LAMULUNGU LA 13 PA CHAKA – B.
“Ambuye Yesu ndiwo opatsa moyo.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA LUNTHA: LUNTHA 01: 13 – 15, 02: 22 – 24. (Koma imfa idalowa m’dziko lino lapansi chifukwa cha dumbo la Satana).
Mulungu sadapange imfa, sakondwera ndi imfa ya anthu amoyo. Iye adalenga zonse kuti zizikhalapo. Zolengedwa zonse m’dziko lapansi nzabwino, zilibe ululu wopha anthu. Imfa ilibe ulamuliro pansi pano, chifukwa chilungamo chidzakhalapo mpaka muyaya. Sadziwa maganizo obisika a Mulungu. Sakhulupirira malipiro a moyo wolungama. Sazindikira konse kuti ilipodi mphotho ya anthu oyera mtima. Ndithu Mulungu adalenga anthu kuti akhale osafa, adawapanga kuti akhale chifaniziro cha m’mene aliri Mwiniwakeyo. Koma imfa idalowa m’dziko lino lapansi chifukwa cha dumbo la Satana. Izi ndi zomwe anthu ogwirizana naye Satanayo adzaonadi.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 30: 02, 04 – 06, 11 – 13.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta, mwandipulumutsa ine.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta,
Pakuti mwanditulutsa m’dzenje la imfa,
Simudalole kuti adani anga akondwere poona ndikuvutika,
Inu Chauta, mwanditulutsa m’dziko la akufa,
Mwandibwezeranso moyo kuti ndingatsikire ku manda.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta, mwandipulumutsa ine.
Imbani nyimbo zotamanda Chauta,
Inu anthu ake oyera mtima,
Mumthokoze chifukwa cha dzina lake loyera,
Mkwiyo wake ndi wa kanthawi chabe,
Koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse,
Misozi ingachezere kugwa usiku,
M’mawa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta, mwandipulumutsa ine.
Imvani, Inu Chauta, ndipo mundikomere mtima,
Inu Chauta, mukhale mthandizi wanga,
Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina,
Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta, mwandipulumutsa ine.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 02 AKORINTO 08: 07, 09, 13 – 15. (Poti inu muli ndi zambiri tsopano, moyenera kumathandiza osowa).
Abale, zonse mudalandira pakulu, monga kukhulupirira, kulankhula, kudziwa zinthu, kuchita changu pa zonse, ndiponso kutikonda. Motero tifuna kuti muperekenso pakulu zachifundozi. Mukudziwa kukoma mtima kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ngakhale anali wolemera, adakhala mmphawi chifukwa cha inu, kuti ndi umphawi wakewo inu mukhale olemera. Sindikufuna kunena kuti inuyo muvutike, ena apepukidwe, ai, koma kuti pakhale kulingana. Poti inu muli ndi zambiri tsopano, muyenera kumathandiza osowa, kuti m’tsogolomo nawonso akadzakhala ndi zochuluka, azidzakuthandizani pa zosowa zanu. Motero padzakhala kulingana. Paja Malembo akuti, amene adapata zambiri, sizidamchulukire amene adapata pang’ono, sizidamchepere.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – 02 TIMOTEYO 01:10.
Alleluia, Alleluia – Mpulumutsi wathu Khristu Yesu adathetsa mphamvu za imfa, ndipo mwa Uthenga Wabwino adaonetsera poyera moyo. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 05: 21 – 43. (Mtsikana iwe, ndikuti dzuka).
Pa nthawi yomweyo, Yesu adaolokanso nyanja. Pamene adafika pa tsidya, chinamtindi cha anthu chidasonkhana pamphepete pa nyanja pamene panali Iyeyo. Tsono kudafika munthu wina, dzina lake Yairo, amene anali mmodzi mwa akulu a nyumba yamapemphero. Ataona Yesu, adadzigwetsa ku mapazi ake, nayamba kumdandaulira kwambiri. Adati, “pepani, mwana wanga wamkazi ali pafupi kufa. Ngati nkotheka, mukamsanjike manja kuti achire ndi kukhala ndi moyo.” Yesu adanyamuka namapita naye. Anthu ambiri adatsagana naye namayenda momupanikiza.
Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziwiri. Adaazunzika zedi ndi asing’anga ochuluka amene ankayesa kumuchiza. Mwakuti adaamwaza chuma chake chonse, komabe osapeza bwino konse. M’malo mwake matendawo analikunka nakulirakulira. Maiyo anali atamva za Yesu. Tsono adalowa m’chinamtindi cha anthu chija, nkuphaphatiza mpaka kukafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza chovala chake. Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Ndikangokhudza ngakhale zovala zake zokhazi, ndichira.”
Ndipodi nthawi yomweyo matenda a msambowo adaleka, mwiniwakeyo nkumva m’thupi mwake kuti matenda ake aja atha. Pomwepo Yesu adazindikira kuti mphamvu zina zatuluka mwa Iye. Tsono adatembenuka nayang’ana anthu aja ndipo adafunsa kuti, “kodi ndani wandikhudza zovala?” Ophunzira ake adati, “ndi inu nomwe mukuwona kuti anthu akukupanikizani, ndiye mungafunse bwanji kuti, ndani wandikhudza?” Koma Yesu adayang’anayang’ama kuti aone yemwe wachita zimenezi. Apo mai uja adachita mantha nayamba kunjenjemera, chifukwa anali atazindikira zimene zidaamuwonekerazo. Adadza pafupi, nadzigwetsa pansi pamaso pa Yesu, nkumufotokozera zonse monga momwe zidaachitikira.
Yesu adamuuza kuti, “inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi Mtendere. Matenda anu atheratu.” Yesu akulankhulabe, kudafika anthu kuchokera kunyumba kwa mkulu uja. Adamuuza mkulu uja kuti, “mwana uja watsirizika. Musawavutenso Aphunzitsiwa.” Koma Yesu sadasamale zimene anthuwo ankanena. Adauza mkulu uja kuti, “musaope ai, inu mungokhulupirira.” Tsono sadalole kuti winanso atsagane naye, koma Petro, ndi Yakobo, mbale wa Yakoboyo. Pamene iwo adafika kunyumba kwa mkulu wa nyumba yamapemphero uja, Yesu adaona chipiringu cha anthu, akulira ndi kubuma. Iye atalowa, adawafunsa kuti, “chifukwa chiyani mukuchita phokoso lonseli ndi kubuma? Mwanayu sadamwalire ai, ali m’tulo chabe.”
Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola. Iye adawatulutsira panja onse, nangotenga bambo wake ndi mai wake wa mwanayo, ndiponso amene adaali naye aja, nkulowa kuchipinda kumene kunali mwana uja. Tsono adagwira mwanayo pa dzanja namuuza kuti, “Talita, kumi.” Ndiye kuti, “Mtsikana iwe, ndikuti dzuka.”) Pomwepo mtsikanayo adadzukadi, nayamba kuyenda, pakuti adaali wa zaka khumi ndi ziwiri. Pamenepo anthu aja adazizwa kwambiri. Koma Yesu adawalamula mwamphamvu kuti zimenezi wina aliyense asazidziwe. Kenaka adawauza kuti ampatse chakudya mtsikanayo.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, monga Yailo uja adagwada kumapazi a Yesu namdandaulira kwambiri, ifenso tiyeni tikweze mapemphero athu kwa Atate athu a Kumwamba:
1. Ambuye, Atsogoleri a mpingo autse chikhulupiriro chachikulu m’mitima ya anthu pakuwatsimikizira za kuuka kwa akufa.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Anthu amene ali pafupi kufa azindikire kuti imfa si mathero a zinthu zonse, koma ndi khomo lolowera kumwamba ndi chiyambi cha chikondwerero chosatha.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Adokotala ndi anesi ogwira ntchito m’zipani aonetse anthu odwala mtima wachifundo pakuwasamala monga momwe angathere.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tomwe tili muno tikhale akhristu achangu pa ntchito zothandizira anzathu pa zosowa zao, makamaka pa matenda ndi pa chisoni.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, tikukupemphani zimenezi potamanda kukoma mtima kwanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment