LAMULUNGU LA 17 PA CHAKA – B.
“Mulungu ndiye amene amachotsa Njala imene ili mu Mtima Mwathu.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LACHIWIRI LA MAFUMU: 02 MAFUMU 04: 42 – 44. (Anthuwo adzadya ndipo chakudyachi chidzatsalako).
Tsiku lina munthu wina wochokera ku Baala-Salira adabwera kwa Elisa atamtengerako buledi wopangidwa ndi zokolola zatsopano, mitanda makumi awiri ya buledi wa barele ndiponso ngala zitirigu zatsopano. Zonsezi adazitengera m’thumba mwake. Tsono Elisa adati, “Agawire anthu chakudyachi kuti adye.” Koma wantchito wake adamufunsa kuti, “kodi chakudya chimenechi ndingachigawe motani kwa anthu 100 onsewa?” Elisayo adanenanso kuti, ‘apatseni anthuwo, pakuti Chauta akunena kuti, ‘Anthuwo adzadya ndipo chakudyacho chidzatsalako.”’ Motero wantchitoyo adagawira anthuwo chakudyacho, naadya, ndipo adasiyako, monga momwe Chauta adaanenera.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 145: 10 – 11, 15 – 18.
Mumafumbatula dzanja lanu, Inu Ambuye, ndipo mumatipatsa zofuna zathu.
Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta,
Anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani,
Adzalankhula za ulemerero wa ufumu wanu,
Adzasimba za mphamvu zanu.
Mumafumbatula dzanja lanu, Inu Ambuye, ndipo mumatipatsa zofuna zathu.
Maso onse amayang’anira kwa Inu,
Ndipo mumawapatsa chakudya pa nthawi yake,
Mumafumbatula dzanja lanu,
Ndipo mumapatsa chamoyo chilichonse zofuna zake.
Mumafumbatula dzanja lanu, Inu Ambuye, ndipo mumatipatsa zofuna zathu.
Chauta ndi wolungama m’zochita zake zonse,
Ndi wachifundo pa zonse zimene achita,
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba,
Ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba,
Mumafumbatula dzanja lanu, Inu Ambuye, ndipo mumatipatsa zofuna zathu.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO: AEFESO 04: 01 – 06. (Pali thupi limodzi, Mbuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi).
Abale, ine, womangidwa m’ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako. Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthawi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi, ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu woyera pa kulunzana mu mtendere. Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu woyera m’modzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene Mulungu adakuitanirani. Pali Mbuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi. Pali mulungu mmodzi amene ali Atate a anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse, amagwira ntchito kudzera mwa onse, amagwira ntchito kudzera mwa onse, ndipo ali mwa onse.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Luka 07: 16.
Alleluia, Alleluia – Mneneri wamkulu waoneka pakati pathu, Mulungu wadzathandiza anthu ake. – – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 06: 01 – 15. (Yesu adatenga buledi uja, adawagawira monga momwe anthuwo ankafunira).
Pa nthawi yomweyo, Yesu adaoloka nyanja ya Galileya – dzina lake lina ndi nyanja ya Tiberiasi. Khamu lalikulu la anthu lidamtsatira, chifukwa lidaaona zizindikiro zozizwitsa zimene adaachita pakuchiritsa anthu odwala. Yesu adakwera m’phiri nakhala pansi ndi ophunzira ake. Chikondwerero chija chachipembedzo chotchedwa Pasaka chidaayandikira. Pamene Yesu adayang’ana, adafunsa Filipo kuti, “Kodi tingakagule kuti chakudya chodyetsa anthu onsewa?’ (Adafunsa zimenezo dala kuti amuyese Filipoyo, koma mwiniwakeyo adaadziwiratu choti achite.) Filipo adayankha kuti, “ngakhale ndalama mazana awiri sizingakwanire konse kugula chakudya choti aliyense mwa anthuwa adyeko ngakhale pang’ono.” Wophunzira wake wina, dzina lake Andrea, mbale wake wa Simoni Petro, adauza Yesu kuti, “Pali mnyamata pano, ali ndi buledi msanu wabarele, ndi tinsomba tiwiri. Koma zimene zingachitenji kwa anthu onsewa?” Yesu adati, “auzeni anthu akhale pansi.” (Pamenepo panali msipu wambiri.) Anthuwo adakhaladi pansi. Amuna okha analipo ngati zikwi zisanu. Tsono Yesu adatenga buledi uja, ndipo atayamika Mulungu, adagawira anthu amene adaakhala pansiwo. Adateronso ndi tinsomba tija, nawagawira monga momwe anthuwo ankafunira, anthu onsewo atakhuta, Yesu adauza ophunzira ake kuti, “tolani zotsala kuti pasatayikepo kanthu.” Adatoladi zotsala zonse za buledi msanu uja, nadzaza madengu khumi ndi awiri. Pamene anthu aja adaona chizindikiro chozizwitsa chimene Yesu adachitacho, adati, “Zoonadi ameneyu ndi Mneneri uja amene ankanena kuti adzabwera pansi panoyu.” Yesu adaadziwa kuti anthuwo ankati adzamgwire ndi kumlonga ufumu. Motero adawachokera nakakweranso m’phiri payekha.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, tiyeni tipereke mapemphero athu kwa Chauta Atate athu, chifukwa Iye ngwachifundo, amafuna kuti anthu onse akhale ndi moyo:
1. Atate, muthandize akhristu onse kuti aonetse anzao kukoma mtima kwanu, pakuwatumikira ndi kuwachitira zabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Atate, anthu ambiri sadziwa kuti ndinu kasupe wa moyo weniweni; muwaunikire kuti akutsekuleni mitima yao.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Atate, anthu ena amasunga chidani m’mitima mwao, posaona mtendere. Muwaongolere ndi Mzimu wanu Woyera, kuti ayanjane ndi kulandira moyo wanu.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Atate, muitane anyamata ndi atsikana ambiri ku ntchito zotumikira Mpingo wanu: aphunzire kuphathana ndi Yesu Khristu, mpaka alowe unsembe, kapena ubrazala, kapena usisiteri.
Tikupemphani, mutivomereze.
Chauta Atate athu, mutithandize kugwirizana ndi Mwana wanu pa ntchito zotumikira anzathu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment