.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 02 AKORINTO 12: 07 – 10. (Ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine).

 

Abale, kuwopa kuti ndingamadzitukumule chifukwa cha zazikulu kwambiri zimene Ambuye adandiwululira, Mulungu adandipatsa cholasa ngati minga m’thupi. Adalola wamthenga wa Satana kuti azindimenya, kuti ndingamanyade kwambiri. Pamenepo ndidapempha Ambuye katatu kuti andichotsere chimenechi, koma Iwo adandiuza kuti, “chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine. Tsono ndimakondwera pamene ndili wofooka, pamene anthu andinyoza, namandizunza, ndiponso pamene ndimva zowawa ndi kusautsidwa chifukwa cha Khristu. Pakuti pamene ndili wofooka, mpamene ndili ndi mphamvu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 04:18.

Alleluia, Alleluia – Ambuye andidzoza kuti ndikalalikire amphawi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am’ndende kuti adzamasulidwa. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 06: 01 – 06. (Mneneri amalemekezeka kwina kulikonse, kupatula kumudzi kwao).

 

Yesu adachoka kumeneko, nakafika kumudzi kwao. Ophunzira ake adatsagana naye. Litafika tsiku la Sabata, Iye adayamba kuphunzitsa m’nyumba yamapemphero. Anthu ambiri amene ankamvetsera adadabwa kwambiri nkumanena kuti, “kodi Iyeyu zonsezi adazitenga kuti? Nzeru zimene adalandirazi nzotani? Akutha bwanji kuchita zinthu zamphamvu zotere? Kodi ameneyu si mmisiri wa matabwa uja, mwana wa Maria? Kodi abale ake si Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Kodi suja alongo ake ali nafe pompano?” Choncho adakhumudwa naye. Koma Yesu adawauza kuti, “mneneri amalemekezeka kwina kulikonse, kupatula kumudzi kwao, pakati pa achibale ake, ndiponso kubanja kwao.” Motero sadathe kuchita zinthu zamphamvu kumeneko. Adangosanjika manja pa odwala owerengeka, nkuwachiritsa. Ndipo adadabwa poona kuti anthu akumeneko sadamkhulupirire. Pambuyo pake Yesu adapita ku midzi yozungulira, namakaphunzitsa anthu.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, tamva lero m’mene Mulungu amatekesekera ndi chipulumutso cha anthu. Tiyeni, timupemphe kuti chithandizo chake chiwafikire anthu onse:

 

1.     Atate athu otikonda, mulimbikitse atsogoleri a Mpingo kuti asenze udindo wao mofatsa ndi mosakayika.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate a ufumu wonse, muwongolere akulu olamulira dziko lathu lino, kuti aliyendetse mwamtendere potsata ubwino wa anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate a chifundo, mukulitse m’mitima ya akhristu chikondi chotumikira anzao, kuti alimbikire pa ntchito zotukula moyo wa anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate a ufulu wonse, mutipatse ife amene tili muno chikhulupiriro cholimba, kuti tiphunzitse bwino ana athu za Ambuye Yesu Mpulumutsi.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, maso athu akuyang’ana kwa Inu, popeza kuti simuleka kuthandiza anthu amene akuzindikira umphawi wao. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...