LAMULUNGU LA 03 MU NYENGO YA PASAKA– B.
“Yesu ndi nsembe yokhululukira machimo athu.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 03: 13 – 15, 17 – 19. (Mudapha wopatsa moyo, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa).
Petro adauza anthu kuti, “Inu Aisraele, Mulungu wa makolo athu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, adapereka ulemerero kwa Yesu, mtumiki wake. Inu mudampereka kwa adani ake ndi kumkana pamaso pa Pilato, pamene Pilatoyo adaatsimikiza kuti ammasula. Yesu anali woyera mtima ndi wolungama, koma inu mudamkana, ndipo m’malo mwake mudapempha kuti akumasulireni chigawenga. Mudapha Wopatsa moyo, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa. Ife ndife mboni za zimenezi. Ndiponso tsopano abale anga, ndikudziwa kuti inu ndi akuluakulu anu mudachita zimenezi mosadziwa. Koma Mulungu adaaneneratu mwa aneneri onse kuti wodzozedwa wake wolonjezedwa uja adzamva zowawa, ndipo zidachitikadi momwemo. Tsono tembenukani mtima ndi kubwera kwa Mulungu, kuti akufafanizireni machimo anu. Motero Ambuye adzakupatsani nthawi ya mpumulo.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 04: 02, 04, 07, 09.
Mutiyang’ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.
Ndikamaitana, mundiyankhe Inu Mulungu, Mtetezi wanga,
Mudabwera pamene ndinali m’mavuto,
Mundichitire chifundo, ndi kumvera pemphero langa.
Mutiyang’ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.
Koma tsono mudziwe kuti Chauta,
Wadzipatulira Iye yemwe anthu olungama,
Chauta amamva ndikamuitana.
Mutiyang’ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.
Ndani angatiwonetse zabwino?
Mutiyang’ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.
Mutiyang’ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.
Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere,
Pakuti Inu nokha Chauta,
Ndinu amene mumandisunga bwino lomwe.
Mutiyang’ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A MKALATA YOYAMBA YA YOHANE WOYERA: 01 YOHANE 02: 01 – 05. (Yesu Khristu ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati anthu okha, komanso a anthu a pa dziko lonse lapansi).
Inu ana anga, ndikukulemberani zimenezi kuti musamachimwa. Komabe wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, ndiye Yesu Khristu amene ali wolungama. Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo anthu, ndipo osati athu okha, komanso anthu a pa dziko lonse lapansi. Pakutsata malamulo a Mulungu, ndi pamene tingatsimikize kuti timamdziwa. Munthu akamati, Ine ndimadziwa Mulungu, koma chikhalirecho satsata malamulo ake, angonama ameneyo, ndipo mwa iye mulibe choona. Koma munthu akamasunga mau a Mulungu, pamenepo chikondi cha Mulungu chafikadi pake penipeni mwa iyeyo. Chotitsimikizitsa kuti tili mwa Iye, ndi chimenechi.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 24: 32.
Alleluia – Ambuye Yesu, mutithandize malembo. Mitima yathu iyake mwa ife pamene mumalankhula nafe. – Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 24: 35 – 48. (Zimene zidalembedwa ndi izi: zakuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adayenera kumva zowawa, nkuuka kwa akufa Patapita masiku atatu).
Ophunzira awiri aja adafotokoza zimene zidaachitika panjira, ndiponso m’mene iwo adaamzindikira pamene Iye ankanyema buledi. Iwo akulankhula choncho, Yesu mwiniwake adadzaimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu.” Koma iwo adadzidzimuka, nkuchita mantha poyesa kuti akuwona mzukwa. Tsono Yesu adati, “mukuvutikiranji, mukudzipheranji ndi mafunso a m’mitima mwanu? Onani manja anga ndi mapazi anga, kuti ndine ndithu. Khudzeni muwone, paja mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuwona kuti Ine ndili nazo.” Atanena zimenezi adawaonetsa manja ake ndi mapazi ake. Iwo sankakhulupirirabe chifukwa cha chimwemwe, ndipo adaathedwa nzeru. Tsono Yesu adawafunsa kuti, “kodi pano muli nako kanthu kakudya?” Adampatsa chidutsu cha nsomba yootcha. Iye atalandira nsombayo, adaidya iwo akuwona. Kenaka adawauza kuti, “nzimenezitu zimene ndinkakuuzani pamene ndinali nanu. Paja ndinkanena kuti zonse ziyenera kuchitikadi zimene zidalembedwa za Ine m’Malamulo a Mose, m’mabuku a aneneri, ndi m’buku la Masalimo.” Tsono adawathandiza kuti amvetse bwino Malembo. Adawauza kuti, “zimene zidalembedwa ndi izi: zakuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adayenera kumva zowawa, nkuuka kwa akufa patapita masiku atatu, kuti m’dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu awakhululukire machimo ao. Inuyo ndinu mboni zake za zimenezi.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale pakuti tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, imene ili Yesu Khristu, tingathe kupempha kwa Atate mosakaika zabwino zonse zotisowa:
1. Akhristu onse amutsire Yesu Khristu umboni pakuyenda m’chikondi chake ndi kusunga malamulo ake.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Anthu amafuko onse atembenukire kwa Mulungu ndi mtima wolapa pokhulupirira chifundo chake chofuna kuwapulumutsa.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu odwala onse ndi onse amene ali otaya mtima alandire chisangalatso panthawi ino ya Pasaka.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife amene tili muno tikhale nawo mtima wokonda kuwerenga mawu a m’Malembo Oyera, kuti tipezemo mphamvu zolimba pa moyo wathu wa chikhristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, tikukuyamikani chifukwa mwa Mwana wanu Yesu Khristu mumatikhululukira mobwerezabwereza, kuti tiziyenda pamaso panu ndi mtima womasuka ndi kukhazikika m’chikondi chanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment