LAMULUNGU LA 21 PA CHAKA – B.
“Muli nawo Mau Opatsa Moyo Wosatha.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA YOSWA: YOSWA 24: 01 – 02, 15 – 18. (Nafenso tidzatumikira Chauta, chifukwa ndiye Mulungu wathu).
Yoswa adasonkhanitsa mafuko onse a Aisraele ku Sekemu. Adaitana akuluakulu, atsogoleri, aweruzi ndi akapitao Aisraele, ndipo onsewo adafika pamaso pa Mulungu. Adauza anthu onsewo kuti, “zimene Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena ndi izi, akuti, ‘kale makolo anu ankakhala pa mbali ina ya mtsinje wa Yufurate, ndi kumapembedza milungu ina. Mmodzi mwa makolo amenewa anali Tera, bambo wa Abrahamu ndi Nahori.’ Tsono ngati simufuna kutumikira Chauta, sankhani lero lomwe lino amene mudzamtumikire, kapena milungu ya Aamori amene mukukhala nawo m’dziko mwao. Koma ine pamodzi ndi banja langa lonse, tidzatumikira Chauta.” Apo anthuwo adayankha kuti, “zoti nkusiya Chauta ndi kumakatumikira mulungu ina ndiye ai, ife sitingathe kuchita zotere mpang’ono pomwe. Chauta, Mulungu wathu, ndiye amene adatulutsa makolo athu pamodzi ndi ife tomwe mu ukapolo, ku dziko la Ejipito. Ndipo tidaonanso ndi maso athu zinthu zazikulu zimene adachita. Ife tikufika, Chauta ankapirikitsa Aamori amene ankakhala m’dziko lino. Motero nafenso tidzatumikira Chauta, chifukwa ndiye Mulungu wathu.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 34: 02 – 03, 16 – 23.
Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.
Ndidzayamika Chauta nthawi zonse,
Pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza,
Moyo wanga umanyadira Chauta,
Anthu Ozunzika amve ndipo akondwere.
Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.
Koma Chauta amawakwiyira anthu ochita zoipa,
Anthuwo sadzakumbukiranso pansi pano,
Chauta samakwiiyira anthu ochita zolungama,
Ndipo amamvera zopempha zawo.
Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.
Pamene anthu ake akulira kuti awathandize,
Chauta amamva nawapulumutsa m’mavuto ao onse,
Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka,
Amapulumutsa otaya mtima.
Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.
Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri,
Komabe Chauta amawapulumutsa m’mavuto awo onse,
Chauta amasunga thupi la munthuyo,
Palibe fupa limene limasweka.
Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.
Choipa chitsata mwini,
Anthu odana ndi munthu wa Mulungu adzalangidwa,
Chauta amaombola moyo wa atumiki ake,
Palibe wothawira kwa Iye amene adzalangidwe.
Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO: AEFESO 05: 21 – 32. (Chinsinsicho nchokhudza Khristu ndi Mpingo.)
Abale, inu amene mumaopa Khristu, muzimverana. Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga mumamvera Ambuye. Paja mwamuna ndi mutu wa mkazi wake, monga momwe Khristu ali mutu wa mpingo, umene uli thupi lake, ndipo Iye mwini ndi Mpulumutsi wa Mpingowo. Tsono monga Mpingo umamvera Khristu, momwemonso akazi azimvera amuna ao pa zonse. Inu amuna, muzikonda akazi anu, monga momwe Khristu adakondera Mpingo, nadzipereka chifukwa cha Mpingowo. Adachita zimenezi kuti aupatule ukhale wakewake, atauyeretsa pakuutsuka ndi madzi ndiponso ndi mau ake. Adafuna kuti akauimike pamaso pake uli waulemerero, wopanda banga kapena makwinya, kapena kanthu kena kalikonse kouipitsa, koma uli woyera ndi wangwiro kotheratu. Momwemonso amuna azikonda akazi ao, monga momwe eni akewo amakondera matupi ao. Amene amakonda mkazi wake ndiye kuti amadzikonda iye yemwe. Palibiretu munthu amene amadana ndi thupi lake, ndipo ife ndife ziwalo zake. Paja mau a Mulungu akuti, “nchifukwa chake mwamuna adzasiye atate ndi amai ake, nkukaphatikizana ndi mkazi wake, kuti awiriwo asanduke thupi limodzi.” Mau amenewa akutiwululira chinsinsi chozama, ndipo ndikuti chinsinsicho nchokhudza Khristu ndi Mpingo.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 06: 60 – 69.
Alleluia, Alleluia – Mau anu, Ambuye, ndiwo amapatsa Mzimu wa Mulungu ndiponso moyo. Muli nawo ndinu mau opatsa moyo wosatha. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 06: 60 – 69. (Ambuye, nanga tingapitenso kwa yani? Muli nawo ndinu mau opatsa moyo wosatha).
Ophunzira ambiri a Yesu atamva zimenezi adati, “mau amenewa ngapatali. Angathe kuwavomera ndani?” Yesu adaadziwa mumtima mwake kuti ophunzira ake akung’ung’udza za zimenezi. Tsono adawafunsa kuti, “kodi zimenezi mukukhumudwa nazo? Nanga mudzatani mukadzaona Mwana wa Munthu akukwera kunka kumene anali kale? Mzimu wa Mulungu ndiwo umapatsa moyo, mphamvu ya munthu siipindula konse. Mau amene ndalankhula nanu ndiwo amapatsa mzimu wa Mulungu ndiponso moyo. Koma pali ena mwa inu amene sakukhulupirira.” (Pakuti Yesu adaadziwiratu mpachiyambi pomwe amene sadzakhulupirira, adaamudziwiratunso amene analikudzampereka kwa adani ake.) Tsono adati, “nchifukwa chake ndinakuuzani kuti palibe munthu amene angabwere kwa Ine ngati Atate sampatsa mphamvu zobwerera kwa Ine.” Kuchokera pamenepo ophunzira ambiri a Yesu adamsiya, osayenda nayenso. Tsono Yesu adafunsa ophunzira khumi ndi awiri aja kuti, “nanga inu, kodi inunso mukufuna kuchoka?” Simoni Petro adati, “Ambuye, nanga tingapitenso kwa yani? Muli nawo ndinu mau opatsa moyo wosatha. Ife ndiye tikukhulupirira ndipo tikudziwa kuti ndinu Woyera uja wochokera kwa Mulungu.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, tiyeni tipereke mapemphero athu kwa Mulungu kuti mau a Mthenga Wabwino aunikire anthu onse:
1. Atate, mupatse nzeru ndi mphamvu kwa akulu a Eklezia kuti aonetse chikhulupiriro cholimba potsogolera mbumba yanu.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Atate, mulimbitse ansembe ndi onse okhala m'zipani, kuti akutumikireni mokhulupirika ndi mwakhama, potsata malonjezo ao.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Atate, muunikire anthu amene akuyenda mu mdima nakhala okayikakayika, kuti aweramuke ndi kuyang’ana Mwana wanu Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Atate, mudalitse mabanja onse kuti eni ake akhale okhulupirika wina kwa m’nzake, ndipo akondane monga momwe Mwana wanu adakondera Mpingo wake.
Tikupemphani, mutivomereze.
Mulungu wathu, mverani mapemphero athuwa, ndipo mutiwonjezere chikhulupiriro, kuti tilondole mosakayika mapazi a Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

No comments:
Post a Comment