LAMULUNGU LA 23 PA CHAKA – B.
“Makutu a Agonthi Adzatsekuka.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 35: 04 – 07. (Makutu a agonthi adzatsekuka, ndipo osalankhula adzaimba mokondwa).
Muuze onse a mtima wamantha kuti, “limbani mtima, musachite mantha. Mulungu wanu akubwera kudzalipsira ndi kulanga adani anu. Akubwera kudzakupulumutsani.” Pamenepo maso a anthu akhungu adzaphenyuka, ndipo makutu a agonthi adzatsekuka. Opunduka adzalumpha ngati mphoyo, ndipo osalankhula adzaimba mokondwa. Akasupe adzatumphuka m’chipululu, ndipo mitsinje idzayenda m’dziko louma. Mchenga wotentha udzasanduka nyanja, ndipo dziko louma lidzasanduka la akasupe. Pamene panali mbuto za nkhandwe padzamera udzu ndi bango.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 146: 07 – 10.
Tamanda Chauta iwe Mtima wanga.
Chauta amasunga malonjezo ake nthawi zonse,
Amachitira anthu opsinjidwa zolungama,
Amawapatsa chakudya anthu anjala,
Chauta amamasula am’ndende.
Tamanda Chauta iwe Mtima wanga.
Chauta amatsekula maso a anthu osapenya,
Chauta amakweza anthu otsitsidwa,
Chauta amakonda anthu ochita chilungamo,
Chauta amateteza alendo.
Tamanda Chauta iwe Mtima wanga.
Chauta amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye,
Koma njira za anthu oipa amazipotoza,
Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya,
Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzalamulira ku mibadwo yonse.
Tamanda Chauta iwe Mtima wanga.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA YAKOBE: YAKOBE 02: 01 – 05. (Mulungu adasankha amphawi kuti alandire madalitso amene Iye adalonjeza anthu omukonda).
Abale anga, popeza kuti mumakhulupirira Ambuye athu Yesu Khristu, Ambuye aulemerero, musamakondera. Mwachitsanzo: munthu wina alowa mumsonkhano wanu atavala mphete zagolide m’manja, alinso ndi zovala zokongola. Winanso nkulowa, koma ali mmphawi, nsanza zili wirawira. Tsono inu pofuna kusamala kwambiri wovala zokongolayo, mumuuza kuti, ‘khalani apa pabwinopa,’ mmphawi uja nkumuuza kuti, ‘iwe, kaimirire apo, kapena dzakhale pansi kumapazi kwangaku.’ Limenelotu ndi tsankho pakati pa inu nokhanokha, ndipo inuyo mwasanduka oweruza a maganizo oipa. Mwerani, abale anga okondedwa, kodi suja Mulungu adasankha ooneka amphawi m’maso mwa anthu, kuti akhale olemera pa chikhulupiriro, ndi kuti alandire madalitso amene Iye adalonjeza anthu omukonda?
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 04: 23.
Alleluia, Alleluia – Yesu adalalika Uthenga Wabwino wonena za ufumu wakumwamba. Ankachiritsanso nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam’thupi. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 07: 31 – 37. (Agonthi amawachiritsa nkumamva, ndipo osalankhula amawalankhulitsa).
Yesu adachokanso ku dera lija la ku Tiro, namayenda kudutsa dera la ku Sidoni, kupita ku nyanja ya ku Galileya, kudzera pakati pa dera la Mizinda Khumi. Anthu ena adabwera kwa Iye ndi munthu yemwe anali gonthi ndi wolunkhula movutikira. Anthuwo adapempha Yesu kuti amchiritse pomusanjika manja munthuyo. Yesu adatengera munthu uja pambali kumchotsa pa khamu la anthu. Adapisa zala m’makutu a munthuyo, nalavula malovu, nkukhudza lilime la munthu uja. Adayang’ana kumwamba, nadzuma, nkumuuza kuti, “Efata!” ndiye kuti “Tsekuka!” Pomwepo makutu a munthuyo adatsekuka, ndipo chimene chinkamanga lilime lake chidamasuka, mpaka adayamba kulankhula bwino lomwe. Yesu adalamula anzake a munthuyo kuti, “musakauzetu wina aliyense zimenezi.” Koma ngakhale adawaletsa mwamphamvu choncho, iwo adanka nalengeza ndithu zimenezi. Ndipo anthu adazizwa kopitirira ndithu. Adati, “ameneyu amachita zonse bwino. Ngakhale agonthi amawachiritsa nkumamva, ndipo osalankhula amawalankhulitsa.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, tsopano tipereke mapemphero athu kwa Mulungu kuti anthu onse amve Mthenga Wabwino ndi kulandira chipulumutso pakukhulupirira Yesu Khristu:
1. Atate, muwongolere Mpingo wanu kuti usonyeze kukoma mtima kwanu kwa anthu onse, pakuwaphunzitsa mau anu ndi Kuwatumikira mwachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Atate, mulimbitse atsogoleri olamulira maiko kuti asamale ubwino wa anthu ao, ndipo ayesetse kutukula miyoyo ya anthu osauka.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Atate, mudalitse adokotala, anesi ndi onse ogwira ntchito m’zipatala, kuti awonetse mtima wachifundo kwa odwala onse, mopanda tsankho.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Atate, mutidzaze ndi Mzimu wanu wachikondi, kuti ifenso tidzetse chimwemwe cha chipulumutso chanu m’mitima ya anthu osauka, pakuwathandiza mwaufulu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Inu Chauta Mulungu wathu, mutikomere mtima polandira mapemphero athuwa, ndipo ife tidzakuyamikani ndi kutamanda chifundo chanu masiku onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment