CHAKA CHA THUPI NDI MAGAZI A AMBUYE – CHAKA B
“Yesu adatisiyira nsembe yake.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA EKSODO: EKSODO 24: 03 – 08 (Magazi amenewa ndiwo amene akutsimikiza chipangano chimene Chauta wapangana nanu).
Mose adapita kukauza anthu mau ndi malangizo onse amene Chauta adamuuza. Ndipo anthu onse adayankha kuti, “tidzachita zonse zimene Chauta wanena.” Apo Mose adalemba mau onse a Chauta. Ndipo adadzuka m’mawa ndithu nayamba kumanga guwa patsinde pa phiri. Kenaka adaimiritsa miyala khumi ndi iwiri ya mafuko khumi ndi awiri a Aisraele. Tsono adatuma Aisraele achinyamata kuti iwowa apereke nsembe zopsereza, ndi kupha ng’ombe kuti apereke nsembe zamtendere kwa Chauta. Mose adatengako theka la magazi, nawathira m’mbale, ndipo magazi otsala adawaza pa guwa. Pambuyo pake adatenga buku lachipangano, nawawerengera momveka anthuwo. Tsono anthuwo adati, “tidzachita zonse zimene Chauta walamula. Tidzamumvera Iyeyo.” Apo Mose adatenga magazi am’mbale aja, nawaza anthuwo, ndipo adati, “magazi amenewa ndiwo amene akutsimikiza chipangano chimene Chauta wapangana nanu pakukupatsani mau onsewa.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 116: 12 – 13, 15 – 18.
Ndidzakweza chikho cha chipulumutso, ndidzapemphera potchula dzina la Chauta.
Ndidzambwezera chiyani Chauta,
Pa zabwino zonse zimene adandichitira?
Ndidzakweza chikho cha chipulumutso,
Ndidzapemphera potchula dzina la Chauta.
Ndidzakweza chikho cha chipulumutso, ndidzapemphera potchula dzina la Chauta.
Imfa ya anthu oyera mtima a Chauta,
Ndi yamtengowapatali pamaso pake,
Chauta, ine ndine mtumiki wanu,
Mtumiki wanu weniweni,
Inu mwamasula maunyolo anga.
Ndidzakweza chikho cha chipulumutso, ndidzapemphera potchula dzina la Chauta.
Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera,
Ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta,
Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta,
Pamaso pa anthu ake onse.
Ndidzakweza chikho cha chipulumutso, ndidzapemphera potchula dzina la Chauta.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA KWA AHEBRI: AHEBRI 09: 11 – 15. (Magazi a Khristu, adzayeretsa mitima yathu pakuichotsera ntchito zosapindulitsa moyo).
Abale, Khristu wafika, ndipo ndiye Mkulu wa ansembe onse wa zokoma zimene zilikudza tsopano. Chihema chimene Iye amatumikiramo nchachikulu ndiponso nchangwiro kopambana. Nchosapangidwa ndi anthu, ndiye kuti si chapansipano. Pamene Khristu adabzola chihemachi, nkukalowa kamodzi kokhako m’malo Opatulika Kopambana, sadalowemo ndi magazi a atonde ndi a anaang’ombe amphongo ai. Adalowamo ndi magazi akeake. Potero adatikonzera chipulumutso chosatha. Magazi a atonde ndi a ng’ombe zamphongo, ndiponso phulusa la mwanawang’ombe wamkazi zimawazidwa pa anthu amene ali odetsedwa chifukwa chosasamala mwambo wachiyuda. Zimenezi zimawayeretsa pakuwachotsa litsiro lam’thupi. Nanji tsono magazi a Khristu, angathe kuchita zoposa. Mwa Mzimu wamuyaya Iye adadzipereka ngati nsembe yopanda chilema kwa Mulungu. Ndiye kuti magazi ake adzayeretsa mitima yathu pakuichotsera ntchito zosapindulitsa moyo, kuti tizitumikira Mulungu wamoyo. Nchifukwa chake Khristu ndi Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kuti amene Mulungu adawaitana, alandire madalitso osatha amene Mulunguyo adalonjeza. Izi zidatheka chifukwa cha imfa ya Khristu, imene imapulumutsa anthu ku zochimwa zozichita akali m’Chipangano choyamba chija.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 6:51
Alleluia – Ine ndine chakudya chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Atero Ambuye. – Alleluia.
-------------------------
NYIMBO YA UKARISTIA (SEQUENCE)
O SIYONI UYAMIKE
Mbusa wabwino, Buledi weniweni,
Mbuye Yesu, mutichitire chisoni.
