Saturday, August 10, 2024

LAMULUNGU LA 19 PA CHAKA – B.

LAMULUNGU LA 19 PA CHAKA – B.

“Yesu Khristu Ndiye Chakudya Chopatsa Moyo.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LOYAMBA LA MAFUMU: 01 MAFUMU 19: 04 – 08. (Motero adapeza Mphamvu zoyendera, mpaka adakafika ku Sinai, phiri la Mulungu).

 

Eliya mwini wake adayenda ulendo wa tsiku limodzi m’chipululu, nakakhala pansi patsinde pa kamtengo ka tsache. Tsono adapempha kuti afe, adati, “zandikola! Inu Chauta, bwanji ndingofa basi! Ine sindingapambane makolo anga.” Atatero adagona tulo patsinde pa kamtengo ka tsache pomwepo. Mwadzidzidzi mngelo adamkhudza namuuza kuti, “dzuka, udye.” Eliya atapenya, adangoona kuti kumutu kwake kuli buledi wootcha pa makala, ndiponso mkhate wa madzi. Adadya, namwera, nkugonanso. Mngelo wa Chauta uja adabweranso kachiwiri, namkhudza nati, “dzuka, udye kuti ulendowu ungakukanike.” Eliya uja adadzuka, nadya nkumwera. Motero adapeza mphamvu zoyendera. Adayenda masiku makumi anai usana ndi usiku mpaka ku Sinai, phiri la Mulungu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 34: 02 – 09.

 

Yesani ndipo Mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.

 

Ndidzayamika Chauta nthawi zonse,

Pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza,

Moyo wanga umanyadira Chauta,

Anthu Ozunzika amve ndipo akondwere.

 

Yesani ndipo Mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.

 

Lalikani pamodzi nane ukulu wa Chauta,

Tiyeni limodzi tiyamike dzina lake,

Ndidapemphera kwa Chauta ndipo adandiyankha,

Adandipulumutsa kwa zonse zimene ndinkaziwopa.

 

Yesani ndipo Mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.

 

Ozunzikawo atayang’ana kwa Chauta,

Nkhope zao zidasangalala, sadachite manyazi,

Munthu wosaukayu adalira, ndipo Chauta adamumva,

Nampulumutsa m’mavuto ake onse.

 

Yesani ndipo Mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.

 

Mngelo wa Chauta amatchinjiriza anthu omvera Iye,

Ndipo amawapulumutsa,

Yesani ndipo Mudzaona kuti Chauta ndi wabwino,

Ngwodala munthu wothawira kwa Chauta.

 

Yesani ndipo Mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO: AEFESO 04: 30 – 05:02. (Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife).

 

Abale, musamvetse chisoni Mzimu Woyera amene Mulungu adakusindikizani chizindikiro chake chotsimikizira kuti ndinu ake pa tsiku limene Mulunguyo adzatipulumutsutse kwathunthu. Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse. Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso. Tsono popeza kuti ndinu ana okondedwa a Mulungu, muziyesa kumtsanzira. Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 06: 51.

Alleluia, Alleluia – Ine ndine Chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Atero Ambuye. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 06: 41 – 51. (Ine ndine chakudya chotsika kuchokera kumwamba).

 

Pamenepo Ayudawo adayamba kung’ung’udza chifukwa Yesu adaati, “Ine ndine chakudya chotsika kuchokera kumwamba.” Iwo ankanena kuti, “kodi ameneyu si Yesu, mwana wa Yosefe uja? Bambo wake ndi mai wake suja tikuwadziwa? Nanga tsono anganene bwanji kuti, ‘ndidatsika Kumwamba?’” Yesu adawayankha kuti, “musang’ung’udze inu. Palibe munthu amene angabwere kwa Ine, ngati Atate amene adandituma samkoka. Ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. Paja aneneri adalemba kuti, ‘onse adzakhala ophunzitsidwa ndi Mulungu.’ Munthu aliyense womva Atate, nkuphunzira kwa Iwo, amadza kwa Ine. Sindiye kutitu wina aliyense adaona Atate ai, koma Ine ndekha amene ndidachokera kwa Mulungu; Ineyo ndi amene ndidaona Atate. Ndithu ndikunenetsa kuti wokhulupirira Ine, ali nawo moyo wosatha. Ine ndine chakudya chopatsa moyo. Makolo anu ankadya mana m’chipululu muja, komabe adafa. Koma chakudya chimene ndikunenachi ndi chimene chidatsika kuchokera Kumwamba, kuti munthu atachidya asafe. Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Ndipo chakudyacho chimene Ine Ndidzapereka ndi thupi langa, limene ndikulipereka kuti anthu a pa dziko lonse lapansi akhale ndi moyo.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Yesu adadzipereka kuti anthu a pa dziko lonse lapansi akhale ndi moyo. Tsono, tiyeni, tiwapempherere anthu onse:

 

1.     Tipempherere ansembe onse kuti akhale a mtima umodzi ndi Yesu Khristu, popereka nsembe yake, ndiponso pa moyo wao wonse.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere akhristu amene adaleka kulandira kuti azindikire umphawi wao, azidzidzimuka m’mitima mwao ndi kubwerera kwa Ambuye ndi mtima wolapa.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere mabanja a chikhristu kuti eni ake ayesetse kuutsa m’mitima ya ana ao njala yofunitsa kulandira Ambuye m’sakramenti la Ukaristia.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse tili muno tipemphererane kuti tisunge umodzi wathu ndi kumakondana mwaubale, pakulandira Ambuye kawirikawiri m’sakramenti la Ukaristia.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, popereka kwa Inu mapemphero athuwa, tikuyamika chifundo chanu chofuna kutisonkhanitsa tonse pamodzi, kuti tikhale amodzidi mwa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...