Saturday, June 29, 2024

LAMULUNGU LA 13 PA CHAKA – B.

LAMULUNGU LA 13 PA CHAKA – B.

“Ambuye Yesu ndiwo opatsa moyo.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA LUNTHA: LUNTHA 01: 13 – 15, 02: 22 – 24. (Koma imfa idalowa m’dziko lino lapansi chifukwa cha dumbo la Satana).

 

Mulungu sadapange imfa, sakondwera ndi imfa ya anthu amoyo. Iye adalenga zonse kuti zizikhalapo. Zolengedwa zonse m’dziko lapansi nzabwino, zilibe ululu wopha anthu. Imfa ilibe ulamuliro pansi pano, chifukwa chilungamo chidzakhalapo mpaka muyaya. Sadziwa maganizo obisika a Mulungu. Sakhulupirira malipiro a moyo wolungama. Sazindikira konse kuti ilipodi mphotho ya anthu oyera mtima. Ndithu Mulungu adalenga anthu kuti akhale osafa, adawapanga kuti akhale chifaniziro cha m’mene aliri Mwiniwakeyo. Koma imfa idalowa m’dziko lino lapansi chifukwa cha dumbo la Satana. Izi ndi zomwe anthu ogwirizana naye Satanayo adzaonadi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 30: 02, 04 – 06, 11 – 13.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, mwandipulumutsa ine.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta,

Pakuti mwanditulutsa m’dzenje la imfa,

Simudalole kuti adani anga akondwere poona ndikuvutika,

Inu Chauta, mwanditulutsa m’dziko la akufa,

Mwandibwezeranso moyo kuti ndingatsikire ku manda.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, mwandipulumutsa ine.

 

Imbani nyimbo zotamanda Chauta,

Inu anthu ake oyera mtima,

Mumthokoze chifukwa cha dzina lake loyera,

Mkwiyo wake ndi wa kanthawi chabe,

Koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse,

Misozi ingachezere kugwa usiku,

M’mawa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, mwandipulumutsa ine.

 

Imvani, Inu Chauta, ndipo mundikomere mtima,

Inu Chauta, mukhale mthandizi wanga,

Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina,

Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya.

 

Ndidzakutamandani, Inu Chauta, mwandipulumutsa ine.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 02 AKORINTO 08: 07, 09, 13 – 15. (Poti inu muli ndi zambiri tsopano, moyenera kumathandiza osowa).

 

Abale, zonse mudalandira pakulu, monga kukhulupirira, kulankhula, kudziwa zinthu, kuchita changu pa zonse, ndiponso kutikonda. Motero tifuna kuti muperekenso pakulu zachifundozi. Mukudziwa kukoma mtima kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ngakhale anali wolemera, adakhala mmphawi chifukwa cha inu, kuti ndi umphawi wakewo inu mukhale olemera. Sindikufuna kunena kuti inuyo muvutike, ena apepukidwe, ai, koma kuti pakhale kulingana. Poti inu muli ndi zambiri tsopano, muyenera kumathandiza osowa, kuti m’tsogolomo nawonso akadzakhala ndi zochuluka, azidzakuthandizani pa zosowa zanu. Motero padzakhala kulingana. Paja Malembo akuti, amene adapata zambiri, sizidamchulukire amene adapata pang’ono, sizidamchepere.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – 02 TIMOTEYO 01:10.

Alleluia, Alleluia – Mpulumutsi wathu Khristu Yesu adathetsa mphamvu za imfa, ndipo mwa Uthenga Wabwino adaonetsera poyera moyo. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 05: 21 – 43. (Mtsikana iwe, ndikuti dzuka).

 

Pa nthawi yomweyo, Yesu adaolokanso nyanja. Pamene adafika pa tsidya, chinamtindi cha anthu chidasonkhana pamphepete pa nyanja pamene panali Iyeyo. Tsono kudafika munthu wina, dzina lake Yairo, amene anali mmodzi mwa akulu a nyumba yamapemphero. Ataona Yesu, adadzigwetsa ku mapazi ake, nayamba kumdandaulira kwambiri. Adati, “pepani, mwana wanga wamkazi ali pafupi kufa. Ngati nkotheka, mukamsanjike manja kuti achire ndi kukhala ndi moyo.” Yesu adanyamuka namapita naye. Anthu ambiri adatsagana naye namayenda momupanikiza.

 

Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziwiri. Adaazunzika zedi ndi asing’anga ochuluka amene ankayesa kumuchiza. Mwakuti adaamwaza chuma chake chonse, komabe osapeza bwino konse. M’malo mwake matendawo analikunka nakulirakulira. Maiyo anali atamva za Yesu. Tsono adalowa m’chinamtindi cha anthu chija, nkuphaphatiza mpaka kukafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza chovala chake. Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Ndikangokhudza ngakhale zovala zake zokhazi, ndichira.”

 

Ndipodi nthawi yomweyo matenda a msambowo adaleka, mwiniwakeyo nkumva m’thupi mwake kuti matenda ake aja atha. Pomwepo Yesu adazindikira kuti mphamvu zina zatuluka mwa Iye. Tsono adatembenuka nayang’ana anthu aja ndipo adafunsa kuti, “kodi ndani wandikhudza zovala?” Ophunzira ake adati, “ndi inu nomwe mukuwona kuti anthu akukupanikizani, ndiye mungafunse bwanji kuti, ndani wandikhudza?” Koma Yesu adayang’anayang’ama kuti aone yemwe wachita zimenezi. Apo mai uja adachita mantha nayamba kunjenjemera, chifukwa anali atazindikira zimene zidaamuwonekerazo. Adadza pafupi, nadzigwetsa pansi pamaso pa Yesu, nkumufotokozera zonse monga momwe zidaachitikira.

 

Yesu adamuuza kuti, “inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi Mtendere. Matenda anu atheratu.” Yesu akulankhulabe, kudafika anthu kuchokera kunyumba kwa mkulu uja. Adamuuza mkulu uja kuti, “mwana uja watsirizika. Musawavutenso Aphunzitsiwa.” Koma Yesu sadasamale zimene anthuwo ankanena. Adauza mkulu uja kuti, “musaope ai, inu mungokhulupirira.” Tsono sadalole kuti winanso atsagane naye, koma Petro, ndi Yakobo, mbale wa Yakoboyo. Pamene iwo adafika kunyumba kwa mkulu wa nyumba yamapemphero uja, Yesu adaona chipiringu cha anthu, akulira ndi kubuma. Iye atalowa, adawafunsa kuti, “chifukwa chiyani mukuchita phokoso lonseli ndi kubuma? Mwanayu sadamwalire ai, ali m’tulo chabe.”

 

Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola. Iye adawatulutsira panja onse, nangotenga bambo wake ndi mai wake wa mwanayo, ndiponso amene adaali naye aja, nkulowa kuchipinda kumene kunali mwana uja. Tsono adagwira mwanayo pa dzanja namuuza kuti, “Talita, kumi.” Ndiye kuti, “Mtsikana iwe, ndikuti dzuka.”) Pomwepo mtsikanayo adadzukadi, nayamba kuyenda, pakuti adaali wa zaka khumi ndi ziwiri. Pamenepo anthu aja adazizwa kwambiri. Koma Yesu adawalamula mwamphamvu kuti zimenezi wina aliyense asazidziwe. Kenaka adawauza kuti ampatse chakudya mtsikanayo.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, monga Yailo uja adagwada kumapazi a Yesu namdandaulira kwambiri, ifenso tiyeni tikweze mapemphero athu kwa Atate athu a Kumwamba:

 

