“Tizikhala ndi chikhulupiriro champhamvu.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA YOBU: YOBU 38: 01, 08 – 11. (Mafunde ako amphamvuwo aime pomwepo).
Chauta adayankha Yobu m’kamvulumvulu kuti: “kodi ndani amene adatsekera nyanja pamene inkalengedwa pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko? Ndinetu amene ndidakuta nyanjayo ndi mitambo, ndidaiveka mdima ngati chovala. Ndidailembera malire, ndidaiikira mipiringidzo ndi zitseko zake. Tsono ndidati, ufike mpaka apo osabzolapo, mafunde ako amphamvuwo aime pomwepo.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 107: 23 – 26, 28 – 31.
Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Ena adakayenda ku Nyanja m’zombo,
Namachita malonda pa Nyanja yaikulu,
Adaona ntchito za Chauta,
Ntchito zake zodabwitsa, pa madzi akuya.
Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Ndiye kuti Chauta adalamula,
Nautsa namondwe amene adawindula mafunde apanyanja,
Zombozo zidakwera mpaka m’mwamba nkutsikiranso kwakuya,
Ndipo anthuwa adataya mtima pa mavuto aowo.
Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Tsono anthu aja adalira kwa Chauta,
Pamene anali m’mavuto amenewo,
Ndipo Chauta adawapulumutsa ku mavuto aowo.
Chauta adatontholetsa namondwe,
Ndipo Mafunde apanyanja adachita bata.
Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Choncho anthuwo adasangalala chifukwa kudachita bata,
Ndipo Chauta adakawafikitsa kudooko kumene ankalinga,
Athokoze Chauta chifukwa cha chikondi chake chosasinthika,
Chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse.
Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 02 AKORINTO 05: 14 – 17. (Zimene zilipo nzatsopano).
Abale, chikondi cha Khristu ndicho chimatiwongolera mokakamiza, popeza kuti tikudziwa mosakayika konse kuti Munthu mmodzi adafera anthu onse, ndiye kuti pamenepo onse adafa. Iye adafera anthu onse, kuti amene ali ndi moyo, asakhalenso ndi moyo wofuna kungodzikondweretsa okha, koma azikondweretsa Iye amene adawafera, nauuka kwa akufa chifukwa cha iwowo. Nchifukwa chake kuyambira tsopano ife sitiganiziranso za munthu aliyense potsata nzeru za anthu chabe. Ngakhale kale tinkaganiza za Khristu potsata nzeru za anthu chabe, koma tsopano sitiganiziranso za Iye motero. Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 07: 16.
Alleluia, Alleluia – Mneneri wamkulu waoneka pakati pathu. Mulungu wadzathandiza anthu ake. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 04: 35 – 41. (Kodi Iyeyu ndi munthu wotani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zizimumvera?)
Tsiku lomwelo, dzuwa litalowa, Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwoloke, tipite ku tsidya.” Tsono iwo adasiya khamu la anthu lija, natenga Yesu m’chombo momwe adaalimo. Padaalinso zombo zina zotsagana naye. Tsono padauka namondwe woopsa. Mafunde ankalowa m’chombomo, kotero kuti chidaayamba kudzaza ndi madzi. Koma nthawi imeneyo Yesu anali kumbuyo m’chombomo, ali mtulo atatsamira mtsamiro. Pamenepo ophunzira aja adamudzutsa, adati, “Aphunzitsi, kodi simukusamalako kuti tikumira?” Yesu adadzuka, ndipo adadzudzula mphepoyo, nalamula nyanja kuti, “tonthola! Khala bata!” Mphepo ija idalekadi, kenaka padagwa bata lalikulu. Apo Yesu adawafunsa kuti, “bwanji mukuchita mantha?” Kani mulibe chikhulupiriro inu?” Koma iwo adaagwidwa ndi mantha kwambiri, nkumafunsana kuti, “kodi Iyeyu ndi munthu wotani kuti ngakhale mphepo ndi nyanja zizimumvera?”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, podziwa kuti Yesu alikupitiriza pakati pathu ntchito zake zotipulumutsa, titule m’manja mwake nkhawa ndi zovuta za anthu onse:
1. Ambuye, muwongolere Mpingo wanu ndi kuuteteza kosalekeza, kuti anthu anu alimbikire m’chikhulupiriro, pozindikira chifundo chanu chowasamalira.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Ambuye, mulimbitse Apapa, Aepiskopi ndi ansembe onse, kuti alalike mthenga wanu mosakayika; adziwe kuti mau anu ali nazo mphamvu zopulumutsira munthu aliyense wowakhulupirira.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Ambuye, mulimbitse mitima ya akhristu amene alikuzunzidwa chifukwa cha dzina lanu, kuti asafooke m’chikhulupiriro chao, koma akondwere podziwa kuti mphoto yao njaikulu kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ambuye, mutipatse ife tomwe chikhupiriro cholimba, kuti tikutumikireni ndi mtima womasuka pomanga moyo wathu pa chikondi chanu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate okoma mtima, mverani mapemphero athuwa, pakuti Inu nomwe mudatipatula kuti tikhale ana anu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment