Saturday, May 25, 2024

CHAKA CHA UTATU WOYERA – CHAKA B

 

CHAKA CHA UTATU WOYERA – CHAKA B

“Ulemu ukhale kwa Atate ndi kwa Mwana ndi kwa Mzimu Woyera.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA DEUTERONOMO: DEUTERONOMO 04: 32 – 34, 39 – 40. (Chauta ndiye Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, palibe wina ai.)

 

Mose adauza anthu kuti: “Tafufuzani zakale, inu musanabadwe, kuyambira pa tsiku lija limene Mulungu adalenga munthu pa dziko lapansi. Tafufuzani pa dziko lonse lapansi. Kodi chachikulu chonga chimenechi chidachitikapo ndi kale lonse? Kodi alipo wina amene adamvapo zotere? Kodi alipo anthu ena amene adakhalabe ndi moyo, atamva mau a Mulungu ali m’moto, monga m’mene mudamvera inu? Kodi alipo mulungu wina aliyense amene adaapita kukadzitengera anthu kuwachotsa pakati pa fuko lina, nawasandutsa anthu akeake, monga muja Chauta, Mulungu wanu, adakuchitirani inu ku Ejipito kuja? Iye adachita zimenezi ndi mphamvu zake zazikulu, inu mukupenya. Adadzetsa miliri pamodzi ndi nkhondo, adachita zozizwitsa ndi zodabwitsa. Choncho dziwani ndipo musamaiwala kuti Chauta ndiye Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, palibe wina ai. Muzimvera malangizo ndi malamulo ake onse amene ndakupatsani lerowa. Mukatero, zinthu zidzakuyenderani bwino inuyo ndi zidzukulu zanu, ndipo mudzakhalitsa m’dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani kuti likhale lanu mpaka muyaya.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 33: 04 – 06, 09, 18 – 22.

 

Ngwodala anthu amene Mulungu awasankha kuti akhale akeake.

 

Mau a Chauta ndi olungama,

Zochita zake zonse amazichita mokhulupirika,

Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera,

Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.

 

Ngwodala anthu amene Mulungu awasankha kuti akhale akeake.

 

Chauta adalankhula ndipo zakumwamba zidalengedwa,

Zonse zakumeneko zidalengedwa,

Pamene Iye adalankhula mau ake,

Pakuti Iye adalankhula, ndipo zidachitikadi,

Adalamula, ndipo zidaonekadi.

 

Ngwodala anthu amene Mulungu awasankha kuti akhale akeake.

 

Chauta amayang’ana anthu omumvera,

Ndi odalira chikondi chake chosasinthika,

Iye amachita izi kuti awapulumutse ku imfa,

Ndi kuwasungira moyo anthuwo pa nthawi ya njala.

 

Ngwodala anthu amene Mulungu awasankha kuti akhale akeake.

 

Mitima yathu ikuyembekeza Chauta,

Chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu,

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika,

Chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

 

Ngwodala anthu amene Mulungu awasankha kuti akhale akeake.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A MKALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA 08: 14 – 17. (Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, timati, ‘Abba! Atate!’”)

 

Abale, onse amene Mzimu wa Mulungu amawatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu. Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, ‘Abba! Atate!’ Mzimu woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – CHIBVUMBULUTSO 01: 08.

Alleluia – Ulemu ukhale kwa Atate ndi Mwana ndi Mzimu Woyera, Mulungu amene alipo, amene analipo kale, amene alikudza. – Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 28: 16 – 20. (Muzikawabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera).

 

Ophunzira khumi ndi mmodzi aja adapita ku Galileya kuphiri kumene Yesu adaapangana nawo kuti akakumane. Pamene adamuwona, adampembedza, koma ena ankakayika. Yesu adadza pafupi nawauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano. Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukawasandutse ophunzira anga. Muzikawabatiza m’dzina ka Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Muzikawaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.


Abale, popeza kuti tidalandira Mzimu Woyera wotitsimikiza kuti ndife ana a Mulungu ndithu, tiyeni tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti atsire madalitso ao pa anthu onse:

 

1.     Atate otikonda, mulunzitse mitima ya akhristu onse kuti akhale amodzi kwenikweni, monga Inu muli amodzi, Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate Oyera, mukhazikitse chikondi chanu pakati pa mafuko onse a m’dziko lapansi pano, kuti ponseponse pakhale bata ndi mtendere.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate a ufulu wonse, mudalitse mabanja onse, kuti eniake akhale omvana ndi olemekezana, ndipo ana ao alandire chisamaliro chokwanira.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate okoma mtima, mutithandize ife amene tili muno kuti mkhalidwe wathu pakati pa anzathu usonyeze chifundo chanu chopanda malire.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Mulungu wathu, ndi mphamvu za Mzimu wanu Woyera, timakutchulani Atate; tikuyamikani chifukwa mumatipatsa zabwino moolowa manja kopitirira umo tingayembekezere. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...