1.     Ambuye, Atsogoleri a mpingo autse chikhulupiriro chachikulu m’mitima ya anthu pakuwatsimikizira za kuuka kwa akufa.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Anthu amene ali pafupi kufa azindikire kuti imfa si mathero a zinthu zonse, koma ndi khomo lolowera kumwamba ndi chiyambi cha chikondwerero chosatha.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Adokotala ndi anesi ogwira ntchito m’zipani aonetse anthu odwala mtima wachifundo pakuwasamala monga momwe angathere.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

4.     Ife tomwe tili muno tikhale akhristu achangu pa ntchito zothandizira anzathu pa zosowa zao, makamaka pa matenda ndi pa chisoni.
Tikupemphani, mutivomereze.

Atate, tikukupemphani zimenezi potamanda kukoma mtima kwanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, June 22, 2024

LAMULUNGU LA 12 PA CHAKA – B.

 
LAMULUNGU LA 12 PA CHAKA – B.

“Tizikhala ndi chikhulupiriro champhamvu.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA YOBU: YOBU 38: 01, 08 – 11. (Mafunde ako amphamvuwo aime pomwepo).

 

Chauta adayankha Yobu m’kamvulumvulu kuti: “kodi ndani amene adatsekera nyanja pamene inkalengedwa pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko? Ndinetu amene ndidakuta nyanjayo ndi mitambo, ndidaiveka mdima ngati chovala. Ndidailembera malire, ndidaiikira mipiringidzo ndi zitseko zake. Tsono ndidati, ufike mpaka apo osabzolapo, mafunde ako amphamvuwo aime pomwepo.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 107: 23 – 26, 28 – 31.

 

Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake nchamuyaya.

 

Ena adakayenda ku Nyanja m’zombo,

Namachita malonda pa Nyanja yaikulu,

Adaona ntchito za Chauta,

Ntchito zake zodabwitsa, pa madzi akuya.

 

Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake nchamuyaya.

 

Ndiye kuti Chauta adalamula,

Nautsa namondwe amene adawindula mafunde apanyanja,

Zombozo zidakwera mpaka m’mwamba nkutsikiranso kwakuya,

Ndipo anthuwa adataya mtima pa mavuto aowo.

 

Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake nchamuyaya.

 

Tsono anthu aja adalira kwa Chauta,

Pamene anali m’mavuto amenewo,

Ndipo Chauta adawapulumutsa ku mavuto aowo.

Chauta adatontholetsa namondwe,

Ndipo Mafunde apanyanja adachita bata.

 

Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake nchamuyaya.

 

Choncho anthuwo adasangalala chifukwa kudachita bata,

Ndipo Chauta adakawafikitsa kudooko kumene ankalinga,

Athokoze Chauta chifukwa cha chikondi chake chosasinthika,

Chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse.

 

Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake nchamuyaya.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 02 AKORINTO 05: 14 – 17. (Zimene zilipo nzatsopano).

 

Abale, chikondi cha Khristu ndicho chimatiwongolera mokakamiza, popeza kuti tikudziwa mosakayika konse kuti Munthu mmodzi adafera anthu onse, ndiye kuti pamenepo onse adafa. Iye adafera anthu onse, kuti amene ali ndi moyo, asakhalenso ndi moyo wofuna kungodzikondweretsa okha, koma azikondweretsa Iye amene adawafera, nauuka kwa akufa chifukwa cha iwowo. Nchifukwa chake kuyambira tsopano ife sitiganiziranso za munthu aliyense potsata nzeru za anthu chabe. Ngakhale kale tinkaganiza za Khristu potsata nzeru za anthu chabe, koma tsopano sitiganiziranso za Iye motero. Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 07: 16.

Alleluia, Alleluia – Mneneri wamkulu waoneka pakati pathu. Mulungu wadzathandiza anthu ake. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 04: 35 – 41. (Kodi Iyeyu ndi munthu wotani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zizimumvera?)

 

Tsiku lomwelo, dzuwa litalowa, Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwoloke, tipite ku tsidya.” Tsono iwo adasiya khamu la anthu lija, natenga Yesu m’chombo momwe adaalimo. Padaalinso zombo zina zotsagana naye. Tsono padauka namondwe woopsa. Mafunde ankalowa m’chombomo, kotero kuti chidaayamba kudzaza ndi madzi. Koma nthawi imeneyo Yesu anali kumbuyo m’chombomo, ali mtulo atatsamira mtsamiro. Pamenepo ophunzira aja adamudzutsa, adati, “Aphunzitsi, kodi simukusamalako kuti tikumira?” Yesu adadzuka, ndipo adadzudzula mphepoyo, nalamula nyanja kuti, “tonthola! Khala bata!” Mphepo ija idalekadi, kenaka padagwa bata lalikulu. Apo Yesu adawafunsa kuti, “bwanji mukuchita mantha?” Kani mulibe chikhulupiriro inu?” Koma iwo adaagwidwa ndi mantha kwambiri, nkumafunsana kuti, “kodi Iyeyu ndi munthu wotani kuti ngakhale mphepo ndi nyanja zizimumvera?”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, podziwa kuti Yesu alikupitiriza pakati pathu ntchito zake zotipulumutsa, titule m’manja mwake nkhawa ndi zovuta za anthu onse:

 

1.     Ambuye, muwongolere Mpingo wanu ndi kuuteteza kosalekeza, kuti anthu anu alimbikire m’chikhulupiriro, pozindikira chifundo chanu chowasamalira.

Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Ambuye, mulimbitse Apapa, Aepiskopi ndi ansembe onse, kuti alalike mthenga wanu mosakayika; adziwe kuti mau anu ali nazo mphamvu zopulumutsira munthu aliyense wowakhulupirira.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Ambuye, mulimbitse mitima ya akhristu amene alikuzunzidwa chifukwa cha dzina lanu, kuti asafooke m’chikhulupiriro chao, koma akondwere podziwa kuti mphoto yao njaikulu kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

4.     Ambuye, mutipatse ife tomwe chikhupiriro cholimba, kuti tikutumikireni ndi mtima womasuka pomanga moyo wathu pa chikondi chanu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate okoma mtima, mverani mapemphero athuwa, pakuti Inu nomwe mudatipatula kuti tikhale ana anu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, June 15, 2024

LAMULUNGU LA 11 PA CHAKA – B.

LAMULUNGU LA 11 PA CHAKA – B.

“Mulungu salephera kukhazikitsa Ufumu wake.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI EZEKIELE: EZEKIELE 17: 22 – 24. (Ndine Chauta amene ndimatalikitsa mitengo yaifupi).

 

Ambuye Chauta akunena izi: “Ine ndemwe ndidzatenga kanthambi ka ku nsonga yapamwamba ya mtengo wa mkungudza, ndipo ndidzakabzala. Pa tinthambi tapamwamba ndidzathyoloka kena kanthete ndipo ndidzakabzala pa phiri lalitali kwambiri. Kadzaphuka ndi kubala zipatso zake. Motero kadzasanduka mkungudza wokoma. Mbalame za mitundu yonse yam’dzikomo idzadziwa kuti ndine Chautane amene ndimafupikitsa mitengo yaitali, ndiponso kutalikitsa mitengo yaifupi. Ndimaumitsa mitengo yobiriwira, ndi kubiriwiritsa mitengo youma. Ine Chauta ndanena zimenezi, ndipo ndidzazichitadi.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 92: 02 – 03, 13 – 16.

 

Nkwabwino kuthokoza Chauta.

 

Nkwabwino kuthokoza Chauta,

Kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse,

Nkwabwino m’mawa kulalika,

Za chikondi chanu chosasinthika,

Ndipo usiku kusimba za kukhulupirika kwanu.

 

Nkwabwino kuthokoza Chauta.