Muteteze, nkulowetsa
Nkhosa zanufe kumwamba.
O Siyoni, uyamike
Mpulumutsi wako, Mbuye,
Mfumu ndinso Mbusa wako.
Sudzafika kuimbira
Mlungu wako mokwanira.
Ukwezetu mawu ako.
Nkofunika ndithu lero
Kutama Buledi wamoyo,
Ngwopatsa moyo womwewo.
Tidziwa mosapeneka
Kuti Yesu anapatsa
Bulediyu kwa apositoli.
Tsono tisankhule nyimbo
Zokoma kwambiri lero
Ndi kuimba mwachimwemwe.
Misa itibweretsera
Tsiku lomwe la kupanga
Phwando loyerayerali.
Ndi Pasaka yatsopano
Ya Mfumu yatsopanonso
Miyambo yakale yatha.
Zalero zibadiritsa
Zakale, monga kuyera
M’mawa kuchotsatu mdima.
Yesu anatilamula
Kubwereza zomwe zija
Anazichita tsikuli.
Pomvera Yesu ifenso
Tisandutsa buledi n’vinyo
Pa nsembe yopulumutsa.
Buledi asanduka Thupi
Ndiponso vinyo Magazi
A Khristu, Ambuye athu.
Sitimvetsa, sitiona,
Koma ndithu tizimvera
Zozizwitsa zimenezi.
Buledi ndinso vinyo ali
Chizindikiro chophimba
Zazikulu zobisika.
Tidya Thupi la Ambuye
Ndi kumwa Magazi ake:
Akhala muziwirizi.
Aliyense amlandira
Wathunthudi, wosasweka,
Ndi wosagawika konse.
Nayo Buledi wa anjelo
Ngwa alendofe tsopano
Manna wotipatsa nyonga.
Mulungu wamphamvuzonse
Ndiponso wodziwa zonse,
Inu mutidyetsa pano.
Mutidyetsenso Kumwamba
M’phwando la anthu oyera.
Amen. Amen. Aleluya.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 14: 12 – 16, 22 – 26. (Ili ndi thupi langa, awa ndi magazi anga).
Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, tsiku lomwe anthu ankapha mwanawankhosa wochitira mphwando la Pasaka, ophunzira a Yesu adamufunsa kuti, “kodi tikakukonzereni kuti malo okadyera phwando la Pasaka?” Yesu adatuma awiri mwa ophunzira ake, nawauza kuti., “pitani m’mudzimu. Mukumana ndi munthu wamwamuna atasenza mtsuko wa madzi. Mukamutsatire. Kunyumba kumene ati akalowe, mukauze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa kuti, kodi nchiti chipinda cha alendo choti Iwowo adzadyeremo phwando la Pasaka ndi ophunzira ao?’ Iyeyo akakuwonetsani chipinda chachikulu cham’mwamba, momwe akonzamo zonse zofunikira. M’menemo mukatikonzere chakudya.” Ophunzira aja adanyamuka nalowa mumzindamo. Adachipedzadi monga momwe Yesu adaawauzira, ndipo adakonza za phwando la Pasaka. Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagawira ophunzira aja, ndipo adati, “kwayani, ili ndi thupi langa.” Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu, nkuchipereka kwa ophunzirawo, naamwa onse. Ndipo adawauza kuti, “Awa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi amenewa ndiwakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka. Kunena zoona, sindidzamwanso chakumwa cha mtengo waphesachi, mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.” Tsono ataimba nyimbo yotamanda Mulungu, onse adatuluka nkumapita ku Phiri la Olivi.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, Ukaristia ukusonyeza umodzi wathu ndi Yesu Akhristu. Tiyeni pamodzi ndi lyeyo tiyamike Mulungu popempherera anthu onse:
1. Akhristu onse apeze m’sakramenti la Ukaristia gwero la moyo wa ungwiro, ndinso chifundo chokondana mwaubale, polumikizana ndi Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Makolo achikhristu adziwe kuphunzitsa bwino ana ao za Ambuye Yesu, ndipo autse m’mitima mwao chifundo chofunitsa kulandira Ukaristia.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Ansembe onse asenze udindo wao mokhulupirika ndi mwachangu, azionetsa chitsanzo chabwino kwa anthu ao powatsogolera m’njira ya ungwiro.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tomwe tili muno tikhale amodzi ndi okondana mwaubale pakulandira Ukaristia kawirikawiri.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate a chifundo, tikukuthokozani chifukwa chotiitana tonse ku phwando lanu, Inu amene mufuna kutisonkhanitsa tonse mu Ufumu wanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment