Saturday, May 11, 2024

CHAKA CHA KUKWERA KWA AMBUYE YESU KUMWAMBA – CHAKA B.

CHAKA CHA KUKWERA KWA AMBUYE YESU KUMWAMBA – CHAKA B.

“Inetu ndili nanu masiku onse.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 01: 01 – 11. (Yesu adatengedwa kupita Kumwamba, iwo akupenya).

 

A Teofilo, m’buku langa loyamba lija ndidakulemberani za zonse zimene Yesu ankachita ndi kuphunzitsa kuyambira pa chiyambi, kufikira tsiku limene adatengedwa kupita kumwamba. Mwa mphamvu ya Mzimu Woyera, anali atauza atumwi amene adawasankha aja zoti iwowo adzachita. Iye ataphedwa, adadziwonetsa wamoyo kwa iwowo mwa njira zambiri zotsimikizika. Adawaonekera nalankhula nawo za ufumu wa Mulungu masiku makumi anai. Pamene anali nawo pamodzi, Yesu adawalamula kuti, “musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate adalonjeza, monga ndidaakuuzani. Pajatu Yohane ankabatiza ndi madzi, koma pasanapite masiku ambiri, inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.” Tsono atumwi aja atasonkhana, adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi ino ndiyo nthawi mukhazikitse ufumu mu Israele?” Iye adati, “si ntchito yanu kuti mudziwe nthawi imene kapena nyengo pamene zidzachitike zimene Atate adakhazikitsa mwa mphamvu yao. Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo inu mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.” Atanena zimenezi, Yesu adatengedwa kupita kumwamba, iwo akupenya. Ndipo mtambo udamlandira nkumubisa, iwo osamuwonanso. M’mene atumwi aja ankayang’ananitsitsabe kumwamba, Iye akupita, mwadzidzidzi anthu awiri ovala zoyera adaimirira pambali pao. Anthuwo adawafunsa kwatani mwangoti chilili pamenepa mukuyang’ana kumwamba? Yesuyo amene watengedwa kuchokera pakati panu kupita kumwamba, adzabweranso monga momwe mwamuwoneramu akupita kumwambako.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 47: 02 – 03, 06 – 09.

 

Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.

 

Ombani m’manja inu anthu a mitundu yonse,

Fuulani kwa Mulungu poimba nyimbo zachimwemwe,

Paja Chauta Wopambanazonse ndi woopsa,

Ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi.

 

Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.

 

Mulungu wakwera, anthu akumfuulira,

Chauta wakwera, akumuimbira lipenga,

Imbani nyimbo zotamanda Mulungu,

Imbani nyimbo zotamanda mfumu yathu.

 

Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.

 

Mulungu ndiye Mfumu ya dziko lonse lapansi,

Imbani mwaluso nyimbo zotamanda,

Mulungu amalamulira mitundu ya anthu,

Mulungu amakhala pa mpando wake woyera waufumu.

 

Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A MKALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO: AEFESO 01: 17 – 23. (Iye wakhala kudzanja lamanja la Atate).

 

Abale, ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziwe kwenikweni. Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m’mitima mwanu, kuti mudziwe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziwe kukula kwake kwa ulemelero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake. Ndiponso ndikufuna kuti mudziwe mphamvu yake yopitirira muyeso imene ikugwira ntchito mwa ife omkhulupirira. Mphamvuyi ndi yomwe ija yolimba koposa, imene Mulungu adaigwiritsa ntchito pamene adaukitsa Khristu kwa akufa, namkhazika pamwamba pa mafumu onse, aulamuliro onse ndi onse amene anthu angawatchule nthawi ino kapenanso nthawi ilikudza. Mulungu adagonyetsa zonse kuti zikhale pansi pa mapazi a Khristu, ndipo adamkhazika pamwamba pa zonse kuti akhale mutu wa Mpingo. Mpingowu ndi thupi la Khristu, ndipo ndi wodzazidwa ndi Khristuyo amene amadzaza zinthu zonse kotheratu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 28: 19a, 20b.

Alleluia – Pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukawasandutse ophunzira anga. Ndipo ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi. – Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 16: 15 – 20. (Yesu atalankhula nawo, adatengedwa kupita kumwamba, nakakhala ku dzanja lamanja la Mulungu).

 

Yesu adawonekera ophunzira ake ndipo adawauza kuti, “Pitani ku dziko lapansi, kalalikireni anthu onse Uthenga Wabwino. Amene akakhulupirire ndi kuwabatiza, adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira, adzaweruzidwa kuti ngwolakwa. Okhulupirira azidzachita zozizwitsa izi: azidzatulutsa mizimu yoipa potchula dzina langa, adzidzalankhula zilankhulo zachilendo, ndipo akagwira njoka kapena kumwa chakumwa chotha kuwapha, sadzapwetekedwa. Akasanjika manja pa anthu odwala, anthuwo azidzachira.” Ambuye Yesu atalankhula nawo, adatengedwa kupita Kumwamba, nakakhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Tsono ophunzira aja adanka nalalika ponseponse. Ambuye ankagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo ankatsimikiza mau ao ndi zozizwitsa zimene ankachita.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, podziwa kuti Yesu Khristu alikutinenera kwa Atate ake Kumwamba. tiyeni, tipemphere ndi mtima wodzaza ndi chikhulupiriro:

 

1.     Atate, mudzaze Mpingo wanu ndi Mzimu Woyera kuti usaleke kuunikira anthu a mafuko onse powalalikira Mthenga Wabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Atate, muitane anyamata ndi atsikana ambiri ku ntchito yofalitsa Mthenga wanu, ndipo muwalimbitse kuti akhale mboni zenizeni za Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Atate, mudalitse akhristu eni ake kuti alimbikire potukula moyo wa anthu ndipo asaope kusaukira anzao; adziwe kuti pakutero‚ alikumchitira Yesu umboni.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate, muyang’ane ndi maso achifundo onse amene akuvutika, muwapatse chikhulupiriro cholimba, adziwe kupirira mavuto mophathana ndi Mpulumutsi wao.
Tikupemphani, mutivomereze.

5.     Atate, ife tonse tili muno, mutithandize kugwirizana ndi Mwana wanu wokhala pakati pathu, kuti tidzetse Ufumu wake m’mitima ya anthu anzathu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, ndinu kasupe wa zabwino zonse, maso athu akuyang’ana Inu. Mverani mapemphero athu ndinso madandaulo a anthu onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...