CHAKA CHA PENTEKOSTE – CHAKA B
“Adawauzira mpweya wopatsa moyo.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 02: 01 – 11. (Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula).
Pamene tsiku la chikondwerero cha Pentekoste lidafika, iwo onse anali pamodzi m’nyumba imodzi. Mwadzidzidzi kudamveka kuchokera kumwamba mkokomo ngati wa mphepo yaukali, nudzaza nyumba yonse imene ankakhalamo. Ndipo adaona ngati timalawi ta moto tooneka ngati malilime tikugawikana nkukhala pa iwo, aliyense kakekake. Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankawalankhulitsira. Tsono, m’Yerusalemu muja munali Ayuda ena, anthu okonda Mulungu, ochokera ku maiko onse a pa dziko lapansi. Pamene mkokomo uja udamveka, anthu ambirimbiri adasonkhana. Onse adadodoma, chifukwa aliyense mwa iwo ankawamva akulankhula chilankhulo chake. Adadabwa, nathedwa nzeru ndipo adati, “kodi onse akulankhulawa, si Agalileya? Nanga bwanji aliyense mwa ife akuwamva akulankhula chilankhulo chakwawo? Ena mwa ife ndi Aparti ndi Amedi ndi Aelami, ena ndi okhala ku Mesapotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya, Ku Frijiya ndi ku Pamfiliya, ku Ejipito, ndi ku madera a Libiya kufupi ndi ku Kirene, ena ndi alendo ochokera ku Roma, ndiye kuti Ayuda ndi ena otsata za Chiyuda. Enanso ndi Akrete ndi Aarabu, komabe tonse tikuwamva anthuwa akulankhula m’zilankhulo zathu za ntchito zazikulu za Mulungu.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 104: 01, 24, 24, 29 – 31.
Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,
Inu Chauta, Mulungu wanga, ndinu aakulu kwambiri,
Inu Chauta ntchito zanu zambiri,
Ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu
Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
Mukazichotsera mpweya, zimafa nkubwerera ku fumbi,
Mukatumiza mpweya wanu zimalengedwa,
Ndipo mumakonzanso maonekedwe a dziko lapansi.
Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
Ulemerero wa Chauta ukhalebe mpaka muyaya,
Chauta akondwe nazo ntchito zakezo,
Mapemphero anga amkomere Chauta,
Popeza kuti ndimakondwa mwa Iye.
Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A MKALATA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 12: 03 – 07, 12 – 13. (Tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi).
Abale, munthu amene Mzimu Woyera samtsogolera, sanganene kuti, ‘Yesu ndi Ambuye.’ Tsonotu pali mphatso zamitundumitundu, koma wozipereka ndi Mzimu Woyera mmodzimodzi. Pali njira zosiyasiyana zotumikira, koma Ambuye amene timawatumikira ndi amodzimodzi. Pali mphamvu zosiyasiyana, koma Mulungu ndi mmodzimodzi amene amagwiritsa ntchito mphamvu zonsezo mwa munthu aliyense. Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakutiyakuti yoti aigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse. Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha. Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA PENTEKOSTE (SEQUENCE) [Nyimboyi itha kunenedwa kapena kuyimbidwa]
1. Bwerani Mzimu Woyera,
Tumizani kuwala kwanu,
Kufumira kumwambako.
2. Bwerani, Tate wa amphawi,
Bwerani, wopatsa mphatso,
Inu muuni wa mitima.
3. Ndinu Msangalatsi ndithu,
Woyendera mitima yathu,
Kuti mudzaithuzitsa.
4. Pa ntchito ndinu Mpumulo,
Mumatichotsera kutentha,
Ndi kutsangula misozi yathu.
5. Ndinu kuwala kokoma,
Dzazani mitima yathu,
Ya ife anthu okumverani.
6. Mutapanda kudzamthandiza,
Munthu sangapeze kanthu,
Zonse zidzamuipira.
7. Tsukani zoipa zathu,
Dzatsirireni zouma,
Chiritsani mabala athu.
8. Dzafewetseni zolimba,
Funditsani zozizira,
Lungamitsani zokhota.
9. Tipatseni anthu anufe,
Okhulupirira Inu,
Mphatso zisanu ndi ziwiri.
10. Kometsani makhalidwe athu,
Katifikitseni kumwamba,
Kukadala nthawi zonse,
Amen.
Alleluia – Bwerani Mzimu Woyera, mudzaze m’mitima ya anthu okhulupirira ndipo chikondi chanu chikhazikike mwa iwo. – Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MARKO YOHANE WOYERA: YOHANE 15: 26 – 27. 16: 12 – 15. (Nkhosweyo ndi Mzimu wa choona. Iyeyo akadzabwera, adzakuphunzitsani zoona zonse).
Yesu adawauza ophunzira aku kuti: “koma pali Nkhoswe imene ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate. Nkhosweyo ndi Mzimu wa choona wofumira mwa Atate. Iyeyo akadzabwera, adzandichitira umboni. Inunso mudzandichitira umboni, popeza kuti mwakhala nane kuyambira pa chiyambi. Ndili nawo mau ena ambiri oti ndikuuzeni, koma simungathe kuwamvetsa tsopano ai. Koma akadzafika Mzimu wodziwitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziwitsani zinthu zam’tsogolo. Adzandilemekeza, pakuti adzatenga zochokera kwa inu nadzakudziwitsani. Zonse za Atate nzanga. Nchifukwa chake ndanena kuti adzatenga zochokera kwa Ine, nadzakudziwitsani inu.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, Yesu adatiuza kuti, “Pemphani ndipo mudzalandira.” Lero tipemphe Ambuye kuti Mzimu Woyera atsike pa anthu onse okhala m’dziko lino lapansi.
1. Atate, mulimbitse Mpingo wanu ndi Mzimu wanu Woyera kuti ulalike Mthenga Wabwino wa Yesu Khristu mosaopa ndi mosakayika.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Atate, muongolere mitima ya akhristu onse ndi Mzimu wanu Woyera, kuti asanduke mboni zenizeni za Yesu Khristu pakati pa anthu anzao.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Atate, muunikire anthu onse ndi Mzimu wanu Woyera, kuti adziwe dzina lanu kuti ndinu Mulungu wachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Atate, mutipatse ife amene tili muno Mzimu Woyera, kuti alunzitse mitima yathu ndi kutikhazikitsa mu chikondi chanu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Mulungu wathu, tikupempha zimenezi mosakayika, osaopa kukutchulani Atate, chifukwa tidasanduka ana anu polandira Mzimu wanu Woyera. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment