Saturday, September 14, 2024

LAMULUNGU LA 24 PA CHAKA – B

LAMULUNGU LA 24 PA CHAKA – B.

“Wotaya Moyo Wake Chifukwa Cha Ine Adzausunga.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA: YESAYA 50: 05 – 09. (Ndidapereka msana wanga kwa ondimenya).

 

Ambuye Chauta anditsekula makutu, ndipo sindidawanyoze kapena kuwapindukira. Ndidapereka msana wanga kwa ondimenya, ndiponso masaya anga kwa ondimwetula ndevu. Sindidawabisire nkhope ondinyoza ndi ondithira malovu. Koma kunyoza kwao sindikuvutika nako, chifukwa Ambuye Chauta amandithandiza. Nchifukwa chake ndalimbitsa mtima wanga ngati mwala. Ndikudziwa kuti sadzandichititsa manyazi. Wondikhalira kumbuyo ali pafupi, ndaninso angandiimbe mlandu? Tipitire limodzi ku bwalo lamilandu. Wofuna kutsutsana nane ndani? Nabwere pafupi. Ambuye Chauta ndi amene amandithandiza, ndani anganene kuti ndine wopalamula? Ndithu, onse ondizenga mlandu adzatheratu. Kutha kwake ngati chovala chodyewa ndi njenjete.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 115: 01 – 06, 08 – 09.

 

Ndimayenda pamaso pa Chauta m’dziko la amoyo.

 

Ndimakonda Chauta chifukwa amamva mau anga omupempha,

Iye amatchera khutu kuti andimve,

Nchifukwa chake ndidzampempha nthawi zonse pamene ndili moyo.

 

Ndimayenda pamaso pa Chauta m’dziko la amoyo.

 

Misampha ya imfa idandizinga, zoopsa za m’dziko la akufa zidandigwera,

Ndidaona mavuto, nkugwidwa ndi nthumazi,

Tsono ndidapemphera potchula dzina la Chauta kuti,

Chauta ndikukupemphani, pulumutsani moyo wanga.

 

Ndimayenda pamaso pa Chauta m’dziko la amoyo.

 

Chauta ndi wokoma mtima ndi wolungama,

Mulungu wathu ndi wachifundo,

Chauta amasunga a mtima wodzichepetsa,

Pamene ndidagwa m’zoopsa, Iye Adandipulumutsa.

 

Ndimayenda pamaso pa Chauta m’dziko la amoyo.

 

Pakuti Inu Chauta, mwandipulumutsa ku imfa,

Mwaletsa misozi yanga,

Mwanditeteza kuti ndisaphunthwe,

Ndimayenda pamaso pa Chauta m’dziko la amoyo.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA YAKOBE: YAKOBE 02: 14 – 18. (Chikhulupiriro pachokha, nchopanda ntchito zake, nchakufa basi).

 

Abale anga, pali phindu lanji, ngati munthu anena kuti, ndili ndi chikhulupiriro, koma popanda chimene akuchitapo? Kodi chikhulupiriro chotere chingampulumutse? Mwachitsanzo: mbale wina kapena mlongo ali ndi usiwa, ndipo masiku onse alibe chakudya chokwanira. Tsono wina mwa inu angowauza kuti, pitani ndi mtendere, mukafundidwe ndipo mukakhute, koma osawapatsa zimene akusowazo, pamenepo phindu lake nchiyani? Choncho, chikhulupiriro pachokha, chopanda ntchito zake, nchakufa basi. Koma kapena wina anganene kuti, inuyo muli ndi chikhulupiriro, ineyo ndili ndi ntchito zabwino. Pamenepo ine nkumuyankha kuti, uyesetse kundiwonetsa chikhulupiriro chako chopanda ntchito zakecho, ine ndi ntchito zanga ndikuwonetsa chikhulupiriro changa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AGALATIYA 06: 14.

Alleluia, Alleluia – Koma ine sindinganyadire kanthu kena kalikonse, koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu. Popeza kuti tsopano zapansipano kwa ine zili ngati zakufa, ndipo inenso kwa zapansipano, ndili ngati wopachikidwa. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 08: 27 – 35. (Mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri).

 

Yesu ndi ophunzira ake adapita ku midzi ya ku Kesareya-Firipi. Pa njira Yesu adafunsa ophunzira akewo kuti, “kodi anthu amati Ine ndine yani?” Iwo adayankha kuti, “ena amati ndi Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya, enanso amati ndinu mmodzi mwa aneneri.” Apo Yesu adawafunsa kuti, “nanga inuyo, mumati ndine yani?” Petro adamuyankha kuti, “inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja.” Yesu adawalamula kuti asauze munthu wina aliyense za Iye. Yesu adayamba kuphunzitsa ophunzira ake kuti, “mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri. Akulu a Ayuda, ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzamkana. Iye adzaphedwa, koma patapita masiku atatu adzauka.” Zimenezi adazinena mosabisa konse. Apo Petro adamtengera pambali, nayamba kumdzudzula. Koma Yesu adacheuka, nayang’ana ophunzira ake ena aja, ndipo adadzudzula Petro. Adati, “choka apa, iwe Satana! Maganizo akowa si maganizo a Mulungu ai, ndi maganizo a anthu chabe.” Pambuyo pake Yesu adaitana khamu la anthu pamodzi ndi ophunzira aja kuti adze pafupi naye, ndipo adawauza kuti, “munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata. Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine ndi Uthenga Wabwino, adzaupulumutsa.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, popereka kwa Mulungu mapemphero athuwa tiperekenso zowawa zonse zimene anthu akuzimva m’dziko lino lapansi:

 

1.     Atate, mulimbitse mtima atsogoleri a Mpingo kuti asenze udindo wao mwakhama. Asaope kusauka ndi kutaya moyo wawo omwe chifukwa cha akhristu ao.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate, mukumbukire akhristu onse amene azunzidwa chifukwa chokhulupirira Mthenga Wabwino. Muwachirikize, azizindikira kuti Ufumu wa Kumwamba ndi wao.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate, mudalitse odwala ndi ena onse amene akuvutika m’mitima mwao. Apeze mphamvu zopirira mavuto ao pokumbukira imfa ya Yesu Mpulumutsi.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate, mutipatse ife tonse chikhulupiriro cholimba, kuti titumikire anzathu modziiwala tokha, osaopa kumva zowawa.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Inu Chauta Mulungu wathu, landirani mapemphero athuwa, ndipo mutiphunzitse kumanga moyo wathu pa chikondi cha Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...