Saturday, August 17, 2024

 LAMULUNGU LA 20 PA CHAKA – B.

“Ndine Chakudya Chopatsa Moyo.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MIYAMBO: MIYAMBO 09: 01 – 06 (Bwera, dzadyeko chakudya changa, ndipo udzamweko vinyo amene ndakonza).

 

Nzeru idamanga nyumba yake, idaimika nsanamira zake zisanu ndi ziwiri. Idapha ziweto zake, idakonza vinyo wake, nkuyala tebulo lake. Idatuma adzakazi ake kuti akakhalire pa malo apamwamba mu minda ndipo akalengeze kuti, “Munthu wamba aliyense abwere kuno!” Kwa munthu wopanda nzeru imati, “Bwera, dzadyeko chakudya changa, ndipo udzamweko vinyo amene ndakonza. Leka kupulukira kwako, kuti ukhale ndi moyo, uziyenda m’njira ya nzeru.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 34: 02 – 03, 10 – 15.

 

Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.

 

Ndidzayamika Chauta nthawi zonse,

Pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza,

Moyo wanga umanyadira Chauta,

Anthu ozunzika amve ndipo akondwere.

 

Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.

 

Muzimvera Chauta, inu anthu ake oyera mtima,

Pakuti amene amamumvera sasowa kanthu,

Ngakhale anaamkango amasowa chakudya ndipo amakhala anjala,

koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasowa zinthu zabwino.

 

Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.

 

Bwerani ana anga, mundimvere,

Ndidzakuphunzitsani kuwopa Chauta,

Ndani mwa inu amakhumba moyo ndi kulakalaka kuti akhale masiku ambiri,

Kuti asangalale ndi zinthu zabwino?

 

Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.

 

Ngati ufunadi moyo, usalankhule zoipa,

Pakamwa pako pasakambe zonyenga,

Lewa zoipa, ndipo uchite zabwino,

Funafuna mtendere ndi kuulondola.

 

Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO: AEFESO 05: 15 – 20 (Dziwani zimene Ambuye afuna kuti muchite).

 

Abale, samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthawi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa. Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziwani zimene Ambuye afuna kuti muchite. Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse. Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, m’dzina la Ambuye athu Yesu Khristu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 6:56

Alleluia, Alleluia – Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga, amakhala mwa Ine, ndipo Ine ndimakhala mwa iyeyo. Atero Ambuye.  – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 06: 51 – 58 (Thupi langa ndi chakudya chenicheni, ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni).

 

Yesu adauza khamu la anthu kuti: “Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Ndipo chakudyacho chimene Ine ndidzapereka ndi thupi langa, limene ndikulipereka kuti anthu a pa dziko lonse lapansi akhale ndi moyo.” Pamenepo Ayuda aja adayamba kukangana okhaokha, ankati, “Munthu ameneyu angathe bwanji kutipatsa thupi lake kuti tidye?” Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati simudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu. Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga, ali ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. Pakuti thupi langa ndi chakudya chenicheni, ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndipo Ine ndimakhala mwa iyeyo. Monga Atate amoyo adandituma, ndipo Ine ndili ndi moyo pokhala mwa Iwo, momwemonso aliyense wodya Ine, adzakhala ndi moyo pokhala mwa Ine. Chakudya chimene chidatsika kuchokera Kumwamba nchimenechi. Nchosiyana ndi mana aja amene makolo anu ankadya koma nkufabe. Wodya chakudya chimenechi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pokhala a mtima umodzi ndi Yesu Khristu amene akutitsogolera, tiyamike Atate a Kumwamba popempherera anthu onse:

 

1.     Ansembe onse ayesetse kuphatikizana kwenikweni ndi Yesu Khristu popereka nsembe ya Ukaristia, kuti azisenza udindo wao molimbika ndi mokhulupirika.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akhristu onse azindikire kuti Ukaristia ndi maziko a moyo wao, poti Ambuye amafuna kukhala mwa iwowo ndi kuwalunzitsa onse m’chikondi chao.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akhristu amene ali ndi ana ayesetse ndithu kuphunzitsa ana awo za Ambuye Yesu, ndipo autse m’mitima mwao njala yofunitsa kulandira Ambuye m’sakramenti la Ukaristia.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse opemphera pano tikhale ndi mtima wosirira kulandira Ambuye kawirikawiri, kuti tikhazikike m’chikondi chao ndi kumagwirizana tonse mwa ubale.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, popereka kwa Inu mapemphero athuwa, tikukuyamikani kuti mwatikonzera phwando mu Ufumu wanu, kuti tizikondwera tonse pamaso panu mpaka muyaya. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...