Saturday, August 3, 2024

LAMULUNGU LA 18 PA CHAKA – B

LAMULUNGU LA 18 PA CHAKA – B.

“Amene Adza kwa Ine, Sadzamva Njala.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA EKSODO: EKSODO 16: 02 – 04, 12 – 15. (Ndikupatsani chakudya chimene chidzagwa ngati Mvula kuchokera Kumwamba).

 

Khamu lonse lidadandaulira Mose ndi Aroni m’chipululu muja kuti, “kukadakhala bwino Chauta akadatiphera ku Ejipito konkuja, kumene tinkakhala tikudya nyama ndi buledi, ndipo tinkakhuta. Koma inu mwatifikitsa kuchipululu kuno kuti mutiphe tonse ndi njala.” Apo Chauta adauza Mose kuti, “chabwino, ndikupatsani chakudya chimene chidzagwa ngati mvula kuchokera kumwamba. Anthu azituluka tsiku ndi tsiku kukatola chakudya chokwanira tsiku limodzi, kuti ndiwayese ndipo ndiwone ngati adzayenda motsata malamulo anga kapena ai. Ndamva madandaulo a Aisraele. Ndiye uwauze kuti, madzulo mudzadya nyama, ndipo m’mawa mudzadya buledi, choncho mudzadziwa kuti Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.” Motero madzulo kudagwa zinziri, ndipo zidadzaza ponseponse pamahemapo. M’mawa ndithu padagwa mame ponse pozungulira mahemawo. Mamewo atangokamuka, panthakapo m’chipululu muja padapezeka tinthu tina topyapyala, tambeee ngati chipale, ndiponso tonyata. Aisraele ataona tinthuto sadatidziwe kuti nchiyani, mwakuti adayamba kufunsana kuti, “kodi timeneti ntiyani?” Mose adawauza kuti, “ameneyu ndi buledi yemwe Chauta wakupatsani kuti mudye.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 78: 03 – 04, 23 – 25, 54.

 

Chauta Adawapatsa buledi wochokera Kumwamba.

 

Zinthu zimene tidazimva ndi kuzidziwa,

Zomwe makolo athu adatifotokozera,

Tidzafotokozera mbadwo wakutsogolo,

Ntchito zotamanda za Chauta.

 

Chauta Adawapatsa buledi wochokera Kumwamba.

 

Iye adalamula mitambo yamumlengalenga,

Natsekula zitseko zakumwamba,

Powagwetsera mana kuti adye,

Adawapatsa tirigu wakumwamba.

 

Chauta Adawapatsa buledi wochokera Kumwamba.

 

Motero anthu adadya buledi wa angelo,

Ndipo Mulungu adawatumizira chakudya chochuluka,

Anawatengera iwo ku dziko lopatulika,

Ku Mapiri kumene dzanja lake lamanja lidagongetsa.

 

Chauta Adawapatsa buledi wochokera Kumwamba.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO: AEFESO 04: 17, 20 – 24. (Muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye).

 

Abale, m’dzina la Ambuye ndikukuuzani, ndipo ndikunenetsa, kuti musayendenso monga amachitira akunja potsata maganizo ao achabe. Koma umu si m’mene inu mudaphunzirira za Khristu ai, ngatitu mudamva za Iyeyo, ngatinso mudaphunzitsidwa za Iye, motsata choona chimene chili mwa Yesu. Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga. Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano. Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 04: 04b.

Alleluia, Alleluia – Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 06: 24 – 35. (Munthu aliyense wodza kwa Ine, sadzamva njala. Ndipo aliyense wokhulupirira Ine, sadzamva ludzu konse).

 

Khamu lija lidaaona kuti Yesu kulibe, ophunzira ake omwe kulibenso. Tsono anthu onsewo adalowa m’zombo zija, napita ku Kapernao kunka nafunafuna Yesu. Pamene anthu aja adampeza Yesu kutsidya kwa nyanja, adamfunsa kuti, “Aphunzitsi, mudafika liti kuno?” Yesu adati, “kunena zoona, inu mukundifuna osati chifukwa mudazimvetsa zizindikiro zozizwitsa zija ai, koma chifukwa mudadya chakudya chija mpaka kukhuta. Musamagwira ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimaonongeka, koma muzigwira ntchito kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chimene chili cha moyo wosatha. Mwana wa Munthu ndiye adzakupatsani chakudya chimenechi, pakuti Mulungu Atate adamuvomereza motsimikiza.” Pamenepo anthu aja adayamba kufunsana kuti, “titanitu tsono kuti titsate bwino zimene Mulungu afuna?” Yesu adawayankha kuti, “chimene Mulungu afuna kuti muchite nchakuti mundikhulupirire Ineyo amene Mulungu adandituma.” Iwo adafunsanso kuti, “mungatiwonetse chizindikiro chotani kuti tikachiwona tikukhulupirireni? Nanga muchitapo chiyani? Makolo athu ankadya mana m’chipululu muja, monga Malembo akunenera kuti, ankawapatsa chakudya chochokera Kumwamba kuti adye.” Yesu adati, “ndithu ndikunenetsa kuti amene ankakupatsani chakudya chochokera Kumwambacho, si Mose ai, Atate anga ndiwo amene amakupatsani chakudya chenicheni chochokera Kumwamba. Pakuti chakudya chimene Mulungu amapereka, ndicho chimene chimatsika kuchokera Kumwamba, ndipo chimapereka moyo kwa anthu a pa dziko lapansi.” Apo anthuwo adapempha Yesu kuti, “Ambuye, muzitipatsa chakudya chimenechi masiku onse.”  

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, tisanapereke, nsembe yathu, tikweze mapemphero athu kwa Atate athu akumwamba:

 

1.     Atate, mulimbitse ansembe onse kuti asamalire akhristu ao masiku onse, pakuwadyetsa mau ndi kuwagawira chakudya chakumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate, muwongolere atsogoleri a maiko onse kuti ayesetse kutukula moyo wa anthu ao, pakukhazikitsa chilungamo ndi mtendere.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate, muunikire anthu opata, kuti asaumire mtima anzawo osauka ndipo asaiwale kuti chuma chenicheni ndinu amene.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate, muyang’ane onse amene alikusauka ndi njala ndi matenda, kuti apeze anzawo achifundo owathandiza m'mavuto ao.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

Inu Chauta, mudasamalira Aisraele pa ulendo wao m’chipululu. Momwemonso mupatse anthu onse a m’dziko la pansi pano chakudya chao chalero. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...