LAMULUNGU LA CHIWIRI MU NYENGO YA PASAKA
(LAMULUNGU LA CHIFUNDO CHA MULUNGU)
“Iwo adakondwa kwambiri poona Ambuye.”
MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 04: 32 – 35. (Gulu lonse la okhulupirira linali la mtima umodzi, ndi la maganizo amodzi).
Gulu lonse la okhulupirira linali la mtima umodzi, ndi la maganizo amodzi. Panalibe munthu amene ankati, “zimene ndili nazo nzangazanga,” koma aliyense ankapereka zake zonse kuti zikhale za onse. Atumwi ankachita umboni ndi mphamvu yaikulu kuti Ambuye Yesu adaukadi kwa akufa, ndipo onse Mulungu ankawakomera mtima kwambiri. Panalibe munthu wosowa kanthu pakati pao, chifukwa onse amene anali ndi minda kapena nyumba, ankazigulitsa, namabwera ndi ndalama zake kudzazipereka kwa atumwi. Ndipo ndalamazo ankagawira munthu aliyense malinga ndi kusowa kwake.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 118: 02 – 04, 15 – 18, 22 – 24.
Tamandani Chauta Pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.
Aisraele anene kuti,
“Chikondi chake nchamuyaya.
Banja la Aroni linene kuti,
Chikondi chake nchamuyaya.
Anthu oopa Chauta anene kuti,
Chikondi chake nchamuyaya.
Tamandani Chauta Pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.
Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu,
Dzanja lamanja la Chauta lapambana,
Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu.”
Sindidzafa, ndidzakhala moyo,
Ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta.
Chauta wandilanga koopsa, koma sadandisiye kuti ndife.
Tamandani Chauta Pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.
Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana
Womwewo wasanduka mwala wapangodya.
Chauta ndiye amene wachita zimenezi,
Zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga.
Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Tamandani Chauta Pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A MKALATA YOYAMBA YA YOHANE WOYERA: 01 YOHANE 05: 01 – 06. (Aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi).
Okondeka anga, munthu aliyense wokhulupirira kuti Yesu ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, iyeyo ndi mwana wa Mulungu. Ndipo aliyense wokonda nakubala, amakonda ndi mwana wake yemwe. Chodziwira kuti timakonda ana a Mulungu nchakuti timakonda Mulungu ndi kutsata malamulo ake. Paja kukonda Mulungu ndiye kuti kutsata malamulo ake, ndipo malamulo ake si olemetsa. Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu. Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Amaligonjetsa si wina ai, koma okhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu. Yesu Khristu ndiye amene adabwera kudzera mwa madzi ndi mwa magazi omwe. Ndipo Mzimu Woyera ndiye amene amachitirapo umboni, pakuti Mzimuyo ndiye choona.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 20: 29.
Alleluia – Yesu adati, wakhulupirira chifukwa wandiona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone. – Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 20: 19 – 31. (Patapita masiku asanu ndi atatu, Yesu adabwera).
Madzulo kutada pa tsiku Lamulungu lomwelo, ophunzira aja anali pamodzi. Zitseko zinali zokhoma, chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Tsono Yesu adadza naimirira pakati pao nkunena kuti, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adawaonetsa manja ake ndi m’nthiti mwake, ndipo ophunzira aja adakondwa kwambiri powaona Ambuyewo. Yesu adatinso, mmodzi mwa ophunzira aja khumi ndi awiri, Tomasi (wotchedwa Didimo), sanali pamodzi ndi anzake pamene Yesu adabwera. Tsono ophunzira anzake aja adamuuza kuti, “ife tawaonatu Ambuye.” Koma Tomasi adati, “ndikapapanda kuwona mabala a misomali m’manja mwao, ndi kupisa chala changa m’mabala a misomaliwo, ndipo ndikapanda kupisa dzanja langa m’nthiti mwao, sindingakhulupirire konse.” Patapita masiku ndi atatu, ophunzira aja analinso m’nyumbamo, ndipo Tomasi anali nawo. Zitseko zinali chikhomere, koma Yesu adadza, naimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adauza Tomasi kuti, “ika chala chako apa, ona manja anga. Tambalitsa dzanja lako, ulipise m’nthiti mwangamu. Leka kukayika, uyambepo kukhulupirira.” Tomasi adati, “Ambuye anga! Mulungu wanga!” Yesu adati, “kodi wakhulupirira chifukwa wandiwona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone.” Yesu adachitanso zizindikiro zina zambiri zozizwitsa pamaso pa ophunzira ake, zimene sizidalembedwe m’buku muno. Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, ndipo kuti pakukhulupirira mukhale ndi moyo m’dzina lake.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, pakuti Yesu Khristu waimirira pakati pathu, tiyeni, pamodzi naye, tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti apitirize ntchito zake zopulumutsa anthu onse:
1. Mzimu Woyera alimbitse chikhulupiriro m’mitima ya akhristu, ndipo awalumikize onse pamodzi m’chikondi choona.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Anthu a mafuko onse akhale ogwirizana mwaubale, ndipo a m’maiko okwera ayesetse kuthandiza anzao a m’maiko ena, pakuwagawirako chuma chao.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Akatekumeni alimbikire pa maphunziro ao, pozindikira kuwala kwa Yesu Khristu kowatsogolera ku moyo wosatha.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse tikhale a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi, monga akhristu oyamba aja, makamaka pakuthandiza anzathu amene ali m’mavuto.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, tikukuyamikani, chifukwa poukitsa Mwana wanu kwa akufa, mudatitsimikizira chifundo chanu chotipulumutsa. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment