Saturday, August 31, 2024

LAMULUNGU LA 22 PA CHAKA – B.

LAMULUNGU LA 22 PA CHAKA – B.

“Anthuwa Amangondilemekeza Pakamwa Pokha.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA DEUTORONOMO: DEUTORONOMO 04: 01 – 02, 06 – 08 (Musaonjezerepo kanthu kena pa zimene ndikulamulani ndipo muzimvera malamulo amene ndakupatsani).

 

Tsono inu Aisraele, muzimvera malamulo ndi malangizo onse amene ndikukuphunzitsani, kuti mukhale ndi moyo. Ndipo mudzalowa ndi kukhazikika m’dziko limene Chauta, Mulungu wa makolo anu, akukupatsani. Musaonjezerepo kanthu kena pa zimene ndakulamulani, ndipo musachotserepo kanthu. Muzimvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndakupatsani. Mukawasunge ndi kuwatsata, ndipo chimenechi chidaonetsa anthu a mitundu ina kuti ndinu anthu anzeru ndi omvetsa zinthu bwino. Akadzamva malamulo onsewa, iwowo adzati, “mtundu umenewo ndi waukulu, wanzeru ndi womvetsa zinthu bwino.” Palibe mtundu wina uliwonse, kaya ndi waukulu chotani, umene uli ndi Mulungu wokhala pafupi nawo, monga m’mene Mulungu wathu amakhalira ndi ife. Nthawi zonse tikamuitana, amatiyankha. Palibe mtundu wina uliwonse kaya ndi waukulu chotani, umene ali ndi malamulo ndi malangizo achilungamo onga awa amene ndakupatsani lerowa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 15: 02 – 05.

 

Munthu wochita zolungama amakhala pa phiri la Chauta.

 

Inu Chauta, kodi ndani angathe kukhala pa phiri lanu loyera?

Ndi munthu amene amayenda mosalakwa,

Amene amachita zolungama nthawi zonse,

Amene amalankhula zinthu ndi mtima woona.

 

Munthu wochita zolungama amakhala pa phiri la Chauta.

 

Ndi amene sasinjirira ndipo sachita anzake zoipa,

Kapena kumafalitsa mbiri yoipa ya anzake,

Ndi amene amanyoza munthu womkana Mulungu,

Koma amamlemekeza anthu omvera Chauta.

 

Munthu wochita zolungama amakhala pa phiri la Chauta.

 

Ndi amene amachitadi zimene walonjeza,

Ngakhale zikhale zowawa chotani,

Ndi amene salandira chiphuphu kuti azunze munthu osalakwa,

Munthu wochita zimenezi, palibe chilichonse chimene chidzamgwedeze.

 

Munthu wochita zolungama amakhala pa phiri la Chauta.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA YAKOBE: YAKOBE 01: 17 – 18, 21 – 22, 27. (Muzichita zimene mau akukuuzani).

 

Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, ndipo Atate a zofunikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuwala kwao sikutsitirika mpang’ono pomwe. Mwa kufuna kwake mwiniwakeyo, adatipatsa moyo kudzera mwa mau ake oona, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, ife tikhale ngati zipatso zoyamba zimene Iye wadzipatulira. Nchifukwa chake siyani chizolowezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muwalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m’mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani. Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena. Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m’dziko lapansi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YAKOBE 01: 18.

Alleluia, Alleluia – Mwa kufuna kwake mwiniwakeyo, adatipatsa moyo kudzera mwa mau ake oona, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, ife tikhale ngati zipatso zoyamba zimene Iye wadzipatulira. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 07: 01 – 08, 14 – 15, 21 – 23. (Inu mumasiya Malamulo a Mulungu, nkumasunga miyambo ya anthu).

 

Tsiku lina Afarisi ena pamodzi ndi aphunzitsi ena a Malamulo, amene adaachokera ku Yerusalemu, adasonkhana kwa Yesu. Iwo adaaona kuti ophunzira ake ena ankangodya chakudya osasamba m’manja moyenera (ndiye kuti mosasamala mwambo wosamba m’manja). Pajatu Afarisi ndi Ayuda ena onse saadya asanasambe m’manja mwa njira yoyenera. Amatero kuti asunge mwambo wa makolo. Ndipo akachokera ku msika, saadya osasamba m’manja. Amasunganso miyambo ina yambiri imene makolo ao adawasiyira, monga kutsuka zikho, miphika, ndi ziwiya zamkuwa [ndi mabedinso]. Choncho Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo aja adamufunsa Yesu kuti, “chifukwa chiyani ophunzira anu sasunga mwambo wa makolo, koma amangodya chakudya osasamba m’manja moyenera?” Yesu adawayankha kuti, “inu anthu achiphamaso, ndithu mneneri Yesaya adaanenadi zoona muja adaalemba kuti, ‘anthu awa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe, koma mtima wao uli kutalitali ndi Ine. Amandipembedza inde, koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu, chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni, ndi malamulo a anthu chabe.’” Kenaka Yesu adati, “inu mumasiya Malamulo a Mulungu, nkumasunga miyambo ya anthu.” Pambuyo pake Yesu adaitananso anthu aja kuti adze pafupi, ndipo adawauza kuti, “mverani nonsenu, ndipo mumvetsetse bwino. Palibe chinthu chochokera kunja ndi kulowa m’kati mwa munthu chimene chingathe kumuipitsa. Koma zimene zimatuluka mwa munthu ndizo zimamuipitsa. Chifukwa m’kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za chiwerewere, za kuba, za kuphana, zigololo, masiriro, kuipa mtima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa. Zoipa zonsezi zimachokera m’kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.


Mapemphero a Akhristu


Abale, mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba kwa Atate. Tiyeni, tipemphe Mulungu kuti mawu ake ndi malamulo ake alowe ndi kuzika mizu m’mitima ya anthu onse:


1. Tipempherere akulu amene ali ndi udindo mu Mpingo, kuti atsogolere anthu awo moona ndi modzichepetsa mtima, pa njira ya kuyera ndi ya chikondi.

Tikupemphani, mutivomereze.


2. Tipempherere akhristu onse kuti kuyera kwao ndi kukondana kwao kuunikire anzao akunja ndi kuwakokera kwa Ambuye.

Tikupemphani, mutivomereze.


3. Tipempherere anthu osauka, odwala ndi amasiye, kuti azindikire kukoma mtima kwa Mulungu, powayendera anzao achikhristu.

Tikupemphani, mutivomereze.


3. Tidzipempherere ife tomwe, kuti chipempbedzo chathu chikhale choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa anzathu.

Tikupemphani, mutivomereze.


Atate, musaleke kuyeretsa mitima yathu ndi kuchotsamo kunyenga kulikonse, kuti mawu athu amveke Kumwamba, ndipo ntchito zathuzikome pamaso panu. Mwana Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.


#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/ 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...