LAMULUNGU LA 25 PA CHAKA – B.
“Wamkulu Adzisandutse Wamng’ono, Wotumukira Anthu Onse.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA LUNTHA: LUNTHA 02: 12, 17 – 20. (Timpereke ku imfa yochititsa manyazi).
Tsono timukhalizire munthu wolungama, popeza kuti amativutitsa, ndipo amatsutsana ndi ntchito zathu. Amatidzudzula chifukwa chopandulira malamulo, amatinena kuti timanyoza mwambo. Tiyeni tiwone ngati mau ake ndi oona, tiwone zimene zidzamufikire pakutha pa moyo wake. Ngati wolungamayo ndi mwanandi wa Mulungu, Mulungu adzamuthandiza, adzampulumutsa kwa adani ake. Timuyese pakumusautsa ndi kumunyoza, kuti tiwone ngati ndi wofatsa, ngati ndi wodziwa kupirira. Timpereke ku imfa yochititsa manyazi, paja iye akuti Mulungu adzamteteza.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 54: 03 – 06, 08.
Ambuye ndiwo amachirikiza moyo wanga.
Inu Mulungu, pulumutsani ndi dzina lanu,
Onetsani ndi mphamvu zanu kuti ndine wosalakwa,
Inu Mulungu, Imvani pemphero langa,
Tcherani khutu kuti mumve mau a pakamwa panga.
Ambuye ndiwo amachirikiza moyo wanga.
Anthu onyada andiwukira,
Anthu ankhalwe amafunafuna moyo wanga,
Iwo saganizako za Inu Mulungu.
Ambuye ndiwo amachirikiza moyo wanga.
Komatu, Mulungu ndiye amandithandiza,
Ambuye ndiwo amachirikiza moyo wanga,
Ndidzapereka nsembe kwa Inu mwaufulu,
Ndidzatamanda dzina lanu, popeza kuti ndinu abwino.
Ambuye ndiwo amachirikiza moyo wanga.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA YAKOBE: YAKOBE 03: 16 – 04: 03. (Chilungamo ndiye chipatso cha mbeu zimene anthu adzetse mtendere amafesa mu mtendere).
Pajatu pamene pali kaduka ndi kudzikonda, pomweponso pali chisokonezo ndi ntchito yoipa ya mtundu uliwonse. Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso. Ndipo chilungamo ndiye chipatso cha mbeu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere. Kodi nkhondo zimachokera kuti? Kukangana pakati panu kumachokera kuti? Kodi suja zimachokera ku zilakolako zanu zathupi, zimene zimachita nkhondo mwa inu? Mumalakalaka zinthu, koma zimakusowani, nchifukwa chake mumapha munthu. Mumasirira zinthu, koma simungathe kuzipeza, nchifukwa chake mumamenyana, nkumachita nkhondo. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu. Ndipo ngakhale mupemphe, simulandira, chifukwa mumapempha molakwa. Zimene mumapempha, mumafuna kungozimwazira pa zokukondweretsani basi.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Cf. 02 ATESALONIKA 02: 14.
Alleluia, Alleluia – Mulungu adakuitanani kudzera mwa Uthenga Wabwino kuti mulandire nao ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 09: 30 – 37. (Ngati wina afuna kukhala wamkulu, adzisandutse wotumikira onse).
Atachoka kumeneko, Yesu ndi ophunzira ake ankadutsa m’dziko la Galileya. Koma Iye sadafune kuti anthu adziwe, chifukwa ankaphunzitsa ophunzira ake. Ankawauza kuti, “Mwana wa Munthu akudzaperekedwa kwa anthu, ndipo iwowo adzamupha. Koma atamupha, Iye adzauka patapita masiku atatu.” Ophunzira ake sadamvetse mau amenewa, komabe ankaopa kumufunsa. Yesu ndi ophunzira ake adafika ku Kapernao. Atalowa m’nyumba, Iye adawafunsa kuti, “kodi panjira paja mumatsutsana zotani?” Ophunzira adangoti chete. Ndiye kuti zimene ankatsutsana panjirapo zinali zakuti wamkulu ndani pakati pao. Yesu adakhala pansi, nawaitana ophunzira khumi ndi awiri aja. Ndipo adawauza kuti, “ngati wina afuna kukhala wamkulu, adzisandutse wamng’ono, wotumikira onse.” Atatero adatenga mwana, namkhazika pakati pao nkumufungata, nawauza kuti, “aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene. Ndipo wondilandira Ine bwino, ndiye kuti akulandira bwino osati Ineyo, koma Atate amene adandituma.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, monga ana amadalira chifundo cha bambo ndi mai, ifenso tsopano tipereke mapemphero athu kwa Atate athu a Kumwamba:
1. Tipempherere akhristu onse, kuti avomere kutumikira Mpingo wa Yesu Khristu, osamangoganiza zao zokha.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Tipempherere atsogoleri onse, kuti asenze udindo wao mosamala ndi modzichepetsa mtima.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Tipempherere anthu opata, kuti asanyadire chuma chao, koma akumbukire kuthandiza anzao m’zosowa zao.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Tidzipempherere ife tomwe kuti tikhale ofatsa ndi a mtima wodzichepetsa monga Yesu analili pa moyo wawo wonse.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, polandira mapemphero athuwa, muwamvere chifundo ana anu onse amene ali m’mavuto. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment