LAMULUNGU LA 10 PA CHAKA – B.
“Mutipulumutse kwa Woipa uja.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS: GENESIS 03: 09 – 15 (Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkazi, padzakhala chidani pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake).
Chauta adamuitana Adamu uja kuti, “Kodi uli kuti?” Adamu adayankha kuti, “Ndinakumvani m’mundamu ndipo ndinaopa, ndiye ndinabisala ntaona kuti ndili maliseche.” Mulungu adamufunsa kuti, “Kodi adakuuza ndani kuti uli maliseche? kapena wadyatu zipatso za mtengo uja ndidakuuza kuti usadyewu eti?” Pamenepo Adamu adayankha kuti, “Mkazi mudandipatsayu ndiye amene anandipatsa zipatsozo kuti ndidye, ndipo ndadyadi.” Apo Chauta adafunsa mkazi kuti, “Kodi iwe, zimene wachitazi wachitiranji?” Mkazi uja adayankha kuti, “Njoka ndiyo imene inandinyenga kuti ndidye.” Pamenepo Chauta adauza njokayo kuti, “Chifukwa chakuti wachita zimenezi, ndiwe wotembereredwa pakati pa nyama zonse za pansi pano, zoweta ndi zakuthengo zomwe. Kuyambira tsopano mpaka muyaya udzakwawa ndi kumimba kwako, ndipo chakudya chako chidzakhala fumbi. Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkazi, padzakhala chidani pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake. Idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaluma chidendene chake.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 130: 01 – 02, 03 – 04, 05 – 06, 07 – 08.
Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.
Ndikulirira Inu Chauta,
Ndili m’dzenje lozama lamavuto,
Ambuye imvani liwu langa,
Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga.
Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.
Inu Chauta, mukadawerengera machimo,
Ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye?
Koma inu mumakhululukira,
Nchifukwa chake timakulemekezani.
Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.
Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta,
Ndimayembekeza ndi mtima wonse,
Ndipo ndimakhulupirira mau ake.
Mtima wanga umayembekeza Chauta,
Kupambanadi m’mene alonda amayembekezera mbandakucha.
Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.
Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika,
Ndi wokonzeka kupulumutsa.
Adzaombola Israele ku machimo ake onse.
Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 02 AKORINTO 04: 13 – 05: 01. (Popeza kuti ife tili ndi Mtima wokhulupirira, ifenso timalankhula).
Abale, Malembo akuti, “Ndidakhulupirira, nchifukwa chake ndidalankhula.” Tsono popeza kuti ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timalankhula. Pakuti tikudziwa kuti Mulungu amene adaukitsa Ambuye Yesu kwa akufa, adzatiwukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatifikitsa pamodzi nanu pamaso раkе. Cholinga cha zonsezi nchakuti inu mupindule, ndipo kuti monga momwe anthu olandira madalitso a Mulungu akunka nachulukirachulukira, momwemonso othokoza Mulungu achulukirechulukire ndi kumchitira ulemu. Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku. Masautso athu ndi opepuka, a nthawi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya. Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya. Thupi limene timakhalamo pansi pano lili ngati msasa chabe. Koma tikudziwa kuti msasawu ukadzapasuka, tidzakhala ndi nyumba ina imene Mulungu adatikonzera Kumwamba. Nyumbayo ndi yosamangidwa ndi manja a anthu, ndipo ndi yamuyaya.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 12: 31b – 32.
Alleluia, Alleluia – Tsopano mfumu ya anthu ochimwa a dziko lino lapansi adzaponyedwa kunja, atero Ambuye. Ndipo Ine, akadzandipachika, ndidzakokera anthu onse kwa Ine. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 03: 20 – 35. (Satanayo sangalimbe, ndiye kuti watha basi).
Pambuyo pake Yesu adapita kwao, ndipo anthu ambiri adasokhananso, kotero kuti Iye ndi ophunzira ake analibe ndi mpata womwe wodyera chakudya. Achibale ake atamva zimenezi, adabwera kuti adzamtenge, chifukwa ankati, “Wachita misala.” Aphunzitsi ena a Malamulo, amene adaabwera kuchokera ku Yerusalemu, ankanena kuti, “Munthu ameneyu wagwidwa ndi Belezebulu” Ankatinso, “Mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipa nzochokera kwa mkulu wa mizimuyo.” Tsono Yesu adaitana anthu kuti adze pafupi, nanena mwafanizo kuti, “Kodi a mu ufumu wa Satana angathe bwanji kutulutsana okhaokha? Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo sungalimbe. Ndipo anthu a m’banja limodzi akayamba kugawikana, banja lotere silingalimbe. Tsono ngati a mu ufumu wa Satana aukirana okhaokha nagawikana, Satanayo sangalimbe, ndiye kuti watha basi. Wina sangathe kungolowa m’nyumba ya munthu wamphamvu nkumulanda katundu wake. Amayamba wammanga, kenaka ndiye kufunkha za m’nyumba mwakemo. Ndithu ndikunenetsa kuti anthu angathe kukhululukidwa machimo onse, ngakhalenso zonena zao zonse zomunyoza Mulunguyo. Koma aliyense wonyoza Mzimu Woyera, sadzakhululukidwa konse. Tchimo lakelo limakhala mpaka muyaya.” Yesu adalankhula zimenezi poona kuti anthu aja ankanena kuti, “Wagwidwa ndi mzimu woipa.” Amai ake ndi abale ake a Yesu adabwera kunyumbako. Adaima panja, natuma anthu kuti akamuitane. Anthu ambirimbiri adaakhala pansi pomzungulira. Ndiye iwo aja adamuuza kuti, “Amai anu ndi abale anu ali panjapa, akukufunani.” Koma Iye adati, “Amai anga! Abale anga! Otinso?” Apo adayang’ana anthu amene anali pomzungulira aja nati, “Inetu amai anga ndi abale anga ndi awa. Aliyense wochita zimene Mulungu akufuna, ameneyo ndiye mbale wanga ndi mlongo wanga ndi amai anga.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, pozindikira umphawi wathu ndi kufooka kwathu, tiyeni titembenukire kwa Atate athu a Kumwamba pokhulupirira chifundo chao chofuna kupulumutsa anthu onse:
1. Atsogoleri a Mpingo alimbikire kufalitsa Mthenga Wabwino
ponse ponse, kuti anthu onse amve za Yesu Khristu ndi kulandira chipulumutso chake.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akhristu ofooka adzidzimuke mumtima mwao ndi kutembenukira kwa Mulungu, pokumbukira chikondi chozama cha Yesu Khristu Mpulumutsi.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Akatekumeni nawonso ayesetse kusiya zoipa ndi kusintha makhalidwe ao, poika chikhulupiriro chao chonse pa Ambuye Yesu.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tomwe tisaleke kutsogolera anzathu pa njira ya kupemphera podziwa kuti patokha, popanda Yesu kutithandiza, sitingathe kuchita kanthu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, mutiwongolere ndi Mzimu wanu Woyera, kuti tikutumikireni mokhulupirika pakuchita kufuna kwanu nthawi zonse, kusonyeza kuti ndifedi abale ake a Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment