Saturday, April 27, 2024

LAMULUNGU LA 05 MU NYENGO YA PASAKA– B

LAMULUNGU LA 05 MU NYENGO YA PASAKA– B.

“Khalani mwa Ine, ndipo mudzabala zipatso zambiri.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 09: 26 – 31. (Barnabasi adawafotokozera za m’mene Saulo adaaonera Ambuye panjira paja.)

 

Saulo atafika ku Yerusalemu, adayesa kulowa m’gulu la ophunzira aja. Koma onse adachita naye mantha, osakhulupirira kuti nayenso ndi wophunzira. Pamenepo munthu wina, dzina lake Barnabasi, adamtenga napita naye kwa atumwi. Iye adawafotokozera za m’mene Saulo adaaonera Ambuye panjira paja, ndipo kuti Ambuye adalankhula naye. Adawasimbiranso za m’mene Saulo ku Damasiko ankalankhulira molimba mtima m’dzina la Yesu. Tsono Saulo adakhala nawo, nayendera Yerusalemu yense akulalika molimba mtima m’dzina la Ambuye. Ankalankhulanso ndi kumatsutsana ndi Ayuda olankhula Chigriki, koma iwowo ankafunafuna kumupha. Pamene abale adamva zimenezi, adaapita naye ku Kesareya namtumiza ku Tariso. Pamenepo Mpingo ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya unali pa Mtendere. Udakhazikika, ndipo anthu ochuluka adalowamo chifukwa anthu ankayenda mooopa Ambuye, ndipo Mzimu Woyera ankawalimbikitsa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO  21: 26 – 28, 30 – 32.

 

Inu, Chauta, ndidzakutamandani pa gulu la anthu.

 

Zimene ndidalonjeza ndidzachita pamaso pa onse okumverani,

Ozunzika adzadya ndi kukhuta,

Ofunafuna Chauta adzamtamanda,

Mitima yanu ikhale ndi moyo nthawi zonse.

 

Inu, Chauta, ndidzakutamandani pa gulu la anthu.

 

Anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi,

Adzakumbukira nadzatembenukira kwa Chauta,

Mabanja a mitundu ina ya anthu adzampembedza,

Pakuti ulamuliro ndi wake wa Chauta,

Iye amalamula anthu a mitundu yonse.

 

Inu, Chauta, ndidzakutamandani pa gulu la anthu.

 

Zidzukulu za m’tsogolo zidzatumikira Ambuye,

Anthu adzauza mbadwo umene ukudzawo za Iye,

Adzalalika za chipulumutso chake kwa anthu,

Amene mpaka tsopano sanabadwe.

 

Inu, Chauta, ndidzakutamandani pa gulu la anthu.

 

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A MKALATA YOYAMBA YA YOHANE WOYERA: 01 YOHANE: 03: 18 – 24. (Chimene Mulungu amalamula nchakuti: tizikhulupirira Mwana wake Yesu Khristu, ndipo kuti tizikondana monga Iye adatilamulira).

 

Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu. Apo tidzadziwa kuti tili pa choona, ndipo tidzakhala okhazikika mtima pamaso pa Mulungu nthawi zonse pamene mtima wathu ukutitsutsa kuti ndife olakwa. Paja Mulungu ndi wamkulu kopambana mtima wathu, ndipo amadziwa zonse. Inu okondedwa, ngati mtima wathu sutitsutsa, titha kuima mopanda mantha pamaso pa Mulungu. Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa. Chimene Mulungu amalamula nchakuti tizikhulupirira Mwana wake Yesu Khristu, ndipo kuti tizikondana monga Iye adatilamulira. Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timamdziwa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 15: 04a, 05b.

Alleluia – Khalani mwa Ine, ndipo Inenso ndidzakhala mwa inu. Munthu wokhala mwa Ine, amabereka zipatso zambiri. – Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 15: 01 – 08. (Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa Iye, amabereka zipatso zambiri).

 

Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndi mlimi. Iwo amadula nthambi iliyonse mwa Ine imene siibala zipatso. Ndipo nthambi iliyonse yobala zipatso, amaitengulira kuti ibale zipatso zambiri koposa kale. Inu mwayera kale chifukwa cha mau amene ndakuuzani. Khalani mwa Ine, ndipo Inenso ndidzakhala mwa inu. Nthambi siingathe kubala zipatso payokha ngati siikhala mwa inu. Nthambi siingathe kubala zipatso payokha ngati siikhala pa mtengo wake. Momwemonso inu ngati simukhala mwa Ine. Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu. Ngati munthu sakhala mwa Ine, amamtaya kunja monga nthambi yodulidwa, ndipo amauma. Nthambi zotere amazitola, naziponya pa moto ndipo zimapsa. Ngati mukhala mwa Ine, ndipo mau anga akhala mwa inu, mupemphe chilichonse chimene mungachifune, ndipo mudzachilandiradi. Atate anga amalemekezedwa pamene mubereka zipatso zambiri, ndipo pakutero mumaonetsa kuti ndinu ophunzira anga enieni.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pakuti Yesu amakhala mwa ife, tingathe kupempha chilichonse ndipo tidzachilandira. Tsono tiyeni, tipemphe Atate kuti agawireko anthu onse zaulere zowathandiza kupulumuka:

 

1.     Atate, mulimbitse chikhulupiriro cha atsogoleri a Mpingo kuti alalike Mthenga Wabwino wa Yesu Khristu mosaopa ndi mosakaika.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate, mulunzitse akhristu ogawikana m’mipingo yosiyanasiyana kuti asaleke kufunafuna umodzi uja umene Yesu adafunira Mpingo wake.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate, mulimbitse chikondi chanu m’mitima ya anthu anu okhala m’zipani, kuti abereke zipatso zambiri zokometsera Mpingo wanu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate, muwamvere chifundo ana anu osokera ndi ofooka, kuti alumikizanenso ndi Yesu Khristu ndi kuwonetsa zipatso za chilungamo.
Tikupemphani, mutivomereze.

5.     Atate, mutidalitse ife tonse tili muno, kuti chikondi chathu chiwonekere pa ntchito zabwino zotumikira anzathu.
Tikupemphani, mutivomereze.

Atate, mwa chifundo chanu, mverani mapemphero athuwa, ndipo mutikhalitse amodzi. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...