 

Anthu okondwetsa Mulungu,

Zinthu zimawayendera bwino ngati mitengo ya mgwalangwa,

Amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni,

Ali ngati mitengo yookedwa m’Nyumba ya Chauta.

 

Nkwabwino kuthokoza Chauta.

 

Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba,

Nthawi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriwira,

Imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama,

Iye ndiye thanthwe langa, mwa Iye mulibe chokhota.

 

Nkwabwino kuthokoza Chauta.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 02 AKORINTO 05: 06 – 10. (Ngakhale tikhalebe kuno, kapena kwa Ambuye, timayesetsa kuwakondweretsa Ambuye).

 

Abale, nchifukwa chake timalimba mtima masiku onse, ndipo tikudziwa kuti nthawi yonse pamene tikukhala m’thupi, ngati kwathu, ndiye kuti tili kutali ndi Ambuye. Pakuti timatsata chikhulupiriro, osati zopenya ndi maso. Ndithu tikulimba mtima, ndipo makamaka tikadakonda kutuluka m’thupi lathu lino ndi kukakhala kwa Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhalebe kuno, kapena tikakhale kwa Ambuye, timayesetsa kuwakondweretsa Ambuyewo. Pakuti tonsefe tiyenera kukaimirira poyera pamaso pa Khristu kuti atiweruze. Kumeneko aliyense adzalandira zomuyenera, molingana ndi zimene adachita pansi pano, zabwino kapena zoipa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 12: 31b – 32.

Alleluia, Alleluia – Mbeu ija ndi mau a Mulungu, amene Khristu anawafesa; amene angapeze mbeuyo adzakhala mwa Iye mpaka muyaya. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 04: 26 – 34 (Pamene aifesa m’nthaka, ndi yaing’ono kwambiri. Koma ikukula ndithu kupambana zitsamba zina zonse).

 

Yesu adawauzanso kuti, “za Ufumu wa Mulungu tingazifanizire motere: munthu afesa mbeu m’munda. Iyeyo atha kumangogona usiku, m’mawa nadzuka, nthawi yonseyo mbeu adafesa zija zikumera ndi kukula, mwiniwakeyo osadziwa m’mene zonsezi zikuchitikira. Paja nthaka imabereketsa mbeuzo yokhayokha. Umayamba ndi mmera, kenaka ngala, pambuyo pake njere m’ngala muja zimakhwima, Tsono mbeuzo zikacha, munthu uja amatenga mpeni wodulira, pakuti nyengo yokolola yafika.” Yesu adatinso, “kodi Ufumu wa Mulungu tingauyerekeze ndi chiyani? Kaya tiwufanizire ndi chiyani? Uli ngati njere ya mbeu ya mpiru. Pamene aifetsa m’nthaka, ndi yaing’ono kwambiri mukaiyerekeza ndi njere zina pansi pano. Koma akaifetsa, imamera, mbeu yake nkukula ndithu kupambana zitsamba zina zonse. Imachita nthambi zazikulu, kotero kuti mbalame zimatha kudzamanga zisa mumthunzi mwake.” Yesu ankaphunzitsa anthu ndi mafanizo ambiri onga amenewa, polinganiza ndi nzeru za anthuwo. Sankawaphunzitsa popanda mafanizo. Koma ankati akakhala payekha ndi ophunzira ake, ankawatanthauzira zonse.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pakuti Mau a Mulungu salephera kuutsa chikhulupiriro m’mitima ya anthu, tiyeni, tipempherere anthu onse.

1.     Tipempherere atsogoleri olalika Mau a Mulungu, kuti alimbikitse kufalitsa Mthenga Wabwino ponseponse.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere akatekumeni ndi anthu onse amene adakali kunja, kuti atsekulire Mulungu mitima yao polandira bwino mau ake.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere akhristu onse amene ali pabanja kuti atsogolere ana awo m’njira ya chipulumutso, pakuwaphunzitsa za Ambuye Yesu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

4.     Tizipemphererana ife tomwe, kuti mau a Mthenga Wabwino akhazikike m’mitima mwathu ndi kulimbitsa chikhulupiriro chathu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, tikukuyamikani chifukwa mau anu ndi opatsa moyo. Mutithandize kuwasunga ndi kuwagwiritsa ntchito kuti tiyende M’chikondi chanu masiku onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, June 8, 2024

LAMULUNGU LA 10 PA CHAKA – B.

LAMULUNGU LA 10 PA CHAKA – B.

“Mutipulumutse kwa Woipa uja.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS: GENESIS 03: 09 – 15 (Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkazi, padzakhala chidani pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake).

 

Chauta adamuitana Adamu uja kuti, “Kodi uli kuti?” Adamu adayankha kuti, “Ndinakumvani m’mundamu ndipo ndinaopa, ndiye ndinabisala ntaona kuti ndili maliseche.” Mulungu adamufunsa kuti, “Kodi adakuuza ndani kuti uli maliseche? kapena wadyatu zipatso za mtengo uja ndidakuuza kuti usadyewu eti?” Pamenepo Adamu adayankha kuti, “Mkazi mudandipatsayu ndiye amene anandipatsa zipatsozo kuti ndidye, ndipo ndadyadi.” Apo Chauta adafunsa mkazi kuti, “Kodi iwe, zimene wachitazi wachitiranji?” Mkazi uja adayankha kuti, “Njoka ndiyo imene inandinyenga kuti ndidye.” Pamenepo Chauta adauza njokayo kuti, “Chifukwa chakuti wachita zimenezi, ndiwe wotembereredwa pakati pa nyama zonse za pansi pano, zoweta ndi zakuthengo zomwe. Kuyambira tsopano mpaka muyaya udzakwawa ndi kumimba kwako, ndipo chakudya chako chidzakhala fumbi. Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkazi, padzakhala chidani pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake. Idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaluma chidendene chake.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 130: 01 – 02, 03 – 04, 05 – 06, 07 – 08.

 

Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.

 

Ndikulirira Inu Chauta,

Ndili m’dzenje lozama lamavuto,

Ambuye imvani liwu langa,

Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga.

 

Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.

 

Inu Chauta, mukadawerengera machimo,

Ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye?

Koma inu mumakhululukira,

Nchifukwa chake timakulemekezani.

 

Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.

 

Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta,

Ndimayembekeza ndi mtima wonse,

Ndipo ndimakhulupirira mau ake.

Mtima wanga umayembekeza Chauta,

Kupambanadi m’mene alonda amayembekezera mbandakucha.

 

Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.

 

Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika,

Ndi wokonzeka kupulumutsa.

Adzaombola Israele ku machimo ake onse.

 

Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 02 AKORINTO 04: 13 – 05: 01. (Popeza kuti ife tili ndi Mtima wokhulupirira, ifenso timalankhula).

 

Abale, Malembo akuti, “Ndidakhulupirira, nchifukwa chake ndidalankhula.” Tsono popeza kuti ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timalankhula. Pakuti tikudziwa kuti Mulungu amene adaukitsa Ambuye Yesu kwa akufa, adzatiwukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatifikitsa pamodzi nanu pamaso раkе. Cholinga cha zonsezi nchakuti inu mupindule, ndipo kuti monga momwe anthu olandira madalitso a Mulungu akunka nachulukirachulukira, momwemonso othokoza Mulungu achulukirechulukire ndi kumchitira ulemu. Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku. Masautso athu ndi opepuka, a nthawi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya. Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya. Thupi limene timakhalamo pansi pano lili ngati msasa chabe. Koma tikudziwa kuti msasawu ukadzapasuka, tidzakhala ndi nyumba ina imene Mulungu adatikonzera Kumwamba. Nyumbayo ndi yosamangidwa ndi manja a anthu, ndipo ndi yamuyaya.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 12: 31b – 32.

Alleluia, Alleluia – Tsopano mfumu ya anthu ochimwa a dziko lino lapansi adzaponyedwa kunja, atero Ambuye. Ndipo Ine, akadzandipachika, ndidzakokera anthu onse kwa Ine. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 03: 20 – 35. (Satanayo sangalimbe, ndiye kuti watha basi).

 

Pambuyo pake Yesu adapita kwao, ndipo anthu ambiri adasokhananso, kotero kuti Iye ndi ophunzira ake analibe ndi mpata womwe wodyera chakudya. Achibale ake atamva zimenezi, adabwera kuti adzamtenge, chifukwa ankati, “Wachita misala.” Aphunzitsi ena a Malamulo, amene adaabwera kuchokera ku Yerusalemu, ankanena kuti, “Munthu ameneyu wagwidwa ndi Belezebulu” Ankatinso, “Mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipa nzochokera kwa mkulu wa mizimuyo.” Tsono Yesu adaitana anthu kuti adze pafupi, nanena mwafanizo kuti, “Kodi a mu ufumu wa Satana angathe bwanji kutulutsana okhaokha? Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo sungalimbe. Ndipo anthu a m’banja limodzi akayamba kugawikana, banja lotere silingalimbe. Tsono ngati a mu ufumu wa Satana aukirana okhaokha nagawikana, Satanayo sangalimbe, ndiye kuti watha basi. Wina sangathe kungolowa m’nyumba ya munthu wamphamvu nkumulanda katundu wake. Amayamba wammanga, kenaka ndiye kufunkha za m’nyumba mwakemo. Ndithu ndikunenetsa kuti anthu angathe kukhululukidwa machimo onse, ngakhalenso zonena zao zonse zomunyoza Mulunguyo. Koma aliyense wonyoza Mzimu Woyera, sadzakhululukidwa konse. Tchimo lakelo limakhala mpaka muyaya.” Yesu adalankhula zimenezi poona kuti anthu aja ankanena kuti, “Wagwidwa ndi mzimu woipa.” Amai ake ndi abale ake a Yesu adabwera kunyumbako. Adaima panja, natuma anthu kuti akamuitane. Anthu ambirimbiri adaakhala pansi pomzungulira. Ndiye iwo aja adamuuza kuti, “Amai anu ndi abale anu ali panjapa, akukufunani.” Koma Iye adati, “Amai anga! Abale anga! Otinso?” Apo adayang’ana anthu amene anali pomzungulira aja nati, “Inetu amai anga ndi abale anga ndi awa. Aliyense wochita zimene Mulungu akufuna, ameneyo ndiye mbale wanga ndi mlongo wanga ndi amai anga.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pozindikira umphawi wathu ndi kufooka kwathu, tiyeni titembenukire kwa Atate athu a Kumwamba pokhulupirira chifundo chao chofuna kupulumutsa anthu onse:

 

1.     Atsogoleri a Mpingo alimbikire kufalitsa Mthenga Wabwinoponse ponse, kuti anthu onse amve za Yesu Khristu ndi kulandira chipulumutso chake.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akhristu ofooka adzidzimuke mumtima mwao ndi kutembenukira kwa Mulungu, pokumbukira chikondi chozama cha Yesu Khristu Mpulumutsi.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akatekumeni nawonso ayesetse kusiya zoipa ndi kusintha makhalidwe ao, poika chikhulupiriro chao chonse pa Ambuye Yesu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe tisaleke kutsogolera anzathu pa njira ya kupemphera podziwa kuti patokha, popanda Yesu kutithandiza, sitingathe kuchita kanthu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, mutiwongolere ndi Mzimu wanu Woyera, kuti tikutumikireni mokhulupirika pakuchita kufuna kwanu nthawi zonse, kusonyeza kuti ndifedi abale ake a Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...