Saturday, April 20, 2024

LAMULUNGU LA 04 MU NYENGO YA PASAKA– B

LAMULUNGU LA 04 MU NYENGO YA PASAKA– B.

[LAMULUNGU LA MAITANIDWE – VOCATION SUNDAY]

“Yesu Ndiye Mbusa Wabwino wotiperekeza kwa Atate.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 04: 08 – 12. (Ili ndi dzanja lokhalo, limene lingatipulumutse).

 

Petro, atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, adawayankha kuti, “Inu atsogoleri ndi akuluakulu muli apa, kodi mukutifunsa ife lero za ntchito yabwino imene idachitika pa munthu wopunduka uja, ndi kuchira kwake? Mudziwetu tsono inu nonse, ndi Aisraele ena onse, kuti munthuyo akuima wamoyo pamaso panu chifukwa cha mphamvu ya dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete. Amene uja inu mudaampachika pa mtanda, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa. Za Yesuyo mau a Mulungu akuti, Mwala umene inu amisiri omanga nyumba mudaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya, wofunika koopsa. Ndipo palibe wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina limene Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 118: 01, 8 – 09, 21 – 23, 26 – 29.

 

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya.

 

Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino,

Ndipo chikondi chake nchamuyaya,

Kuthawira kwa Chauta nkwabwino,

Kupambana kukhulupirira munthu.

Kuthawira kwa Chauta nkwabwino,

Kupambana kukhulupirira mfumu.

 

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya.

 

Ndikuyamikani popeza kuti mwandiyankha,

Ndipo mwasanduka Mpulumutsi wanga,

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana,

Womwewo wasanduka mwala wapangodya,

Chauta ndiye amene wachita zimenezi,

Zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu.

 

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya.

 

Ngwodala amene alikudza m’dzina la Chauta,

Tikufunirani madalitso ochokera m’nyumba ya Chauta,

Inu ndinu Mulungu wanga ndidzakuthokozani,

Thokozani Chauta pakuti ngwabwino,

Ndipo chikondi chake chosasinthika nchamuyaya.

 

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A MKALATA YOYAMBA YA YOHANE WOYERA: 01 YOHANE: 01 – 02. (Tidzamuwona Mulungu monga momwe aliri).

 

Okondeka anga, onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziwa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziwe. Inu okondedwa, ndife ana a Mulungu tsopano. Mulungu sadatiwonetsebe chimene tidzakhale. Koma tikudziwa kuti Iye akadzaoneka, tidzakhala ofanafana naye, pakuti tidzamuwona monga momwe aliri.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 10: 14.

Alleluia – Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziwa, ndipo izozo Ineyo zimandidziwa. – Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 10: 11 – 18. (Mbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake).

 

Yesu adati, “Ine ndine Mbusa wabwino. Mbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake. Koma wolembedwa ntchito chabe akaona mmbulu ulikudza, amazisiya nkhosazo iye nkuthawa. Amatero popeza kuti si mbusa weniweni, ndipo nkhosa sizake ai. Tsono mmbulu uja umagwirapo zina, zina nkumwazikana. Wolembedwa ntchito uja amathawa, chifukwa amangotsata malipiro chabe, ndipo salabadirako za nkhosazo. Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziwa, ndipo izozo Ineyo zimandidziwa, monga momwe Atate amadziwira Ine, nanenso nkuwadziwa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo. Ndili nazo nkhosa zina zimene sizili za m’khola lino. Zimenezonso ndiyenera kuzikusa. Zidzamva mau anga, ndipo padzakhala gulu limodzi mbusa wakenso mmodzi. Nchifukwa chake Atate amandikonda, popeza kuti ndikupereka moyo wanga kuti ndikautengenso. Palibe munthu wondilanda moyo wangawu, koma ndikuupereka ndekha. Ndili nazo mphamvu zoutaya moyo wanga, ndili nazonso mphamvu zoutenganso. Udindo umenewo ndidaulandira kwa Atate anga.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, popeza kuti ndife ana a Mulungu ndithu, tingathe kupemphera mosaopa ndi mosakaika. Tsono tiyeni, tipemphe Mulungu Atate athu kuti atsire madalitso ake pa anthu onse:

 

1.     Atate, mulimbitse Apapa, Aepiskopi, Ansembe onse, kuti azitsogolera akhristu ao ndi kuwasamalira, asaope kutaya moyo wao chifukwa cha nkhosa zao.
Tikukupemphani, Mutivomereze.

2.     Atate muitane anyamata ndi atsikana ku ntchito yofalitsa Mthenga Wabwino, ndipo muwalimbikitse kuti akhale mboni zenizeni za Yesu Khristu.
Tikukupemphani, Mutivomereze.

3.     Atate, muunikire anthu akunja okhala m’maiko osiyanasiyana kuti nawonso amve Mthenga Wabwino ndi kukhulupirira Yesu Khristu Mpulumutsi wao.
Tikukupemphani, Mutivomereze.

4.     Atate mutithandize ife tomwe kuti tisenze mwachangu udindo wathu wachikhristu ndipo mayendedwe athu atsimikize kuti ndifedi anthu ake a Yesu Khristu.
Tikukupemphani, Mutivomereze.

 

Atate, tikudziwa kuti palibe dzina lina loti tipulumuke nalo: nchifukwa chake tikukupemphani zonsezi m’dzina la Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...