Saturday, May 4, 2024

LAMULUNGU LA 06 MU NYENGO YA PASAKA– B

LAMULUNGU LA 06 MU NYENGO YA PASAKA– B.

“Mukondane monga momwe Ine ndakukonderani.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 10: 25 – 26, 34 – 35, 44 – 48. (Mzimu Woyera adawatsikira anthu onse amene ankamva mauwo).

 

Pamene Petro ankati azilowa, Kornelio adadzakumana naye, nadzigwetsa kumapazi kwake, namuweramira. Koma Petro adamuimiritsa nati, “iyayi, imirirani, inenso ndine munthu chabe.” Petro adayamba kuyankhula, adati, “zoonadi ndazindikira tsopano kuti Mulungu alibe tsankho. Amalandira bwino munthu wa mtundu uliwonse womuopa nkumachita chilungamo.” Petro akulankhulabe, Mzimu Woyera adawatsikira anthu onse amene ankamva mauwo. Ndipo okhulupirira achiyuda amene adaaperekeza Petro, adadabwa kuti Mulungu adapereka mphatso ya Mzimu Woyera ndi kwa anthu akunja omwe. Pakuti adawamva akulankhula zilankhulo zosadziwika ndi kutamanda ukulu wa Mulungu. Tsono Petro adati, “anthu awa alandira Mzimu Woyera monga ife. Nanga alipo amene angawaletse kubatizidwa ndi madzi?” Motero adalamula kuti abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu. Ndipo anthuwo adampempha kuti akhale nawo masiku angapo.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 98: 01 – 04.

 

Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo pamaso pa anthu a mitundu yonse.

 

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano,

Popeza kuti wachita zodabwitsa,

Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa.

 

Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo pamaso pa anthu a mitundu yonse.

 

Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo,

Waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse kuti Iye ndi wolungama,

Wakumbukira chikondi chake chosasinthika,

Ndi kukhulupirika kwa pa fuko la Israele.

 

Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo pamaso pa anthu a mitundu yonse.

 

Anthu aku mathero a dziko lonse lapansi,

Aona chipulumutso cha Mulungu wathu,

Fuulani Chauta ndi chimwemwe inu dziko lonse lapansi,

Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda.

 

Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo pamaso pa anthu a mitundu yonse.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A MKALATA YOYAMBA YA YOHANE WOYERA: 01 YOHANE: 04: 07 – 10 (Mulungu ndi wachikondi).

 

Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziwa Mulungu. Koma munthu wopanda chikondi sadziwa Mulungu, pakuti Mulungu ndiye chikondi chimene. Mulungu adaonetsa chikondi chake kwa ife motere: Iye nkukhala ndi mwana mmodzi yekha, koma adamtuma pansi pano, kuti mwa Iye tikhale ndi moyo. Chikondi chenicheni ndi ichi, chakuti sindife tidakonda Mulungu ai, koma Mulungu ndiye adatikonda ifeyo, natuma Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 14: 23.

Alleluia – Yesu adati, ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine, Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 15: 09 – 17 (Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake).

 

Yesu adauza ophunzira ake kuti, “monga momwe Atate andikondera, Inenso ndakukondani. Muzikhala m’chikondi changachi. Ngati mutsata malamulo anga, mudzakhala m’chikondi changa, monga momwe Ine ndatsatira malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala m’chikondi chao. Ndakuuzani zimenezi kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu. Lamulo langa ndi lakuti muzikondana monga momwe Ine ndakukonderani. Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene ndikulamulani. Sindikutchulanisno antchito ai, pakuti wantchito sadziwa zimene mbuye wake akuchita. Koma ndikukutchulani abwenzi, chifukwa zonse zimene ndidamva kwa Atate anga, ndidakudziwitsani. Si ndinutu mudandisankha Ine ai, koma ndine ndidakusankhani inu. Ndipo ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso zake zokhalitsa. Motero chilichonse chimene mungapemphe Atate potchula dzina langa, adzakupatsani. Choncho lamulo langa ndi lakuti muzikondana.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Yesu watiwuza kuti: “Ndinu abwenzi anga; chili chonse chimene mungapemphe m’dzina la Atate anga adzakupatsani.” Tiyeni tipempherere anthu onse adziko lapansi:

 

1.     Atate, mulunzitse mitima ya akhristu onse, kuti Mpingo ukhale chizindikiro chosonyeza chikondi chanu kwa anthu a mafuko onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate, mulimbitse anthu a m’zipani kuti kukondana kwawo kutionetseko moyo wodala umene tidzaupeze mu ufumu wanu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate, mukhazikitse chikondi choona m’mabanja onse, kuti ana aphunzire kwa makolo ao kuti ndinu okoma mtima kopambana.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate, ife tomwe tili muno mutikhalitse m’chikondi chanu, kuti m’khalidwe wathu pakati pa anzathu usonyeze kuti ndifedi abwenzi a Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, mverani mau athuwa kuti chimwemwe chanu chikhale mwa ife. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...